2 Samueli
15 Kenako Abisalomu anapeza galeta lokokedwa ndi mahatchi komanso amuna 50 oti azithamanga patsogolo pake.+ 2 Abisalomu ankadzuka mʼmawa kwambiri nʼkukaima mʼmbali mwa msewu wopita kugeti la mzinda.+ Ndiyeno munthu aliyense akafika ndi mlandu woti uweruzidwe ndi mfumu,+ Abisalomu ankamuitana nʼkumufunsa kuti: “Wachokera mzinda uti?” Munthuyo ankamuuza fuko la Isiraeli limene wachokera. 3 Kenako Abisalomu ankamuuza kuti: “Zimene ukunenazi ndi zoona komanso zomveka. Koma kwa mfumu kulibe aliyense woti amvetsere nkhani yakoyi.” 4 Abisalomu ankanenanso kuti: “Zikanakhala bwino ndikanaikidwa kukhala woweruza mʼdzikoli. Bwenzi ndikuonetsetsa kuti munthu aliyense amene wabwera ndi mlandu kwa ine, wachitiridwa chilungamo.”
5 Komanso munthu akafika pafupi kuti amuweramire, Abisalomu ankamugwira nʼkumuletsa ndipo kenako ankamukisa.+ 6 Abisalomu ankachita zimenezi kwa Aisiraeli onse amene ankabwera kwa mfumu kuti awaweruzire milandu yawo. Choncho Abisalomu anapitiriza kukopa anthu mu Isiraeli.+
7 Patatha zaka 4,* Abisalomu anauza mfumu kuti: “Ndikupempha kuti ndipite ku Heburoni+ ndikakwaniritse lonjezo limene ndinalonjeza Yehova. 8 Ine mtumiki wanu pamene ndinali ku Gesuri,+ ku Siriya ndinalonjeza+ kuti: ‘Yehova akandilola kubwerera ku Yerusalemu, ndidzapereka nsembe kwa* Yehova.’” 9 Mfumu inamuyankha kuti: “Pita mwamtendere.” Zitatero, ananyamuka nʼkupita ku Heburoni.
10 Ndiyeno Abisalomu anatumiza akazitape ku mafuko onse a Isiraeli ndipo anawauza kuti: “Mukangomva kulira kwa lipenga la nyanga ya nkhosa, mufuule kuti, ‘Tsopano Abisalomu ndi mfumu ku Heburoni!’”+ 11 Pochoka ku Yerusalemu, Abisalomu anatenga amuna 200. Anthuwa anawaitana ndipo anapita mʼchimbulimbuli osadziwa chilichonse. 12 Komanso pamene Abisalomu ankapereka nsembe, anaitanitsa Ahitofeli+ wa ku Gilo, mlangizi wa Davide,+ kuchoka kumzinda wakwawo wa Gilo.+ Anthu amene anagwirizana ndi Abisalomu pa chiwembuchi anapitiriza kuwonjezeka.+
13 Patapita nthawi, munthu wina anauza Davide kuti: “Anthu a mu Isiraeli ayamba kutsatira Abisalomu.” 14 Nthawi yomweyo, Davide anauza atumiki ake onse amene anali naye ku Yerusalemu kuti: “Konzekani msangamsanga! Tiyeni tithawe,+ chifukwa palibe amene angapulumuke mʼmanja mwa Abisalomu. Fulumirani! Chifukwa akhoza kutipeza nʼkutigonjetsa kenako nʼkupha anthu onse amumzindawu ndi lupanga!”+ 15 Atumiki a mfumu anayankha kuti: “Ndife okonzeka kuchita chilichonse chimene inu mbuyathu mfumu mwasankha.”+ 16 Choncho mfumu inanyamuka limodzi ndi anthu onse amʼnyumba yake. Koma mfumuyo inasiya akazi ake aangʼono*+ 10, kuti azisamalira nyumba.* 17 Mfumu inapitiriza ulendo wake pamodzi ndi anthu onse amene ankaitsatira ndipo anaima ku Beti-merehaki.
18 Ndiyeno atumiki onse a mfumu amene ananyamuka nawo limodzi, Akereti onse, Apeleti+ onse, Agiti+ onse ndiponso amuna 600 amene anamutsatira* kuchokera ku Gati+ anayamba kudutsa kutsogolo kwa mfumuyo kuti idziwe anthu amene alipo. 19 Kenako mfumu inauza Itai+ wa ku Gati kuti: “Kodi iwenso ukupita nafe? Bwerera ukakhale ndi mfumu yatsopano popeza unachoka kwanu ndipo kuno ndiwe mlendo. 20 Iwe wabwera dzulodzuloli, ndiye lero uyambe kuyendayenda ndi ife nʼkumapita kumene ine ndikupita? Bwerera, utengenso abale akowa ndipo Yehova akusonyeze chikondi komanso kukhulupirika kwake!”+ 21 Koma Itai anayankha mfumu kuti: “Ndikulumbira mʼdzina la Yehova Mulungu wamoyo komanso mbuyanga mfumu muli apa, kulikonse kumene inu mungapite, ine mtumiki wanu ndipitanso komweko, ndipo ndine wokonzeka ngakhale kufa nanu limodzi!”+ 22 Atatero Davide anamuuza kuti:+ “Dutsa upite.” Choncho Itai wa ku Gati anadutsa limodzi ndi amuna onse amene anali naye komanso ana onse.
23 Anthu onse amʼdzikoli ankalira mokweza mawu, pamene anthu onse amene anali ndi Davide ankadutsa. Mfumu inali itaimirira pafupi ndi chigwa cha Kidironi+ ndipo anthu onse ankawoloka kulowera kumsewu wopita kuchipululu. 24 Zadoki+ nayenso anali komweko limodzi ndi Alevi+ onse atanyamula likasa+ la pangano la Mulungu woona.+ Aleviwo anatula pansi Likasa la Mulungu woona ndipo Abiyatara+ anali pomwepo mpaka anthu onse anamaliza kudutsa kuchokera mumzinda. 25 Koma mfumu inauza Zadoki kuti: “Tengani Likasa la Mulungu woona mubwerere nalo mumzinda.+ Yehova akandikomera mtima adzandilola kuti ndibwerere mumzinda ndipo ndidzaliona. Ndidzaonanso malo amene limakhala.+ 26 Koma akanena kuti, ‘Sindikusangalala nawe,’ ine ndidzavomereza zilizonse zimene adzandichitire.” 27 Mfumu inauza Zadoki wansembe kuti: “Paja iwe ndiwe wamasomphenya.+ Iwe ndi Abiyatara bwererani kumzinda mwamtendere. Mubwerere pamodzi ndi ana anu awiri, Ahimazi mwana wako wamwamuna ndi Yonatani+ mwana wamwamuna wa Abiyatara. 28 Ine ndikhala pamalo owolokera amene ali pafupi ndi chipululu mpaka nditalandira uthenga wochokera kwa inuyo wondidziwitsa mmene zinthu zilili.”+ 29 Choncho Zadoki ndi Abiyatara anatenga Likasa la Mulungu woona nʼkubwerera nalo ku Yerusalemu, ndipo ankakhala kumeneko.
30 Pamene Davide ankakwera phiri la Maolivi,+ ankalira komanso anaphimba kumutu. Iye ankayenda wopanda nsapato ndipo anthu onse amene anali naye nawonso anaphimba kumutu ndipo ankalira. 31 Kenako Davide anauzidwa kuti: “Ahitofeli nayenso ali mʼgulu la anthu amene akukonza chiwembu+ ndi Abisalomu.”+ Davide atamva zimenezi anati: “Chonde Yehova,+ chititsani kuti malangizo a Ahitofeli akhale opusa.”+
32 Davide atafika pamwamba pa phiri, pomwe anthu ankapita kukalambira Mulungu, anaona Husai+ mbadwa ya Areki+ akubwera kudzakumana naye, atangʼamba mkanjo wake ndiponso atadzithira dothi kumutu. 33 Davide anamuuza kuti: “Ukapita nane limodzi, sizithandiza. 34 Koma ubwerere kumzinda ndipo ukauze Abisalomu kuti, ‘Mfumu, ine ndine mtumiki wanu. Poyamba ndinali mtumiki wa bambo anu koma tsopano ndine mtumiki wanu.’+ Ukakatero, ukatha kunditsutsira malangizo a Ahitofeli.+ 35 Zadoki ndi Abiyatara omwe ndi ansembe ali komweko. Chilichonse chimene ukamve kunyumba ya mfumu ukauze Zadoki ndi Abiyatara.+ 36 Iwo alinso ndi ana awo awiri komweko, Ahimazi+ mwana wa Zadoki ndi Yonatani+ mwana wa Abiyatara. Ndiye mukatume ana awowo kuti adzandiuze zonse zimene mungamve.” 37 Choncho Husai, mnzake wa Davide,+ anapita ku Yerusalemu pa nthawi imene Abisalomu ankalowa mumzindawu.