Nyimbo ya Davide yotamanda Mulungu.
א [Aleph]
145 Ndidzakukwezani, inu Mfumu ndi Mulungu wanga,+
Ndidzatamanda dzina lanu kwamuyaya.+
ב [Beth]
2 Ndidzakutamandani tsiku lonse.+
Ndidzatamanda dzina lanu kwamuyaya.+
ג [Gimel]
3 Yehova ndi wamkulu komanso woyenera kutamandidwa kwambiri,+
Palibe amene angamvetse ukulu wake.+
ד [Daleth]
4 Anthu adzatamanda ntchito zanu ku mibadwomibadwo.
Adzanena za ntchito zanu zamphamvu.+
ה [He]
5 Iwo adzanena za mphamvu zanu zodabwitsa+
Ndipo ndidzaganizira mozama za ntchito zanu zodabwitsa.
ו [Waw]
6 Anthu adzanena za zochita zanu zochititsa mantha,
Ndipo ine ndidzalengeza za ukulu wanu.
ז [Zayin]
7 Iwo azidzalankhula mosangalala akadzakumbukira ubwino wanu wochuluka,+
Ndipo adzafuula mosangalala chifukwa cha chilungamo chanu.+
ח [Heth]
8 Yehova ndi wokoma mtima komanso wachifundo,+
Wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi chikondi chokhulupirika.+
ט [Teth]
9 Yehova ndi wabwino kwa aliyense,+
Ndipo ntchito zake zonse zimasonyeza kuti ndi wachifundo.
י [Yod]
10 Ntchito zanu zonse zidzakutamandani, inu Yehova,+
Ndipo okhulupirika anu adzakutamandani.+
כ [Kaph]
11 Iwo adzalengeza za ulemerero wa ufumu wanu+
Komanso adzalankhula za mphamvu zanu,+
ל [Lamed]
12 Kuti anthu adziwe za ntchito zanu zamphamvu+
Ndiponso kukula kwa ulemerero wa ufumu wanu.+
מ [Mem]
13 Ufumu wanu ndi ufumu wamuyaya,
Ndipo ulamuliro wanu udzakhalapo ku mibadwo yonse.+
ס [Samekh]
14 Yehova amathandiza anthu onse amene atsala pangʼono kugwa+
Ndipo amadzutsa onse amene awerama chifukwa cha mavuto.+
ע [Ayin]
15 Zamoyo zonse zimayangʼana kwa inu mwachiyembekezo.
Mumazipatsa chakudya pa nyengo yake.+
פ [Pe]
16 Mumatambasula dzanja lanu
Nʼkukwaniritsa zolakalaka za chamoyo chilichonse.+
צ [Tsade]
17 Yehova ndi wolungama mʼnjira zake zonse,+
Ndipo ndi wokhulupirika pa chilichonse chimene amachita.+
ק [Qoph]
18 Yehova ali pafupi ndi onse amene amamuitana,+
Onse amene amamuitana mʼchoonadi.+
ר [Resh]
19 Amakwaniritsa zolakalaka za anthu amene amamuopa.+
Amamva kufuula kwawo kopempha thandizo ndipo amawapulumutsa.+
ש [Shin]
20 Yehova amayangʼanira onse amene amamukonda,+
Koma oipa onse adzawawononga.+
ת [Taw]
21 Pakamwa panga padzalankhula zotamanda Yehova.+
Zamoyo zonse zitamande dzina lake loyera mpaka kalekale.+