Ekisodo
31 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 2 “Inetu ndasankha* Bezaleli+ mwana wamwamuna wa Uri, mwana wa Hura wa fuko la Yuda.+ 3 Ndidzamupatsa mzimu wa Mulungu kuti akhale wanzeru, wozindikira komanso wodziwa kupanga zinthu mwaluso pa ntchito iliyonse, 4 kupanga mapulani a mmene angapangire zinthu mwaluso, kupanga zinthu zagolide, zasiliva ndi zakopa, 5 waluso losema miyala ndi kupanga zoikamo miyala+ komanso wodziwa kupanga chilichonse chamatabwa.+ 6 Kuwonjezera pamenepo ine ndaika Oholiabu+ mwana wamwamuna wa Ahisama wa fuko la Dani kuti athandize Bezaleli. Komanso ndaika nzeru mumtima wa anthu onse amene ali ndi luso,* kuti apange zonse zimene ndakulamulazi:+ 7 chihema chokumanako,+ likasa la Umboni,+ chivundikiro+ chimene chili pamwamba pake ndi zipangizo zonse zamʼchihema. 8 Kutinso apange tebulo+ ndi zipangizo zake, choikapo nyale chagolide woyenga bwino ndi zipangizo zake zonse,+ guwa lansembe zofukiza,+ 9 guwa lansembe zopsereza+ ndi zipangizo zake zonse, beseni ndi choikapo chake,+ 10 zovala zolukidwa bwino, zovala zopatulika za Aroni wansembe, zovala za ana ake zoti azivala potumikira monga ansembe,+ 11 mafuta odzozera ndi zofukiza zonunkhira zapamalo opatulika.+ Iwo adzapanga zonse zimene ndakulamula.”
12 Yehova anauzanso Mose kuti: 13 “Uuze Aisiraeli kuti, ‘Muonetsetse kuti mukusunga masiku anga a sabata.+ Chimenechi ndi chizindikiro pakati pa ine ndi inu mʼmibadwo yanu yonse, kuti mudziwe kuti ine Yehova ndakusankhani kukhala opatulika. 14 Muzisunga Sabata chifukwa ndi lopatulika kwa inu.+ Aliyense wosatsatira lamulo lokhudza sabata ayenera kuphedwa ndithu. Munthu aliyense wogwira ntchito pa tsikuli ayenera kuphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake.+ 15 Muzigwira ntchito masiku 6, koma tsiku la 7 likhale sabata lopuma pa ntchito zonse.+ Limeneli ndi tsiku lopatulika kwa Yehova. Aliyense wogwira ntchito pa tsiku la Sabata ayenera kuphedwa. 16 Aisiraeli azisunga Sabata ndipo azichita zimenezi mʼmibadwo yawo yonse. Limeneli ndi pangano mpaka kalekale. 17 Chimenechi nʼchizindikiro pakati pa ine ndi Aisiraeli mpaka kalekale,+ chifukwa mʼmasiku 6, Yehova anapanga kumwamba ndi dziko lapansi, koma pa tsiku la 7 anapuma pa ntchito yake ndipo anasangalala.’”+
18 Ndiyeno atamaliza kulankhula naye paphiri la Sinai, anapatsa Mose miyala iwiri yosema ya Umboni,+ miyala yolembedwa ndi chala cha Mulungu.+