MUTU 22
Kodi Mumagwiritsa Ntchito “Nzeru Yochokera Kumwamba”?
1-3. (a) Kodi Solomo anasonyeza bwanji nzeru zapadera pamene anathetsa mkangano wolimbirana mwana? (b) Kodi Yehova amalonjeza kuti azitipatsa chiyani, nanga zimenezi zingachititse kuti pakhale mafunso ati?
UNALI mlandu wovuta kwambiri, azimayi awiri ankalimbirana mwana. Azimayiwa ankakhala m’nyumba imodzi ndipo onse anabereka ana aamuna m’masiku oyandikana. Kenako mwana mmodzi anapezeka kuti wafa. Ndiyeno azimayiwo anayamba kulimbirana mwana wamoyoyo.a Panalibe aliyense woti aperekere umboni wa zimene zinachitikazi. N’kutheka kuti nkhaniyi inapita kukhoti laling’ono koma analephera kuithetsa. Pamapeto pake anapita nayo kwa Solomo, mfumu ya Isiraeli. Kodi iye akanakwanitsa kudziwa mayi wake weniweni wa mwanayo?
2 Atamvetsera kwa kanthawi azimayiwo akukangana, Solomo anaitanitsa lupanga. Kenako analamula kuti mwanayo amudule pakati ndipo mayi aliyense amupatse mbali imodzi. Ndipo zinkaoneka ngati watsimikizadi kuti mwanayo adulidwe pakati. Nthawi yomweyo mayi wake weniweni anachonderera mfumuyo kuti mwana wake wokondedwayo aperekedwe kwa mnzakeyo. Koma mayi winayo ankaumirira kuti mwanayo amudule basi. Apa Solomo anadziwa zoona zake. Iye ankadziwa kuti mayi amakonda kwambiri mwana wobereka yekha ndipo anagwiritsa ntchito zimenezi pothetsa mkanganowo. Taganizirani mmene mayi wake wa mwanayu anasangalalira Solomo atamupatsa mwanayo n’kunena kuti: “Mayi ake ndi amenewa.”—1 Mafumu 3:16-27.
3 Zimenezitu zinali nzeru zapadera. Anthu atamva mmene Solomo anaweruzira mlanduwo, anagoma kwambiri “chifukwa anaona kuti Mulungu wamupatsa nzeru.” Zoonadi, nzeru za Solomo zinali zochokera kwa Mulungu. Yehova anamupatsa “mtima wanzeru ndi womvetsa zinthu.” (1 Mafumu 3:12, 28) Koma bwanji ifeyo? Kodi ifenso Mulungu angatipatse nzeru? Inde, chifukwa mouziridwa ndi Mulungu, Solomo analemba kuti: “Yehova ndi amene amapereka nzeru.” (Miyambo 2:6) Yehova amalonjeza kuti azipereka nzeru, lomwe ndi luso lotha kugwiritsa ntchito zimene ukudziwa, kwa anthu onse omwe amafunitsitsa kukhala nazo. Ndiye kodi tingatani kuti tikhale ndi nzeru zochokera kumwamba? Ndipo kodi tingatani kuti tizigwiritsa ntchito nzeru zimenezi pa moyo wathu?
Kodi Tingatani Kuti ‘Tipeze Nzeru’?
4-7. Tchulani zinthu 4 zofunika kuti munthu akhale wanzeru.
4 Kodi tiyenera kukhala anzeru mwachibadwa kapena ophunzira kwambiri kuti tipeze nzeru za Mulungu? Ayi. Yehova ndi wokonzeka kutipatsa nzeru zake posatengera maphunziro athu kapenanso kuti ndife ndani. (1 Akorinto 1:26-29) Koma timafunika kuchita mbali yathu, chifukwa Baibulo limatilimbikitsa kuti ‘tipeze nzeru.’ (Miyambo 4:7) Kodi tingachite bwanji zimenezi?
5 Choyamba, tiyenera kumaopa Mulungu. Lemba la Miyambo 9:10 limati: “Kuopa Yehova ndi chiyambi cha nzeru.” Choncho kuti tikhale ndi nzeru zenizeni tiyenera kumaopa Mulungu. N’chifukwa chiyani zili choncho? Kumbukirani kuti nzeru zimatanthauza kudziwa mfundo zokhudza nkhani inayake, kuonetsetsa kuti tazimvetsa kenako n’kuzigwiritsa ntchito moyenera. Kuopa Mulungu sikutanthauza kunjenjemera chifukwa chochita naye mantha, koma kumatanthauza kumumvera chifukwa chomulemekeza kwambiri. Kuchita zimenezi n’kwabwino ndipo kumatithandiza kuti tizichita zoyenera komanso zogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna kuti tizichita. Palibe chinthu chanzeru kwambiri chimene tingachite kuposa zimenezi chifukwa anthu amene amatsatira mfundo za Yehova zinthu zimawayendera bwino kwambiri nthawi zonse.
6 Chachiwiri, tiyenera kukhala odzichepetsa. Munthu sangakhale ndi nzeru za Mulungu ngati si wodzichepetsa. (Miyambo 11:2) N’chifukwa chiyani zili choncho? Tikakhala odzichepetsa, timavomereza kuti sitidziwa zonse, si nthawi zonse pamene maganizo athu amakhala olondola ndiponso kuti timafunika kudziwa maganizo a Yehova pa nkhani zosiyanasiyana. Yehova “amatsutsa odzikuza” koma amasangalala kupereka nzeru kwa anthu odzichepetsa.—Yakobo 4:6.
7 Chachitatu, tiyenera kumaphunzira Mawu a Mulungu. Timadziwa nzeru za Yehova tikamawerenga Mawu ake. Kuti tipeze nzeruzi, tiyenera kumazifunafuna mwakhama. (Miyambo 2:1-5) Chinthu cha 4 ndi pemphero. Tikamapempha nzeru za Mulungu mochokera pansi pa mtima, iye adzatipatsa mosaumira. (Yakobo 1:5) Adzatithandizanso pogwiritsa ntchito mzimu wake woyera ngati titamupempha. Ndipo mzimu wake ungatithandize kupeza malangizo anzeru m’Mawu ake. Malangizowa angatithandize kulimbana ndi mavuto, kupewa zinthu zoopsa ndiponso kusankha zochita mwanzeru.—Luka 11:13.
Kuti tipeze nzeru za Mulungu, tiyenera kuzifufuza mwakhama
8. Ngati tilidi ndi nzeru zochokera kwa Mulungu, kodi zotsatira zake zingakhale zotani?
8 Monga tinaonera m’Mutu 17, nzeru za Yehova n’zothandiza. Choncho ngati tilidi ndi nzeru zochokera kwa Mulungu, zimene timachita zimasonyeza zimenezi. Yakobo, yemwe anali wophunzira wa Yesu, anafotokoza zimene zimachitika munthu akakhala ndi nzeru za Mulungu. Anati: “Nzeru yochokera kumwamba, choyamba, ndi yoyera, kenako yamtendere, yololera, yokonzeka kumvera, yodzaza ndi chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankho, ndiponso yopanda chinyengo.” (Yakobo 3:17) Tikamakambirana mbali iliyonse yokhudza nzeru za Mulunguzi, muzidzifunsa kuti, ‘Kodi ndimagwiritsa ntchito nzeru yochokera kumwamba pa moyo wanga?’
“Yoyera, Kenako Yamtendere”
9. Kodi kukhala woyera kumatanthauza chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani n’zomveka kuti choyamba tiyenera kukhala oyera kuti tithe kusonyeza nzeru ya Mulungu?
9 “Choyamba, ndi yoyera.” Kukhala woyera kumatanthauza kukhala wosadetsedwa, kunja ndi mkati momwe. Baibulo limati nzeru zimalowa mumtima. Komatu nzeru yochokera kumwamba singalowe mumtima umene wadetsedwa ndi maganizo olakwika, zilakolako zoipa komanso zolinga zosayenera. (Miyambo 2:10; Mateyu 15:19, 20) Koma tikamayesetsa kuti mtima wathu ukhale woyera, ‘timapewa kuchita zoipa ndipo timachita zabwino.’ (Salimo 37:27; Miyambo 3:7) M’pake kuti Baibulo limati choyamba tiyenera kukhala oyera kuti tikwanitse kusonyeza makhalidwe ena amene munthu amakhala nawo ngati ali ndi nzeru zochokera kwa Mulungu.
10, 11. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kumakhala mwamtendere ndi ena? (b) Ngati mwazindikira kuti mwakhumudwitsa Mkhristu mnzanu, kodi mungatani kuti mukhazikitse mtendere? (Onaninso mawu a m’munsi.)
10 “Kenako yamtendere.” Nzeru yochokera kumwamba imatithandiza kuti tiziyesetsa kukhala mwamtendere. Khalidweli timakhala nalo mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu. (Agalatiya 5:22) Timayesetsa kuti tisasokoneze ‘mtendere umene uli ngati chomangira chimene chimagwirizanitsa’ anthu a Yehova. (Aefeso 4:3) Timayesetsanso kubwezeretsa mtendere ukasokonekera. N’chifukwa chiyani zimenezi n’zofunika? Baibulo limati: “Pitirizani . . . kukhala mwamtendere. Mukatero, Mulungu amene ndi wachikondi komanso wamtendere adzakhala nanu.” (2 Akorinto 13:11) Choncho tikamapitiriza kukhala mwamtendere, Mulungu wamtendere adzakhala nafe. Mmene timachitira zinthu ndi Akhristu anzathu zimakhudza ubwenzi wathu ndi Yehova. Ndiye kodi tingakhazikitse bwanji mtendere? Taganizirani chitsanzo ichi.
11 Kodi mungatani ngati mwazindikira kuti mwakhumudwitsa Mkhristu mnzanu? Yesu anati: “Ngati wabweretsa mphatso yako paguwa lansembe, ndipo uli pomwepo wakumbukira kuti m’bale wako ali nawe chifukwa, siya mphatso yako patsogolo pa guwa lansembe pomwepo n’kuchokapo. Choyamba pita ukakhazikitse mtendere ndi m’bale wakoyo. Kenako ukabwerenso n’kudzapereka mphatso yakoyo.” (Mateyu 5:23, 24) Muziyamba ndi inuyo kupita kukakambirana ndi m’bale wanuyo ndipo mukamatero mumasonyeza kuti mukutsatira malangizo amenewa. Kodi cholinga chanu chiyenera kukhala chiyani? ‘Kukakhazikitsa mtendere.’b Kuti zimenezi zitheke mungafunike kuvomereza, osati kukana, kuti nkhaniyo yamukhumudwitsa mnzanuyo. Ngati pa nthawi yonse imene mukulankhulana mutakhala ndi cholinga choti mubwezeretse mtendere, mukhoza kuthetsa kusamvana, kupepesana ndiponso kukhululukirana. Mukayesetsa kuti mukhazikitse mtendere, mumasonyeza kuti mukutsogoleredwa ndi nzeru za Mulungu.
“Yololera, Yokonzeka Kumvera”
12, 13. (a) Kodi mawu amene anawamasulira kuti “kulolera” pa Yakobo 3:17, amatanthauza chiyani? (b) Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife ololera?
12 “Yololera.” Kodi kulolera kumatanthauza chiyani? Akatswiri ena a Baibulo amati mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “yololera” pa Yakobo 3:17 ndi ovuta kuwamasulira. Omasulira ena anamasulira mawuwa kuti “yodekha,” “yoleza mtima” ndi “yokoma mtima.” Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife ololera?
13 Lemba la Afilipi 4:5 limati: “Anthu onse adziwe kuti ndinu ololera.” Baibulo lina limati: “Mukhale ndi mbiri yoti ndinu wololera.” (The New Testament in Modern English, lomasuliridwa ndi J. B. Phillips) Onani kuti nkhani si mmene timadzionera koma mmene ena amationera, kuti timadziwika ndi mbiri yotani. Munthu wololera saumirira malamulo kapenanso kufuna kuti nthawi zonse zinthu zichitike mmene iye akufunira. Koma amakhala wokonzeka kumva maganizo a ena ndipo amachita zimene anthuwo akufuna ngati kuchita zimenezo kuli koyenera. Amakhala wodekha, osati waukali kapena wankhanza. Ngakhale kuti zimenezi n’zofunika kwa Akhristu onse, n’zofunika kwambiri makamaka kwa akulu. Anthu amakopeka ndi munthu wodekha, ndipo mkulu wodekha savuta kulankhula naye. (1 Atesalonika 2:7, 8) Choncho tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi anthu amandiona kuti ndine wokoma mtima, wololera komanso wodekha?’
14. Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife ‘okonzeka kumvera’?
14 “Yokonzeka kumvera.” Mawu a Chigiriki omwe anawamasulira kuti “yokonzeka kumvera” amapezeka pamalo okhawa m’Malemba a Chigiriki a Chikhristu. Katswiri wina ananena kuti mawu amenewa “nthawi zambiri amagwiritsidwa ntchito ponena za asilikali amene ndi ofunitsitsa kumvera malamulo ankhondo.” Amanena za “kukopeka mosavuta” ndiponso “kugonjera.” Munthu amene akutsogoleredwa ndi nzeru yochokera kumwamba amagonjera mosavuta zimene Malemba amanena. Sadziwika kuti ndi munthu womva zake zokha yemwe safuna kumva mfundo zotsutsana ndi zake. Koma amasintha mofulumira akapatsidwa umboni womveka bwino wochokera m’Malemba woti akuchita zolakwika kapena sanasankhe bwino. Kodi inuyo mumadziwika kuti ndinu munthu wotero?
“Yodzaza ndi Chifundo ndi Zipatso Zabwino”
15. Kodi chifundo n’chiyani, nanga n’chifukwa chiyani chatchulidwa limodzi ndi “zipatso zabwino” pa Yakobo 3:17?
15 “Yodzaza ndi chifundo ndi zipatso zabwino.”c Chifundo ndi mbali yofunika kwambiri ya nzeru yochokera kumwamba, chifukwa nzeruyi imatchulidwa kuti ndi “yodzaza ndi chifundo.” Onani kuti “chifundo” chatchulidwa limodzi ndi “zipatso zabwino.” Zimenezi n’zoyenera, chifukwa m’Baibulo mawu akuti chifundo nthawi zambiri amanena za kudera nkhawa munthu kapena kumumvera chisoni n’kumuchitira zinthu zabwino. Buku lina linanena kuti chifundo ndi “kumvera chisoni munthu amene zoipa zamuchitikira kenako n’kuyesetsa kumuthandiza.” Choncho munthu amene ali ndi nzeru yochokera kumwamba sikuti amangodziwa zimene anthu ena akumana nazo, koma amakhala wokoma mtima komanso woganizira ena. Ndiye kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife odzaza ndi chifundo?
16, 17. (a) Kuwonjezera pa kukonda Mulungu, n’chiyaninso chimatichititsa kuti tizigwira nawo ntchito yolalikira? (b) Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife odzadza ndi chifundo?
16 Njira yofunika kwambiri ndi kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. N’chifukwa chiyani timagwira ntchitoyi? Chifukwa chachikulu n’chakuti timakonda Mulungu. Koma timagwiranso ntchitoyi chifukwa choti timachitira ena chifundo. (Mateyu 22:37-39) Masiku ano anthu ambiri ndi “onyukanyuka komanso opanda wowasamalira ngati nkhosa zimene zilibe m’busa.” (Mateyu 9:36) Atsogoleri awo achipembedzo samawasamalira komanso amawasocheretsa. Zotsatira zake n’zakuti anthuwa sadziwa malangizo anzeru omwe amapezeka m’Mawu a Mulungu ndiponso madalitso amene Ufumu wa Mulungu ubweretse padzikoli posachedwa. Choncho tikamaganizira kuti anthu akufunika kumva uthenga wabwino, timawamvera chisoni ndipo timafuna kuchita chilichonse chimene tingathe kuti tiwauze uthengawu.
17 Kodi tingasonyeze kuti ndife odzadza ndi chifundo m’njira zinanso ziti? Kumbukirani fanizo la Yesu la Msamariya amene anapeza munthu atagona m’mbali mwa msewu, atamubera ndiponso kumumenya. Msamariyayo anamva chisoni ndipo ‘anamuchitira chifundo’ n’kumumanga mabala ake ndiponso kumusamalira. (Luka 10:29-37) Zimenezitu zikusonyeza kuti munthu wachifundo amathandiza anthu amene akuvutika. Baibulo limatiuza kuti ‘tizichitira onse zabwino, koma makamaka abale ndi alongo athu m’chikhulupiriro.’ (Agalatiya 6:10) Taonani zina zimene tingachite pa nkhaniyi. Mkhristu wachikulire angafunike kumuthandiza kuti apite kumisonkhano yampingo. Mlongo wamasiye mumpingo angafunike kumuthandiza kukonza nyumba yake. (Yakobo 1:27) Munthu amene ali ndi nkhawa angafunike kumuuza “mawu abwino” omwe angamulimbikitse. (Miyambo 12:25) Tikamasonyeza chifundo m’njira ngati zimenezi, ndi umboni wakuti nzeru yochokera kumwamba ikutitsogolera.
“Yopanda Tsankho, Ndiponso Yopanda Chinyengo”
18. Ngati tikutsogoleredwa ndi nzeru yochokera kumwamba, kodi tiyenera kuyesetsa kuchotsa chiyani mumtima mwathu ndipo n’chifukwa chiyani?
18 “Yopanda tsankho.” Nzeru yochokera kumwamba imatithandiza kuti tisamaganize kuti ndife apamwamba kusiyana ndi anthu amitundu ina kapena a m’mayiko ena. Tikamatsogoleredwa ndi nzeru imeneyi, timayesetsa kuchotsa tsankho mumtima mwathu. (Yakobo 2:9) Tikamachitira ena zabwino, sititengera kuti ndi ophunzira, opeza bwino kapena ali ndi udindo mumpingo. Ndiponso timaona kuti Mkhristu aliyense ndi wofunika ngakhale amene amaoneka ngati wonyozeka. Ngati Yehova amakonda anthu amenewa, ndiye kuti nafenso tiyenera kuwakonda.
19, 20. (a) Kodi mawu a Chigiriki omwe anawamasulira kuti “wachinyengo,” anayambira pati? (b) Kodi timasonyeza bwanji kuti ‘timakonda abale mopanda chinyengo,’ ndipo n’chifukwa chiyani zimenezi zili zofunika?
19 “Yopanda Chinyengo.” Mawu a Chigiriki omwe anawamasulira kuti “wachinyengo,” anganene za “munthu amene wachita nawo sewero pabwalo la masewera.” Kale, Agiriki ndi Aroma akamachita masewero ankavala zinthu zobisa nkhope. Choncho mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “wachinyengo,” anayamba kuwagwiritsa ntchito ponena za munthu amene ankachita zinthu mwachinyengo kapena amene ankapusitsa anthu. Mbali imeneyi ya nzeru yochokera kumwamba, imakhudza mmene timachitira zinthu ndi Akhristu anzathu komanso mmene timawaonera mumtima mwathu.
20 Mtumwi Petulo ananena kuti popeza ‘timamvera choonadi,’ tiyenera ‘kumakonda abale mopanda chinyengo.’ (1 Petulo 1:22) Zoonadi, sitiyenera kukonda abale ndi alongo athu n’cholinga chongofuna kudzionetsera kapena kuoneka ngati abwino. Chikondi chathu chiyenera kukhala chenicheni komanso chochokera pansi pa mtima. Tikamachita zimenezi, abale ndi alongo athu azitikhulupirira chifukwa adzadziwa kuti si ife achinyengo. Zimenezi zingathandize kuti tizigwirizana kwambiri ndiponso kuti anthu mumpingo azidalirana.
“Uteteze Nzeru Zopindulitsa”
21, 22. (a) Kodi Solomo analephera bwanji kuteteza nzeru? (b) Kodi tingateteze bwanji nzeru, nanga kuchita zimenezi kungatithandize bwanji?
21 Nzeru yochokera kumwamba ndi mphatso imene Yehova amatipatsa, choncho tiyenera kuiteteza. Solomo anati: “Mwana wanga, . . . uteteze nzeru zopindulitsa ndiponso kuganiza bwino.” (Miyambo 3:21) Koma n’zomvetsa chisoni kuti Solomoyo analephera kuchita zimenezi. Anali wanzeru pa nthawi yonse imene ankamvera Mulungu. Koma patapita nthawi, akazi ake ambirimbiri achilendo anamuchititsa kuti asamalambire Yehova movomerezeka. (1 Mafumu 11:1-8) Zimene zinachitikira Solomo zimatiphunzitsa kuti zinthu zimene timadziwa sizingatithandize ngati sitingazigwiritse ntchito bwino.
22 Kodi tingateteze bwanji nzeru zopindulitsa? Kuwonjezera pa kuwerenga Baibulo nthawi zonse ndiponso mabuku ofotokoza Baibulo omwe “kapolo wokhulupirika komanso wanzeru” amapereka, tiyenera kuyesetsa kumagwiritsa ntchito zimene timaphunzira. (Mateyu 24:45). Tili ndi zifukwa zambiri zotichititsa kugwiritsira ntchito nzeru za Mulungu pa moyo wathu. Nzeruzi zimatithandiza kuti zinthu zizitiyendera bwino panopa. Zimatithandizanso kuti ‘tigwire mwamphamvu moyo weniweniwo’ womwe tidzakhale nawo m’dziko latsopano. (1 Timoteyo 6:19) Ndipo chofunika kwambiri n’chakuti kukhala ndi nzeru yochokera kumwamba kumatithandiza kuti tikhale pa ubwenzi ndi Yehova Mulungu, yemwe ndi Mwiniwake wa nzeru zonse.
a Mogwirizana ndi 1 Mafumu 3:16, azimayi awiriwo anali mahule. Buku la Insight on the Scriptures limati: “N’kutheka kuti azimayiwa sanali oyendayenda, koma anali mahule m’njira yakuti ankachita zachiwerewere. Mwina anali Ayuda kapenanso sanali Ayuda.”—Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
b Mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “ukakhazikitse mtendere,” amatanthauza “kusiya kukhala adani n’kukhala mabwenzi, kugwirizananso ndiponso kuyambiranso kuchitira zinthu limodzi.” Choncho cholinga chanu n’kuthandiza m’bale wanu amene wakhumudwayo kuti ngati zingatheke asiye kukhumudwa nanu.—Aroma 12:18.
c Baibulo lina linamasulira mawu amenewa kuti “yodzaza ndi chifundo ndi ntchito zabwino.”—A Translation in the Language of the People, lomasuliridwa ndi Charles B. Williams.