Hoseya
3 Koma ndine amene ndinaphunzitsa Efuraimu kuyenda,+ ndipo ndinkamunyamula mʼmanja mwanga+
Koma iye sanavomereze kuti ndinamuchiritsa.
4 Ndinkawakoka mokoma mtima ndiponso mwachikondi,*+
Kwa iwo ndinali ngati wochotsa goli mʼkhosi* mwawo,
Ndipo mwachikondi ndinkabweretsera aliyense chakudya.
5 Iwo sadzabwerera kudziko la Iguputo, koma Asuri adzakhala mfumu yawo,+
Chifukwa anakana kubwerera kwa ine.+
6 Lupanga lidzazungulira mʼmizinda yake+
Ndipo lidzawononga mipiringidzo nʼkupha anthu chifukwa cha zoipa zimene ankafuna kuchita.+
7 Anthu anga atsimikiza kuti akhale osakhulupirika kwa ine.+
Ngakhale kuti anawaitanira kumwamba,* palibe amene anaimirira.
8 Kodi ndikusiye chifukwa chiyani iwe Efuraimu?+
Kodi ndikupereke kwa adani chifukwa chiyani iwe Isiraeli?
Kodi ndikuchitire zinthu ngati Adima chifukwa chiyani?
Kodi ndikusinthirenji kukhala ngati Zeboyimu?+
Koma ndasintha maganizo
Ndipo ndayamba kukumvera chisoni.+
9 Sindidzasonyeza mkwiyo wanga woyaka moto.
Sindidzawononganso Efuraimu+
Chifukwa ndine Mulungu, osati munthu.
Ndine Woyera pakati panu,
Ndipo sindidzabwera kwa inu nditakwiya.
10 Iwo adzatsatira Yehova ndipo iye adzabangula ngati mkango.+
Ndipo akadzabangula, ana ake adzabwera akunjenjemera kuchokera kumadzulo.+
11 Iwo adzabwera akunjenjemera ngati mbalame akamadzachokera ku Iguputo.
Adzabwera ngati njiwa kuchokera kudziko la Asuri.+
Ndipo ndidzawachititsa kukhazikika mʼnyumba zawo,” watero Yehova.+
12 “Efuraimu amandiuza mabodza okhaokha.
Kulikonse kumene ndingayangʼane, ndikuona chinyengo cha Isiraeli.+
Koma Yuda akuyendabe ndi Mulungu,
Ndipo iye ndi wokhulupirika kwa Woyera Koposa.”+