Kwa Afilipi
1 Ine Paulo limodzi ndi Timoteyo, akapolo a Khristu Yesu, ndikulembera oyera onse amene ndi ophunzira a Khristu Yesu amene ali ku Filipi,+ komanso oyangʼanira ndi atumiki othandiza:+
2 Mulungu Atate wathu komanso Ambuye Yesu Khristu akupatseni kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere.
3 Nthawi zonse ndimathokoza Mulungu wanga ndikakumbukira za inu. 4 Ndimachita zimenezi mʼpemphero langa lililonse lopembedzera limene ndimapereka mosangalala chifukwa cha nonsenu.+ 5 Ndimamuthokoza chifukwa cha chopereka chanu chimene mwakhala mukupereka kuti chithandize pa ntchito yolengeza* uthenga wabwino, kuyambira pa tsiku loyamba mpaka pano. 6 Chifukwa sindikukayikira kuti amene anayambitsa ntchito yabwino kwa inu, adzaipitiriza nʼkuimalizitsa+ mpaka tsiku la Khristu Yesu.+ 7 Nʼzoyenera kwa ine kuti ndiganizire nonsenu mwa njira imeneyi, chifukwa ndinu apamtima panga. Inu amene munandithandiza pa nthawi imene ndinamangidwa maunyolo mʼndende+ komanso poteteza uthenga wabwino ndi kukhazikitsa mwalamulo ntchito yolengeza uthenga wabwino.+ Inu limodzi ndi ine tinapindula ndi kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.
8 Ndipo Mulungu ndi mboni yanga kuti ndikufunitsitsa nditakuonani nonsenu. Chikondi changa pa inu ndi chachikulu ngati chimene Khristu Yesu ali nacho. 9 Ndipo ine ndikupitiriza kupemphera kuti chikondi chanu chipitirize kukula kwambiri,+ limodzi ndi kudziwa zinthu molondola+ komanso kuzindikira zinthu bwino kwambiri.+ 10 Chitani zimenezi kuti muzitha kusankha zinthu zimene ndi zofunikadi kwambiri+ nʼcholinga choti mukhale opanda cholakwa ndiponso osakhumudwitsa ena+ mpaka tsiku la Khristu. 11 Muchite zimenezi kutinso mudzazidwe ndi zipatso zolungama mothandizidwa ndi Yesu Khristu,+ kuti Mulungu alemekezedwe ndi kutamandidwa.
12 Tsopano abale, ndikufuna mudziwe kuti zimene zandichitikira, zathandiza kuti uthenga wabwino ufalikire. 13 Chifukwa Asilikali Oteteza Mfumu ndi ena onse amva+ kuti ndamangidwa+ chifukwa cha Khristu. 14 Ndipo abale ambiri amene akutumikira Ambuye alimba mtima chifukwa cha kumangidwa kwanga, komanso akupitiriza kusonyeza kulimba mtima polankhula mawu a Mulungu mopanda mantha.
15 Nʼzoona kuti ena akulalikira zokhudza Khristu chifukwa akundichitira kaduka komanso akupikisana nane, koma ena akulalikira ndi cholinga chabwino. 16 Achiwiriwa akufalitsa uthenga wokhudza Khristu chifukwa cha chikondi, popeza akudziwa kuti ndinasankhidwa kuti nditeteze uthenga wabwino.+ 17 Koma oyambawo akuchita zimenezo chifukwa cha mtima wokonda mikangano, osati ndi cholinga chabwino. Iwo akungofuna kundiyambitsira mavuto mʼndende muno. 18 Ndiye kodi zotsatira zake nʼzotani? Ndi zoti uthenga wokhudza Khristu ukufalitsidwabe, kaya ndi mwachiphamaso kapena mʼchoonadi ndipo ine ndikusangalala chifukwa cha zimenezi. Ndipotu ndipitirizabe kusangalala 19 chifukwa ndikudziwa kuti zimenezi zidzachititsa kuti ndipulumutsidwe chifukwa cha mapembedzero anu+ komanso ndi thandizo la mzimu wa Yesu Khristu.+ 20 Zimenezi nʼzogwirizana ndi zimene ndikudikirira mwachidwi ndiponso chiyembekezo changa chakuti sindidzachititsidwa manyazi mwa njira iliyonse. Koma kuti mwa ufulu wanga wonse wa kulankhula, tsopano Khristu alemekezedwa kudzera mwa ine,* ngati mmene zakhala zikuchitikira mʼmbuyo monsemu. Iye alemekezedwabe kaya ndikhala ndi moyo kapena ndimwalira.+
21 Chifukwa kwa ine, ndikakhala ndi moyo, ndikhala ndi moyo kuti ndizitumikira Khristu+ ndipo ndikamwalira ndipindula.+ 22 Tsopano ngati ndipitirizabe kukhala ndi moyo mʼthupi limene ndili naloli, ntchito ya manja anga idzawonjezeka, koma choti ndisankhe pamenepa sindinena. 23 Ndagwira njakata kuti ndisankhe chiti pa zinthu ziwirizi, chifukwa ndikulakalaka nditamasulidwa nʼkukakhala ndi Khristu,+ zimene kunena zoona ndi zabwino kwambiri.+ 24 Komabe, ndi bwino kuti ndipitirizebe kukhala ndi moyo mʼthupi limene ndili naloli chifukwa cha inu. 25 Choncho, popeza kuti ndatsimikizira zimenezi, ndikudziwa kuti ndikhalabe ndi moyo ndipo ndipitiriza kukhala ndi nonsenu kuti mupite patsogolo komanso kuti musangalale chifukwa cha chikhulupiriro chanu. 26 Inde, kuti ndikadzabweranso kwa inu chisangalalo chanu chidzasefukire chifukwa ndinu otsatira a Khristu Yesu.
27 Koma chimene ndikungofuna nʼchakuti makhalidwe anu akhale ogwirizana* ndi uthenga wabwino wa Khristu,+ kuti kaya ndabwera kudzakuonani kapena pamene ine kulibe, ndizimva za inu, kuti mukupitirizabe kukhala ogwirizana.*+ Ndipo ndi mtima umodzi, mukuyesetsa mogwirizana kuti mupitirize kukhulupirira uthenga wabwino. 28 Komanso simukuchita mantha mʼnjira iliyonse ndi amene akukutsutsani. Umenewu ndi umboni wakuti adzawonongedwa,+ koma kwa inu, ndi umboni wakuti mudzapulumutsidwa+ ndipo umboni umenewu ndi wochokera kwa Mulungu. 29 Zili choncho chifukwa inu munapatsidwa mwayi, osati wokhulupirira Khristu wokha, komanso wovutika chifukwa cha iye.+ 30 Nʼchifukwa chake inunso mukukumana ndi mavuto ofanana ndi amene munaona ine ndikukumana nawo,+ amene panopa mukumva kuti ndikukumana nawobe.