Mutu 5
Yohane Anaona Yesu Ali mu Ulemerero Wake
Masomphenya 1—Chivumbulutso 1:10–3:22
Nkhani yake: Yesu akuyendera ndi kulimbikitsa Isiraeli wauzimu padziko lapansi
Nthawi ya kukwaniritsidwa kwake: Mbali imeneyi ya tsiku la Ambuye, inayamba m’chaka cha 1914 ndipo ipitiriza mpaka Mkhristu wokhulupirika womaliza mumpingo wa Akhristu odzozedwa, atamwalira ndi kuukitsidwa
1. Kodi masomphenya oyamba akugwirizana ndi zimene zinkachitika m’nthawi iti, nanga Yohane anasonyeza bwanji nthawi yeniyeni imene masomphenyawo adzakwaniritsidwe?
MASOMPHENYA oyamba a m’buku la Chivumbulutso anayambira pachaputala 1, vesi 10. Masomphenya amenewa, mofanana ndi masomphenya ena a m’bukuli, anayamba ndi mawu osonyeza kuti Yohane anamva kapena kuona zinthu zinazake zochititsa chidwi. (Chivumbulutso 1:10, 12; 4:1; 6:1) Masomphenya oyamba amenewa akugwirizana ndi zimene zinkachitika m’nthawi ya atumwi ndipo uthenga wake ukupita ku mipingo 7 imene inalipo m’nthawi ya Yohane. Koma Yohane anasonyeza nthawi yeniyeni imene masomphenyawo adzakwaniritsidwe. Iye ananena kuti: “Mwa mzimu, ndinapezeka kuti ndili m’tsiku la Ambuye.” (Chivumbulutso 1:10a) Kodi “tsiku” limeneli likuimira nthawi iti? Kodi zinthu zoopsa zimene zikuchitika m’nthawi yathu yovuta ino, zikugwirizana ndi tsiku limeneli? Ngati zikugwirizana, tiyenera kutsatira mosamala kwambiri ulosi umenewu chifukwa chakuti ukukhudza moyo wathu komanso chipulumutso chathu.—1 Atesalonika 5:20, 21.
M’tsiku la Ambuye
2. Kodi tsiku la Ambuye likuyamba liti, ndipo lidzatha liti?
2 Kodi mawu amene Yohane ananena akusonyeza kuti masomphenya a m’buku la Chivumbulutso adzakwaniritsidwa liti? Choyamba, tiyeni tidziwe tanthauzo la tsiku la Ambuye. Mtumwi Paulo anafotokoza kuti tsiku limeneli ndi nthawi yachiweruzo ndiponso yokwaniritsa malonjezo a Mulungu. (1 Akorinto 1:8; 2 Akorinto 1:14; Afilipi 1:6, 10; 2:16) Kuyambika kwa “tsiku” limeneli kukuchititsa kuti Yehova apitirize kukwaniritsa zolinga zake zazikulu popanda cholepheretsa chilichonse mpaka zonse zitakwaniritsidwa. “Tsiku” limeneli likuyamba pamene Yesu akupatsidwa ufumu kumwamba. Yesu akadzaweruza dziko la Satanali, tsiku la Ambuye lidzapitirizabe mpaka Paradaiso atabwezeretsedwa ndiponso anthu atakhalanso angwiro. Tsikuli lidzapitirizabe mpaka pamene Yesu ‘adzapereke ufumu kwa Mulungu wake ndi Atate wake.’—1 Akorinto 15:24-26; Chivumbulutso 6:1, 2.
3. (a) Kodi ulosi wa Danieli wonena za “nthawi zokwanira 7” umatithandiza bwanji kudziwa nthawi imene tsiku la Ambuye linayamba? (b) Kodi ndi zinthu ziti zimene zikuchitika padziko lapansi, zotsimikizira kuti tsiku la Ambuye linayamba m’chaka cha 1914?
3 Kukwaniritsidwa kwa maulosi ena a m’Baibulo kumatithandiza kudziwa nthawi imene tsiku la Ambuye linayamba. Mwachitsanzo, Danieli anafotokoza za kugwetsedwa kwa mtengo, kumene kunkaimira kudukiza kwa ulamuliro wa mafumu amene anali mbadwa za Mfumu Davide. Patadutsa “nthawi zokwanira 7,” zinadziwika kuti “Wam’mwambamwamba ndiye Wolamulira wa maufumu a anthu, ndiponso kuti akafuna kupereka ulamuliro kwa munthu aliyense, amamupatsa.” (Danieli 4:23, 24, 31, 32) Kukwaniritsidwa kwakukulu kwa ulosi umenewu kunayamba pamene ufumu wa Yuda unawonongedwa, ndipo umboni wa m’Baibulo ukusonyeza kuti kunatha m’chaka cha 607 B.C.E., m’mwezi wa October. Lemba la Chivumbulutso 12:6, 14 limasonyeza kuti nthawi zitatu ndi hafu zikukwana masiku 1,260. Choncho, nthawi 7 (kuchulukitsa nambala imeneyi kawiri) zikukwana masiku 2,520. Tikawerenga “tsiku limodzi kuimira chaka chimodzi” tikupeza kuti “nthawi zokwanira 7” ndi zaka 2,520. (Ezekieli 4:6) Choncho Khristu Yesu anayamba kulamulira ali kumwamba, chakumapeto kwa chaka cha 1914. Kuyambika kwa nkhondo yoyamba yapadziko lonse m’chakachi, kunali “chiyambi cha masautso, ngati mmene zimayambira zowawa za pobereka.” Ndipo anthu akupitirizabe kuvutika ndi masautso amenewo. Zochitika za m’dzikoli, lomwe anthu akungophana mwachisawawa, zikutsimikizira kuti “tsiku” la kukhalapo kwa Yesu linayamba m’chaka cha 1914.—Mateyu 24:3-14.a
4. (a) Kodi mawu a m’buku la Chivumbulutso amasonyeza kuti masomphenya oyamba anayamba liti kukwaniritsidwa? (b) Kodi kukwaniritsidwa kwa masomphenya oyambawo kudzatha liti?
4 Choncho masomphenya oyambawa anayamba kukwaniritsidwa m’tsiku la Ambuye, limene linayamba m’chaka cha 1914, ndipo malangizo amene ali m’masomphenyawo anayamba kugwira ntchito pa nthawi imeneyo. Nthawi imeneyi ikugwirizana ndi zimene buku la Chivumbulutso lafotokoza kutsogoloku. Bukuli limafotokoza kuti Ambuye Yesu adzatsogolera pa ntchito yopereka chiweruzo cha Mulungu chimene ndi choona ndi cholungama. (Chivumbulutso 11:18; 16:15; 17:1; 19:2, 11) Ngati kukwaniritsidwa kwa masomphenya oyamba kunayamba m’chaka cha 1914, kodi kudzatha liti? Monga mmene masomphenyawo akusonyezera, uthenga wake ukupita kumpingo wa Mulungu wa Akhristu odzozedwa amene ali padziko lapansi. Choncho kukwaniritsidwa kwa masomphenya oyambawa kudzatha Mkhristu wokhulupirika womaliza mumpingo wa Akhristu odzozedwawo akadzamwalira ndi kuukitsidwa kuti akakhale kumwamba. Komabe, Tsiku la Ambuye ndiponso madalitso amene anthu a m’gulu la nkhosa zina akupeza padziko lapansi, zidzapitirizabe mpaka kumapeto kwa Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Yesu Khristu.—Yohane 10:16; Chivumbulutso 20:4, 5.
5. (a) Kodi Yohane anamva mawu omulamula kuchita chiyani? (b) N’chifukwa chiyani zinali zosavuta kutumiza mpukutu m’dera limene munali “mipingo 7”?
5 Yohane asanaone chilichonse m’masomphenya oyambawa anamva mawu amphamvu. Iye anati: “Ndinamva mawu amphamvu ngati kulira kwa lipenga. Mawuwo anali akuti: ‘Zimene uone, lemba mumpukutu ndi kuutumiza kumipingo 7 yotsatirayi: wa ku Efeso, wa ku Simuna, wa ku Pegamo, wa ku Tiyatira, wa ku Sade, wa ku Filadefiya, ndi wa ku Laodikaya.’” (Chivumbulutso 1:10b, 11) Yohane anamva mawu amphamvu ngati kulira kwa lipenga komanso osonyeza kuti akuchokera kwa munthu waulamuliro, omuuza kuti alembe mauthenga opita “kumipingo 7.” Iye anali atatsala pang’ono kulandira mauthenga osiyanasiyana ndiponso kulemba zinthu zimene aone ndi kumva. Kumbukirani kuti mipingo imene inatchulidwa m’masomphenyawa inalipodi m’nthawi ya Yohane. Mipingo yonseyi inali ku Asia Minor, kutsidya lina la nyanja, kuchokera pachilumba cha Patimo. Anthu a m’mipingoyi ankayenderana mosavuta chifukwa m’derali munali misewu yabwino kwambiri imene Aroma anamanga. Choncho zinali zosavuta kuti munthu amene watumidwa kukapereka mpukutu ayende kuchokera kumpingo wina kupita kumpingo wina. Mipingo 7 imeneyi ingafanane ndi mbali imodzi ya dera limene woyang’anira dera wa Mboni za Yehova amayendera masiku ano.
6. (a) Kodi mawu akuti “zimene zikuchitika panopa,” akutanthauza chiyani? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti mmene zinthu zilili mumpingo wa Akhristu odzozedwa masiku ano zikufanana ndi mmene zinalili m’nthawi ya Yohane?
6 Maulosi ambiri a m’buku la Chivumbulutso anali oti adzakwaniritsidwa m’tsogolo, osati m’nthawi ya Yohane. Maulosi amenewo ankanena za “zimene zidzachitike pambuyo pa zimenezi.” Koma malangizo amene ankapita kumipingo 7 imeneyo ankanena za “zimene zikuchitika panopa,” kutanthauza zinthu zimene zinkachitikadi m’mipingo 7 ija pa nthawiyo. Mauthenga amenewo anali ndi mfundo zothandiza kwambiri kwa akulu okhulupirika amene anaikidwa m’mipingo 7 imeneyo, komanso m’mipingo yonse ya Akhristu odzozedwa pa nthawiyo.b Popeza kuti mbali yaikulu ya masomphenya a m’buku la Chivumbulutso ikukwaniritsidwa m’tsiku la Ambuye, zimene Yesu ananena m’masomphenyawo zikusonyeza kuti zimene zinkachitika m’mipingo ya m’nthawi imeneyo zingathenso kuchitika mumpingo wa Akhristu odzozedwa masiku ano.—Chivumbulutso 1:10, 19.
7. Kodi Yohane anaona ndani m’masomphenya oyambawa, ndipo n’chifukwa chiyani zimene anaonazo zili zofunika komanso zosangalatsa kwa ife masiku ano?
7 M’masomphenya oyambawo, Yohane anaona Ambuye Yesu Khristu akuwala mu ulemerero wake kumwamba. Zimenezitu n’zoyenera kulembedwa m’buku la maulosi ochokera kumwamba onena za tsiku lalikulu la Ambuye. Ndipotu masomphenyawo ndi ofunika kwambiri kwa ife amene tili ndi moyo ndiponso tikutsatira mosamala malangizo a Yesu, m’nthawi ino pamene masomphenyawo akukwaniritsidwa. Komanso, n’zosangalatsa kwambiri kwa anthu amene akugwirizana ndi ulamuliro wa Yehova kudziwa kuti Mesiya, yemwenso ndi Mbewu, ali ndi moyo kumwamba ndipo Mulungu wamupatsa mphamvu kuti akwaniritse chifuniro cha Mulunguyo. Iye wamupatsa mphamvuzi chifukwa chakuti pafupifupi zaka 2,000 zapitazo, anapirira pamene Satana ankamuyesa ndiponso kumuzunza kwambiri mpaka kufa mozunzika, kapena kuti kuvulazidwa “chidendene.”—Genesis 3:15.
8. Kodi Yesu wakonzeka kuchita chiyani?
8 N’zoonekeratu kuti Yesu, amene ndi Mfumu, tsopano wakonzeka kupereka chiweruzo kwa adani ake. Yehova wamuika kuti akhale Woweruza Wamkulu n’cholinga choti apereke chiweruzo chomaliza cha Yehovayo kudziko loipali ndiponso kwa Satana, yemwe ndi mulungu wankhanza wadzikoli. Yesu wakonzekanso kuweruza anthu odzozedwa a mumpingo wake pamodzi ndi anzawo a khamu lalikulu ndiponso dziko lonse lapansi.—Chivumbulutso 7:4, 9; Machitidwe 17:31.
9. (a) Kodi Yohane anamufotokoza bwanji Yesu Khristu ali mu ulemerero pakati pa zoikapo nyale zagolide? (b) Kodi malo ooneka ngati mkati mwa kachisi ndiponso chovala chimene Yesu anavala zikuimira chiyani? (c) Kodi lamba wake wagolide akuimira chiyani?
9 Kenako Yohane anacheuka atamva mawu amphamvu. Pofotokoza zimene anaona, iye anati: “Ndinacheuka kuti ndione, kuti ndani amene anali kundilankhula. Nditacheuka, ndinaona zoikapo nyale 7 zagolide.” (Chivumbulutso 1:12) Patapita nthawi, Yohane anauzidwa tanthauzo la zoikapo nyale 7 zimenezi. Koma iye anachita chidwi kwambiri ndi munthu amene anaima pakati pa zoikapo nyalezo. “Pakati pa zoikapo nyalezo, panali wina wooneka ngati mwana wa munthu atavala chovala chofika kumapazi, atamanga lamba wagolide pachifuwa.” (Chivumbulutso 1:13) Apa Yesu, yemwe ndi “mwana wa munthu,” anaonekera ali mu ulemerero komanso akuwala. Iye anaonekera kwa Yohane, mboni imene pa nthawiyi inali ndi mantha chifukwa cha masomphenyawo. Yesu anaonekera mu ulemerero, akuwala kwambiri pakati pa zoikapo nyale zagolide ndipo nyalezo zinkayaka. Malo amenewa ankaoneka ngati mkati mwa kachisi ndipo anamuthandiza Yohane kumvetsa kuti Yesu ndi Mkulu wa Ansembe wapamwamba wa Yehova ndipo ali ndi mphamvu zoweruza anthu. (Aheberi 4:14; 7:21-25) Chovala chachitali komanso chokongola chimene anavala chikugwirizana ndi ntchito yake monga wansembe. Komanso iye anavala lamba wagolide pachifuwa ngati mmene akulu a ansembe achiyuda ankavalira, ndipo lambayo anaphimba mtima wake. Zimenezi zikutanthauza kuti iye adzagwira ndi mtima wonse ntchito imene Yehova Mulungu anam’patsa.—Ekisodo 28:8, 30; Aheberi 8:1, 2.
10. (a) Kodi tsitsi loyera kwambiri la Yesu ndiponso maso ake ooneka ngati lawi la moto zikutanthauza chiyani? (b) Kodi miyendo ya Yesu imene inkanyezimira ngati mkuwa ikutanthauza chiyani?
10 Yohane anapitiriza kufotokoza kuti: “Komanso, mutu ndi tsitsi lake zinali zoyera ngati ubweya wa nkhosa woyera, zoyera kwambiri kuti mbee! Ndipo maso ake anali ngati lawi la moto.” (Chivumbulutso 1:14) Tsitsi lake loyera kwambiri likusonyeza kuti ali ndi nzeru chifukwa chakuti wakhala ndi moyo nthawi yaitali. (Yerekezerani ndi Miyambo 16:31.) Ndipo maso ake ooneka ngati lawi la motowo akusonyeza kuti amachita zinthu mozindikira komanso mwatcheru akamafufuza, akamayesa ndiponso akamasonyeza kuti wakwiya. Yohane anachitanso chidwi ndi miyendo ya Yesu. Iye anati: “Miyendo yake inali ngati mkuwa woyengedwa bwino ukamanyezimira m’ng’anjo, ndipo mawu ake anali ngati mkokomo wa madzi ambiri.” (Chivumbulutso 1:15) M’masomphenyawo miyendo ya Yesu inkaoneka ngati mkuwa wonyezimira ndiponso wowala kwambiri. M’pake kuti miyendo ya Yesu inkaoneka motere chifukwa amayenda mokhulupirika komanso ali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova Mulungu. Komanso m’Baibulo nthawi zambiri akamafotokoza zinthu zokhudza Mulungu amaziyerekezera ndi golide, ndipo zinthu zokhudza anthu amaziyerekezera ndi mkuwa.c Choncho miyendo ndi mapazi onyezimira a Yesu, amene anali ngati mkuwa woyengedwa bwino, akutikumbutsa ‘kukongola’ kwa mapazi ake pamene ankalalikira uthenga wabwino padziko lapansi.—Yesaya 52:7; Aroma 10:15.
11. (a) Kodi miyendo yonyezimira ya Yesu ikutikumbutsa chiyani? (b) Kodi mawu a Yesu amene ankamveka ngati “mkokomo wa madzi ambiri” akusonyeza chiyani?
11 Monga munthu wangwiro, Yesu anali ndi ulemerero umene angelo komanso anthu ankatha kuuona. (Yohane 1:14) Miyendo yake yonyezimirayo ikutikumbutsanso kuti waima pamalo opatulika m’gulu la Yehova ndipo akutumikira monga Mkulu wa Ansembe. (Yerekezerani ndi Ekisodo 3:5.) Komanso mawu ake akumveka amphamvu kwambiri ngati mkokomo wa mathithi aakulu. Zimenezi n’zochititsa chidwi ndiponso zochititsa mantha. Zili choncho chifukwa zikufotokoza moyenerera munthu amene amatchedwa Mawu a Mulungu, amenenso akubwera “kudzaweruza m’chilungamo dziko lapansi kumene kuli anthu.”—Machitidwe 17:31; Yohane 1:1.
12. Kodi “lupanga lalitali, lakuthwa konsekonse” likutanthauza chiyani?
12 “M’dzanja lake lamanja anali ndi nyenyezi 7. M’kamwa mwake munali kutuluka lupanga lalitali, lakuthwa konsekonse. Nkhope yake inali yowala ngati dzuwa limene likuwala kwambiri. Nditamuona, ndinagwa pamapazi ake ngati kuti ndafa.” (Chivumbulutso 1:16, 17a) Kutsogolo kwa ulosiwu Yesu anafotokoza tanthauzo la nyenyezi 7 zimene zinali m’dzanja lake. Ndipo m’kamwa mwake munkatuluka “lupanga lalitali, lakuthwa konsekonse.” Zimenezi n’zoyenerera, chifukwa Yehova anapatsa Yesu udindo wopereka chiweruzo chomaliza kwa adani a Yehovayo. Choncho m’kamwa mwakemo mudzatuluka mawu amphamvu olamula kuti oipa onse aphedwe.—Chivumbulutso 19:13, 15.
13. (a) Kodi nkhope yowala kwambiri ya Yesu ikutikumbutsa chiyani? (b) Kodi zimene Yohane anaona m’masomphenya zokhudza Yesu zikusonyeza chiyani?
13 Nkhope yowala kwambiri ya Yesu ikutikumbutsa za nkhope ya Mose, yomwenso inawala kwambiri atalankhula ndi Yehova m’phiri la Sinai. (Ekisodo 34:29, 30) Kumbukiraninso kuti Yesu atasandulika pamaso pa atumwi ake atatu pafupifupi zaka 2,000 zapitazo, “nkhope yake inawala ngati dzuwa. Malaya ake akunja anawala kwambiri.” (Mateyu 17:2) Koma masomphenyawa anasonyeza Yesu ali m’tsiku la Ambuye, ndipo nkhope yake inawalanso kwambiri, kusonyeza kuti akukhala pafupi ndi Yehova. (2 Akorinto 3:18) Ndipotu m’masomphenya onse a Yohane muli kuwala kwambiri kwa ulemerero. Choncho zimene taona m’masomphenya apamwamba kwambiri amenewa, monga tsitsi loyera kwambiri, maso ooneka ngati lawi la moto, nkhope yowala ndiponso miyendo yonyezimira, zikusonyeza kuti Yesu tsopano akukhala “m’kuwala kosafikirika.” (1 Timoteyo 6:16) Zimene Yohane anaona m’masomphenya amenewa zinkaoneka bwino kwambiri, ndipo zinkaoneka ngati zikuchitikadi pa nthawiyo. Kodi Yohane amene pa nthawiyi anali ndi mantha kwambiri, anachita chiyani? Mtumwiyu akuyankha kuti: “Nditamuona, ndinagwa pamapazi ake ngati kuti ndafa.”—Chivumbulutso 1:17.
14. Tikamawerenga masomphenya a Yohane onena za Yesu ali mu ulemerero wake, kodi tiyenera kukhudzidwa bwanji?
14 Masiku ano, anthu a Mulungu amasangalala kwambiri akamawerenga mmene Yohane anafotokozera mwatsatanetsatane masomphenya ake osangalatsawo. Tsopano patha zaka zoposa 90 kuchokera pamene tsiku la Ambuye linayamba, ndipo masomphenyawo akupitirizabe kukwaniritsidwa mochititsa chidwi. Ifeyo sitikuyembekezera kuti Yesu adzayamba kulamulira m’tsogolo chifukwa tikudziwa kuti iye akulamulira mu Ufumu wake panopa. Choncho, ife amene timagonjera Ufumuwo mokhulupirika tiyenera kupitiriza kuphunzira zimene Yohane akufotokoza m’masomphenya oyambawa ndi kumvera mawu a Yesu Khristu, yemwe ali mu ulemerero wake.
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mumve zambiri pa nkhaniyi, onani buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? tsamba 88 mpaka 92, komanso tsamba 215 mpaka 218, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
b M’nthawi ya atumwi, mpingo ukalandira kalata kuchokera kwa mtumwi, nthawi zambiri ankaitumizanso kumipingo ina kuti nawonso apindule ndi malangizo a m’kalatayo.—Yerekezerani ndi Akolose 4:16.
c Zinthu zokongoletsera mkati mwa kachisi wa Solomo ndiponso zipangizo zimene zinali m’kachisimo anazipanga kapena kuzikutira ndi golide, koma zinthu za m’bwalo la kachisiyo zinali zamkuwa.—1 Mafumu 6:19-23, 28-35; 7:15, 16, 27, 30, 38-50; 8:64.
[Zithunzi patsamba 23]
Zinthu zakale zimene zinapezeka m’mizinda imene munali mipingo 7 imeneyi zimagwirizana ndi zimene Baibulo limanena. M’mizinda imeneyi, Akhristu a m’nthawi ya atumwi analandira mauthenga olimbikitsa a Yesu amene amalimbikitsanso mipingo padziko lonse masiku ano
PEGAMO
SIMUNA
TIYATIRA
SADE
EFESO
FILADEFIYA
LAODIKAYA