2 Mafumu
10 Ku Samariya kunali ana aamuna a Ahabu+ okwana 70. Choncho Yehu analemba makalata nʼkuwatumiza ku Samariya kwa atsogoleri a ku Yezereeli, kwa akuluakulu+ ndiponso kwa anthu amene ankasamalira ana a Ahabu. Mʼmakalatamo analembamo kuti: 2 “Inu muli ndi ana aamuna a mbuye wanu, magaleta ankhondo, mahatchi, mzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ndiponso zida zankhondo. Choncho mukangolandira kalatayi, 3 musankhe mwana mmodzi woyenera ndiponso wabwino pakati pa ana aamuna a mbuye wanu, nʼkumuika pampando wachifumu wa bambo ake. Kenako mumenyere nkhondo nyumba ya mbuye wanu.”
4 Koma iwo atamva zimenezi anachita mantha kwambiri ndipo anati: “Mafumu awiri sanathe kulimbana naye,+ ndiye ife tingalimbane naye?” 5 Choncho woyangʼanira nyumba ya mfumu, woyangʼanira mzinda, akuluakulu komanso amene ankasamalira ana a Ahabu, anatumiza uthenga kwa Yehu, wakuti: “Ife ndife atumiki anu ndipo tichita chilichonse chimene mungatiuze. Sitisankha munthu aliyense kuti akhale mfumu yathu. Inuyo chitani chilichonse chimene mukuona kuti nʼchabwino.”
6 Kenako Yehu anawalemberanso kalata ina yonena kuti: “Ngati muli kumbali yanga ndipo muzimvera mawu anga, mudule mitu ya ana aamuna a mbuye wanu ndipo mawa nthawi ngati yomwe ino mubwere nayo ku Yezereeli kuno.”
Ana 70 a mfumuwo ankakhala ndi akuluakulu a mumzindawo omwe ankawasamalira. 7 Anthuwo atangolandira kalatayo, anatenga ana a mfumu 70 aja nʼkuwapha.+ Kenako anatenga mitu yawo nʼkuiika mʼmadengu ndipo anaitumiza kwa Yehu ku Yezereeli. 8 Munthu wina anapita kwa Yehu kukamuuza kuti: “Mitu ya ana a mfumu ija abwera nayo.” Yehu anati: “Kaiunjikeni milu iwiri pageti la mzinda ndipo ikhale pompo mpaka mʼmawa.” 9 Mʼmawa kutacha, Yehu anapita kukaima patsogolo pa anthu onse nʼkunena kuti: “Anthu inu ndinu osalakwa. Ine ndinachitira chiwembu mbuye wanga ndipo ndinamupha,+ koma ndani wapha anthu onsewa? 10 Tsopano dziwani kuti mawu onse a Yehova otsutsa nyumba ya Ahabu amene Yehova ananena, adzakwaniritsidwa.+ Yehova wachita zimene ananena kudzera mwa mtumiki wake Eliya.”+ 11 Kuwonjezera apo, Yehu anapha anthu onse a mʼbanja la Ahabu amene anatsala ku Yezereeli komanso anthu ake onse olemekezeka, anzake ndiponso ansembe ake+ mpaka onse anatha.+
12 Kenako Yehu ananyamuka kupita ku Samariya. Ali pa ulendowo, anafika panyumba imene abusa ankameteramo ubweya wa nkhosa. 13 Kumeneko Yehu anakumana ndi abale ake a Ahaziya+ mfumu ya Yuda ndipo anawafunsa kuti, “Ndinu ndani?” Iwo anayankha kuti: “Ndife abale ake a Ahaziya ndipo tikupita kukaona ngati ana a mfumu ndi ana a mfumukazi ali bwino.” 14 Nthawi yomweyo Yehu anati: “Agwireni amoyo anthuwa!” Choncho anawagwiradi amoyo nʼkukawaphera pachitsime cha panyumba imene abusa ankameteramo ubweya wa nkhosa. Onse 42 anawapha ndipo palibe amene anamusiya ndi moyo.+
15 Yehu atachoka pamenepo, anakumana ndi Yehonadabu+ mwana wa Rekabu+ amene anabwera kudzakumana naye. Atamupatsa moni,* anamʼfunsa kuti: “Kodi mtima wako wonse uli ndi ine ngati mmene mtima wanga ulili ndi mtima wako?”
Yehonadabu anayankha kuti: “Inde.”
Ndiyeno Yehu anati: “Ngati ndi choncho ndipatse dzanja lako.”
Choncho Yehonadabu anapereka dzanja lake ndipo Yehu anamukweza mʼgaleta lake. 16 Kenako anamuuza kuti: “Tiye tipitire limodzi ukaone kuti sindilekerera zoti anthu azipikisana* ndi Yehova.”+ Choncho Yehonadabu anapita limodzi ndi anthuwo mʼgaleta lankhondo la Yehu. 17 Kenako Yehu anafika ku Samariya ndipo anapha anthu onse a mʼbanja la Ahabu amene anatsala ku Samariya, mpaka onse anatha,+ mogwirizana ndi mawu a Yehova amene anauza Eliya.+
18 Komanso Yehu anasonkhanitsa anthu onse nʼkuwauza kuti: “Ahabu ankalambira Baala pangʼono+ koma Yehu alambira Baala kwambiri. 19 Ndiye itanani aneneri onse a Baala,+ anthu onse amene amamulambira ndiponso ansembe ake onse+ kuti abwere kwa ine. Pasapezeke aliyense wotsala chifukwa ndakonza nsembe yaikulu yoti ndipereke kwa Baala. Aliyense amene sabwera aphedwa.” Koma Yehu anawapusitsa nʼcholinga choti aphe anthu olambira Baala.
20 Ndiyeno Yehu anati: “Lengezani* kuti kuli msonkhano wapadera wa Baala.” Choncho analengezadi. 21 Kenako Yehu anatumiza uthenga ku Isiraeli konse, moti anthu onse olambira Baala anabwera. Palibe amene sanabwere. Iwo analowa mʼkachisi wa Baala+ ndipo kachisiyo anadzaza kuchokera kutsogolo mpaka kumbuyo. 22 Tsopano iye anauza munthu amene ankayangʼanira chipinda chosungira zovala kuti: “Bweretsa zovala zoti anthu onse omwe amalambira Baala avale.” Choncho iye anawabweretseradi zovalazo. 23 Kenako Yehu ndi Yehonadabu+ mwana wa Rekabu analowa mʼkachisimo. Ndiyeno Yehu anauza anthu olambira Baala kuti: “Fufuzani mosamala ndipo muonetsetse kuti muno mulibe aliyense wolambira Yehova, koma olambira Baala okhaokha.” 24 Zitatero, iwo anabwera kudzapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zina. Yehu anali ataika amuna 80 panja nʼkuwauza kuti: “Aliyense amene athawitse munthu, pa anthu amene ndikuwapereka mʼmanja mwanu, moyo wake ulowa mʼmalo mwa munthuyo.”
25 Yehu atangomaliza kupereka nsembe yopserezayo, anauza asilikali ake othamanga ndi othandiza pamagaleta kuti: “Lowani muwaphe! Pasapezeke aliyense wothawira panja.”+ Choncho asilikali othamanga ndi othandiza pamagaletawo anayamba kupha anthuwo ndi lupanga nʼkumaponya mitembo yawo panja. Anakafika mpaka mʼchipinda chamkati* cha kachisi wa Baalayo. 26 Kenako anatulutsa zipilala zopatulika+ za mʼkachisi wa Baala nʼkuzitentha.+ 27 Anagwetsa chipilala chopatulika+ cha Baala ndi kachisi wa Baala+ ndipo malowo anawasandutsa zimbudzi mpaka lero.
28 Choncho Yehu anathetsa kulambira Baala mu Isiraeli. 29 Komabe iye sanasiye kuchita machimo amene Aisiraeli ankachita chifukwa cha Yerobowamu mwana wa Nebati. Machimo ake anali akuti sanachotse mwana wa ngʼombe wagolide amene anali ku Beteli komanso amene anali ku Dani.+ 30 Choncho Yehova anauza Yehu kuti: “Chifukwa chakuti wachita bwino komanso wachita zoyenera kwa ine pochitira nyumba ya Ahabu+ zonse zimene zinali mumtima mwanga, ana ako aamuna adzakhala pampando wachifumu wa Isiraeli mpaka mʼbadwo wa 4.”+ 31 Koma Yehu sanayesetse kutsatira Chilamulo cha Yehova Mulungu wa Isiraeli ndi mtima wake wonse.+ Sanasiye kuchita machimo amene Aisiraeli anachita chifukwa cha Yerobowamu.+
32 Mʼmasiku amenewo, Yehova anayamba kuchepetsa dziko la Isiraeli pangʼono ndi pangʼono. Ndipo Hazaeli anapitiriza kuukira Aisiraeli mʼmadera awo onse.+ 33 Anayambira kumʼmawa kwa Yorodano, ku Giliyadi konse, dera lonse la Gadi, la Rubeni ndi la Manase,+ kuyambira ku Aroweli yemwe ali pafupi ndi chigwa* cha Arinoni mpaka ku Giliyadi ndi Basana.+
34 Nkhani zina zokhudza Yehu, zonse zimene anachita ndiponso mphamvu zake, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Isiraeli. 35 Kenako Yehu, mofanana ndi makolo ake, anamwalira ndipo anamuika mʼmanda ku Samariya. Ndiyeno Yehoahazi+ mwana wake anakhala mfumu mʼmalo mwake. 36 Yehu analamulira Aisiraeli ku Samariya kwa zaka 28.