Miyambo
17 Ndi bwino kudya mkate wouma pali mtendere,*+
Kusiyana ndi kuchita maphwando ochuluka* mʼnyumba imene muli mikangano.+
2 Wantchito wozindikira adzalamulira mwana wa mbuye wake amene amachita zinthu zochititsa manyazi.
Adzalandira nawo cholowa pamodzi ndi ana a mbuye wake.
3 Siliva amamuyengera mʼmbiya yoyengera ndipo golide amamuyengera mungʼanjo,+
Koma Yehova ndi amene amayesa mitima.+
4 Munthu woipa amakonda kumvetsera mawu opweteka.
Ndipo munthu wachinyengo amamvetsera lilime loyambitsa mavuto.+
5 Wonyoza munthu wosauka amanyoza amene anamupanga.+
Ndipo amene amasangalala ndi tsoka la wina sadzalephera kulangidwa.+
6 Zidzukulu zili ngati chisoti chaulemu kwa anthu okalamba,
Ndipo ana amalemekezeka chifukwa cha bambo awo.*
7 Sitingayembekezere kuti munthu wopusa alankhule zinthu zanzeru.*+
Ndipo nʼzosayenera kuti wolamulira* azilankhula zabodza.+
8 Mphatso ili ngati mwala wamtengo wapatali kwa mwiniwake.*+
Kulikonse kumene wapita, imachititsa kuti zinthu zimuyendere bwino.+
9 Aliyense amene amakhululuka* zolakwa akufunafuna chikondi,+
Koma amene amangokhalira kulankhula za nkhani inayake amalekanitsa mabwenzi apamtima.+
10 Kudzudzula kumamufika pamtima munthu womvetsa zinthu,+
Kuposa kukwapula munthu wopusa zikwapu 100.+
12 Ndi bwino kukumana ndi chimbalangondo chimene ana ake asowa,
Kusiyana ndi kukumana ndi chitsiru chimene chimachita zopusa.+
14 Kuyambitsa ndewu kuli ngati kuboola damu kuti madzi atulukemo.*
Choncho mkangano usanabuke, chokapo.+
15 Aliyense wonena kuti munthu woipa alibe mlandu ndiponso aliyense wonena kuti munthu wolungama ndi wolakwa,+
Onsewa ndi onyansa kwa Yehova.
16 Kodi pali phindu lililonse ngati munthu wopusa ali ndi njira yopezera nzeru,
17 Mnzako weniweni amakusonyeza chikondi nthawi zonse,+
Ndipo ndi mʼbale amene anabadwa kuti akuthandize pakagwa mavuto.+
18 Munthu wopanda nzeru amagwirana dzanja ndi munthu wina
Ndipo amalonjeza pamaso pa mnzake kuti iye akhala chikole.+
19 Aliyense amene amakonda mikangano amakonda zolakwa.+
Aliyense woika khomo la nyumba yake pamwamba akudziitanira mavuto.+
20 Munthu amene mtima wake ndi wopotoka zinthu sizidzamuyendera bwino,*+
Ndipo amene amalankhula mwachinyengo adzagwera mʼmavuto.
21 Bambo amene wabereka mwana wopusa adzamva chisoni.
Ndipo bambo wa mwana wopanda nzeru sasangalala.+
24 Munthu wozindikira amakhala ndi cholinga choti apeze nzeru,
Koma maso a munthu wopusa amangoyendayenda mpaka kumalekezero a dziko lapansi.+
25 Mwana wopusa amamvetsa chisoni bambo ake,
Komanso amapweteketsa mtima wa* mayi ake amene anamubereka.+
27 Munthu wodziwa zinthu amayamba waganiza asanalankhule,+
Ndipo munthu wozindikira amapitiriza kukhala wodekha.+
28 Ngakhale munthu wopusa amene wakhala chete adzaonedwa ngati wanzeru,
Ndipo amene watseka pakamwa pake adzaonedwa ngati wozindikira.