1 Samueli
10 Ndiyeno Samueli anatenga botolo ladothi lomwe munali mafuta nʼkuthira mafutawo pamutu pa Sauli.+ Kenako anamukisa nʼkunena kuti: “Yehova wakudzoza kuti ukhale mtsogoleri+ wa anthu ake.*+ 2 Tikangosiyana, ukumana ndi amuna awiri pafupi ndi manda a Rakele+ pa Zeliza, mʼdera la Benjamini. Iwo akuuza kuti, ‘Abulu amene unapita kukawafunafuna apezeka. Panopa bambo ako asiya kuganizira za abuluwo+ koma akudera nkhawa za inuyo, moti akunena kuti: “Nditani ine, mwana wanga sakubwera!”’ 3 Ukakachoka pamenepo ukapitirize ulendo wako mpaka ukafike kumtengo waukulu wa ku Tabori. Kumeneko ukakumana ndi amuna atatu akupita ku Beteli+ kukalambira Mulungu woona. Mmodzi akhala atanyamula ana atatu a mbuzi, wina atanyamula mikate itatu ndipo winayo atanyamula mtsuko waukulu wa vinyo. 4 Anthuwo akakulonjera nʼkukupatsa mikate iwiri ndipo ukalandire. 5 Ukakachoka pamenepo, ukafika kuphiri la Mulungu woona, kumene kukukhala asilikali a Afilisiti. Ukakafika mumzinda ukakumana ndi kagulu ka aneneri akuchokera kumalo okwezeka, akulosera. Patsogolo pawo pakakhala anthu oimba maseche, chitoliro, zeze ndi choimbira cha zingwe. 6 Mzimu wa Yehova ukakupatsa mphamvu+ ndipo iweyo ukayamba kulosera pamodzi ndi aneneriwo ndiponso ukasintha kwambiri.+ 7 Ndiyeno zinthu zonsezi zikakachitika, ukachite chilichonse chimene ungathe chifukwa Mulungu woona ali nawe. 8 Kenako ukatsogole kupita ku Giligala.+ Inenso ndipita kumeneko kuti ndikapereke nsembe zopsereza ndi nsembe zamgwirizano. Ukandidikire masiku 7 mpaka nditabwera ndipo ndikadzafika ndidzakuuza zoti uchite.”
9 Sauli atangosiyana ndi Samueli, Mulungu anayamba kusintha mtima wake kukhala ngati wa munthu wina, moti zinthu zonse zija zinachitikadi tsiku limenelo. 10 Sauli ndi mtumiki wake ananyamuka kupita kuphiri kuja. Kumeneko anakumana ndi kagulu ka aneneri. Nthawi yomweyo, mzimu wa Mulungu unamʼpatsa mphamvu+ ndipo nayenso anayamba kulosera.+ 11 Anthu onse amene ankamudziwa atamuona akulosera pamodzi ndi aneneri, anayamba kufunsana kuti: “Kodi mwana wa Kisiyu watani? Kodi Sauli nayenso ndi mneneri?” 12 Ndiyeno munthu wina anati: “Nanga aneneri enawo bambo awo ndi ndani?” Mʼpamene panabwerera mawu* akuti: “Kodi Sauli nayenso ndi mneneri?”+
13 Atamaliza kulosera, Sauli anafika kumalo okwezeka. 14 Kenako mchimwene wawo wa bambo ake anafunsa Sauli ndi wantchito wake kuti: “Kodi munapita kuti?” Iye anayankha kuti: “Tinapita kukafunafuna abulu+ koma sitinawapeze. Ndiye tinapita kwa Samueli.” 15 Mchimwene wawo wa bambo akewo anati: “Tandiuzani, kodi Samueli anakuuzani chiyani?” 16 Sauli anayankha kuti: “Anatiuza kuti abulu apezeka kale.” Koma sanatchulepo nkhani ya ufumu imene Samueli anamuuza ija.
17 Kenako Samueli anasonkhanitsa anthu ku Mizipa kuti akakumane ndi Yehova.+ 18 Iye anauza Aisiraeliwo kuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Ndine amene ndinatulutsa Aisiraeli ku Iguputo komanso amene ndinakupulumutsani mʼmanja mwa Aiguputo+ ndi mafumu onse amene ankakuponderezani. 19 Koma lero mwakana Mulungu wanu+ amene anakupulumutsani mʼmasautso anu onse ndiponso mʼmavuto anu, ndipo munanena kuti: “Ayi, mutisankhire mfumu yoti izitilamulira.” Tsopano imani pamaso pa Yehova potengera mafuko anu ndiponso mabanja anu.’”*
20 Kenako Samueli anabweretsa pafupi fuko lililonse+ ndipo fuko la Benjamini linasankhidwa.+ 21 Kenako anabweretsa pafupi fuko la Benjamini potengera mabanja awo ndipo banja la Amatiri linasankhidwa. Pomaliza, Sauli mwana wa Kisi anasankhidwa.+ Koma atamufufuza, sanamupeze. 22 Choncho anafunsanso Yehova kuti:+ “Kodi munthu ameneyu wafika kale pano?” Yehova anayankha kuti: “Uyo wabisala pakati pa katunduyo.” 23 Choncho anthu anathamanga nʼkukamutenga. Ataimirira pakati pa anthuwo, ankaoneka wamtali kwambiri moti palibe aliyense amene ankapitirira mʼmapewa ake.+ 24 Ndiyeno Samueli anauza anthu onsewo kuti: “Kodi mwaona munthu amene Yehova wamusankha,+ kuti palibe aliyense wofanana naye?” Anthu onsewo anayamba kufuula kuti: “Mfumu ikhale ndi moyo wautali!”
25 Samueli anauza anthuwo zinthu zimene mfumu iyenera kulandira kwa iwo+ ndipo anazilemba mʼbuku nʼkuliika mʼchihema cha Yehova. Kenako Samueli anauza anthuwo kuti abwerere kwawo. 26 Nayenso Sauli anapita kwawo ku Gibeya, ndipo anali ndi asilikali amene Yehova anawachititsa kuti apite naye limodzi. 27 Koma anthu ena opanda pake ankanena kuti: “Kodi ameneyu angathedi kutipulumutsa?”+ Choncho anayamba kumunyoza, moti sanamʼbweretsere mphatso iliyonse.+ Koma Sauli sanayankhe chilichonse.*