Hoseya
4 Tamverani mawu a Yehova inu Aisiraeli.
Yehova ali ndi mlandu ndi anthu amʼdzikoli,+
Chifukwa mʼdzikoli mulibe choonadi, chikondi chokhulupirika ndipo anthu ake sadziwa Mulungu.+
2 Kulumbira monama, bodza,+ kuphana,+
Kuba ndi chigololo+ zafala mʼdzikoli.
Ndipo kukhetsa magazi kukuchitika pafupipafupi.+
3 Nʼchifukwa chake dzikoli lidzalira maliro,+
Ndipo aliyense wokhala mmenemo adzalefukiratu.
Nyama zakutchire ndi mbalame zamumlengalenga,
Ngakhalenso nsomba zamʼnyanja, zidzafa.
4 “Komabe, munthu asakutsutseni kapena kukudzudzulani,+
Chifukwa muli ngati anthu otsutsana ndi wansembe.+
5 Choncho mudzapunthwa masanasana.
Ndipo mneneri adzapunthwa nanu limodzi ngati kuti ndi usiku.
Komanso mayi anu ndidzawakhalitsa chete.*
6 Anthu anga adzakhalitsidwa chete* chifukwa cha kusadziwa.
Popeza iwo akana kundidziwa,+
Inenso ndidzawakana kuti asamanditumikire ngati wansembe wanga.
Komanso chifukwa chakuti iwo aiwala lamulo* la ine Mulungu wawo,+
Inenso ndidzaiwala ana awo.
7 Pamene akuchuluka, mʼpamenenso akundichimwira kwambiri.+
Ndidzasintha ulemerero wawo nʼkukhala kunyozeka.*
8 Iwo akupindula mwadyera ndi machimo a anthu anga,
Ndipo amalakalaka mwadyera machimo a anthuwo.
9 Zimene zidzachitikire anthuwo zidzachitikiranso ansembe.
Onse ndidzawaimba mlandu chifukwa cha njira zawo,
Ndipo ndidzachititsa kuti zotsatira za zochita zawo ziwabwerere.+
10 Iwo adzadya, koma sadzakhuta.+
Adzachita zachiwerewere, koma sadzachulukana,+
Chifukwa chakuti sakumvera Yehova.
12 Anthu anga amafunsira kwa mafano awo amtengo,
Ndipo amachita zimene ndodo yawo* yawauza.
Chifukwa chakuti mtima wachiwerewere umawasocheretsa,
Ndiponso chifukwa cha chiwerewere chawocho, amakana kugonjera Mulungu wawo.
13 Iwo amapereka nsembe pamwamba pa mapiri akuluakulu,+
Ndipo amapereka nsembe zautsi pamapiri angʼonoangʼono.
Amachitanso zimenezi pansi pa mitengo yokhala ndi nthambi zambiri ndi masamba ambiri, pansi pa mitengo ya mlanje ndiponso pa mtengo uliwonse waukulu,+
Chifukwa mitengo imeneyi imakhala ndi mthunzi wabwino.
Nʼchifukwa chake ana anu aakazi amachita uhule
Ndipo akazi a ana anu amachita chigololo.
14 Sindidzaimba mlandu ana anu aakazi chifukwa cha chiwerewere chawo,
Komanso akazi a ana anu chifukwa cha chigololo chawo.
Chifukwa amuna akuyenda ndi mahule
Ndipo amapereka nsembe limodzi ndi mahule apakachisi.
Anthu osamvetsa zinthu amenewa+ adzawonongedwa.
Musabwere ku Giligala+ kapena ku Beti-aveni,+
Ndipo musalumbire kuti, ‘Mʼdzina la Yehova Mulungu wamoyo!’+
16 Isiraeli wakhala wamakani ngati ngʼombe yomwe ikuchita makani.+
Ndiye kodi Yehova adzawaweta ngati nkhosa yamphongo yaingʼono pamalo odyetsera ziweto?
17 Efuraimu wagwirizana ndi mafano.+
Musiyeni aona!
Ndipo atsogoleri awo amakonda kwambiri zinthu zochititsa manyazi.+
19 Mphepo idzawakulunga mʼmapiko ake,
Ndipo adzachita manyazi ndi nsembe zawo.”