Mutu 16
Mvetserani Uphungu, Labadirani Mwambo
1. (a) Kodi pali aliyense wa ife amene samafunikira uphungu ndi mwambo? (b) Koma kodi ndimafunso otani amene timachita bwino kupenda?
UNYINJI wa ife umavomerezana kwambiri ndi lemba limene limati: “Tonsefe timakhumudwa nthawi zambiri.” (Yak. 3:2, NW) Sikuli kovuta kulingalira nthawi m’zimene talephera kukhala mtundu wa munthu amene Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kukhala ndi amene timafuna kukhala. Chotero timavomereza kuti Baibulo nlolondola pamene limatiuza kuti: “Tamvera uphungu, nulandire mwambo, kuti ukhale wanzeru pachimaliziro chako.” (Miy. 19:20) Tidzidwa kuti tifunikira chithandizo. Mosakaikira tapanga masinthidwe m’miyoyo yathu kuti tiigwirizanitse ndi zimene taphunzira kuchokera m’Baibulo. Koma kodi ndimotani mmene timachitira ngati Mkristu mnzathu atipatsa uphungu waumwini pankhani yakutiyakuti pa imene tinachita mopusa? Kapena kodi bwanji ngati iye akupereka kokha malingaliro onena za mmene tingawongolere mu utumiki wina?
2. (a) Kodi nchifukwa ninji tiyenera kusonyeza chiyamikiro kaamba ka uphungu umene timapatsidwa? (b) Kodi tiyenera kulabadira motani?
2 Mosasamala kanthu ndi kulabadira kwathu kwa mkati kwadzidzidzi kaamba ka chibadidwe chaumunthu chopanda ungwiro, tiyenera mowona mtima kusonyeza chiyamikiro kaamba ka uphungu ndi kuyesayesa kuugwiritsira ntchito. Chotulukapo cha kuchita kwathu motero chingakhale chopindulitsa. (Aheb. 12:11) Komabe, mwinamwake, pamene tipatsidwa uphungu, tayesa kudzilungamitsa, tikumaluluza kuopsa kwa mkhalidwewo kapena kukankhira liwongo pamunthu winawake. Kodi munayamba mwachitapo mwanjira imeneyo? Pamene tilingaliranso za nyengoyo, kodi timalingalira kukwiya ndi munthu amene anapereka uphunguwo? Kodi tiri ndi chikhoterero cha kuwona zophophonya za munthu amene anatipatsa uphungu kapena dongosolo m’limene anaperekera uphungu, monga ngati kuti mwanjira iyi tikulungamitsa chofooka cha ife eni? Kodi Baibulo lingathandize munthu kugonjetsa zikhoterero zotero?
Zitsanzo Zolembedwera Chilangizo Chathu
3. (a) Kodi Baibulo liri nchiyani chimene chingatithandize kukulitsa lingaliro loyenera la uphungu ndi mwambo? (b) Gwiritsirani ntchito mafunso operekedwa pamwambapa kupenda zochita za Sauli ndi Uziya kulinga ku uphungu.
3 M’kuwonjezera kupereka chilangizo chachindunji chambiri pankhani iyi, Mawu a Mulungu ali ndi zokumana nazo zenizeni za anthu amene apatsidwa uphungu. Kawirikawiri uphunguwo unalinso chilango, m’chakuti wowulandira anafunikira kusintha kaimidwe kake kamaganizo kapena mkhalidwe wake. Pamene mukugwiritsira ntchito mafunso pansipa kupenda zina za zitsanzo izi, mudzapeza kuti pali zambiri kuchokera ku zimene tonsefe tingapindule:
SAULI, MWANA WA KISI: Anali atalephera kumvera Yehova mokwanira chakuti, pamene anachita nkhondo ndi a Amaleki, sanaphe mfumuyo ndi zinyama zawo zabwino koposa. (1 Sam. 15:1-11)
M’kulabadira kwa Sauli ku uphungu wodzudzula woperekedwa ndi Samueli, kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti anali kuyesayesa kuchepetsa cholakwacho? (Vesi 20) Kodi nkwayani kumene anayesayesa kusamutsira liwongo? (Vesi 21) Pamene potsirizira pake anavomereza cholakwacho, kodi nchodzikhululukira chiti chimene anapereka? (Vesi 24) Kodi nchiyani chimene anawonekera kukhala wodera nacho nkhawa koposa ngakhale pamfundo ino? (Vesi 25, 30)
UZIYA: Analowa m’kachisi wa Yehova kukafukiza nsembe yofukiza, ngakhale kuti anali ansembe okha amene analoledwa kutero. (2 Mbiri. 26:16-20)
Pamene mkulu wa ansembe anayesa kukaniza Mfumu Uziya, kodi nchifukwa ninji anachita mwaukali? (Yerekezerani ndi vesi 16.) Kodi nchiyani chimene chinali chotulukapo? (Vesi 19-21)
4. (a) Kodi nchifukwa ninji onse awiri Sauli ndi Uziya anakupeza kukhala kovuta kulandira uphungu? (b) Kodi nchifukwa ninji lirinso vuto lalikulu lerolino?
4 M’chirichonse cha zochitika zimenezi, kodi nchifukwa ninji aliyense wa iwo anakupeza kukhala kovuta kwambiri kuvomereza kufunikira kwake kulandira uphungu? Vuto lalikulu linali kunyada, kulingalira mopambanitsa pa iwo eni. Anthu ambiri lerolino amadzibweretsera chisoni chifukwa cha chikhoterero chimenechi. Atapeza chimene akuchilingalira kukhala ulemu wakutiwakuti, kaya chifukwa cha msinkhu kapena malo a ntchito, iwo samafuna konse kupatsidwa uphungu. Amawonekera kukhala akulingalira kuti kumatanthauza kuperewera mwa iwo kapena kuwaipitsira mbiri. Koma chimene kwenikweni chimasonyeza chifooko ndicho kunyada. Ichi sindicho kanthu kena kodzikhululukira mwa munthuwe kokha chifukwa chakuti cholakwacho nchofala. Uli msampha umene Satana amagwiritsira ntchito kudodometsa maganizo a munthuyo kotero kuti amakana chithandizo chachikondi choperekedwa ndi Yehova kupyolera mwa Mawu ake ndi gulu lake lowoneka. Yehova amachenjeza kuti: “Kunyada kutsogolera kukuwonongeka; mtima wodzikuza ndi kutsogolera kukupunthwa.”—Miy. 16:18; wonaninso Aroma 12:3; Miyambo 16:5.
5. Gwiritsirani ntchito mafunso amene ali mbali ya ndime ino kupenda zimene zingaphunziridwe kuchokera m’zolembedwa zosimba za Mose ndi Davide.
5 Kumbali ina, Malemba ali ndi zitsanzo zabwino kwambiri za awo amene anavomereza uphungu. Tingapezenso maphunziro opindulitsa kuchokera ku zimenezi. Talingalirani:
MOSE: Mpongozi wake anampatsa uphungu wothandiza ponena za mmene akanasamalirira ntchito yake yolemerayo popanda kuwononga thanzi lake. Mose anamvetsera ndipo anaugwiritsira ntchito mwamsanga. (Eks. 18:13-24)
Ngakhale kuti Mose anali ndi ukumu waukulu, kodi nchifukwa ninji iye anali wokonzekera kwambiri kulabadira uphungu wanzeru? (Yerekezerani ndi Numeri 12:3.) Kodi khalidwelo nlofunika motani kwa ife? (Zef. 2:3)
DAVIDE: Anali ndi liwongo la kuchita chigololo, ndiyeno mwachiwembu analinganiza kuti mwamuna wa mkaziyo aphedwe kotero kuti Davide amkwatire ndipo chotero aphimbe chigololocho. Miyezi yambiri inapita Yehova asanatumize Natani kukadzudzula Davide. (2 Sam. 11:2–12:12)
Kodi Davide anakwiya ndi uphunguwo, nachepsa cholakwacho kapena kuyesa kusamutsa liwongolo? (2 Sam. 12:13; Sal. 51: mawu oyambirira ndi vesi 1-3) Kodi chenicheni chakuti Mulungu anavomereza kulapa kwa Davide chimatanthauza kuti Davide ndi a m’nyumba mwake anawonjoka paziyambukiro zoipa zochokera mu mkhalidwe wake wolakwa? (2 Sam. 12:10, 11, 14; Eks. 34:6, 7)
6. (a) Kodi ndimotani mmene Davide analingalirira ponena za amene anampatsa uphungu wabwino? (b) Kodi ndimotani mmene ife tingapindulire ngati tivomerezadi uphungu wotero? (c) Kodi nchiyani chimene sitiyenera kuiwala ngati tapatsidwa uphungu wamphamvu?
6 Mfumu Davide anadziwa bwino lomwe phindu la kumvetsera ku uphungu wabwino, ndipo panthawi ina anayamika Mulungu kaamba ka munthuyo kupyolera mwa amene unadza. (1 Sam. 25:32-35; wonaninso Miyambo 9:8.) Kodi ife tiri otero? Ngati ziri choncho, tidzatetezeredwa motsutsana ndi kunena ndi kuchita zinthu zambiri zimene zingatichititse kumva chisoni koma ngati ife tilowa m’mikhalidwe imene imatsogolera kukupatsidwa kwathu uphungu wamphamvu, monga momwe Davide analiri malingana ndi uchimo wake ndi Batiseba, tisataikiridwetu ndi chenicheni chakuti uphungu uli umboni wachikondi cha Yehova, wokhala ndi cholinga cha ubwino wathu wosatha.—Miy. 3:11, 12; 4:13.
Mikhalidwe Yamtengo Wapatali Yakuikulitsa
7. Kodi ndikhalidwe lotani limene Yesu anasonyeza kuti anthu ayenera kukhala nalo kuti alowe mu Ufumu?
7 Kukhala ndi unansi wabwino ndi Yehova ndi abale athu Achikristu, tifunikira kukulitsa mikhalidwe yathu yakutiyakuti. Yesu anagogomezera umodzi wa imeneyi pamene anaimiriritsa kamwana pakati pa ophunzira ake ndi kunena kuti: “Ngati simutembenuka, nimukhala monga tianato, simudzalowa konse mu ufumu wakumwamba. Chifukwa chake yense amene adzichepetsa yekha monga kamwana aka, yemweyo ali wopambana mu ufumu wakumwamba.” (Mat. 18:3, 4) Ophunzira amenewo anafunikira kupanga masinthidwe. Anafunikira kuchotsa kunyada kwawo ndi kukulitsa kudzichepetsa.
8. (a) Kodi tiyenera kukhala odzichepetsa pamaso payani, ndipo chifukwa ninji? (b) Ngati ife tiri otero, kodi ndimotani mmene tidzalabadirira ku uphungu?
8 Pambuyo pake mtumwi Petro analembera Akristu anzake kuti: “Nonsenu dzimangireni kudzichepetsa maganizo kwa wina ndi mnzake, chifukwa Mulungu amatsutsa odzikuza, koma iye amapereka kukoma mtima kwapadera kwa odzichepetsa.” (1 Pet. 5:5, NW) Tidziwa kuti tifunikira kukhala odzichepetsa pamaso pa Mulungu, koma lemba iri likunena kuti tifunikira kukhala odzichepetsa, kapena ofatsa maganizo, ndiponso m’maunansi athu ndi okhulupirira anzathu. Ngati tiri otero, sitidzakhala opusa mwa kukana malingaliro amene iwo amatiposa. Tidzakhala ofunitsitsa kuphunzira kwa wina ndi mnzake. (Miy. 12:15) Ndipo ngati abale athu akupeza kukhala koyenerera kutipatsa uphungu wotiwongolera, pamenepo, pozindikira kuti Yehova mwachikondi akugwiritsira ntchito njira iyi kutiumba, sitidzaukana.—Sal. 141:5.
9. (a) Kodi ndikhalidwe lofunika lotani liri logwirizana kwambiri ndi kudzichepetsa? (b) Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukhala odera nkhawa ndi chiyambukiro cha mkhalidwe wathu pa ena?
9 Mkhalidwe wina, wogwirizana kwambiri ndi kudzichepetsa, ndiwo kudera nkhawa kowona mtima ndi ubwino wa ena. Sitingakhoze kuzemba chenicheni chakuti chimene timachita chimayambukira anthu ena. Mtumwi Paulo anapereka uphungu kwa Akristu oyambirira m’Korinto ndi Roma kusonyeza kudera nkhawa ndi chikumbumtima cha ena. Sanali kunena kuti anafunikira kuika pambali zinthu zonse zimene iwo anakhumba, koma anawalimbikitsa kusachita kanthu kalikonse kamene kangalimbikitse munthu wina kuchita chimene chikumbumtima chake chinamuuza kukhala cholakwa, chotero kutsogolera ku chivulazo chake chauzimu. Akumalankhula momvekera bwino lamulo lonse lamakhalidwe abwino, Paulo analemba kuti: “Munthu asafune zake za iye yekha, koma za mnzake. . . . Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu. Khalani osakhumudwitsa, kapena Ayuda, kapena Ahelene, kapena mpingo wa Mulungu.”—1 Akor. 10:24-33; 8:4-13; Aroma 14:13-23.
10. Kodi nchiyani chimene chingasonyeze kuti kaya tiri ndi chizolowezi cha kugwiritsira ntchito uphungu Wamalemba?
10 Kodi ndinu munthu amene muli ndi chizolowezi cha kuika ubwino wa anthu ena patsogolo pazikhumbo za inu mwini? Pali njira zambiri m’zimene izi zingachitidwire, koma talingalirani chitsanzo ichi: Kawirikawiri, mavalidwe ndi mapesedwe a tsitsi ziri kokha nkhani ya zofuna zaumwini, malinga ngati tiri odekha, audongo ndi aukhondo. Koma ngati chifukwa cha magwero a anthu m’chitaganya chanu, mukanamva kuti, mavalidwe anu kapena mapesedwe anu a tsitsi akulepheretsa ena kumvetsera uthenga wa Ufumu, kodi mukanapanga masinthidwewo? Kodi moyo wa munthu winayo uli wofunika kwambiri kwa inu koposa kudzikondweretsa nokha?
11. Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti nkofunika kukulitsa mikhalidwe imeneyi ngati tifunadi kukhala Akristu?
11 Pamene mikhalidwe yokambitsiridwa pamwambapa ifikira kukhala mbali yaumunthu wathu, ichi chimapereka umboni wakuti tayamba kukhala ndi maganizo a Kristu. M’kukhala odzichepetsa, Yesu anapereka chitsanzo changwiro. (Yoh. 13:12-15; Afil. 2:5-8) M’kusonyeza kudera nkhawa ndi ena, mmalo mwakungodzikondweretsa, anapereka chitsanzo choti ife titsanzire.—Aroma 15:2, 3.
Musakane Chilango cha Yehova
12. (a) Kodi ndimasinthidwe otani amene tonsefe tifunikira kupanga kukhala ndi umunthu wokondweretsa kwa Mulungu? (b) Kodi tidzathandizidwa nchiyani?
12 Chifukwa chakuti tonsefe tiri ochimwa, masinthidwe m’kaimidwe kathu kamaganizo, kalankhulidwe kathu ndi khalidwe lathu ziri zofunika kuti ife tisonyeze umunthu wa Mulungu wathu. Tifunikira kuvala “umunthu watsopano.” (Akol. 3:5-14; Tito 2:11-14) Uphungu ndi mwambo zimatithandiza kudziwa mbali m’zimene masinthidwe ali ofunika ndiyeno kuwona mmene angapangidwire.
13. (a) Kodi Yehova wagawira uphungu ndi mwambo kaamba ka tonsefe kupyolera mwa chiyani? (b) Kodi ife tiyenera kuchitanji ndi uphunguwo?
13 Magwero aakulu a malangizo amenewo ndiwo Baibulo lenilenilo. (2 Tim. 3:16, 17) Ndiyeno kupyolera mwa mabukhu othandizira Baibulo ndi misonkhano yoperekedwa ndi gulu lowoneka la Yehova iye amatithandiza kuwona mmene tingawagwiritsirire ntchito. Kodi ife tidzakhala odzichepetsa kuvomereza kufunikira kwathu chilangizocho—ngakhale ngati tachimvapo kale—ndipo kufunafuna mosalekeza kupanga kuwongokera?
14. Kodi nchithandizo chowonjezereka chotani chimene Yehova amatipatsa monga anthu aliwonse paokha?
14 Yehova samatisiya kuti tivutike tokha ndi nkhani zimene zingakhale vuto lapadera kwa ife. Mwa kudera nkhawa kwachikondi, amachititsa makonzedwe a chithandizo chaumwini. Anthu mamiliyoni ambiri apindula ndi chithandizo chotero mwanjira ya maphunziro a Baibulo a panyumba. Makolo ali ndi thayo lapadera lakulanga ana awo kuchitira kuti awatetezere ku mkhalidwe umene ungamvetse chisoni pambuyo pake m’moyo. (Miy. 6:20-35; 15:5) Ndiponso, mkati mwa mpingo, awo amene ali ndi ziyeneretso zauzimu ali ndi thayo lakugwiritsira ntchito Malemba kubweza ena pamene awona kufunika, koma angatero mu mzimu wodekha. (Agal. 6:1, 2) Mwanjira izi Yehova amatipatsa uphungu ndi kutilanga kotero kuti timlambire monga anthu ogwirizanitsidwa.
Makambitsirano Openda
● Kodi ndimotani mmene Yehova mwachikondi amatithandizira kuwona kumene ife ali yense payekha tifunikira kupanga masinthidwe?
● Kodi nchifukwa ninji anthu ambiri ali ndi vuto m’kulandira uphungu? Kodi izi nzowopsa motani?
● Kodi ndimikhalidwe yamtengo wapatali yotani imene idzatithandiza kulabadira uphungu? Kodi ndimotani mmene Yesu anaperekera chitsanzo mu iyi?