Nzeru Zathu Zodziŵira Zinthu—Mphatso Zodabwitsa
POWONA ice cream, maso a Luke akhumbira. Pamene akutambasula dzanja kuti atenge cone yopatsidwa kwa iye mwa mawu, mkamwa mwake muchita mate. Iye akwezera chotsekemeracho kukamwa kwake, kununkhiza kukoma kwake pamene akutero. Kenaka, iye alaŵa ubwino wake wozuna ndi kunyambita koyamba kwa ice cream yofeŵa, yozizira.
M’chokumana nacho chosangalatsa chimenechi, Luke akugwiritsira ntchito nzeru [zisanu zodabwitsa] zodziŵira zinthu za thupi lake—kuwona, kumva, kukhudza, kununkhiza, ndi kulaŵa. Komabe tiri ndi nzeru zina zambiri zodziŵira zinthu; ponena za kudziŵa unyinji wake chimadalira pa mmene wina akhumbira kuzigawa izo. Mwachitsanzo, khungu limamva osati kokha kukhudza komanso mkhalidwe wa mphepo (kufunda ndi kuzizira) limodzinso ndi kuwawa. Mkati mwa khutu pambali pa kukhala momvera mawu, mumasamalira kulinganiza kwa nzeru zathu zodziŵira zinthu mogwiritsira ntchito madzi omayenda mkati mwa njira zake zozungulira. Mowonjezerapo, pali mitsempha yolandira zizindikiro m’thupi imene iri ndi thayo kaamba ka nzeru zathu zodziŵira njala ndi ludzu, limodzinso ndi nzeru [zina] zodziŵira zithu.
Chotero, mwanjira ya dongosolo locholoŵanacholoŵana lomvana, thupi lathu limayankha ku zogalamutsa zosiyanasiyana kuyesa mikhalidwe yakuthupi ndi ya zipangizo za mphepo za malo athu otizinga. Lingalirani zachindunji zoŵerengeka.
Diso limalandira mpambo wosalekeza wa zithunzi zowoneka. Kuwala kumawunikiridwa pa mamiliyoni a mitsempha yolandira zizindikiro ya chiŵiya cholandirira zithunzi cha diso (retina), imene imayankha ku cheza cha kuwunika mwakutulutsa zizindikiro zosawoneka mofanana ndi magetsi. Mtsempha waukulu wa diso umapereka zizindikirozo ku ubongo, kumene izo zimazindikiridwa kukhala zithunzithunzi zowoneka.
Khutu liri ndi tiubweya tokhala m’mbali yake ya mkati timene timalandizana m’kumvekera kwa kudukizadukiza kwa mawu amene ito timagwira. Kenaka ito timapereka chidziŵitso chosawoneka mofanana ndi magetsi chimene ubongo wathu umazindikira kukhala mawu.
Kukhudza kuli nzeru yodziŵira zinthu yodalira pa mitsempha yolandira zizindikiro yaing’ono yokhala mkati mwa khungu. Mwachiwonekere, maselo a mitsempha yolandira zizindikiro osiyanasiyana ali ndi thayo lakumva kukhudza kosiyanasiyana, kuwawa, kuzizira, ndi kutentha.
Kulaŵa kuli nzeru yodziŵira zinthu ndi tinsonga tating’ono ta mitsempha totchedwa taste buds. Ndi tinsonga timeneti tokhala kwakukulukulu pa lilime, ndipo pa mlingo wochepera m’mbali zina za kamwa, tingalaŵe chakudya chathu ndi chakumwa.
Kununkhiza kuli kogwirizana kwenikweni ndi kulaŵa. Kudziŵa kodabwitsa kwa maselo a mitsempha yolandira zizindikiro yokhala kumwamba kwa njira ya mphuno kumaitheketsa iyo kuzindikira kokha kachipangizo kamodzi ka zinthu zina zokhala ndi fungo mu mbali 1,000,000,000,000 za mpweya! Koma mmene maselo amenewa amazindikirira fungo ndi kupereka zizindikiro ku mitsempha ya ubongo chikuthetsabe nzeru ofufuza.
Ndithudi, nzeru zathu zodziŵira zinthu ziri mphatso zodabwitsa. Komabe, nchiyani chomwe chimachitika, pamene izo zalemazidwa? Kodi timachita motani? Kodi nchiyani chomwe tingachite?