Genesis
49 Kenako Yakobo anaitana ana ake nʼkuwauza kuti: “Sonkhanani pamodzi kuti ndikuuzeni zimene zidzachitike kwa inu mʼtsogolo.* 2 Bwerani nonse kuti mumvetsere, inu ana a Yakobo. Bwerani mumvetsere kwa Isiraeli bambo anu.
3 Rubeni,+ iwe ndi mwana wanga woyamba kubadwa,+ nyonga yanga ndi poyambira mphamvu zanga zobereka. Unayenera kukhala ndi ulemu waukulu ndi mphamvu zochuluka. 4 Koma sudzakhala wapamwamba kuposa abale ako, chifukwa mofanana ndi madzi osefukira unalephera kudziletsa, ndipo unakwera pogona pa bambo ako.+ Pa nthawiyo unadetsa* bedi langa. Anagonapo ndithu ameneyu!
5 Simiyoni ndi Levi mʼpachibale.+ Malupanga awo ndi zida zochitira zachiwawa.+ 6 Iwe moyo wanga, usakhale nawo pagulu lawo. Iwe mtima wanga,* usagwirizane ndi mpingo wawo, chifukwa atakwiya anapha anthu,+ ndipo anapundula* ngʼombe zamphongo pofuna kusangalala. 7 Mkwiyo wawo ukhale wotembereredwa chifukwa ndi wankhanza, komanso ukali wawo chifukwa umachita zinthu mwachiwawa.+ Ndidzawamwaza mwa Yakobo, ndipo ndidzawabalalitsa mwa Isiraeli.+
8 Koma iwe Yuda,+ abale ako adzakutamanda.+ Dzanja lako lidzakhala pakhosi la adani ako.+ Ana a bambo ako adzakuweramira.+ 9 Yuda ndi mwana wa mkango.+ Mwana wanga, ukadzadya nyama imene wapha udzachokapo. Iye wapinda mawondo ake nʼkudziwongola ngati mkango umene wagona pansi. Ndipo mofanana ndi mkango, ndi ndani amene angamudzutse? 10 Ndodo yachifumu sidzachoka kwa Yuda,+ ndiponso chibonga cha wolamulira sichidzachoka pakati pa mapazi ake, mpaka Silo* atabwera.+ Ndipo mitundu ya anthu idzamumvera.+ 11 Atamanga bulu wake pamtengo wa mpesa ndi kamwana ka bulu wake pamtengo wa mpesa wabwino, adzachapa zovala zake muvinyo komanso malaya ake mʼmadzi ofiira a mphesa. 12 Maso ake ndi ofiira chifukwa cha vinyo, ndipo mano ake ndi oyera chifukwa cha mkaka.
13 Zebuloni+ adzakhala mʼmbali mwa nyanja, adzakhala pafupi ndi doko pamene pamaima sitima.+ Malire ake akutali adzakhala cha ku Sidoni.+
14 Isakara+ ndi bulu wa mafupa olimba. Amagona pansi kuti apume, atanyamula matumba awiri a katundu. 15 Adzaona kuti malo opumirawo ndi abwino, komanso kuti dzikolo ndi losangalatsa. Adzaweramitsa phewa lake kuti anyamule katundu, ndipo adzalolera kugwira ntchito mokakamizidwa.
16 Dani+ adzaweruza anthu a mtundu wake ngati mmodzi wa mafuko a Isiraeli.+ 17 Dani adzakhala njoka yobisala mʼmbali mwa msewu, njoka yokhala ndi tinyanga yobisala mʼmphepete mwa njira, imene imaluma zidendene za hatchi ndipo wokwerapo amagwa chagada.+ 18 Ndidzayembekezera chipulumutso kuchokera kwa inu, Yehova.
19 Kunena za Gadi,+ gulu la achifwamba lidzamuukira, koma iye adzalimbana nawo, ndipo achifwambawo pothawa adzawamenya koopsa.+
20 Chakudya cha Aseri+ chidzakhala chochuluka, ndipo adzapereka chakudya choyenera mfumu.+
21 Nafitali+ ndi mbawala yaikazi yopepuka miyendo, ndipo amalankhula mawu osangalatsa.+
22 Yosefe+ ndi mphukira yamtengo wobala zipatso. Iye ndi mtengo wobala zipatso pakasupe, umene nthambi zake zimafika pamwamba pa khoma la mpanda. 23 Koma oponya mivi ndi uta sanaleke kumuzunza, kumulasa ndi kumusungira chidani.+ 24 Koma uta wake unakhalabe pamalo ake,+ ndipo manja ake anakhalabe amphamvu ndi ochenjera.+ Zimenezi zinachokera mʼmanja mwa wamphamvu wa Yakobo, zinachokera kwa mʼbusa, mwala wa Isiraeli. 25 Iye* ndi wochokera kwa Mulungu wa bambo ako ndipo adzakuthandiza. Iye ali ndi Wamphamvuyonse, ndipo Mulunguyo adzakudalitsa pokupatsa madzi ochokera kumwamba ndi pansi pa nthaka.+ Adzakudalitsa pokupatsa ana ndi ziweto zambiri.* 26 Madalitso a bambo ako adzaposa madalitso a mapiri amene adzakhalapo mpaka kalekale. Adzaposanso zinthu zosiririka za zitunda zosatha.+ Madalitsowo adzapitiriza kukhala pamutu pa Yosefe, paliwombo pa wosankhidwa pakati pa abale ake.+
27 Benjamini+ adzapitiriza kukhadzula ngati mmbulu.+ Mʼmawa adzadya nyama imene wagwira, ndipo madzulo adzagawa zinthu zimene watenga atagonjetsa adani ake.”+
28 Onsewa ndi mafuko 12 a Isiraeli, ndipo zimenezi ndi zimene bambo awo anawauza pamene ankawadalitsa. Aliyense anamupatsa madalitso omuyenerera.+
29 Atatero anawalamula kuti: “Ine uno ndi ulendo wopita kumene kunapita makolo anga.*+ Mukandiike limodzi ndi makolo anga, mʼphanga limene lili mʼmunda wa Efuroni, Muhiti.+ 30 Ndithu mukandiike mʼphanga limene lili mʼmunda wa Makipela, umene uli moyangʼanizana ndi munda wa Mamure, mʼdziko la Kanani. Mundawo ndi umene Abulahamu anagula kwa Efuroni, Muhiti, kuti akhale manda. 31 Kumeneko nʼkumene anaika Abulahamu ndi mkazi wake Sara.+ Nʼkumene anaika Isaki+ ndi mkazi wake Rabeka, ndipo nʼkumenenso ndinaika Leya. 32 Mundawo ndiponso phanga limene lili mmenemo, anagula kwa ana a Heti.”+
33 Yakobo atamaliza kupereka malangizo kwa ana akewo, anabwezeranso miyendo yake pabedi, nʼkumwalira. Kenako anaikidwa mʼmanda ngati mmene anachitira ndi makolo ake.*+