Ekisodo
35 Kenako Mose anaitana gulu lonse la Aisiraeli nʼkuwauza kuti: “Yehova walamula kuti tizichita zinthu izi:+ 2 Muzigwira ntchito masiku 6, koma tsiku la 7 likhale lopatulika kwa inu, likhale sabata la Yehova lopuma pa ntchito zanu zonse.+ Aliyense wogwira ntchito pa tsikuli adzaphedwa.+ 3 Pa tsiku la Sabata, musamayatse moto mʼmalo anu alionse amene mukukhala.”
4 Ndiyeno Mose anauza gulu lonse la Aisiraeli kuti: “Yehova walamula kuti, 5 ‘Nonse mupereke zopereka kwa Yehova.+ Aliyense amene ali ndi mtima wofunitsitsa+ apereke kwa Yehova zinthu monga golide, siliva, kopa,* 6 ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri, nsalu zabwino kwambiri ndi ubweya wa mbuzi.+ 7 Aperekenso zikopa za nkhosa zonyika mu utoto wofiira, zikopa za akatumbu,* matabwa a mthethe, 8 mafuta a nyale, basamu wopangira mafuta odzozera ndi zofukiza zonunkhira,+ 9 miyala ya onekisi ndi miyala ina yoika pa efodi+ komanso pachovala pachifuwa.+
10 Anthu onse aluso*+ pakati panu abwere ndipo adzapange zinthu zonse zimene Yehova walamula. 11 Adzapange chihema ndi nsalu yoyala pachihemacho, chophimba chake, ngowe zake, mafelemu ake, ndodo zake, zipilala zake ndi zitsulo zake zokhazikapo mafelemu ndi zipilala. 12 Apangenso Likasa+ ndi ndodo zake zonyamulira,+ chivundikiro,+ katani,+ 13 tebulo+ ndi zipangizo zake zonse ndi ndodo zake zonyamulira, mkate wachionetsero,+ 14 choikapo nyale+ zounikira komanso zipangizo zake ndiponso nyale zake ndi mafuta a nyalezo.+ 15 Apangenso guwa lansembe zofukiza+ ndi ndodo zake zonyamulira, mafuta odzozera ndi zofukiza zonunkhira,+ nsalu yotchinga pakhomo la chihema, 16 guwa lansembe zopsereza+ ndi sefa wake wa zitsulo zakopa, ndodo zake zonyamulira ndi zipangizo zake zonse komanso beseni ndi choikapo chake.+ 17 Apange nsalu za mpanda wa bwalo,+ zipilala zake ndi zitsulo zake zokhazikapo zipilalazo, nsalu yotchinga pakhomo la bwalolo, 18 zikhomo za chihema, zikhomo za bwalo ndi zingwe zake.+ 19 Apangenso zovala zolukidwa bwino+ zoti azivala potumikira mʼmalo opatulika, zovala zopatulika za Aroni+ wansembe ndi zovala za ana ake zoti azivala potumikira monga ansembe.’”
20 Choncho gulu lonse la Aisiraeli linachoka pamaso pa Mose. 21 Kenako aliyense amene anali ndi mtima wofunitsitsa,+ komanso aliyense amene anali ndi mzimu wofunitsitsa, anabwera ndipo anabweretsa zopereka kwa Yehova zoti zikagwire ntchito pachihema chokumanako ndi pa utumiki wonse wochitika pamenepo. Anabweretsanso zinthu zopangira zovala zopatulika. 22 Iwo anapitiriza kubwera, amuna pamodzi ndi akazi, aliyense amene anali ndi mtima wofunitsitsa. Anabweretsa zokongoletsera zomanga pazovala, ndolo, mphete ndi zokongoletsera zina komanso zinthu zosiyanasiyana zagolide. Onse anapereka zopereka zawo zagolide* kwa Yehova.+ 23 Ndipo onse amene anali ndi ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri, nsalu zabwino kwambiri, ubweya wa mbuzi, zikopa za nkhosa zonyika mu utoto wofiira ndi zikopa za akatumbu, anabwera nazo. 24 Onse amene anapereka chopereka chasiliva ndi kopa anapereka zoperekazo kwa Yehova, ndipo onse amene anali ndi matabwa a mthethe oti akagwire ntchito pa utumiki wonse wapachihema anabwera nawo.
25 Akazi onse aluso+ anawomba nsalu ndi manja awo, ndipo ankabweretsa zingwe zopota za ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi nsalu zabwino kwambiri. 26 Ndipo akazi onse aluso amene anali ndi mtima wofunitsitsa anawomba nsalu za ubweya wa mbuzi.
27 Atsogoleri anabweretsa miyala ya onekisi komanso miyala ina yoika pa efodi ndi pachovala pachifuwa,+ 28 mafuta a nyale, basamu wopangira mafuta odzozera+ ndi zofukiza zonunkhira.+ 29 Amuna ndi akazi onse amene anali ndi mtima wofunitsitsa anapereka kenakake kuti kathandize pa ntchito imene Yehova analamula kudzera mwa Mose. Aisiraeli anabweretsa zinthu zimenezi ngati nsembe yaufulu kwa Yehova.+
30 Kenako Mose anauza Aisiraeli kuti: “Yehova wasankha Bezaleli, mwana wamwamuna wa Uri, mwana wa Hura wa fuko la Yuda.+ 31 Ndipo wamupatsa mzimu wa Mulungu kuti akhale wanzeru, wozindikira komanso wodziwa kupanga zinthu mwaluso pa ntchito iliyonse. 32 Wodziwa kupanga mapulani a mmene angapangire zinthu mwaluso, kupanga zinthu zagolide, zasiliva ndi zakopa, 33 waluso losema miyala ndiponso kupanga zoikamo miyala komanso wodziwa kupanga mwaluso chilichonse chamatabwa. 34 Mulungu waika luso lophunzitsa mumtima mwa Bezaleli komanso mwa Oholiabu+ mwana wamwamuna wa Ahisama wa fuko la Dani. 35 Iye wawapatsa luso*+ kuti agwire ntchito zonse. Wawapatsa luso lopeta nsalu komanso luso loluka nsalu ndi ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri, nsalu zabwino kwambiri ndi luso lowomba nsalu. Amuna amenewa adzagwira ntchito iliyonse komanso kukonza kapangidwe ka zinthu zosiyanasiyana.”