Numeri
6 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 2 “Lankhula ndi Aisiraeli ndipo uwauze kuti, ‘Ngati mwamuna kapena mkazi wachita lonjezo lapadera kwa Yehova lokhala Mnaziri,*+ 3 asamamwe vinyo ndi zakumwa zina zoledzeretsa. Asamamwenso viniga* wokhala ndi vinyo, kapena viniga wochokera ku zakumwa zina zoledzeretsa,+ kapenanso madzi a mphesa. Ndiponso asamadye mphesa zaziwisi kapena zouma. 4 Masiku ake onse okhala Mnaziri, asamadye chilichonse chochokera kumtengo wa mpesa, kaya zikhale mphesa zosapsa kapena khungu lake.
5 Masiku onse a lonjezo lake lokhala Mnaziri, lezala lisamadutse mʼmutu wake.+ Azikhala woyera posiya tsitsi lakumutu kwake kuti likule mpaka masiku amene anadzipereka kwa Yehova atatha. 6 Iye asamayandikire munthu wakufa masiku onse amene wadzipereka kwa Yehova. 7 Ngakhale kuti amene amwalira ndi bambo ake, mayi ake, mchimwene wake kapena mchemwali wake, iye asamadzidetse,+ chifukwa chizindikiro cha unaziri wake kwa Mulungu chili kumutu kwake.
8 Iye ndi woyera kwa Yehova masiku onse a unaziri wake. 9 Koma ngati munthu wina wafera pambali pake+ mwadzidzidzi, moti Mnaziriyo wadetsa tsitsi limene lili ngati chizindikiro choti wadzipereka kwa Mulungu, azimeta tsitsi lakumutu kwake+ pa tsiku limene wayeretsedwa. Azilimeta pa tsiku la 7. 10 Ndipo pa tsiku la 8, azibweretsa njiwa ziwiri kapena ana a nkhunda awiri kwa wansembe pakhomo la chihema chokumanako. 11 Wansembeyo azitenga mwana mmodzi wa njiwa kapena wa nkhunda nʼkumupereka monga nsembe yamachimo. Azitenganso mwana wa njiwa kapena wa nkhunda winayo nʼkumupereka monga nsembe yopsereza kuti aphimbe machimo+ amene munthuyo anachita pokhudza munthu wakufa. Akatero aziyeretsa mutu wake pa tsikulo. 12 Munthuyo aziyambiranso masiku ake odzipereka kwa Yehova ngati Mnaziri, ndipo azibweretsa nkhosa yaingʼono yamphongo yosapitirira chaka chimodzi monga nsembe yakupalamula. Koma masiku oyamba aja sadzawerengedwa chifukwa anadetsa unaziri wake.
13 Tsopano lamulo lokhudza Mnaziri ndi ili: Pa tsiku limene masiku a unaziri+ wake atha, azimubweretsa pakhomo la chihema chokumanako. 14 Kumeneko azipereka nsembe yake kwa Yehova. Azipereka nkhosa yaingʼono yamphongo yopanda chilema, yosapitirira chaka chimodzi, monga nsembe yopsereza.+ Aziperekanso mwana wa nkhosa wamkazi wopanda chilema, wosapitirira chaka chimodzi, monga nsembe yamachimo.+ Komanso azipereka nkhosa yamphongo yopanda chilema, monga nsembe yamgwirizano.+ 15 Aziperekanso dengu la mikate yozungulira yoboola pakati yopanda zofufumitsa, yophika ndi ufa wosalala ndi yopaka mafuta, timikate topyapyala topanda zofufumitsa topaka mafuta, limodzi ndi nsembe yake yambewu+ ndiponso nsembe zake zachakumwa.+ 16 Wansembeyo azibweretsa zinthuzo pamaso pa Yehova, ndipo azimuperekera nsembe yake yamachimo ndi nsembe yake yopsereza. 17 Aziperekanso kwa Yehova nkhosa yamphongo monga nsembe yamgwirizano, limodzi ndi dengu la mikate yopanda zofufumitsa ija. Kenako wansembeyo azipereka nsembe yambewu+ ndi nsembe yachakumwa, zimene zimayendera limodzi ndi nsembe yamgwirizanoyo.
18 Kenako Mnaziriyo azimeta tsitsi lakumutu kwake+ ndipo azimetera pakhomo la chihema chokumanako. Akatero, azitenga tsitsi lakumutu kwake limene linamera pa nthawi yomwe anali Mnaziri, nʼkuliponya pamoto umene uli pansi pa nsembe yamgwirizano. 19 Wansembe azitenga mwendo wakutsogolo wa nkhosa yamphongo umene wawiritsidwa.+ Azitenganso mʼdengumo mkate woboola pakati wopanda zofufumitsa ndi kamkate kopyapyala kopanda zofufumitsa. Zinthuzi aziike mʼmanja mwa Mnaziriyo atameta chizindikiro cha unaziri wake. 20 Wansembeyo aziyendetsa zinthuzo uku ndi uku monga nsembe yoperekedwa kwa Yehova.+ Zinthuzi ziziperekedwa kwa wansembeyo ngati mphatso yopatulika, limodzi ndi chidale cha nsembe yoyendetsa uku ndi uku, komanso mwendo womwe ndi gawo lopatulika.+ Pambuyo pake munthu yemwe anali Mnaziriyo angathe kumwa vinyo.
21 Lamulo lokhudza Mnaziri+ amene wachita lonjezo ndi ili: Ngati analonjeza ndipo angakwanitse kupereka nsembe kwa Yehova, kuwonjezera pa zimene amayenera kupereka monga Mnaziri, azikwaniritsa lonjezo lake, posonyeza kuti akulemekeza lamulo la unaziri wake.’”
22 Kenako Yehova anauza Mose kuti: 23 “Uza Aroni ndi ana ake kuti, ‘Mukamadalitsa+ Aisiraeli muziwauza kuti:
24 “Yehova akudalitseni+ ndipo akutetezeni.
25 Yehova asonyeze kuti akusangalala nanu+ ndipo akukomereni mtima.
26 Yehova akuyangʼaneni mokondwera ndipo akupatseni mtendere.”’+
27 Aroni ndi ana ake azigwiritsa ntchito dzina langa podalitsa Aisiraeli+ kuti ine ndiwadalitse.”+