Yesaya
7 Tsopano mʼmasiku a Ahazi+ mwana wa Yotamu mwana wa Uziya mfumu ya Yuda, Rezini mfumu ya Siriya ndi Peka+ mwana wa Remaliya mfumu ya Isiraeli, anapita kukamenyana ndi anthu amumzinda wa Yerusalemu koma analephera kulanda mzindawo.+ 2 Ndiyeno kunyumba ya Davide kunapita uthenga wakuti: “Dziko la Siriya lachita mgwirizano ndi dziko la Efuraimu.”
Choncho mtima wa Ahazi ndi wa anthu ake unayamba kunjenjemera, ngati mitengo ya mʼnkhalango imene ikugwedezeka ndi mphepo.
3 Kenako Yehova anauza Yesaya kuti: “Pita ukakumane ndi Ahazi. Upite ndi mwana wako Seari-yasubu.*+ Ukakumane naye kumapeto kwa ngalande yochokera kudziwe lakumtunda,+ mʼmphepete mwa msewu waukulu wopita kumalo a wochapa zovala. 4 Ukamuuze kuti, ‘Mtima wako ukhale mʼmalo. Usachite mantha ndipo usataye mtima chifukwa cha zitsa ziwirizi zimene zikungofuka utsi, chifukwa cha mkwiyo waukulu wa Rezini mfumu ya Siriya ndiponso mkwiyo wa mwana wa Remaliya.+ 5 Chifukwa Siriya ndi Efuraimu ndiponso mwana wa Remaliya akukonzera zoipa ndipo anena kuti: 6 “Tiyeni tikamenyane ndi dziko la Yuda ndipo tikalisakaze. Tikaligonjetse* nʼkulilanda ndipo tikaike mwana wa Tabeeli kuti akhale mfumu yake.”+
7 Koma Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti:
“Zimenezo sizitheka,
Ndipo sizichitika.
8 Chifukwa likulu la Siriya ndi Damasiko,
Ndipo mfumu ya Damasiko ndi Rezini.
Zaka 65 zisanathe,
Efuraimu adzakhala ataphwanyidwaphwanyidwa ndipo sadzakhalanso mtundu wa anthu.+
Mukapanda kukhala ndi chikhulupiriro cholimba,
Mukhala osatetezeka.”’”
10 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Ahazi kuti: 11 “Pempha chizindikiro kwa Yehova Mulungu wako.+ Chikhoza kukhala chozama ngati Manda* kapena chachitali ngati kumwamba.” 12 Koma Ahazi anati: “Sindipempha ndipo sindimuyesa Yehova.”
13 Kenako Yesaya ananena kuti: “Tamverani inu a mʼnyumba ya Davide. Kodi zimene mukuchita poyesa kuleza mtima kwa anthu nʼzosakwanira kwa inu? Kodi mukufunanso kuyesa kuleza mtima kwa Mulungu?+ 14 Choncho Yehova akupatsani chizindikiro: Tamverani! Mtsikana* adzakhala woyembekezera ndipo adzabereka mwana wamwamuna.+ Mwanayo adzamʼpatsa dzina lakuti Emanueli.*+ 15 Iye azidzadya bata* ndi uchi pamene azidzafika nthawi imene adzadziwe kukana choipa ndi kusankha chabwino. 16 Mwanayo asanafike podziwa kukana choipa ndi kusankha chabwino, mayiko a mafumu awiri amene ukuchita nawo manthawo, adzakhala atasiyidwiratu.+ 17 Yehova adzabweretsera iweyo, anthu ako komanso nyumba ya bambo ako nthawi yovuta imene sinakhaleponso kuyambira tsiku limene Efuraimu anapatukana ndi Yuda.+ Iye adzakubweretserani mfumu ya Asuri.+
18 Pa tsiku limenelo, Yehova adzaimbira likhweru ntchentche zimene zili mʼmitsinje ingʼonoingʼono yakutali yotuluka mumtsinje wa Nailo ku Iguputo komanso njuchi zimene zili mʼdziko la Asuri. 19 Ndipo zonse zidzabwera nʼkudzatera mʼzigwa zokhala* ndi maphompho, mʼmingʼalu ya mʼmatanthwe, pazitsamba zonse zaminga ndiponso mʼmalo onse omwetserapo ziweto.
20 Pa tsiku limenelo Yehova adzakumetani tsitsi la kumutu ndi tsitsi la mʼmiyendo pogwiritsira ntchito lezala lobwereka la kuchigawo cha ku Mtsinje,* pogwiritsira ntchito mfumu ya Asuri,+ ndipo lezalalo lidzametanso ndevu zanu.
21 Pa tsiku limenelo munthu adzasiya ngʼombe yaingʼono ndiponso nkhosa ziwiri zili zamoyo. 22 Chifukwa cha kuchuluka kwa mkaka, iye azidzadya bata, chifukwa bata ndi uchi nʼzimene munthu aliyense wotsala mʼdzikolo azidzadya.
23 Tsiku limenelo, pamalo alionse pamene panali mitengo ya mpesa 1,000, yokwana ndalama zasiliva 1,000, padzangokhala zitsamba zaminga ndi udzu. 24 Anthu azidzapita kumeneko atanyamula mivi ndi mauta, chifukwa mʼdziko lonselo mudzamera zitsamba zaminga ndi udzu. 25 Ndipo mʼmapiri onse amene anthu ankalambulako ndi makasu, sudzapitakonso chifukwa choopa zitsamba zaminga ndi udzu. Malowo adzakhala odyetserako ngʼombe zamphongo ndiponso oti nkhosa zizipondapondapo.”