Hoseya
8 “Ika lipenga la nyanga ya nkhosa pakamwa pako.+
Mdani akubwera ngati chiwombankhanga kudzaukira nyumba ya Yehova.+
Chifukwa Aisiraeli aphwanya pangano langa+ ndiponso sanatsatire malamulo anga.+
2 Iwo akundilirira kuti, ‘Inu Mulungu wathu, ife Aisiraeli tikukudziwani!’+
3 Aisiraeli akana kuchita zabwino,+
Choncho mdani awathamangitse.
4 Iwo asankha mafumu, koma osati mwa kufuna kwanga.
Asankha akalonga, popanda ine kuvomereza.
5 Iwe Samariya, fano lako la mwana wa ngʼombe lakanidwa.+
Ndakwiyira kwambiri anthu ako.+
Kodi iwo adzalephera kukhala osalakwa mpaka liti?
6 Zimenezi zachokera ku Isiraeli.
Mmisiri ndi amene anapanga fano limeneli, ndipo fanoli si Mulungu.
Fano la ku Samariya lidzangokhala ngati nkhuni zowazawaza.
Mbewu zawo sizidzakula mpaka kukhwima.+
Ndipo zimene zidzakule, sizidzawapatsa ufa.
Ngati zina zingabereke, alendo adzazimeza.+
Moti adzakhala pakati pa anthu a mitundu ina,+
Ngati chiwiya chosafunika.
9 Iwo akafika mpaka kudziko la Asuri+ ngati bulu wamʼtchire.
Efuraimu walipira akazi kuti azigona nawo.+
10 Ngakhale kuti akulipira akazi a mitundu ina,
Ine ndidzawasonkhanitsa pamodzi.
Adzayamba kuvutika+ chifukwa choponderezedwa ndi mafumu ndiponso akalonga.
11 Efuraimu wapanga maguwa ansembe ambiri ndipo wachimwa.+
Akugwiritsa ntchito maguwa akewa kuti azichimwa.+
Tsopano ndidzakumbukira zolakwa zawo ndipo ndidzawalanga chifukwa cha machimo awo.+
14 Isiraeli anaiwala amene anamupanga+ ndipo wamanga akachisi.+
Yuda nayenso wamanga mizinda yambiri yokhala ndi mipanda yolimba.+
Koma ine ndidzatumiza moto mʼmizinda yake
Ndipo udzawotcha nsanja zamumzinda uliwonse.”+