Chitani Khama pa Kuŵerenga
NYAMA sizingachite zimene inuyo mukuchita tsopano lino. Kaŵirikaŵiri chifukwa chosoŵa mwayi wopita kusukulu, munthu mmodzi mwa anthu sikisi alionse sanaphunzire kuŵerenga—ndipo amene anaphunzira, saŵerenga kaŵirikaŵiri. Komabe, luso lanu la kuŵerenga mawu olembedwa limakupatsani mwayi woyenda kumadera ena, kukumana ndi anthu amene miyoyo yawo ingakupindulitseni, ndi kudziŵa zinthu zimene zingakuthandizeni kuthana ndi nkhaŵa za moyo.
Mapindu amene mwana wasukulu angapeze kusukulu amadalira luso lake la kuŵerenga. Pokafuna ntchito, luso lake la kuŵerenga lidzakhudza mtundu wa ntchito imene angapeze ndi kuchuluka kwa maola amene ayenera kugwira ntchito yoti im’thandize pamoyo. Akazi apanyumba amene amaŵerenga bwino amatha kusamalira bwino mabanja awo pankhani ya zakudya zoyenerera, ukhondo, ndi kuwateteza ku matenda. Anakubala amene amatha kuŵerenga bwino angathandizenso ana awo kukula m’nzeru.
Komabe, phindu lalikulu koposa la kuŵerenga n’lakuti kumathandiza “kum’dziŵadi Mulungu.” (Miy. 2:5) Njira zambiri zimene timatumikira nazo Mulungu zimafuna luso la kuŵerenga. Pamisonkhano yampingo pamakhala kuŵerenga Malemba ndi mabuku ozikidwa pa Baibulo. Kuti ulaliki wanu m’munda ukhale wogwira mtima zimadalira kwambiri kaŵerengedwe kanu. Ndipo kukonzekera mbali zimenezi kumafuna kuŵerenga. Pachifukwa chimenechi, kukula kwanu mwauzimu kumadalira kwambiri chizoloŵezi chanu cha kuŵerenga.
Gwiritsani Ntchito Bwino Mwayiwo
Ena amene amaphunzira njira za Mulungu sanaphunzire kwambiri sukulu. Iwo angafunikire kuphunzitsidwa kuŵerenga kuti apite patsogolo mwauzimu. Kapena angafunikire kuwathandiza kuti akulitse luso lawo la kuŵerenga. Ngati pali chosoŵa chimenechi, mipingo imayesetsa kulinganiza makalasi ophunzitsa kuŵerenga ndi kulemba mwa kugwiritsa ntchito buku lakuti Dziperekeni pa Kuŵerenga ndi Kulemba. Anthu zikwizikwi apindula kwambiri ndi makonzedwe ameneŵa. Chifukwa chakuti kuŵerenga bwino n’kofunika kwambiri, mipingo ina yakhazikitsa makalasi othandiza anthu kuŵerenga bwino. Makalasiwo amachitika panthaŵi ya Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Ngakhale kumene kulibe masukulu amenewa, munthu akhoza kupitabe patsogolo mwa kupatula nthaŵi tsiku lililonse ndi kumaŵerenga motulutsa mawu ndi kumafika pa sukulu ya utumiki nthaŵi zonse komanso kumatengamo mbali.
Mwatsoka, kuchuluka kwa mabuku a zithunzi ndi mawailesi akanema, mwa zinthu zina, kwapangitsa anthu ambiri kusakondanso kuŵerenga. Kuonerera kwambiri wailesi yakanema ndi kusaŵerenga kungalepheretse munthu kupita patsogolo m’maluso a kuŵerenga ndi kuganiza bwino. Sakhalanso ndi luso la kulingalira ndi kulankhula bwino.
“Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndiye amapereka mabuku omwe amatithandiza kulimvetsa Baibulo. Mabukuwo amakhala ndi mfundo zothandiza pankhani zofunika zauzimu. (Mat. 24:45; 1 Akor. 2:12, 13) Amatifotokozeranso zochitika za m’dziko zofunika kuzidziŵa ndi tanthauzo lake, amatithandiza kudziŵanso zina ndi zina za chilengedwe, ndipo amatiphunzitsa mmene tingachitire ndi zinthu zimene zingatidetse nkhaŵa. Koposa zonse, amatiphunzitsa mmene tingatumikirire Mulungu moyenerera kuti atiyanje. Kuŵerenga kwabwino koteroko kudzatithandiza kukula mwauzimu.
Komabe, luso la kuŵerenga palokha silipindula kanthu. Tiyenera kuligwiritsa ntchito m’njira yoyenerera. Mofanana ndi kudya, tiyenera kusankha bwino zoŵerenga. N’kudyeranji chakudya chosathandiza thupi kapena chimene chingakudwalitseni? Mofananamo, n’kuŵerengeranji, ngakhale mongofuna kutayirapo nthaŵi, nkhani zimene zingaipitse maganizo ndi mtima wanu? Mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo ziyenera kutithandiza kusankha nkhani zimene tingaŵerenge. Musanasankhe zimene mungaŵerenge, kumbukirani malemba monga Mlaliki 12:12, 13; Aefeso 4:22-24; 5:3, 4; Afilipi 4:8; Akolose 2:8; 1 Yohane 2:15-17; ndi 2 Yohane 10.
Ŵerengani ndi Cholinga Chabwino
Kupenda nkhani zolembedwa m’Mauthenga Abwino anayiwo kumaonetsa kuti kuŵerenga ndi cholinga chabwino n’kofunika kwambiri. Mwachitsanzo, mu Uthenga Wabwino wa Mateyu, timaona kuti Yesu asanapereke mayankho a m’Malemba kwa atsogoleri achipembedzo ophunzirawo, pamafunso awo amachenjero, choyamba anawafunsa kuti “Kodi simunaŵerenga?” ndi kuti “Simunaŵerenga kodi?” (Mat. 12:3, 5; 19:4; 21:16, 42; 22:31) Phunziro limene tikutolapo apa n’lakuti ngati tiŵerenga ndi cholinga cholakwika, tikhoza kutengapo maganizo olakwika kapena kuphonyeratu mfundo yonse. Afarisi anali kuŵerenga Malemba chifukwa anali kuganiza kuti mwa kutero, akapeza moyo wosatha. Malinga ndi kunena kwa Yesu, mphatso imeneyo siipatsidwa kwa anthu amene sakonda Mulungu amenenso salandira njira Yake ya chipulumutso. (Yoh. 5:39-43) Zolinga za Afarisi zinali zadyera; choncho, zinthu zambiri anali kuzimva molakwika.
Cholinga chabwino koposa choŵerengera Mawu a Mulungu ndicho chikondi chathu pa Yehova. Chikondi chotero chimatilimbikitsa kuphunzira chifuniro cha Mulungu, pakuti chikondi “chikondwera ndi choonadi.” (1 Akor. 13:6) Ngakhale kuti m’mbuyomu sitinali kukonda kuŵerenga, kukonda Yehova ndi ‘nzeru zathu zonse’ kudzalimbikitsa maganizo athu kuti tiphunzire za Mulungu. (Mat. 22:37) Chikondi chimadzutsa chidwi, ndipo chidwi chimalimbikitsa kuphunzira.
Ganizirani Liŵiro la Kaŵerengedwe
Kuŵerenga kumayendera pamodzi ndi kuzindikira. Ngakhale mmene mukuŵerengeramu panopo, mukuzindikira mawu ndi kukumbukira matanthauzo ake. Mukhoza kuŵirikiza liŵiro la kaŵerengedwe kanu ngati mukulitsa luso lanu la kuzindikira. M’malo moona liwu limodzi ndi limodzi, yesani kuona mawu ambiri nthaŵi imodzi. Mmene luso limeneli likukula, mudzaona kuti mukumvetsa bwino kwambiri zimene mukuŵerenga.
Komabe, pamene muŵerenga nkhani zozama, kuti mumvetse zambiri muyenera kugwiritsa ntchito njira ina. Yehova popatsa uphungu Yoswa za kuŵerenga Malemba anati: “Buku ili la chilamulo lisachoke pakamwa pako; koma ulingiriremo.” (Yos. 1:8) Liwu lachihebri limene linamasuliridwa kuti, ‘kulingiriramo’ limatanthauzanso kusinkhasinkha. (Sal. 63:6; 77:12; 143:5) Posinkhasinkha, munthu amalingalira mozama; safulumira ayi. Kulingalira poŵerenga kumachititsa Mawu a Mulungu kukhomerezeka m’maganizo ndi m’mtima. Baibulo lili ndi maulosi, uphungu, miyambo, ndakatulo, ziweruzo za Mulungu, mfundo zokhudza chifuniro cha Yehova, ndi zitsanzo zambiri za zochitika zenizeni m’moyo—zonsezo n’zopindulitsa kwa aja ofuna kuyenda m’njira za Yehova. Baibulo ndi lopindulitsa kwabasi ngati muliŵerenga m’njira imene ingakhomereze mawu ake mozama m’maganizo ndi m’mtima mwanu!
Phunzirani Kuzika Maganizo Pankhani
Pamene mukuŵerenga, dziloŵetseni m’chochitika chimene chikufotokozedwacho. Yesani kuona anthuwo m’maganizo mwanu, ndiponso khalani okhudzidwa ndi mmene iwo akumvera m’zochitikazo. Zimenezi n’zosavuta poŵerenga nkhani ngati ya Davide ndi Goliati, yolembedwa m’chaputala 17 cha 1 Samueli. Ndipo ngakhale zinthu zofokozedwa mu Eksodo ndi Levitiko zokhudza kumangidwa kwa chihema kapena kuikidwa kwa ansembe zingakhale zosangalatsa kwambiri. Zingakhale zochititsa chidwi pamene muona m’maganizo mwanu mmene anali kupimira zinthu ndi kuona zipangizo zomangira. Kapena pamene muyerekeza kumva kununkhira kwa fungo lokoma la nsembe za mbewu zokazinga ndi nyama zimene zinali kuwotchedwa. Taganizani mmene kunalili koopsa kutumikira monga wansembe! (Luka 1:8-10) Kuzika maganizo anu ndi kuikirapo mtima mwa njira imeneyi kudzakuthandizani kumvetsa tanthauzo la zimene mukuŵerenga ndipo kudzakuthandizani kumakumbukira zinthu.
Komabe, ngati simusamala poŵerenga, maganizo anu angayambe kuthaŵathaŵa. Maso anu angamayang’ane patsambapo, koma maganizo anu angakhale atapita kwinakwake. Kodi pali nyimbo imene ikuimba? Kodi wailesi yakanema ndi yotsegula? Kodi ena m’nyumbamo akulankhula? Ngati n’kotheka, ndi bwino kuŵerengera m’malo abata. Komabe, zosokoneza zingachokere mwa inu mwini. Mwina munatanganidwa kwambiri tsikulo. Eya, n’zosavuta kumangokumbukira zimene mwachita tsikulo! Zoona, ndi chinthu chabwino kukumbukira zochitika za tsikulo—koma osati pamene mukuŵerenga. Mwina maganizo anu amakhala ozikika poyamba, mwinanso mumapereka pemphero musanayambe kuŵerenga. Komano pamene mukuŵerenga, maganizo anu angayambe kuthaŵathaŵa. Zikatero yesaninso kuzika maganizo anu. Dziumirizeni kuzika maganizo anu pankhani imene mukuŵerenga. Pang’ono ndi pang’ono, mudzaona kuti mukuyamba kuchita bwino.
Kodi muyenera kuchitanji mukapeza mawu amene simukuwamvetsa? Mawu ena achilendo amawamasulira kapena kuwafotokoza m’nkhani momwemo. Kapena mutha kuzindikira tanthauzo lake kuchokera m’nkhanimo. Apo ayi, yang’anani mawuwo mu mtanthauzira mawu (dikishonale) ngati muli nayo, kapena lembani mzera kunsi kwa mawuwo kuti mukafunse tanthauzo lake kwa munthu wina. Zimenezi zidzakuthandizani kudziŵa mawu ambiri ndi kumvetsa bwino zimene mukuŵerenga.
Kuŵerenga Pamaso pa Anthu
Pamene mtumwi Paulo anauza Timoteo kuti apitirize kuchita khama pa kuŵerenga, makamaka amatanthauza kuŵerenga kopindulitsa ena. (1 Tim. 4:13) Kuŵerenga pamaso pa anthu kogwira mtima kumafuna luso, osati kungotchula chisawawa mawu olembedwa. Woŵerengayo ayenera kudziŵa tanthauzo la mawuwo ndi kuzindikira zimene akunena. Pokhapokha akatero, m’pamene mfundo ndi malingaliro amene akuŵerenga angamveke molondola. Koma zimenezi zimafuna kukonzekera ndi kuyeseza bwinobwino. N’chifukwa chake Paulo analimbikitsa kuti: ‘Usamalire kuŵerenga.’ Luso limeneli mudzaliphunzira m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu.
Patulani Nthaŵi Yoŵerenga
“Zolinganiza za wakhama zimapinduladi, koma waphuma mapeto ake amakhala wosoŵa.” (Miy. 21:5, NW) Zimenezi n’zoona ponena za chilakolako chathu cha kuŵerenga! Kuti ‘tipindule,’ tiyenera kulinganiza zinthu mwakhama kuti zochita zina zisatisoŵetse nthaŵi yoŵerenga.
Kodi inuyo mumaŵerenga nthaŵi yanji? Kodi mumapindula mwa kuŵerenga m’mamaŵa? Kapena maganizo anu amagwira bwino zinthu masana? Ngati mungapatule mphindi 15 kapena 20 za kuŵerenga tsiku lililonse, mungadabwe mmene mungapindulire. Chinsinsi chake ndi kuŵerenga tsiku ndi tsiku mosalekeza.
Kodi Yehova anafuniranji kuti zifuniro zake zazikulu zilembedwe m’buku? Kuti anthu akathe kufufuza m’Mawu ake olembedwa. Zimenezi zimawatheketsa kusinkhasinkha ntchito zodabwitsa za Yehova, kuzifotokozera ana awo, ndi kusunga m’maganizo mwawo zochita za Mulungu. (Sal. 78:5-7) Timaonetsa kuyamikira mphatso ya Yehova imeneyi mwa kuchita khama pa kuŵerenga Mawu ake opatsa moyo.