Kupsinjika Maganizo—“Poizoni Wowononga Pang’onopang’ono”
“Nthaŵi zonse timamva anthu akunena kuti, ‘Osamada nkhaŵa kwambiri ungadwale.’ Mwina sazindikira kuti zimenezo zimachitikadi.”—anatero Dr. David Felten.
JILL ndi wosakwatiwa, ali ndi mwana wamwamuna wachinyamata, ndalama zake kubanki zikutha, ndipo sagwirizana ndi makolo ake, motero ali ndi zifukwa zambiri zodandaulira. Mosayembekezereka padzanja lake panatuluka chotupa chomwe chimanyerekesa ndi kuŵaŵa kwambiri. Anayesera kupakapo mankhwala osiyanasiyana otchedwa antibiotic, cortisone cream, ndi antihistamine, koma palibe mwa ameneŵa amene anathandiza. M’malo mwake zotupa zinafalikira thupi lonse kuphatikizapo kumaso kwake. Nkhaŵa yake inali kukulirakulira.
Jill anamtengera kuchipatala choona za khungu kumene amafunsa za mmene malingaliro a wodwalayo alili. “Timayesetsa kuti tipeze zimene zikuwachitikira pamoyo wawo,” anatero Dr. Thomas Gragg, mmodzi mwa oyambitsa chipatalacho. Kaŵirikaŵiri amapeza kuti kuwonjezera pa mankhwala, anthu okhala ndi khungu louma amafunika kuwathandiza pakupsinjika maganizo. Dr. Gragg anavomereza kuti, “Kunena kuti malingaliro amayambitsa matenda a pakhungu, kukhoza kukhala kunama, koma titha kunena kuti kalingaliridwe ka munthu kakhoza kupangitsa kuti pakhale mpata woti munthu agwidwe matenda pakhungu, motero sitiyenera kumangopereka mankhwala posamthandiza munthuyo kuchepetsa kupsinjika maganizo m’moyo wake.”
Jill anapeza kuti kuphunzira kusakhala wopsinjika maganizo kunateteza khungu lake. Iye anati, “Ndimapsabe mtima, koma khungu langa sikuti ndilowonongeka monga muja linalili.” Zodabwitsa? Ayi ndithu. Madokotala ambiri amakhulupirira kuti kupsinjika maganizo ndiko kumapangitsa kuti pakhale matenda ambiri akhungu monga hives, psoriasis, acne, ndi eczema. Koma kupsinjika maganizo kukhoza kuwononga zambiri koposa khungu chabe.
Kupsinjika Maganizo ndi Mphamvu Yanu Yotetezera Thupi
Kufufuza kwaposachedwa kwasonyeza kuti kupsinjika maganizo kukhoza kuwononga mphamvu yanu yotetezera thupi, motero zikumapangitsa kuti mukhale pangozi yogwidwa ndi matenda osiyanasiyana. Ronald Glaser, katswiri wa tizilombo tonyamula matenda anati, “Simudwala ndi kupsinjika maganizoko ayi, koma kumangokulitsa mpata woti mudwale matenda ena chifukwa cha zimene kumachita pa chitetezo chanu cha m’thupi.” Pali umboni wogwira mtima kwambiri wakuti kupsinjika maganizo kumadwalitsa chimfine, ndi zotupa pakhungu. Ngakhale kuti timakhala nawo mavairasi amenewo, mwachibadwa mphamvu yathu yoteteza matenda m’thupi imalimbana nawo. Koma akatswiri ena amati pamene munthu ali wopsinjika maganizo, chitetezo chimenechi chimalephera kugwira ntchito.
Zomwe zimachitikadi sanafike pozimvetsetsa bwino, koma ena amati mahomoni amene amapangitsa kuti mukhale okonzeka kuchita kanthu pamene maganizo anu apsinjika amalepheretsa mphamvu yanu yoteteza m’thupi kugwira ntchito bwino pamene akuyenda m’magazi anu. Kaŵirikaŵiri, izi sizodetsa nkhaŵa chifukwa mahomoni ameneŵa amagwira ntchito kwakanthaŵi kochepa chabe. Komabe, ena amati ngati munthu akhala wopsinjika maganizo kwambiri ndipo kwa nthaŵi yaitali, mphamvu yoteteza m’thupi mwake imachepa mwakuti sachedwa kugwidwa matenda.
Izi zikhoza kutithandiza kulongosola chifukwa chake madokotala a ku Canada anayerekezera kuti pakati pa 50 ndi 70 peresenti ya omwe amabwera kufuna chithandizo amakhala ndi mavuto okhudzana ndi kupsinjika maganizo, monga kudwala mutu, kulephera kugona, kuledzera ndi ntchito, ndiponso matenda a m’mimba. Ku United States, chiŵerengerocho akuchiyerekezera kuti chimafika pa 75 mpaka 90 peresenti. Dr. Jean King amaona kuti sangakhale akukuza zinthu ndi mkamwa ngati atati: “Kupsinjika maganizo kwambiri ndi poizoni wakupha pang’onopang’ono.”
Sindiko Chopangitsa Chokha Komanso Sindiko Mankhwala Okha
Ngakhale kuti pali zomwe tanena kalezo, asayansi sakhulupirira kuti kupsinjika maganizo kokha kungakhudze chitetezo cha m’thupi cha munthu kwakuti nkupangitsa munthu kudwala. Motero sitinganene mwatchutchutchu kuti aliyense amene ali wopsinjika maganizo, ngakhale wopsinjika maganizo kwambiri, kuti akhoza kudwala. Chimodzimodzinso, sitinganene kuti ngati uli wosapsinjika maganizo ndiye ukhala ndi thanzi labwino, ndiponso si kwabwino kukana mankhwala chifukwa cha malingaliro akuti matenda akhoza kutha ngati mwatsimikiza mumtima kuti mudzachira. Dr. Daniel Goleman anachenjeza kuti: “Kalingaliridwe kameneka kakuti matenda onse akhoza kutha malinga ngati ukhulupirira kuti zitero, kapangitsa chisokonezo ndi kusamvetsetsa pa za mmene matenda angakhudzirane ndi malingaliro, ndipo mwina kuposa apo kupangitsa anthu kumadzimva olakwa chifukwa chokhala ndi matenda ena, amaona monga chizindikiro cha kukhala osalingalira bwino kapena kukhala osayenera mwauzimu.”
Motero nkoyenera kuzindikira kuti chopangitsa matenda sichikhala chinthu chimodzi. Komabe, popeza pali kugwirizana pakati pa kupanikizika maganizo ndi matenda, zimangosonyeza kufunika kwa kuphunzira kuchepetsako “poizoni wakupha pang’onopang’ono” ameneyo nthaŵi iliyonse pamene kungakhale kotheka.
Tisanalongosole mmene zimenezi zingachitidwire, tiyeni tiyambe tapenda mmene kupanikizika maganizo kumakhalira ndiponso mmene nthaŵi zina kungakhalire kwabwino kwa inu.
[Bokosi patsamba 23]
Matenda Ena Amene Amakhudzana ndi Kupsinjika Maganizo
• ziŵengo
• nyamakazi
• asima
• msana, khosi, ndi kuwawa kwa mapewa
• chimfine
• tondovi
• kutsegula m’mimba
• kuwawa kwa m’mimba
• mutu
• matenda a mtima
• kulephera kugona
• litsipa
• zilonda za m’mimba
• kulephera kugwira ntchito kwa ziwalo zogonanirana
• matenda a khungu
[Chithunzi patsamba 24]
Anthu ambiri amapita kwa dokotala chifukwa cha kupsinjika maganizo