Machitidwe a Atumwi
12 Pa nthawi imeneyi Mfumu Herode* anayamba kuzunza anthu ena amumpingo.+ 2 Iye anapha ndi lupanga+ Yakobo, mchimwene wake wa Yohane.+ 3 Ataona kuti zimenezi zasangalatsa Ayuda, anamanganso Petulo. (Anamumanga mʼmasiku a Mikate Yopanda Zofufumitsa.)+ 4 Anamugwira nʼkumutsekera mʼndende+ ndipo anamusiya mʼmanja mwa magulu 4 a asilikali kuti azisinthana pomulondera. Gulu lililonse linali ndi asilikali 4. Cholinga cha Herode chinali chakuti adzamuzenge mlandu pamaso pa anthu Pasika akatha. 5 Choncho Petulo anatsekeredwa mʼndendemo, koma mpingo unkamupempherera kwambiri kwa Mulungu.+
6 Pamene Herode ankakonza zoti abweretse Petulo kwa anthu, usiku umenewo Petuloyo anagona pakati pa asilikali awiri atamumanga ndi maunyolo awiri. Pakhomo panalinso alonda omwe ankalondera ndendeyo. 7 Koma mwadzidzidzi, mngelo wa Yehova* anafika,+ ndipo mʼchipinda cha ndendeyo munawala. Kenako mngeloyo anadzutsa Petulo pomugwedeza mʼnthiti nʼkunena kuti: “Dzuka msanga!” Atatero maunyolo amene anamumanga nawo manjawo anagwa pansi.+ 8 Mngeloyo anamuuza kuti: “Vala zovala zako ndi nsapato zako.” Iye anachitadi zimenezo. Kenako anamuuza kuti: “Vala malaya ako akunja ndipo uzinditsatira.” 9 Iye anatuluka nʼkumamutsatira, koma sanadziwe kuti zimene zinkachitika ndi mngelozo zinalidi zenizeni. Ankangoganiza kuti akuona masomphenya. 10 Atapitirira gulu loyamba la asilikali apageti ndi lachiwiri, anafika pageti lachitsulo lotulukira popita mumzinda, ndipo linatseguka lokha. Atatuluka anayenda limodzi msewu umodzi, ndipo mwadzidzidzi mngelo uja anachoka. 11 Koma Petulo atayamba kuzindikira zimene zikuchitika anati: “Tsopano ndadziwa kuti Yehova* ndi amene watumiza mngelo wake kudzandipulumutsa mʼmanja mwa Herode komanso ku zinthu zonse zimene Ayuda amayembekezera kuti zichitike.”+
12 Atazindikira zimenezi, iye anapita kunyumba kwa Mariya, mayi ake a Yohane wotchedwanso Maliko.+ Kumeneko anthu ambiri anali atasonkhana nʼkumapemphera. 13 Atagogoda pachitseko cha pageti mtsikana wantchito dzina lake Roda anapita kuti akaone amene akugogoda. 14 Koma atazindikira mawu a Petulo, anasangalala kwambiri moti mʼmalo motsegula getilo, anathamangira mkati nʼkukanena kuti Petulo ali pageti. 15 Koma iwo anamuyankha kuti: “Misalatu imeneyo!” Iye atalimbikira kuti akunena zoona, anthuwo anayamba kunena kuti: “Ndi mngelo wake ameneyo.” 16 Koma Petulo anapitiriza kugogoda. Iwo atatsegula, anaona kuti ndi iyeyodi ndipo anadabwa kwambiri. 17 Koma iye anawauza ndi manja kuti akhale chete, ndipo anawafotokozera mwatsatanetsatane mmene Yehova* anamutulutsira mʼndende. Kenako anati: “Nkhani imeneyi mukauze Yakobo+ ndi abale.” Atatero anatuluka nʼkupita kwina.
18 Kutacha, asilikali aja anasokonezeka kwambiri posadziwa zimene zachitikira Petulo. 19 Herode anafunafuna Petulo paliponse ndipo atalephera kumupeza, anapanikiza alonda aja ndi mafunso komanso analamula kuti awatenge nʼkukawapatsa chilango.+ Kenako Herode anachoka ku Yudeya nʼkupita ku Kaisareya, komwe anakhalako kwakanthawi ndithu.
20 Herode anakwiyira kwambiri* anthu a ku Turo ndi ku Sidoni. Choncho anthuwo anabwera kwa iye mogwirizana ndipo atamunyengerera Balasito, amene ankayangʼanira nyumba ya mfumu,* anapempha mtendere. Iwo anachita zimenezi chifukwa dziko lawo linkadalira chakudya chochokera mʼdziko la mfumuyo. 21 Pa tsiku lina lomwe anasankha, Herode anavala zovala zake zachifumu nʼkukhala pampando wake woweruzira milandu ndipo anayamba kulankhula ndi anthu. 22 Anthuwo atamva mawu ake anayamba kufuula kuti: “Amenewa ndi mawu a mulungu, osati a munthu!” 23 Nthawi yomweyo mngelo wa Yehova* anamudwalitsa, chifukwa sanalemekeze Mulungu. Ndipo anadyedwa ndi mphutsi nʼkufa.
24 Koma mawu a Yehova* anapitiriza kufalikira ndipo anthu ambiri anakhala okhulupirira.+
25 Baranaba+ ndi Saulo atamaliza ntchito yopereka thandizo ku Yerusalemu+ anabwerera. Popita anatenga Yohane,+ wotchedwanso Maliko.