Lingaliro la Baibulo
Kodi Ana Ayenera Kudzisankhira Chipembedzo Chawo?
KUNGOYAMBIRA pamene mwana wabadwa mpaka unyamata wake, makolo amampangira mwana wawoyo zosankha. Panthaŵi imodzimodziyo, kholo lanzeru limadziŵa pamene liyenera kukhala lololera, nthaŵi zonse kulingalira chimene mwana wake angakonde.
Komabe, kungakhale kovuta kwa makolo kudziŵa mlingo wa ufulu umene mwana angapatsidwe. Pamene zili zoona kuti ana angapange zosankha zabwino ndi kupindula nawo ufulu pa mlingo woyenerera, nzoonanso kuti angapange zosankha zolakwa, zimene zingakhale zatsoka.—2 Mafumu 2:23-25; Aefeso 6:1-3.
Mwachitsanzo, kaŵirikaŵiri ana amasankha chakudya chosamanga thupi m’malo mwa chomanga thupi. Chifukwa? Chifukwa chakuti pausinkhu wanthete, samatha kuganiza mwanzeru paokha. Kodi kungakhale kwanzeru kuti makolo angowalola ana awo kuchita zimene afuna pankhaniyo, namayembekezera kuti potsirizira pake adzasankha zakudya zomanga thupi? Ayi. M’malo mwake, makolo ayenera kuwasankhira ana awo pofuna kuti anawo akhale ndi mtsogolo mwabwino.
Chotero, nkoyenera kuti makolo azisankhira ana awo zakudya, zovala, kapesedwe, ndi khalidwe. Koma nanga bwanji za chipembedzo? Kodi makolo ayenera kuwasankhiranso?
Chosankha
Ena anganene motsutsa kuti makolo sayenera kukakamizira ana awo m’chipembedzo chawo. Ndithudi, zaka zoposa 160 zapitazo, ena omwe ankadzitcha Akristu anayambitsa lingaliro lakuti “ana sayenera kuphunzitsidwa chipembedzo kuopera kuti maganizo awo angatengeke ndi chiphunzitso chakutichakuti, koma muyenera kungowasiya mpaka adzathe okha kupanga chosankha, ndipo nkusankhadi.”
Komabe, ganizo limeneli silikugwirizana ndi lingaliro la Baibulo. Baibulo limagogomezera kuti nkofunika kuphunzitsa ana zikhulupiriro za chipembedzo atangobadwa. Miyambo 22:6 imati: “Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.”
Liwu lachihebri lotembenuzidwa “mwana” limaphatikiza usinkhu woyambira paukhanda mpaka paunyamata. Ponena za kufunika kwa kuphunzira msanga, Dr. Joseph M. Hunt, wa Yunivesite ya Illinois, mu U.S.A., anati: “M’zaka zinayi kapena zisanu zoyambirira za moyo mpamene mwana amakula mofulumira kwambiri ndipo mpamenenso amaumbika mosavuta. . . . Mwinamwake 20 peresenti ya maluso [ake] oyambirira amawaphunzira asanakwanitse chaka chimodzi, kapena theka asanafike zaka zinayi.” Izi zingogogomezera uphungu wouziridwa wa Baibulo kuti nkofunika kuti kuchiyambiyambi kwa moyo wa mwana makolo atsogoze mwanzeru, kumphunzitsa mwana njira za Mulungu.—Deuteronomo 11:18-21.
Kwenikweni, Malemba amalangiza makolo oopa Mulungu kuphunzitsa ana awo kukonda Yehova. Deuteronomo 6:5-7 amati: “Ndipo muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, ndi mphamvu yanu yonse. Ndipo mawu awa ndikuuzani lero, azikhala pamtima panu; ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.” Liwu lachihebri lotembenuzidwa “muziwaphunzitsa mwachangu” lili ndi lingaliro lakunola chipangizo pa mwala. Sikungatheke mwa kungonola kangapo chabe koma kuyenera kuchitidwa mwakhama, mobwerezabwereza. The New English Bible limatembenuza verebu lachihebrilo kuti “bwereza.” Mwachidule, “kuphunzitsa mwachangu” kumatanthauza kukhomereza zokhalitsa.—Miyambo 27:17.
Chotero, makolo achikristu enieni ayenera kusenza thayo lawo mwamphamvu kuti akhomereze zikhulupiriro zachipembedzo chawo mwa ana awo. Sayenera kunyalanyaza thayoli mwa kuwalola ana awo kusankha okha. Izi zikuphatikizapo kupita kumisonkhano ndi “ana” awo. Kumeneko makolo azikhala pamodzi nawo ndi kuwathandiza kumvetsetsa phindu lauzimu limene banja logwirizana lingapeze mwa kumvetsera nkhani za m’Malemba ndi kutengamo mbali.—Deuteronomo 31:12, 13; Yesaya 48:17-19; 1 Timoteo 1:5; 2 Timoteo 3:15.
Thayo la Makolo
Kungomuuza mwana kudya kanthu kena sikumatanthauza kuti mwanayo adzakakonda. Choncho, mayi wanzeru amadziŵa kuphika chakudya chonunkhira kuti chimkondweretse mwanayo. Ndithudi, amakonza chakudyacho kukhala chofeŵa kuti mwanayo akhoze kuchipukusa.
Mofananamo, poyamba mwana angakane malangizo achipembedzo, ndipo kholo lingaone kuti kuyesa kukambitsirana pankhaniyo nkosaphula kanthu. Komabe, uphungu wa Baibulo ngwachimvekere—makolo ayenera kuchita zimene angathe kuti aphunzitse ana awo kuyambira paukhanda. Chotero, makolo anzeru amapangitsa malangizo achipembedzo kukhala osangalatsa mwa kuwapereka mwanjira imene imakondweretsa mwanayo, polingalira luntha lake lochepalo kuti awamvetsetse.
Makolo achikondi ngakhama ndi thayo la kupezera ana awo zofunika za moyo, ndipo nthaŵi zambiri palibe wina amadziŵa bwinopo zosoŵa za mwana kuposa makolo. Mogwirizana ndi zimenezi, Baibulo limapatsa makolo, makamaka atate—thayo lalikulu lowasamalira mwakuthupi ndi mwauzimu. (Aefeso 6:4) Choncho, makolo sayenera kuzemba thayo lawo mwa kulisiyira winawake. Ngakhale kuti angayamikire chithandizo choperekedwa, ichi chidzangowonjezera, osati kuloŵa m’malo mwa chiphunzitso cha makolo.—1 Timoteo 5:8.
Nthaŵi ina m’moyo, munthu aliyense amasankha zikhulupiriro zachipembedzo zimene akufuna kutsatira, ngati zilipo nkomwe zomwe angakonde. Ngati makolo achikristu asenza thayo lakupatsa ana awo malangizo achipembedzo kuyambira paukhanda ndipo ngati agwiritsira ntchito nthaŵi imeneyi kuwalangiza kulingalira pa maziko a mapulinsipulo abwino, chosankha chimene anawo angapange pambuyo pake m’moyo chingakhale choyenera.—2 Mbiri 34:1, 2; Miyambo 2:1-9.
[Mawu a Chithunzi patsamba 20]
The Doré Bible Illustrations/Dover Publications, Inc.