Genesis
38 Pa nthawi imeneyi, Yuda anasiyana ndi abale ake, ndipo anakamanga tenti yake pafupi ndi munthu wina wa Chiadulamu, dzina lake Hira. 2 Kumeneko Yuda anaona mwana wamkazi wa munthu wina wa Chikanani+ ndipo anamukwatira. Munthuyo dzina lake anali Sua. 3 Mkaziyo anakhala woyembekezera. Kenako, anabereka mwana wamwamuna, ndipo Yuda anamupatsa dzina lakuti Ere.+ 4 Anakhalanso woyembekezera nʼkubereka mwana wamwamuna ndipo anamupatsa dzina lakuti Onani. 5 Anaberekanso mwana wina wamwamuna nʼkumupatsa dzina lakuti Shela. Pa nthawi imene mwanayu ankabadwa, Yuda anali ku Akizibu.+
6 Patapita nthawi, Yuda anatengera mkazi Ere, mwana wake woyamba. Mkaziyo dzina lake anali Tamara.+ 7 Koma makhalidwe a Ere, mwana woyamba wa Yuda, sanasangalatse Yehova ndipo Yehova anamupha. 8 Yuda ataona zimenezi anauza Onani kuti: “Gona ndi mkazi wa mchimwene wako ndipo ulowe chokolo,* kuti umuberekere ana mchimwene wako.”+ 9 Koma Onani anadziwa kuti anawo sadzakhala ake.+ Choncho, nthawi zonse akagona ndi mkazi wa mʼbale wakeyo, ankataya pansi umuna wake kuti asamuberekere ana mʼbale wakeyo.+ 10 Zimene ankachitazo zinali zoipa pamaso pa Yehova, choncho nayenso anamupha.+ 11 Yuda anauza Tamara mpongozi wake kuti: “Pita kunyumba kwa bambo ako, ukakhale kumeneko monga mkazi wamasiye kufikira Shela mwana wanga wamwamuna atakula.” Anatero chifukwa mumtima mwake anati: “Nayenso Shela angamwalire ngati abale ake aja.”+ Choncho Tamara anapita kukakhala kunyumba kwa bambo ake.
12 Patapita nthawi, mkazi wa Yuda, yemwe anali mwana wa Sua,+ anamwalira. Nthawi yolira maliro itatha Yuda anapita ku Timuna,+ kumene anyamata ake ankameta ubweya wa nkhosa zake. Anapita ndi mnzake Hira wa Chiadulamu uja.+ 13 Ndiye munthu wina anauza Tamara kuti: “Apongozi ako akupita ku Timuna kukameta nkhosa zawo.” 14 Tamara atamva zimenezo, anavula zovala zake zaumasiye nʼkufunda nsalu. Kenako anaphimba nkhope yake ndi nsalu ina. Atatero anakakhala pansi pachipata cha Enaimu mʼmbali mwa msewu wopita ku Timuna. Tamara anachita zimenezi poona kuti Shela wakula, koma apongozi ake sakudzamutenga kuti akakhale mkazi wa Shelayo.+
15 Yuda atamuona mkaziyo, anaganiza kuti ndi hule chifukwa anali ataphimba nkhope yake. 16 Choncho Yuda anapatuka nʼkupita pamene panali mkaziyo mʼmbali mwa msewu nʼkumuuza kuti: “Ndikufuna ndigone nawe.” Anamuuza zimenezi chifukwa sankadziwa kuti anali mpongozi wake.+ Koma mkaziyo anayankha kuti: “Mundipatsa chiyani kuti mugone nane?” 17 Iye anayankha kuti: “Ndidzakutumizira mwana wa mbuzi.” Koma mkaziyo anati: “Mundipatse chikole choti ndisunge kufikira pamene mudzaitumize.” 18 Iye anati: “Ukufuna ndikupatse chikole chotani?” Mkaziyo anapitiriza kuti: “Mundipatse mphete ya udindo+ wanuyo ndi chingwe chake, ndiponso ndodo yanuyo.” Pamenepo iye anapereka zinthuzo kwa mkaziyo, nʼkugona naye ndipo mkaziyo anakhala woyembekezera. 19 Atagona naye, mkaziyo ananyamuka nʼkubwerera kwawo. Atafika anavula nsalu imene anadziphimba nayo ija nʼkuvala zovala zake zaumasiye.
20 Yuda anatumiza mwana wa mbuzi kudzera mwa mnzake wa Chiadulamu uja+ nʼcholinga choti akamutengere chikole chake kwa mkazi uja, koma sanakamupeze. 21 Kenako anafunsa amuna akuderalo kuti: “Kodi hule lapakachisi lija, limene limaima mʼmbali mwa msewu kuno ku Enaimu lili kuti?” Koma amunawo anayankha kuti: “Kunotu sikunakhalepo hule lapakachisi.” 22 Pamapeto pake, mnzakeyo anabwerera kwa Yuda nʼkumuuza kuti: “Mkazi ujatu sindinamupeze. Ndiponso amuna akumeneko anena kuti, ‘Kunotu sikunakhalepo hule lapakachisi.’” 23 Choncho Yuda anati: “Mulekeni atenge zinthuzo zikhale zake, kuopera kuti anthu angatiseke. Ndipotu mwana wa mbuziyo ndinatumiza ndithu, koma mkaziyo sunakamupeze.”
24 Patapita miyezi itatu, Yuda anauzidwa kuti: “Tamara mpongozi wako wayamba uhule, ndipo ndi woyembekezera.” Yuda atamva zimenezo anati: “Mutulutseni ndipo mumuphe kenako mumuotche.”+ 25 Pamene ankamutulutsa, Tamarayo anatumiza uthenga kwa apongozi ake kuti: “Mwiniwake wa zinthu izi ndi amene anandipatsa mimbayi.” Ananenanso kuti: “Chonde ziyangʼanitsitseni, muone kuti mpheteyo ndi chingwe chake komanso ndodoyo nʼzandani.”+ 26 Ndiyeno Yuda atayangʼanitsitsa zinthuzo, ananena kuti: “Mkaziyu ndi wolungama koposa ine, chifukwa sindinamupereke kwa mwana wanga Shela.”+ Zitatero, Yuda sanagonenso naye.
27 Nthawi yoti Tamara abereke itakwana, anapezeka kuti ali ndi mapasa mʼmimba mwake. 28 Pamene ankabereka, mwana mmodzi anatulutsa dzanja lake. Nthawi yomweyo mzamba anatenga kachingwe kofiira nʼkumanga dzanjalo, ndipo ananena kuti: “Uyu ndi amene wayamba kubadwa.” 29 Koma mwanayo anabweza dzanja lake. Nthawi yomweyo mchimwene wake anatuluka, moti mzambayo anafuula kuti: “Bwanji ukuchita kungʼamba njira?” Nʼchifukwa chake anamupatsa dzina lakuti Perezi.*+ 30 Pambuyo pake, mʼbale wake yemwe anali ndi kachingwe kofiira padzanja lake uja anatuluka, ndipo anamupatsa dzina lakuti Zera.+