Mutu 15
Kodi Ndimotani Mmene Yehova Amatsogozera Gulu Lake?
1. Kodi nchidziwitso chotani chonena za gulu la Yehova chimene Baibulo limavumbula, ndipo nchifukwa ninji icho chiri chofunika kwa ife?
KUPYOLERA m’Malemba ouziridwa, Yehova amatipatsa masomphenya a gulu lake lakumwamba lodabwitsa. (Yes. 6:2, 3; Ezek. 1:1, 4-28; Dan. 7:9, 10, 13, 14) Ngakhale kuli kwakuti sitingathe kuwona zolengedwa zauzimu, iye amatichenjeza za njira m’zimene ntchito ya angelo oyera imayambukirira olambira owona padziko lapansi. (Gen. 28:12, 13; 2 Maf. 6:15-17; Sal. 34:7; Mat. 13:41, 42; 25:31, 32) Baibulo limalongosolanso mbali yowoneka ya gulu la Yehova ndi kutithandiza kuzindikira mmene amalitsogozera. Ngati tiridi ndi kuzindikira kwauzimu kwa zinthu zimenezi, uku kudzatithandiza “kuyenda moyenera Ambuye kukamkondweretsa monsemo.”—Akol. 1:9, 10.
Kudziwikitsa Mbali Yowoneka
2. Chiyambire Pentekoste wa 33 C.E. kodi ndiuti umene wakhala mpingo wa Mulungu?
2 Kwa zaka 1 545 mtundu wa Israyeli unali mpingo wa Mulugu. Koma analephera kusunga pangano Lachilamulo ndipo anakana Mwana wa Mulungu. Chotero Yehova anachititsa kukhalapo kwa mpingo watsopano, umene anachita nawo pangano latsopano. Mpingo umenewo umadziwikitsidwa m’Malemba monga “mkwatibwi” wa Kristu, wopangidwa ndi 144 000 osankhidwa ndi Mulungu kugwirizana ndi Mwana wake kumwamba. (Aef. 5:22-32; Chiv. 14:1; 21:9, 10) Oyambirira anadzozedwa ndi mzimu woyera panthawi ya Pentekoste, 33 C.E. Kupyolera mwa mzimu woyera Yehova anapereka umboni wosalakwa wakuti uwu unali mpingo umene akagwiritsira ntchito kuchita chifuno chake.—Aheb. 2:2-4.
3. Kodi ndani lerolino amene akupanga gulu lowoneka la Yehova?
3 Lerolino pali otsalira okha a 144 000 padziko lapansi. Koma, m’kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Baibulo, khamu lalikulu la “nkhosa zina” lagwirizana mokangalika ndi iwo. Yesu Kristu, Mbusa Wabwino, wagwirizanitsa “nkhosa zina” zimenezi ndi awo amene ali otsalira a otsatira ake obadwa ndi mzimu kotero kuti apange “gulu limodzi” pansi pake ‘monga mbusa wawo mmodzi’. (Yoh. 10:11, 16; Chiv. 7:9, 10) Onsewa akupanga gulu limodzi logwirizana, gulu lowoneka la Yehova lerolino.
Lopangidwa Mwateokratiki
4. Kodi ndani amatsogoza gululo, ndipo motani?
4 Mawu Am’malemba akuti “mpingo wa Mulungu wamoyo” akusonyeza amene akulitsogoza. Gululi nlateokratiki, kapena lolamulidwa ndi Mulungu. Yehova amapereka chitsogozo kaamba ka anthu ake kupyolera mwa uyo amene Iye anamuika kukhala mutu wosawoneka wa mpingowo, Ambuye Yesu Kristu, ndi kupyolera mwa Mawu a Iye mwini ouziridwa, Baibulo.—1 Tim. 3:14, 15; Aef. 1:22, 23; 2 Tim. 3:16, 17.
5. (a) Kodi ndimotani mmene chitsogozo chakumwamba champingo chinawonekera m’zaka za zana loyamba? (b) Kodi nchiyani chimasonyeza kuti Yesu akali chikhalirebe mutu wampingo?
5 Chitsogozo chateokratiki chotero chinali chachiwonekere kwambiri pamene ziwalo zoyamba zampingowo zinasonkhezeredwa kuntchito mwamzimu woyera pa Pentekoste wa 33 C.E. (Mac. 2:1-4, 32, 33) Chinawonekera pamene mngelo wa Yehova anatsogoza zochitika zimene zinatsogolera kukufalitsidwa kwa mbiri yabwino kulowa mu Afirika. (Mac. 8:26-39) Mofananamo, pamene mawu a Yesu anapereka malangizo pakutembenuzidwa kwa Saulo wa ku Tariso ndiponso pamene ntchito yaumishonale pakati pa Akunja inayambitsidwa. (Mac. 9:3-7, 10-17; 10:9-16, 19-23; 11:12) Koma chitsogozo chofunika sichinaperekedwe nthawi zonse m’njira zapadera zotero. M’kupita kwa nthawi panalibe mawu aliwonse omvedwa kuchokera kumwamba, panalibenso angelo amene anawonekera kwa anthu ndipo panalibenso mphatso zozizwitsa zamzimu. Komabe Yesu anali atalonjeza otsatira ake okhulupirika kuti: “Tawonani! Ndiri nanu masiku onse kufikira mapeto a dongosolo lazinthu,” ndipo zenizeni zikusonyeza kuti iye ali. (Mat. 28:20, NW; 1 Akor. 13:8) Sikokha kuti Mboni za Yehova zimavomereza umutu wake, koma nkwachiwonekere kuti kukanakhala kosatheka kwa iwo kupitirizabe kulengeza uthenga wa Ufumu pamaso paudani waukulu popanda chithandizo chake.
6. (a) Kodi ndani amapanga “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” ndipo chifukwa ninji? (b) Kodi ndigawo la ntchito lotani limene iye anapatsa kwa “kapolo” ameneyo?
6 Mwamsanga imfa ya Yesu isanachitike analankhula kwa ophunzira ake za “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amene iye monga Mbuye akamuikizira thayo lapadera. “Kapolo,” ameneyo mogwirizana ndi malongosoledwe a Yesu, akakhala wopezeka pamene Mbuye akachoka kupita kumwamba ndipo akakhala akali ndi moyo panthawi ya kubweranso kwa Kristu. Malongosoledwe otere sakanayenerera konse munthu mmodzi aliyense. Koma amayenerera mpingo wa odzozedwa okhulupirika wa Kristu powonedwa monga gulu. Yesu anadziwa kuti adzawagula ndi mwazi wa iyemwini, chotero moyenerera anasonya kwa iwo mwa chiungwe kukhala “kapolo” wake. Iye anawapatsa ntchito yochita, akumawatumiza iwo onse kukapanga ophunzira ndiyeno mopita patsogolo kudyetsa amenewa mwauzimu, kuwapatsa “chakudya chawo [chauzimu] panthawi yoyenerera.” Kuikidwa kwawo kunatsimikiziridwa mwa mzimu woyera pa Pentekoste wa 33 C.E.—Mat. 24:45-47; 28:19, 20; 1 Akor. 6:19, 20; yerekezerani ndi Yesaya 43:10.
7. (a) Kodi ndimathayo owonjezereka otani amene “kapolo” tsopano alinawo? (b) Kodi nchifukwa ninji kulabadira kwathu malangizo odzera mwa ngalande imeneyi kuli kofunika?
7 Pakubweranso kwa Mbuye, ngati “kapolo” anali kugwira ntchito yake mokhulupirika, akamuikizira mathayo okulirapo. Zaka zimene zinatsatira zikakhala nthawi yaumboni wadziko lonse wa Ufumu, ndipo “khamu lalikulu” la olambira a Yehova likanasonkhanitsidwa ncholinga cha kupulumutsidwa kwawo kupyola “chisautso chachikulu.” (Mat. 24:14; Chiv. 7:9, 10) Ndiponso, amenewa, akafunikira chakudya chauzimu, ndipo chikaperekedwa kwa iwo ndi “kapolo” wachiungwe, atumiki odzozedwa ndi mzimu a Kristu. Kuti tikondweretse Yehova, tifunikira kuvomereza malangizo amene amawapereka kupyolera mwa ngalande imeneyi ndi kuchita mogwirizana nawo kotheratu.
8, 9. (a) M’zaka za zana loyamba kodi ndikakonzedwe kotani kamene kanaliko kothetsera mafunso onena za chiphunzitso ndi kuperekera chitsogozo chofunika ponena za kulalikira mbiri yabwino? (b) Kodi ndikakonzedwe kofanana kotani kamene kalipo lerolino?
8 Ndithudi, panthawi zina, mafunso onena za chiphunzitso ndi mchitidwe angabuke. Pamenepo chiyani? Mutu 15 wa Machitidwe umatiuza za mmene nkhani yonena za zofunika za otembenuka Achikunja inathetsedwera. Inatuliridwa kwa Atumwi ndi akulu ku Yerusalemu, amene anatumikira monga bungwe lolamulira lapakati. Akulu amenewo sanali osachimwa; sanali anthu amene sanapange konse cholakwa. (Yerekezerani Agalatiya 2:11-14.) Koma Mulungu anawagwiritsira ntchito. Anapenda chimene Malemba ouziridwa ananena ponena za nkhani imene anali kukambitsiranayo kudzanso umboni wa kugwira ntchito kwa mzimu wa Mulungu potsegulira mwayi Akunja, ndiyeno anapereka chosankha. Mulungu anadalitsa kakonzedwe kameneko. (Mac 15:1-29; 16:4, 5) Kuchokera ku bungwe lapakati limenelo, anthu aliwonse pawokha anatumizidwanso kukapititsa patsogolo kulalikidwa kwa mbiri yabwino mogwirizana ndi zimene Ambuye iyemwiniyo anali atalamula.—Mac. 8:14; Agal. 2:9.
9 M’tsiku lathu Bungwe Lolamulira lapangidwa ndi abale odzozedwa ndi mzimu ochokera ku maiko osiyanasiyana. Liri pamalikulu adziko lonse a Mboni za Yehova. Mokhulupirika limapititsa patsogolo zinthu za kulambira koyera pansi paumutu wa Yesu Kristu. Abale amenewa ali ndi malingaliro ofanana ndi a mtumwi Paulo, amene, potumiza uphungu wauzimu kwa Akristu anzake, analemba: “Sikuti tichita ufumu pa chikhulupiriro chanu, koma tikhala othandizana nacho chimwemwe chanu; pakuti ndi chikhulupiriro muimadi.”—2 Akor. 1:24.
10. (a) Kodi kumatsimikiziridwa motani amene adzakhala akulu kapena atumiki otumikira? (b) Kodi nchifukwa ninji tiyenera kugwirizana mwathithithi ndi anthu oikidwa ku malo a ntchito otero?
10 Kakonzedwe kateokratiki aka kakuvomerezedwa ndi Mboni za Yehova padziko lonse. Mipingo yawo ya m’malowo yonse imagwira ntchito mogwirizana nako mwathithithi. Imayang’ana ku Bungwe lolamulira kuchita maikidwe a akulu ndi atumiki otumikira kusamalira kugwira ntchito kwa mipingo kwa myaa. Kodi anthu amasankhidwa pamaziko otani kaamba ka maikidwe otero? Zofunika zalongosoledwa momvekera bwino m’Baibulo. Onse awiri akulu amene amapanga mavomerezedwewo ndi awo opatsidwa ukumu wa kupanga maikidwewo ali ndi thayo lalikulu pamaso pa Mulungu la kumamatira ku zimenezi. (1 Tim. 3:1-10, 12, 13; 5:22; Tito 1:5-9) Palibe mpangidwe wa kuchita masankho pakati pa ziwalo zampingo kapena kuchita voti kwampingo kulikonse. M’malo mwake, mogwirizana ndi zimene zinachitidwa ndi atumwi pamene maikidwe anapangidwa m’zaka za zana loyamba, oyang’anira okhala ndi thayo lakuvomereza amenewo, ndi awo amene pambuyo pake amapanga maikidwe, amapereka pemphero kaamba ka chithandizo cha mzimu wa Mulungu ndi kufunafuna chitsogozo kuchokera m’Mawu ake ouziridwa. (Mac. 6:2-4, 6; 14:23 yerekezerani ndi Salmo 75:6, 7.) Mwakulabadira kwathu chitsogozo chimene akulu amapereka, tingakhoze kusonyeza chiyamikiro chathu kaamba ka makonzedwe achikondi a Kristu a “mphatso za anthu” zimenezi kutithandiza tonsefe m’kufikira “umodzi wa chikhulupiriro.”—Aef. 4:8, 11-16.
11. (a) Kodi ndimautumiki ofunika otani amene amachitidwa ndi akazi mkati mwa kakonzedwe kateokratiki? (b) Kodi ndi liti pamene afunikira kuvala chophimba kumutu, ndipo chifukwa ninji?
11 Malemba amalangiza kuti malo a kuyang’anira mu mpingo asamaliridwe ndi amuna. Uku sindiko mwanjira iriyonse kululuza akazi, pakuti unyinji wa iwo ukuphatikizidwa pakati pa olowa nyumba a Ufumu wakumwamba. Mwakhalidwe la kudekha, chiyero ndi changu m’kusamalira mabanja awo, akazi Achikristu amathandiziranso mkhalidwe wabwino kwambiri wampingo. (Tito 2:3-5) Kawirikawiri iwo amachita zambiri m’ntchito ya kupeza anthu okondwerera chatsopano ndi kuwabweretsa kuti agwirizane ndi gulu. (Sal. 68:11) Koma kuphunzitsa m’kati mwa mpingo, kukusamaliridwa ndi amuna amene ali oikidwa. (1 Tim. 2:12, 13) Ndipo ngati palibe amuna oyeneretsedwa pamsonkhano wolinganizidwa ndi mpingo, pamenepo mkazi akavala chophimba kumutu potsogoza kapena popemphera.a Mwanjira iyi akusonyeza ulemu kaamba ka makonzedwe a Yehova, monga momwedi Yesu anaperekera chitsanzo kaamba ka onse m’kugonjera kwa Atate wake.—1 Akor. 11:3-16; Yoh. 8:28, 29.
12. (a) Kodi ndilingaliro lotani limene Baibulo limalimbikitsa akulu kukhala nalo kulinga ku malo awo a ntchito? (b) Kodi ndi mwayi waukulu wotani umene tonsefe tiri nawo?
12 M’dziko munthu amene ali ndi malo otchuka amalingaliridwa kukhala wofunika, koma m’gulu la Mulungu chilangizo nchakuti: “Iye wokhala wang’onong’ono wa inu nonse, yemweyo ndiye wamkulu.” (Luka 9:46-48; 22:24-26) Chotero Malemba amalangiza akulu kukhala osamala kusachita umbuye pa awo amene ali cholowa cha Mulungu koma, m’malo mwake, kukhala zitsanzo za gulu lankhosa. (1 Pet. 5:2, 3) Osati osankhidwa owerengeka chabe, koma onse a Mboni za Yehova, amuna ndi akazi, ali ndi mwayi waukulu wa kuimira Wolamulira wachilengedwe chonse, modzichepetsa kulankhula m’dzina lake ndi kuuza anthu kulikonse za Ufumu wake.
13. Mogwiritsira ntchito malemba olembedwa, kambitsiranani mafunso ondandalikidwa pamapeto a ndime ino.
13 Timachita bwino kudzifunsa kuti: “Kodi timazindikiradi mmene Yehova akutsogozera gulu lake lowoneka? Kodi mikhalidwe yathu, kalankhulidwe ndi machitidwe zimasonyeza zimenezo?” Kusinkhasinkha pamfundo zotsatira kungathandize aliyense wa ife kupanga mapendedwe otero:
Ngati tigonjeradi kwa Kristu monga mutu wampingo, pamenepa, monga momwe kwasonyezedwera m’malemba otsatirawa, kodi nchiyani chimene tidzakhala tikuchita? (Mat. 24:14; 28:19, 20; Luka 21:34-36; Yoh. 13:34, 35)
M’zoyesayesa zawo za kukhala Akristu obala zipatso, kodi nkumlingo wotani kumene onse amene ali mbali ya gulu ayenera kumvera kukhala odalira pa Mulungu ndi Kristu? (Yoh. 15:5; 1 Akor. 3:5-7)
Pamene akulu ayesa kubweza maganizo a anthu kotero kuti awone zinthu mogwirizana ndi gulu lonselo, kodi ndinkhawa yachifundo yayani imene tiyenera kuizindikira m’zimenezi? (Aef. 4:7, 8, 11-13; 2 Akor. 13:11)
Pamene moyamikira tivomereza makonzedwe auzimu amene amadza kupyolera mwa kagulu ka “kapolo” ndi Bungwe lake Lolamulira, kodi ndani amene tikumsonyeza ulemu? Koma bwanji ngati tinalankhula mowanyoza? (Luka 10:16; yerekezerani 3 Yohane 9, 10.)
Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kukhala osuliza mwaukali akulu oikidwa? (Mac. 20:28; Aroma 12:10)
14. (a) Mwa kulingalira kwathu kulinga ku gulu lateokratiki, kodi timasonyeza chiyani? (b) Pamfundoyi, kodi ndi mwayi wotani umene ulipo kwa ife kutsimikizira Mdyerekezi kukhala wabodza ndi kusangalatsa mtima wa Yehova?
14 Kuli kupyolera mwa gulu lake lowoneka lotsogozedwa ndi Kristu monga mutu woikidwa limene Yehova akutitsogoza nalo lerolino. Chotero khalidwe lathu kulinga ku gulu limeneli limasonyeza mwanjira yeniyeni kaimidwe kamene tikutenga m’nkhani ya ufumu. (Aheb. 13:17) Satana akuumirira kunena kuti ife tonse tikusonkhezeredwa ndi chikhumbo chakupeza phindu laumwini, kuti nkhawa yathu yaikulu ndiyo ife eni. Koma ngati ife mwachimwemwe tidzipangitsa ife eni kupezeka kutumikira m’njira iriyonse imene iri yofunika, pamene tikupewa kunena ndi kuchita zinthu zimene zikanapereka chisamaliro chosayenerera kwa ife eni, tikutsimikizira kuti Mdyerekezi ngwabodza. Ngati tikonda ndi kulemekeza awo amene ‘akutsogoza’ pakati pathu, tikumatsanzira chikhulupiriro chawo, kukana kukhala mtundu wamunthu amene ‘amakhumba maumunthu kaamba ka phindu la iyemwini,’ timasangalatsa mtima wa Yehova. (Aheb. 13:7; Yuda 16) Mwa kukulitsa ulemu wabwino kaamba ka gulu la Yehova ndi kuchita ntchito imene amalangiza ndi mtima wonse, timapereka umboni wakuti Yehova alidi Mulungu wathu ndikuti tiri ogwirizana m’kulambiridwa kwake.—Akor. 15:58.
[Mawu a M’munsi]
a Komabe, iye safunikira chophimba kumutu, pamene alalikira kunyumba ndi nyumba, chifukwa chakuti thayo la kulalikira mbiri yabwino liri la Akristu onse. Koma ngati mikhalidwe imafunikiritsa kuti achititse phunziro la Baibulo la panyumba pamene mwamuna wake alipo (mutu wake, ngakhale kuti saali Mkristu), ayenera kugwiritsira ntchito chophimba mutu. Ndiponso, ngati, mkhalidwe wapadera, chiwalo chodzipatulira champingo chiripo pamene akuchititsa phunziro la Baibulo la panyumba lolinganizidwa pasadakhale, ayenera kuphimba mutu wake, koma mbaleyo adzayenera kupereka pemphero.
Makambitsirano Openda
● Kodi gulu lowoneka la Yehova lerolino nliti? Kodi chifuno chake nchiyani?
● Kodi mutu woikidwa wampingo ndani? Kodi iye amagawira chitsogozo chachikondi kwa ife kupyolera mwa makonzedwe ati owoneka?
● Kodi ndi lingaliro labwino lotani kulinga ku thayo ndi anthu m’gulu limene tiyenera kukulitsa?