Lingaliro la Baibulo
Kristu Alipo!
“MANDELA akudza! Mandela akudza!” anaimba motero ana a ku Soweto, South Africa. Kumasulidwa kwa Nelson Mandela mundende pa February 11, 1990, kunayembekezeredwa kwambiri monga chiyambi cha kusintha kwa zinthu mu South Africa. Komabe, zaka zambiri iyeyo asanatuluke m’ndende, chiyambukiro chake chinkamvedwa. Akali kundendeko, anali atachitapo kanthu kusonkhezera “nkhondo yosaneneka ya kuchotsa kusankhana mitundu.” Monga momwe magazini ena opezeka padziko lonse ananenera, zaka 27 za kuikidwa m’ndendezo “sizinathetse kukhalapo kwake—kapena mkhalidwe wake wa nkhondo.” Kumasulidwa kwake m’ndende kumachitira fanizo bwino lomwe za kusiyana kumene kulipo pakati pa kudza ndi kukhalapo.
Mofananamo, ponena za Yesu Kristu akumadzitengera mphamvu ya ufumu wake, olemba Baibulo a m’zaka za zana loyamba amasiyanitsa nkhani ya kudza kwake ndi kukhalapo kwake. Kukhalapo kwa Kristu Yesu mumphamvu ya ufumu kukamvedwa ndi kuzindikiridwa zaka zambiri iye ‘asanadze pamitambo ya kumwamba ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.’ (Mateyu 24:30) Kukhalapo (Chigiriki, pa·rou·siʹa) kosawoneka kwa Kristu kukayambirira kufika kudza (Chigiriki, erʹkho·mai) kwake kudzapereka chiweruzo pambadwo wopanduka ndi woipa kusanafike.
Pa·rou·siʹa—Kodi Limatanthauzanji?
Liwu Lachigriki lakuti pa·rou·siʹa kwenikweni limatanthauza “kukhala pambali pake” ndipo “linakhala liwu lodziŵika ndi kucheza kwa munthu wokhala ndi udindo wapamwamba, [makamaka] kwa mafumu ndi olamulira poyendera chigawo.” Theological Dictionary of the New Testament imati: “[Parousia] amapereka lingaliro [makamaka] la kukhalapo kokangalika.” Ndipo ponena za kukhalapo kwa Kristu Yesu, buku lakuti The Parousia limati: “Malemba samanena konse za ‘Parousia wachiŵiri.’ Mulimonse mmene liwulo linalili, ilo linali kanthu kena kachilendo, kamene sikanachitikepo, ndi kamene sikadzachitikanso. Kunayenera kukhala kukhalapo kosiyana ndi kokwezeka kuposa kuwonekera kwake kulikonse kwa anthu.”
Pothirira ndemanga pamawu a ulosi wa Yesu poyankha mafunso ofunsidwa ndi atumwi pa Phiri la Azitona, Profesa A. T. Robertson mu Word Pictures in the New Testament akulemba kuti Yesu anali “kugwiritsira ntchito chiwonongeko cha kachisi ndi Yerusalemu chimene chinachitika mumbadwo umenewo mu A.D. 70, kukhalanso chizindikiro cha kudza kwake kwachiŵiri ndi cha mapeto a dziko . . . kapena kutha kwa nyengo.” Kodi mafunsowo anali otani, ndipo kodi Yesu anayankha motani?
Chizindikiro cha Kukhalapo kwa Kristu
Monga momwe kwalembedwera pa Mateyu 24:3, atumwiwo anafunsa kuti: “Mutiuze ife zija zidzawoneka liti? ndipo chizindikiro cha kufika kwanu nchiyani, ndi cha mathedwe a nthaŵi ya pansi pano?” Poyankha, Yesu anapatsa ophunzirawo chizindikiro chimene chikakhala umboni wowoneka wa kukhalapo kwake kosawoneka mumphamvu ya Ufumu. Chizindikiro chonse chinaphatikizapo mtundu wa nkhondo zimene sizinachitikepo, kupereŵera kwa chakudya kofalikira, zivomezi zowononga kwambiri, miliri, ndi kuwonjezereka kwa upandu ndi mantha. Kukhalapo kwa Kristu kukakhala nthaŵi ya chipwirikiti cha padziko lonse ndi nkhaŵa. Maboma aumunthu ndi atsogoleri adziko akakhala osakhoza kulimbana mwachipambano ndi dongosolo lomagwa.—Mateyu 24:7, 12; Luka 21:11.
Pogogomezera kuwona kwa mawu a ulosi a Yesu, profesa wa maphunziro a zandale, John Meisel, ananena kuti: “Nyengo yaikulu koposa ikufika kumapeto, yoti iloŵedwe mmalo ndi ina imene mpangidwe wake udakali wosadziŵika bwino.” Atapereka ndemanga pakufa kwa Chikomyunizimu, kulephera kwa Chisosholizimu, ndi kusakhoza kwa chikapitolizimu, Profesa Meisel akupitiriza kunena kuti: “Zovuta zambiri za anthu zili zosatheka kulamuliridwa ndi sayansi ya zitaganya ndipo zifunikira kuthetsedwa ndi njira zina.” Ndipo kodi zimenezo zimatanthauzanji? “Maziko a malingaliro a anthu anzeru omwe analipo akuwonongeka ndipo afunikira kuloŵedwa mmalo ndi ena.”
Kukhalapo kwa Yesu Kokangalika
Mosasamala kanthu za mikhalidwe yothetsa nzeru ya zochitika za dziko lomanyonyosokali, kukhalapo kwa Yesu mumphamvu yaufumu kunayamba zaka zoposa 75 zapitazo ndipo kwakhala kukumvedwa m’njira yosalakwika ndi yotsimikizirika.a Mosasamala kanthu ndi kuwononga kumene kunachititsidwa ndi nkhondo ziŵiri za dziko, Mfumu yokhazikitsidwa pampando, Kristu Yesu, wakhala akutenga mbali mokangalika m’kulinganiza mtundu wa anthu watsopano—anthu a dzina la Yehova “ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe.” Kukhalapo kokangalika kwa Kristu kwasonkhezera programu ya kulalikira kwapadziko lonse ndi kuphunzitsa imene yakhudza mitima ya anthu a maganizo abwino miyandamiyanda. Iwo asonkhezeredwa kuima kumbali ya Ufumu wa Yehova umene uli m’manja mwa Kristu Yesu.—Chivumbulutso 7:9, 10.
Poyang’anizana ndi umboni womawonjezereka tsiku ndi tsiku wakuti chizindikiro chokhala ndi mbali zosiyanasiyana cha kukhalapo kwa Kristu chikukwaniritsidwa, kuli kwachiwonekere kuti Akristu akuchenjezedwa kuti tikuyang’anizana ndi mapeto a nyengo. Tsopano ndiyo nthaŵi ya ‘kupereka chisamaliro choposa cha nthaŵi zonse’ kwa Mfumu yokhazikitsidwa pampandoyo, Kristu Yesu. (Ahebri 2:1) Iye amatilangiza kuti: “Dikirani nyengo zonse, ndi kupemphera, kuti mukalimbike kupulumuka zonse zimene zidzachitika, ndi kuimirira pamaso pa Mwana wa munthu.”—Luka 21:36.
[Mawu a M’munsi]
a Ulamuliro waufumu wa Yesu Kristu unayamba mu 1914. Kuti mupeze mafokozedwe atsatanetsatane a nkhaniyi, onani mitu 16 mpaka 18 ya buku lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi, lofalitsidwa mu 1982 ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.