Kalata Yoyamba Yopita kwa Akorinto
5 Mbiri yamvekatu kuti pakati panu pakuchitika chiwerewere*+ ndipo chiwerewere chake ndi choti ngakhale anthu a mitundu ina sachita. Akuti mwamuna wina watengana ndi mkazi wa bambo ake.+ 2 Kodi mukunyadira zimenezi mʼmalo momva chisoni,+ kuti munthu amene wachita zimenezi achotsedwe pakati panu?+ 3 Ngakhale kuti sindili kumeneko, mumzimu ndili komweko, ndipo ndamuweruza kale munthu amene wachita zimenezi, ngati kuti ndili nanu komweko. 4 Mukasonkhana mʼdzina la Ambuye wathu Yesu, mudziwe kuti ndili nanu limodzi mumzimu komanso mumphamvu ya Ambuye wathu Yesu. 5 Choncho mupereke munthu ameneyu kwa Satana+ kuti thupilo liwonongedwe, nʼcholinga choti mzimuwo* upulumutsidwe mʼtsiku la Ambuye.+
6 Kudzitama kwanu si kwabwino. Kodi simukudziwa kuti zofufumitsa zapangʼono zimafufumitsa mtanda wonse wa ufa wokandakanda?+ 7 Chotsani zofufumitsa zakalezo, kuti mukhale mtanda watsopano, popeza ndinu opanda zofufumitsa. Chifukwa Khristu waperekedwa ngati nsembe+ yathu ya Pasika.+ 8 Choncho tiyeni tichite Chikondwerero cha Pasikachi,+ osati ndi zofufumitsa zakale, kapena zofufumitsa zoimira zoipa ndi uchimo, koma ndi mkate wopanda zofufumitsa woimira kuona mtima ndi choonadi.
9 Mʼkalata yanga, ndinakulemberani kuti musiye kugwirizana ndi anthu achiwerewere.* 10 Sindikutanthauza kuti muzipeweratu anthu achiwerewere* amʼdzikoli+ kapenanso adyera, olanda ndi opembedza mafano. Kuti muchite zimenezo, ndiye mungafunike kutuluka mʼdzikoli.+ 11 Koma tsopano ndikukulemberani kuti musiye kugwirizana+ ndi aliyense wotchedwa mʼbale, amene ndi wachiwerewere* kapena wadyera,+ wopembedza mafano, wolalata, chidakwa+ kapenanso wolanda,+ ngakhale kudya naye munthu wotereyu ayi. 12 Nanga ndi udindo wanga kuweruza anthu amene ali kunja?* Kodi inu si paja mumaweruza anthu amene ali mkati, 13 ndipo Mulungu amaweruza amene ali kunja?+ “Mʼchotseni munthu woipayo pakati panu.”+