Mutu 12
Munthu Wolemera mu Hade
POPEZA kuti hade ndi manda onse chabe a mtundu wa anthu wakufa, kodi n’chifukwa ninji Baibulo limanena za munthu wolemera kukhala akubvutika ndi mazunzo m’moto wa Hade? Kodi kumene’ku kumasonyeza kuti Hade, kapena pafupi-fupi mbali yake imodzi, ali malo a chizunzo cha moto?
Ophunzitsa helo wamoto mwaphamphu amasonyeza cholembedwa chimene’chi kukhala umboni wotsimikizirika wakuti kuli’di helo wa chizunzo amene akuyembekezera oipa. Koma, m’kutero, iwo amanyalanyaza mau omvekera bwino ndi obwerezedwa-bwerezedwa a Baibulo onga ngati: “Moyo wochimwa’wo ndiwo udzafa” (Ezekieli 18:4, 20) Ndi: “Akufa sadziwa kanthu bi.” (Mlaliki 9:5) Moonekera bwino mau amene’wa samachirikiza lingaliro la kuzunzidwa kwa “miyoyo yotayika” mu helo wamoto.
Chifukwa cha chimene’cho chiphunzitso cha Baibulo chonena za mkhalidwe wa akufa chimasiya atsogoleri ambiri achipembedzo a Chikristu cha Dziko ali mu mkhalidwe wobvuta. Bukhu leni-leni’lo limene iwo amanena kukhala akuzikapo ziphunzitso zao, Baibulo, limaombana ndi ziphunzitso zao. Komabe, modziwa kapena mosadziwa, iwo amaona kukhala okakamizika kumka m’Baibulo kukagwiramo kanthu kena kochirikiza nsonga yao, mwa njira imene’yo akumadzichititsa okha ndi ena kusaona choonadi. Kawiri-kawiri kumene’ku kumachitidwa mwadala.
Ndipo’nso, ofuna-funa choonadi oona mtima amafuna kudziwa chimene chiri choyenera. Iwo amazindikia kuti iwo akhala akungodzinyenga ngati iwo akakana mbali zina za Mau a Mulungu pamene akunena kuti akuzika zikhulupiriro zao pa mbali zina. Iwo amafuna kudziwa chimene Baibulo limanena kweni-kweni ponena za mkhalidwe wa akufa. Ndipo, kuti adzadzitse chithunzi-thunzi’cho, iwo amafuna kudziwa tanthauzo la zimene zanenedwa ponena za munthu wolemera amene anazunzika m’Hade, ndi m’mene zimene’zo zikugwirizanira ndi mbali ina yonse ya Baibulo.
Anali Yesu Kristu amene ananena za munthu wina wolemera ndipo’nso wopempha-pempha Lazaro. Mau ake akupeza pa Luka 16:19-31 ndipo amati:
“Panali munthu mwini chuma amabvala chibakuwa ndi nsalu yabafuta, nasekera, nadyerera masiku onse; ndipo wopempha-pempha wina, dzina lake Lazaro, adaikidwa pakhomo pake wodzala ndi zironda, ndipo anafuna kukhuta ndi zakugwa pa gome la mwini chuma’yo; komatu agalu’nso, anadza nanyambita zironda zake. Ndipo kunali kuti wopempha-pempha’yo adafa, ndipo kuti anatengedwa iye ndi angelo kunka ku chifuwa cha Abrahamu.
“Ndipo mwini chuma’yo adafa’nso, naikidwa m’manda. Ndipo m’Hade anakweza maso ake, pokhala nao mazunzo, naona Abrahamu patali, ndi Lazaro m’chifukwa mwake. Ndipo anakweza mau nati, Atate Abrahamu, mundichitire chifundo, mutume Lazaro, kuti abviike nsonga ya chala chake m’madzi, naziziritse lilime langa; pakuti ndizunzidwa’di m’lawi iri la moto. Koma Abrahamu anati, Mwana, kumbukira kuti unalandira zokoma zako pakukhala m’moyo iwe, momwemo’nso Lazaro zoipa; ndipo tsopano iye asangalatsidwa pano, koma iwe uzunzidwa’di. Ndipo pamwamba pa izi, pakati pa ife ndi inu pakhazikika phompho lalikulu, kotero kuti iwo akufuna kuoloka kuchokera kuno kunka kwa inu sangathe, kapena kuchokera kwanuko kuyambuka kudza kwa ife, sangathe’nso. Koma anati, Pamenepo ndikupemphani, Atate, kuti mum’tume ku nyumba ya atate wanga; pakuti ndiri nao abale asanu; awachitire umboni iwo kuti iwo’nso angadze ku malo ano a mazunzo. Koma Abrahamu anati, Ali ndi Mose ndi aneneri; amvere iwo. Koma anati, Iai, Atate Abrahamu, komatu ngati wina akapita kwa iwo wochokera kwa akufa adzasandulika mtima. Koma anati kwa iye, Ngati samvera Mose ndi aneneri, sadzakopeka mtima ngakhale wina akauka kwa akufa.”
Onani zimene zikunenedwa ponena za munthu wolemera’yo. Kodi n’chifukwa ninji iye anazunzidwa m’Hade? Kodi iye anali atachitanji? Yesu sananene kuti munthu wolemera’yo anali ndi moyo woipa, kodi anatero? Zokha zimene Yesu ananena zinali zakuti munthu’yo anali wolemera, anabvala bwino ndipo anadya motayikira. Kodi khalidwe lotero’lo mwa iro lokha limayenerera chirango mwa chizunzo? Zoona, cholakwa chachikulu chikusonyezedwa m’khalidwe la munthu wolemera’yo kulinga kwa Lazaro wopempha-pempha’yo. Munthu wolemera’yo sanachitire chifundo. Koma kodi cholakwa chotero’cho chinam’siyanitsa mokwanira ndi Lazaro?
Talingalirani zimene Yesu ananena ponena za Lazaro. Kodi muli chiri chonse m’cholembedwa’cho chotichititsa kunena kuti, ngati mkhalidwe’wo ukanasinthidwa, Lazaro akanakhala munthu wachifundo? Kodi timawerenga kuti Lazaro anadzipangira mbiri ya ntchito zabwino kwambiri kwa Mulungu, yomachititsa kufika kwake “m’chifukwa cha Abrahamu,” ndiko kuti, malo a chiyanjo cha Mulungu? Yesu sananene zimene’zo. Iye anangolongosola Lazaro kukhala wopempha-pempha wodwala.
Chotero kodi n’koyenera kunena kuti opempha-pempha onse odwala adzalandira madalitso a Mulungu pa imfa, pamene anthu onse olemera adzapita ku malo a chizunzo chozindikira? Kutali-tali. Kupempha-pempha mwa iko kokha sindiko chizindikiro cha chiyanjo cha Mulungu. Mosemphana ndi zimene’zo, Baibulo liri ndi mau a pemphero akuti: “Musandipatse umphawi, ngakhale chuma.” (Miyambo 30:8) Ndipo ponena za nthawi yake, Mfumu Davide analemba kuti: “Sindinapenya wolungama wasiyidwa, kapena mbumba zake zirinkupempha chakudya.”—Salmo 37:25.
Ngati titatenga mau a Yesu monga momwe aliri, tikafunikira kupeza malingaliro ena’nso amene akapangitsa fanizo’lo kukhala lodabwitsa’di. Amene’wa akuphatikizamo; Kuti awo okhala ndi chimwemwe chakumwamba ali okhoza kuona kuti kulankhula ndi awo ozunzidwa mu Hade. Kuti madzi okangamira ku nsonga ya chala cha munthu samaumitsidwa ndi moto wa Hade. Ndipo, kuti, ngakhale kuli kwakuti chizunzo cha Hade n’chachikulu, dontho chabe la madzi likadzetsa mpumulo kwa wobvutika’yo.
Zitamvedwa monga momwe ziriri, kodi zinthu zimene’zi zikumveka kukhala zoyenera kwa inu? Kapena, kodi m’malo mwake, mukulingalira kuti zimene Yesu ananena sizinayenera kumvedwa monga momwe ziriri? Kodi pali njira iri yonse yotsimikizirira?
“MWINI CHUMA” NDI “LAZARO” ADZIWIKITSIDWA
Pendani mau a pambuyo ndi patsogolo. Kodi Yesu anali kulankhula ndi yani? Pa Luka 16:14 tikuuzidwa kuti: “Koma Afarisi, ndiwo okonda ndalama, anamva izi zones; ndipo anam’seka.”
Popeza kuti Yesu analankhula Afarisi akumva, kodi iye anali kulongosola chochitika cheni-cheni kapena kodi iye anali kungogwiritsira ntchito fanizo? Ponena za njira ya Yesu yophunzitsira makamu, timawerenga kuti: “Ndipo kopanda fanizo sanalankhula kanthu kwa iwo.” (Mateyu 13:34) Chifukwa cha chimene’cho, cholembedwa chonena za munthu wolemera ndi Lazaro chiyenera kukhala fanizo.
Fanizo limene’li mwachionekere linalunjikitsidwa kwa Afarisi. Monga kagulu iwo anali ngati munthu wolemera. Iwo anakonda ndalama, kudza’nso kuchuka ndi maina aulemu okometsera. Ponena za iwo Yesu anati: “Amachita ntchito zao zonse kuti aonekere kwa anthu; pakuti akulitsa chitando chake cha njirisi zao, nakulitsa mphonje, nakonda malo a ulemu pamapwando, ndi mipando ya ulemu m’masunagoge, ndi kulankhulidwa m’misika, ndi kuchedwa ndi anthu, Rabi.”—Mateyu 23:5-7.
Afarisi ananyozetsa ena, maka-maka okhometsa msonkho, akazi achigololo ndi ena okhala ndi mbiri ya kukhala ochimwa. (Luka 18:11, 12) Pa chochitika china pamene asilikali otumidwa kukagwira Yesu, anabwera opanda kanthu chifukwa cha kukhala atagwidwa mtima ndi kuphunzitsa kwake, Afarisi ananena kuti: “Kodi mwasokeretsedwa inu’nso? Kodi wina wa akulu anakhulupirira Iye, kapena wa Afarisi? Koma khamu iri losadziwa chilamulo, likhala lotembereredwa.”—Yohane 7:47-49.
Chifukwa cha chimene’cho, m’fanizo lonena za Lazaro wopempha-pempha’yo amaimira bwino lomwe anthu onyozeka amane’wo amene Afarisi anawonyoza koma amene analapa nakhala otsatira a Yesu Kristu. Yesu anasonyeza kuti ochimwa onyozedwa amene’wa, atalapa, akapeza malo a chiyanjo cha Mulungu, pamene Afarisi ndi atsogoleri ena ochuka achipembedzo monga kagulu akalephera. Iye anati: “Indetu ndinena kwa inu, kuti amisonkho ndi akazi achiwerewere amatsogolera inu, kulowa mu Ufumu wa Kumwamba. Popeza Yohane anadza kwa inu m’njira ya chilungamo, ndipo simunam’mvera iye; koma amisonkho ndi akazi achiwerewere anamvera iye; ndipo inu, m’mene munachiona, simunalapa pambuyo pake, kuti mumvere iye.”—Mateyu 21:31, 32.
IMFA YA “MWINI CHUMA” NDI YA “LAZARO”
Pamenepa, kodi n’chiani, chimene chikutanthauzidwa ndi imfa ya “munthu mwini chuma” ndi ya “Lazaro”? Sitifunikira kunena kuti imanena za imfa yeni-yeni. Monga momwe yagwiritsiridwira ntchito m’Baibulo, imfa ingaimire’nso kusintha kwakukukulu mu mkhalidwe wa anthu. Mwa chitsanzo: Anthu olondola njira ya moyo yosemphana ndi chifuniro cha Mulungu amanenedwa kukhaka ‘akufa m’zolakwa ndi machimo.’ Koma pamene iwo afika m’kaimidwe kobvomerezeka pamaso pa Mulungu monga ophunzira a Yesu Kristu iwo amanenedwa kukhala akukhala’nso ndi “moyo.” (Aefeso 2:1, 5; Akolose 2:13) Pa nthawi imodzi-modzi’yo anthu amoyo otero’wo amakhala “akufa” ku uchimo. Timawerenga kuti: “Mudziwerengere inu nokha ofafa ku uchimo, koma amoyo kwa Mulungu mwa Kristu Yesu.”—Aroma 6:11.
Popeza kuti onse awiri “mwini chuma” ndi “Lazaro” a m’fanizo la Yesu mwachionekere ali ophiphiritsira, moyenerera imfa yao iri’nso yophiphiritsira. Koma kodi iwo akufa m’lingaliro lotani?
Mfungulo yoyankhira funso limene’li iri m’zimene Yesu ananena asanayambe kunena fanozo’lo: “Yense wakusudzula mkazi wake, nakwatira wina, achita chigololo; ndipo iye mene akwatira wosudzulidwa’yo achita chigololo.” (Luka 16:18) Mau amene’wa angaonekere kukhala osagwirizana kotheratu ndi fanizo’lo. Koma siziri choncho.
Mwa chilamulo cha Mose mtundu wa Israyeli unali mu unansi wa pangano ndi Mulungu ndipo chifukwa cha chimene’cho ukanatha kunenedwa kukhala mkazi kwa iye. Pa Yeremiya 3:14, mwa chitsanzo, Mulungu akunena kwa mtundu’wo monga mkazi wosakhulupirika kuti: “Bwererani ananu obwerera, ati Yehova; pakuti Ine ndine mbuye [mwamuna] wanu.” Ndiyeno, mwa kudza kwa Yesu, mwai unaperekedwa kwa Ayuda wa kukhala mbali ya “mkwatibwi” wake. Ndicho chifukwa chake Yohane M’batizi ananena kwa ophunzira ake kuti: “Inu nokha mundichitira umboni, kuti ndinati, Sindine Kristu, koma kuti ndiri wotumidwa m’tsogolo mwake mwa Iye. Iye amene ali naye mkwatibwi ali mkwati, koma mnzake wa mkati’yo, wakuimirira ndi kumvera iye, akondwera kwakukulu chifukwa cha mau a mkwati’yo; chifukwa chake chimwemwe changa chimene chakwanira. Iyeyo [Yesu] ayenera kukula koma ndi ndichepe.”—Yohane 3:28-30.
M’malo mwakuti akhale mbali ya “mkwatibwi” wa Kristu, Ayuda anayera kumasulidwa ku Chilamulo chimene chinawapangitsa, kunena mophimphiritsira, kukhala mkazi wa Mulungu. Popanda chimasuko chotero’cho, iwo sakanalowa mu unansi wa ukwati ndi Kristu monga mkazi, pakuti umene’wo ukanakhala unansi wachigololo. Mau a Aroma 7:1-6 akutsimikizira chimene’chi:
“Nanga kodi simudziwa, abale, pakuti ndilankhula ndi anthu akudziwa lamulo, kuti lamulo’lo lichita ufumu pa munthu nthawi zones iye ali wamoyo? Pakuti mkazi wokwatidwa amangidwa ndi lamulo kwa mwamuna wake wamoyo; koma mwamuna’yo akafa, iye amasulidwa ku lamulo la mwamuna’yo. Ndipo chifukwa chake, ngati iye akwatiwa ndi mwamuna wina, pokhala mwamuna wake wamoyo, adzanenedwa mkazi wachigololo; koma mwamuna’yo akafa, iye amasulidwa ku lamulo’li; chotero sakhala wachigololo ngati akwatiwa ndi mwamuna wina.
“Chotero, abale anga, inu’nso munayesedwa akufa ku chilamulo ndi thupi la Kristu; kuti mukakhale ake a wina, ndiye amene anaukitsidwa kwa akufa, kuti ife tim’balire Mulungu zipatso . . . Tsopano tinamasulidwa kuchilamulo, popeza tinafa kwa ichi chimene tinagwidwa nacho kale; chotero kuti titumikire mu mzimu watsopano, si m’chilembo chakale ai.”
Pamene imfa ya Yesu Kristu inali maziko omasulira Ayuda ku Chilamulo, ngakhale imfa yake isanakhale anthu olapa anatha kulowa mu mkhalidwe woyanjidwa ndi Mulungu monga ophunzira a Mwana wake. Uthenga ndi ntchito ya Yohane M’batizi ndi ya Yesu Kristu zinatsegula khomo kwa Ayuda kuti apeze mwai wa kupeza chibvomerezo cha Mulungu ndi kukhala oyenera cholowa cha kumwamba monga ziwalo za mkwatibwi wa Kristu. Monga momwe Yesu iye mwini analongosolera kuti: “Kuyambira masiku a Yohane M’batizi, kufikira tsopano lino, Ufumu wa Kumwamba uli wokangamizidwa, ndipo okangamira’wo aukwatula ndi mphamvu.”—Mateyu 11:12.
Chifukwa cha chimene’cho, ntchito ndi uthenga wa Yohane M’batizi ndi wa Yesu Kristu zinayamba kuchititsa kusintha kotheratu mu mkhalidwe wa “mwini chuma” ndi “Lazaro” ophiphiritsira’wo. Timagulu tonseto tinafa ku mkhalidwe wao wakale. Kagulu ka “Lazaro” kolapa’ko kanalowa mu mkhalidwe wa chiyanjo cha Mulungu, pamene kagulu ka “mwini chuma” kanalowa m’kupanda chiyanjo cha Mulungu chifukwa cha kupitirizabe m’kusalapa. Pa nthawi ina kagulu ka “Lazaro” kanayang’ana kwa Afarisi ndi atsogoleri ena achipembedzo a Chiyuda kaamba ka “nyenyeswa za chakudya” chauzimu. Koma kupereka kwa Yesu choonadi kwa iwo kunakwaniritsa zosowa zao zauzimu. Poyerekezera kudyetsa kwauzimu koperekedwa ndi Yesu ndi kuja kwa atsogoleri achipembedzo, Baibulo limasimba kuti: “Makamu a anthu anazizwa ndi chiphunzitso chake: pakuti anawaphunzitsa monga mwini mphamvu, wosanga alembi ao.” (Mateyu 7:28, 29) Ndithudi kusintha kotheratu kunali kutachitika. Atsogoleri achipembedzo a Chiyuda anasonyezedwa kukhala opanda kanthu koti apereke ku kagulu ka “Lazaro.”
Pa tsiku la Pentekoste wa chaka cha 33 C.E. kusintha m’mikhalidwe’ko kunachitidwa. Pa nthawi imene’yo pangano latsopano linalowa m’malo mwa pangano lakale Lachilamulo. Awo amene anali atalapa ndi kulandira Yesu pa nthawi imene’yo anamasulidwa kotheratu ku pangano lakale Lachilamulo. Iwo anafa ku iro. Pa tsiku limene’lo la Pentekoste panali’nso umboni wosalakwika wakuti ophunzira a Yesu Kristu anali atakwezedwa kwambiri koposa Afarisi ndi atsogoleri ena ochuka achipembedzo. Osati atsogoleri achipembedzo a Chiyuda, koma ophunzira amene’wa analandira mzimu wa Mulungu, ukumawatheketsa kulankhula “[zinthu] zazikulu za Mulungu” m’zinenero za anthu ochokera m’malo akutali osiyana-sinyana. (Machitidwe 2:5-11) Ha, chimene’chi chinali chisonyezero chodabwitsa chotani nanga cha kukhala kwao ndi dalitso ndi chibvomerezo cha Mulungu! Kagulu ka Lazaro kanali katalowa’di mu mkhalidwe woyanjidwa mwa kukhla mbeu yauzimu ya Abrahamu Wamkulu kwambiri’yo, Yehova. Umene’wu unaphiphiritsiridwa ndi “chifuwa.”—Yerekezerani ndi Yohane 1:18.
Ponena za Afarisi osalapa ndi atsogoleri achipembedzo ena ochuluka’wo, iwo anali akufa kumalo ao akale oonekera kukhala achiyanjo’wo. Iwo anali mu “Hade.” Pokhala osalapa, iwo analekanitsidwa ndi ophunzira a Yesu monga ngati ndi “phompho lalikulu.” Limene’li linali “phompho” la chiweruzo cholungama ndi chosasintha cha Mulungu. Ponena za limene’li timawerenga m’Lemba kuti: “Maweruzo anu akunga chozama chachikulu.”—Salmo 36:6
CHIZUNZO CHA “MWINI CHUMA”
Kagulu ka “mwini chuma” kanazunzidwa’nso. Motani? Mwa mauthenga a Mulungu achiweruzo amoto omalengezedwa ndi ophunzira a Yesu.—Yerekezerani ndi Chibvumbulutso 14:10.
Chakuti atsogoleri achipembedzo anazunzidwa ndi uthenga wolengezedwa ndi ophunzira a Yesu sipangakhale chikaikiro. Iwo anayesa-yesa mwamphamvu kuletsa kulengeza’ko. Pamene atumwi a Yesu anadzitetezera pamaso pa khothi lalikulu Lachiyuda lokhala ndi amuna ochuka achipembedzo, oweruza’wo “analaswa mtima, nafuna kuwapha.” (Machitidwe 5:33) Pambuyo pake, kudzitetezera kwa wophunzira Stephano kunali ndi chiyambukiro chozunza chofanana’cho pa ziwalo za khothi limene’lo. “Analaswa mtima, nam’kukutira mano.”—Machitidwe 7:54.
Atsogoleri achipembedzo amene’wa anafuna kuti ophunzira a Yesu adze ndi ‘kuziziritsa lirime lao.’ Iwo anafuna kuti kagulu ka “Lazaro” kachoke “m’chifuwa” cha chiyanjo cha Mulungu ndi kupereka uthenga wake m’njira yakuti usawachititse ululu. Mofananamo, iwo anafuna kuti kagulu ka “Lazaro” kasukuluze uthenga wa Mulungu kotero usaike ‘abale ao asanu,’ ogwirizana nao ao achipembedzo, mu “malo a chizunzo.” Inde, iwo sanafune ali yense wa ogwirizana nawo ao kuti azunzidwe ndi mauthenga a chiweruzo’wo.
Koma, monga momwe kwasonyezedwera ndi fanizo la Yesu, kagulu ka “mwini chuma” ngakhale’nso ogwirizana nawo ake achipembedzo sakapewetsedwa konse ziyambukiro zozunza za uthenga wolengezedwa ndi kagulu ka “Lazaro.” Atumwi a Ambuye Yesu Kristu anakana kusukuluza uthenga’wo. Iwo anakana kuleka kuphunzitsa za dzina la Yesu. Yankho lao ku khothi lalikulu Lachiyuda linali lakuti: “Tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira koposa anthu.”—Machitidwe 5:29, NW.
Ngati ogwirizana naye achipembedzo a “mwini chuma” anafuna kupewa chizunzo chimene’cho, iwo akanatha kutero. Iwo anali ndi “Mose ndi aneneri,” ndiko kuti, iwo anali ndi Malemba Oyera ouziridwa olembedwa ndi Mose ndi aneneri ena akale. Palibe n’kamodzi komwe kamene Malemba ouziridwa amene’wo anasonyeza kuti malo eni-eni onse a chizunzo pambuyo pa imfa, koma iwo anali ndi zones zofunika kudziwira Yesu monga Mesiya kapena Kristu wolonjezedwa. (Deuteronomo 18:15, 18, 19; 1 Petro 1:10, 11) Chifukwa cha chimene’cho, ngati kagulu ka “mwini chuma” ndi ‘abale ake asanu’wo’ kakanamvetsera” Mose ndi Aneneri,” iwo akanalandira Yesu monga Mesiya. Kumene’ko kukanawachititsa kukhala oyenera kulandira chiyanjo cha Mulungu ndi kuwatetezera ziyambukiro zozunza za uthenga wa chiweruzo wa Mulungu.
CHIKRISTU CHA DZIKO CHIYENERA KUDZIWA
Pali chifukwa chochepa kwa atsogoleri achipembedzo a Chikristu cha Dziko chosadziwira tanthauzo la fanizo la Yesu limene’li. Ndemanga yochuka Yachiprotestanti, yochedwa The Interpreters’s Bible, imasonyeza kalongosoledwe kofanana’ko. Iyo imasonyeza kuti otanthauzira ambiri amakhulupirira mau a Yesu kukhala “mau ofanizira ofotokoza amene amasonyeza kuombana pakati pa Chikristu choyambirira ndi Chiyuda chobvomerezedwa. Munthu wolemera’yo ndi abale ake akuimira Ayuda osakhulupirira. Yesu akuchititsidwa kunena kuti iwo mouma khosi akana kulapa mosasamala kanthu za umboni woonekera bwino kwa iye mwini m’Malemba ndi kuneneratu kuti iwo adzalephera kukhutiritsidwa maganizo ndi chiukiriro chake. N’kothekera kuti Luka ndi owerenga ake anaika kutanthauzira kwina kotero’ko pa mavesi amene’wa.” Ndipo, m’mau am’tsinde pa Luka chaputala 16, Catholic Jerusalem Bible imabvomereza kuti limene’li ndi “fanizo mu mpangidwe wa nthano losanena munthu ali yense wa mu mbiri.”
Polingalira zimene’zi, moyenerera tingafunse kuti: Kodi n’chifukwa ninji mpag’ono pomwe atsogoleri achipembedzo a Chikristu cha Dziko sanabvomereze kwa anthu ao a ku chalichi kuti limene’li ndi fanizo? Kodi n’chifukwa ninji awo amene amadziwa kuti Baibulo silimaphunzitsa kusafa kwa moyo wa munthu amapitirizabe kuika tanthauzo leni-leni pa fanizo loonekera bwino lomwe? Kodi kumene’ku si kusaona mtima? Kodi iwo sakusonyeza kunyoza Mau a Mulungu, akumabisa mwadala zeni-zeni?
Fanizo lonena za munthu wolemera ndi Lazaro liri ndi maphunziro ofunika kwambiri kwa ife lero lino. Kodi ife tikumvetsera Mau ouziridwa a Mulungu? Kodi ife tikufuna kuwatsatira monga ophunzira odzipereka a Yesu Kristu? Awo amene amakana kutero, mofanana ndi Afarisi Achiyuda, sadzapewa ziyambukiro zozunza za uthenga wachiweruzo wa Mulungu kwa iwo. Atumiki ake okhulupirika adzapitirizabe kulengeza choonadi, mopanda mantha akumabvumbula cholakwa chachipembedzo.
Kodi inu mwaima pati m’nkhani imene’yi? Kodi mukukhulupirira kuti payenera kukhala kuleka pa kubvumbula kotero’ko, mukumalingalira kuti m’zipembedzo zonse muli abwino? Kapena, kodi mumaipidwa ndi kunamizira Mulungu kwa Chikristu cha Dziko mwa njira ya ziphunzitso zake zonyenga zonena za akufa? Kodi mumafuna kuona dzina la Mulungu likuchotseredwa chitonzo choikidwa pa iro mwa kuphunzitsidwa kwa ziphunzitso zonyenga? Kodi mumafuna kuona kuyesa-yesa kotheratu kukupangidwa m’kumasula anthu oona mtima ku ukapolo wa zinyengo zachipembedzo? Ngati mukutero, mudzaona chifuno cha Mulungu chonena za akufa ndi amoyo kukhala chotonthoza kopambana.