Numeri
33 Awa ndi malo amene Aisiraeli ankaima pa ulendo wawo, atatuluka mʼdziko la Iguputo+ mʼmagulu awo*+ motsogoleredwa ndi Mose komanso Aroni.+ 2 Mose ankalemba malo amene ankanyamukira ulendo uliwonse mogwirizana ndi zimene Yehova anamulamula. Awa ndi maulendo amene anayenda kuchokera kumalo ena kukafika kumalo ena:+ 3 Ananyamuka ku Ramese+ mʼmwezi woyamba, pa tsiku la 15.+ Tsiku lotsatira atachita Pasika,+ Aisiraeli ananyamuka molimba mtima* pamaso pa Aiguputo onse. 4 Pa nthawiyi nʼkuti Aiguputo ali pa ntchito yoika mʼmanda ana onse oyamba kubadwa,+ amene Yehova anawapha pakati pawo. Yehovayo anali atapereka ziweruzo pa milungu yawo.+
5 Ndiyeno Aisiraeli ananyamuka ku Ramese nʼkukamanga msasa ku Sukoti.+ 6 Kenako ananyamuka ku Sukoti nʼkukamanga msasa ku Etamu,+ pafupi ndi chipululu. 7 Atanyamuka ku Etamu anabwerera mʼmbuyo kulowera ku Pihahiroti amene anali moyangʼanizana ndi Baala-zefoni.+ Ndipo anakamanga msasa pafupi ndi Migidoli.+ 8 Pambuyo pake ananyamuka ku Pihahiroti, nʼkukadutsa panyanja+ kuwolokera kuchipululu.+ Anayenda ulendo wamasiku atatu mʼchipululu cha Etamu,+ nʼkukamanga msasa ku Mara.+
9 Kenako ananyamuka ku Mara nʼkukafika ku Elimu. Ku Elimuko kunali akasupe 12 a madzi komanso mitengo 70 ya kanjedza, ndipo anamanga msasa kumeneko.+ 10 Atachoka ku Elimu, anakamanga msasa pafupi ndi Nyanja Yofiira. 11 Atanyamuka ku Nyanja Yofiira, anakamanga msasa mʼchipululu cha Sini.+ 12 Kenako ananyamuka mʼchipululu cha Sini, nʼkukamanga msasa ku Dofika. 13 Atachoka ku Dofika, anakamanga msasa ku Alusi. 14 Atanyamuka ku Alusi, anakamanga msasa ku Refidimu,+ kumene kunalibe madzi oti anthu amwe. 15 Pambuyo pake anachoka ku Refidimu nʼkukamanga msasa mʼchipululu cha Sinai.+
16 Kenako ananyamuka mʼchipululu cha Sinai, nʼkukamanga msasa ku Kibiroti-hatava.+ 17 Atachoka ku Kibiroti-hatava, anakamanga msasa ku Hazeroti.+ 18 Pambuyo pake ananyamuka ku Hazeroti nʼkukamanga msasa ku Ritima. 19 Atachoka ku Ritima anakamanga msasa ku Rimoni-perezi. 20 Atanyamuka ku Rimoni-perezi, anakamanga msasa ku Libina. 21 Kenako anachoka ku Libina nʼkukamanga msasa ku Risa. 22 Atanyamuka ku Risa, anakamanga msasa ku Kehelata. 23 Atachoka ku Kehelata, anakamanga msasa kuphiri la Saferi.
24 Pambuyo pake ananyamuka kuphiri la Saferi, nʼkukamanga msasa ku Harada. 25 Atachoka ku Harada, anakamanga msasa ku Makeloti. 26 Atanyamuka+ ku Makeloti, anakamanga msasa ku Tahati. 27 Atachoka ku Tahati, anakamanga msasa ku Tera. 28 Kenako ananyamuka ku Tera nʼkukamanga msasa ku Mitika. 29 Pambuyo pake anachoka ku Mitika nʼkukamanga msasa ku Hasimona. 30 Atanyamuka ku Hasimona anakamanga msasa ku Mosera. 31 Kenako ananyamuka ku Mosera nʼkukamanga msasa ku Bene-yaakana.+ 32 Atachoka ku Bene-yaakana anakamanga msasa ku Hori-hagidigadi. 33 Atanyamuka ku Hori-hagidigadi anakamanga msasa ku Yotibata.+ 34 Pambuyo pake ananyamuka ku Yotibata nʼkukamanga msasa ku Abirona. 35 Kenako anachoka ku Abirona nʼkukamanga msasa ku Ezioni-geberi.+ 36 Atanyamuka ku Ezioni-geberi anakamanga msasa mʼchipululu cha Zini,+ ku Kadesi.
37 Pambuyo pake ananyamuka ku Kadesi, nʼkukamanga msasa kuphiri la Hora,+ kumalire ndi dziko la Edomu. 38 Wansembe Aroni anakwera mʼphiri la Hora mogwirizana ndi zimene Yehova analamula, ndipo anamwalira mʼphirimo mʼchaka cha 40 mʼmwezi wa 5 pa tsiku loyamba la mweziwo kuchokera pamene Aisiraeli anatuluka mʼdziko la Iguputo.+ 39 Aroni anamwalira mʼphiri la Hora ali ndi zaka 123.
40 Tsopano mfumu ya ku Aradi+ ya Chikanani, imene inkakhala ku Negebu mʼdziko la Kanani, inamva kuti Aisiraeli akubwera.
41 Patapita nthawi Aisiraeli ananyamuka kuphiri la Hora,+ nʼkukamanga msasa ku Tsalimona. 42 Pambuyo pake anachoka ku Tsalimona, nʼkukamanga msasa ku Punoni. 43 Kenako ananyamuka ku Punoni nʼkukamanga msasa ku Oboti.+ 44 Atachoka ku Oboti anakamanga msasa ku Iye-abarimu, kumalire ndi Mowabu.+ 45 Kenako ananyamuka ku Iyimu* nʼkukamanga msasa ku Diboni-gadi.+ 46 Pambuyo pake ananyamuka ku Diboni-gadi, nʼkukamanga msasa ku Alimoni-dibilataimu. 47 Kenako ananyamuka ku Alimoni-dibilataimu, nʼkukamanga msasa kumapiri a Abarimu,+ pafupi ndi Nebo.+ 48 Potsirizira pake ananyamuka kumapiri a Abarimu nʼkukamanga msasa ku Yeriko, pafupi ndi mtsinje wa Yorodano, mʼchipululu cha Mowabu.+ 49 Anapitiriza kukhala mumsasa pafupi ndi Yorodano, kuyambira ku Beti-yesimoti mpaka ku Abele-sitimu,+ mʼchipululu cha Mowabu.
50 Yehova analankhula ndi Mose ku Yeriko, pafupi ndi mtsinje wa Yorodano, mʼchipululu cha Mowabu. Anamuuza kuti: 51 “Lankhula ndi Aisiraeli, uwauze kuti, ‘Tsopano muwoloka Yorodano kuti mulowe mʼdziko la Kanani.+ 52 Mukathamangitse anthu onse amene akukhala mʼdzikolo, ndipo mukawononge zifaniziro zawo zonse zamiyala+ ndi mafano awo onse achitsulo*+ komanso mukagwetse malo awo onse opatulika.+ 53 Mukalande dzikolo kuti muzikakhalamo, chifukwa ndidzalipereka ndithu kwa inu kuti likhale lanu.+ 54 Mukagwiritse ntchito maere+ pogawa dzikolo kwa mabanja anu kuti likhale cholowa chanu. Banja la anthu ambiri mukaliwonjezere cholowa chawo, ndipo banja la anthu ochepa mukalichepetsere cholowa chawo.+ Banja lililonse mukalipatse cholowa mogwirizana ndi kumene maere a banjalo agwera. Mukalandira malo kuti akhale cholowa chanu potsata mafuko a makolo anu.+
55 Koma ngati simukathamangitsa anthu amene akukhala mʼdzikolo,+ anthu amene mukawasiyewo adzakhala ngati zitsotso mʼmaso mwanu, ndiponso ngati minga yokubayani mʼnthiti mwanu. Ndipo iwo azidzakuvutitsani mʼdziko limene muzidzakhala.+ 56 Zikadzatero, chilango chimene ndimafuna kupereka kwa anthuwo ndidzachipereka kwa inu.’”+