Yesaya
17 Uwu ndi uthenga wokhudza Damasiko:+
“Taonani! Damasiko sadzakhalanso mzinda,
Adzawonongedwa nʼkukhala mabwinja okhaokha.+
2 Mizinda ya Aroweri+ idzasiyidwa.
Idzasanduka malo amene ziweto zimagona
Popanda aliyense woziopseza.
3 Mu Efuraimu simudzakhalanso mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri+
Ndipo mu Damasiko simudzakhalanso ufumu.+
Anthu amene adzatsale mu Siriya
Adzakhala ngati ulemerero wa Aisiraeli,”* akutero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.
4 “Pa tsiku limenelo, ulemerero wa Yakobo udzachepa,
Ndipo thupi lake lonenepa lidzaonda.
5 Zidzakhala ngati zimene zimachitika wokolola akamadula tirigu mʼmunda
Komanso dzanja lake likamakolola ngala za tirigu.
Zidzakhala ngati mmene zimakhalira munthu akamakunkha tirigu mʼchigwa cha Arefai.+
6 Mʼdzikomo mudzangotsala zokunkha zokha
Ngati mmene zimatsalira mumtengo wa maolivi akaugwedeza:
Panthambi imene ili pamwamba kwambiri pamangotsala maolivi awiri kapena atatu okha akupsa.
Panthambi zake zobala zipatso pamangotsala maolivi 4 kapena 5 okha,”+ akutero Yehova, Mulungu wa Isiraeli.
7 Tsiku limenelo, munthu adzayangʼana kumwamba, kwa amene anamupanga ndipo maso ake adzayangʼanitsitsa Woyera wa Isiraeli. 8 Iye sadzayangʼana maguwa a nsembe,+ omwe ndi ntchito ya manja ake.+ Sadzayangʼanitsitsa zinthu zimene zala zake zinapanga, kaya ndi mizati yopatulika* kapena maguwa ofukizirapo zonunkhira.
9 Tsiku limenelo mizinda yake yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri idzakhala ngati malo amene angosiyidwa mʼnkhalango.+
Idzakhala ngati nthambi imene anthu anangoisiya chifukwa cha Aisiraeli,
Ndipo idzakhala chipululu.
11 Masana umamanga mpanda bwinobwino kuzungulira munda wakowo,
Ndipo mʼmawa umachititsa kuti mbewu yako iphuke.
Koma zokolola zake zidzasowa pa tsiku la matenda ndi ululu wosachiritsika.+
12 Tamverani! Kuli chipwirikiti cha anthu ambirimbiri,
Amene akuchita mkokomo ngati nyanja.
Mitundu ya anthu ikuchita chipolowe,
Ndipo phokoso lawo lili ngati mkokomo wa madzi amphamvu.
13 Mitundu ya anthu idzachita phokoso ngati mkokomo wa madzi ambiri.
Iye adzawadzudzula ndipo iwo adzathawira kutali.
Adzathamangitsidwa ngati mankhusu* ouluzika ndi mphepo mʼmapiri
Ndiponso ngati udzu wouma wouluzika ndi mphepo yamkuntho.
14 Madzulo kudzakhala zoopsa.
Kusanache, adaniwo kudzakhala kulibe.
Izi nʼzimene zidzachitikire anthu amene akutilanda zinthu zathu
Ndipo ndi cholowa cha anthu amene akuba katundu wathu.