Mukhale Nzika Kapena Mlendo, Mulungu Akulandirani!
“Ndi [munthu, “NW”] mmodzi analenga mitundu yonse ya anthu, kuti akhale ponse pa nkhope ya dziko lapansi.”—MACHITIDWE 17:26.
1. Kodi ndivuto lotani lomwe liripo lerolino m’maiko ambiri ponena zakulandira anthu amiyambo yakwina?
MALIPOTI apanyuzi amasonyeza kuti m’maiko ambiri nkhaŵa ikukula ponena za alendo, anthu odzakhala m’dziko, ndi othaŵa kwawo. Mamiliyoni akulakalaka kusamuka kuchoka m’mbali zina za Asia, Afirika, Yuropu, ndi Amereka. Mwinamwake amafuna kuthaŵa umphaŵi waukulu, nkhondo yachiŵeniŵeni, kapena chizunzo. Koma kodi iwo amalandiridwa kwina kulikonse? Magazini a Time ananena kuti: “Pamene kulolera mafuko ena kwa ku Yuropu kuyamba kusintha, maiko ena amapeza kuti sangalolere miyambo yachilendo monga momwe ankalingalirira.” Mwa anthu othaŵa kwawo okwanira 18,000,000 “osafunidwa,” Time inati: “Vuto limene amalipereka pa maiko osatekeseka silidzatha.”
2, 3. (a) Kodi ndichiyembekezo chotonthoza mtima chotani chimene Baibulo limachipereka ponena za kulandiridwa? (b) Kodi nchifukwa ninji tingapindule mwakusanthula zimene Malemba amanena ponena za zochita za Mulungu ndi anthu?
2 Zirizonse zimene zingachitike m’nkhani iyi, Baibulo limasonyeza kuti Mulungu amalandira anthu a mitundu yonse—kaya munthuyo akhale nzika yobadwira m’dzikomo, wodzakhala m’dzikomo, kapena wothaŵa kwawo. (Machitidwe 10:34, 35) ‘Komabe,’ ena angafunse kuti, ‘kodi munganene bwanji zimenezo? Kodi Mulungu sindiye anasankha Israyeli wakale yekha monga anthu ake, nasiya ena onse?’
3 Eya, tiyeni tiwone mmene Mulungu anachitira ndi anthu ake akale. Tikhoza kupendanso maulosi ena amene amasonyeza mwaŵi umene ulipo kwa olambira owona lerolino. Kupenda nkhani zaulosi kumeneku kungakupatseni kumvetsetsa kokwanira kumene mungakupeze kukhala kolimbikitsa koposa. Kumasonyezanso mmene Mulungu angachitire ndi anthu a ‘mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe’ pambuyo pa chisautso chachikulu.—Chivumbulutso 7:9, 14-17.
‘Mitundu Yonse Idzadalitsidwa’
4. Kodi vuto la mtundu linayamba motani, koma kodi Mulungu anachitaponji?
4 Pambuyo pa Chigumula, banja lenilenilo la Nowa ndilo lidali mtundu wonse wa anthu, ndipo onse adali olambira owona. Koma mwamsanga, kugwirizana kumeneko kunasintha. Posapita nthaŵi, anthu ena, akunyalanyaza chifuniro cha Mulungu, anayamba kumanga nsanja. Izi zinatsogolera kukugaŵikana kwa anthu m’magulu a zinenero amene anafikira kukhala anthu ndi mitundu yomwazikana. (Genesis 11:1-9) Chikhalirechobe, kulambira kowona kunapitirizabe mumzera wotsogolera kwa Abrahamu. Mulungu anadalitsa Abrahamu wokhulupirika namlonjeza kuti mbadwa yake ikakhala mtundu waukulu. (Genesis 12:1-3) Mtundu umenewo unali Israyeli wakale.
5. Kodi nchifukwa ninji tonsefe tingapeze chilimbikitso m’zochita za Mulungu ndi Abrahamu?
5 Komabe, Yehova sanachite tsankhu kwa anthu ena kusiyapo Israyeli, chifukwa chakuti chifuno chake chinali kaamba ka mtundu wonse wa anthu. Timawona zimenezi bwino lomwe mwa zimene Mulungu analonjeza Abrahamu kuti: ‘M’mbewu yako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa; chifukwa wamvera mawu anga.’ (Genesis 22:18) Ngakhale ndichoncho, Mulungu anachita ndi Israyeli mwanjira yapadera kwa zaka mazana ambiri, kuwapatsa mpambo wa Chilamulo cha mtundu wonsewo, napanga makonzedwe akuti ansembe ndiwo adzipereka nsembe pakachisi wake, ndi kupereka Dziko Lolonjezedwa lokhalamo.
6. Kodi ndimotani mmene makonzedwe a Mulungu ndi Israyeli amapindulira onse?
6 Lamulo la Mulungu kwa Israyeli linali labwino kwa anthu a mitundu yonse kaamba kakuti linavumbula kuchimwa kwa anthu, kusonyeza kufunika kwa nsembe yangwiro yokwirira machimo a anthu kamodzi kwatha. (Agalatiya 3:19; Ahebri 7:26-28; 9:9; 10:1-12) Komabe, kodi ndichitsimikizo chotani chimene chinalipo chakuti Mbewu ya Abrahamu—kupyolera mwa imene mitundu yonse ikadalitsidwa—ikafika ndi kukwaniritsa ziyeneretso? Apanso, Chilamulo cha Israyeli chinathandiza. Chinaletsa kukwatirana ndi Akanani, anthu oluluzika m’machitachita oipa ndi madzoma, monga ngati mwambo wakutentha ana amoyo. (Levitiko 18:6-24; 20:2, 3; Deuteronomo 12:29-31; 18:9-12) Mulungu analamula kuti anthuwo ndi machitachita awo anayenera kuwonongedwa. Zimenezo zikakhala zaphindu mtsogolo kwa onse, kuphatikizapo alendo ogonera, popeza kuti zikatetezera mzera wa Mbewuyo kusaluluzidwa.—Levitiko 18:24-28; Deuteronomo 7:1-5; 9:5; 20:15-18.
7. Kodi nchisonyezero choyambirira chotani chimene chinalipo chakuti Mulungu analandira alendo?
7 Ngakhale pamene Chilamulo chinali kugwira ntchito ndipo Mulungu anawona Israyeli monga wapadera, anasonyeza chifundo kwa osakhala Aisrayeli. Kufunitsitsa kwake kwakuchita zimenezo kunasonyezedwa pamene Israyeli anatuluka muukapolo wa Igupto kulinga ku dziko lake. ‘Anthu ambiri osakanizika anakwera nawo.’ (Eksodo 12:38) Profesa C. F. Keil akutchula amenewo kukhala “gulu la alendo . . . gulu losakanizana, kapena khamu la anthu a mitundu yosiyanasiyana.” (Levitiko 24:10; Numeri 11:4) Mwachiwonekere ambiri omwe analandira Mulungu wowona anali Aigupto.
Kulandira Alendo
8. Kodi ndimotani mmene Agibeoni anapezera malo pakati pa anthu a Mulungu?
8 Pamene Israyeli analabadira lamulo la Mulungu lakuchotsa m’Dziko Lolonjezedwa mitundu yonyansa, anatetezera gulu limodzi la alendo, Agibeoni, omwe ankakhala kumpoto kwa Yerusalemu. Iwo anatumiza oimira omwe anavala modzibisa kwa Yoswa, akupempha kupanga nawo mtendere ndipo anaupeza. Pamene machenjera awo anadziŵika, Yoswa analamula kuti Agibeoni akatumikira monga ‘otema nkhuni, ndi otungira madzi msonkhanowo, ndi guwa lansembe la Yehova.’ (Yoswa 9:3-27) Lerolino, obwera kudzakhala m’dziko nawonso amalandira maudindo otsika kotero kuti akhale mbali ya mtundu watsopano.
9. Kodi chitsanzo cha Rahabi ndi banja lake ncholimbikitsa motani kwa alendo mu Israyeli?
9 Kungakulimbikitseni kudziŵa kuti Mulungu sanangolandira magulu a alendo okha kalero; anthu mmodzi ndi mmodzi analandiridwanso. Lerolino maiko ena amalandira kokha anthu odzakhala m’dziko amene ali ndi malo apamwamba, chuma chodzachitira malonda, kapena maphunziro apamwamba. Siziri tero ndi Yehova, monga momwe tikuwonera m’chochitika chotsatiridwa ndi kukumana ndi Agibeoni. Ichi chikuloŵetsamo Mkanani amene sanalidi ndi malo apamwamba. Baibulo limamutcha “Rahabi wadama.” Chifukwa cha chikhulupiriro chake mwa Mulungu wowona, iye ndi abanja lake anapulumutsidwa pamene Yeriko anagwa. Ngakhale kuti Rahabi anali mlendo, Aisrayeli anamlandira. Iye anali chitsanzo cha chikhulupiriro choyenera kuchitsanzira. (Ahebri 11:30, 31, 39, 40; Yoswa 2:1-21; 6:1-25) Ndipo iye anafikiradi kukhala kholo la Mesiya.—Mateyu 1:5, 16.
10. Kodi kulonjeredwa kwa alendo mu Israyeli kunadalira pachiyani?
10 Osakhala Aisrayeli analandiridwa m’Dziko Lolonjezedwa chifukwa cha zoyesayesa zawo zakukondweretsa Mulungu wowona. Aisrayeli anauzidwa kusayanjana, makamaka ponena za kupembedza, ndi anthu amene sanatumikire Yehova. (Yoswa 23:6, 7, 12, 13; 1 Mafumu 11:1-8; Miyambo 6:23-28) Chikhalirechobe, osakhala Aisrayeli ambiri odzakhala m’dzikomo analabadira malamulo ofunika kwambiri. Ena anakhaladi otembenuzidwa odulidwa, ndipo Yehova anawalandira ndi manja onse monga ziŵalo za mpingo wake.—Levitiko 20:2; 24:22; Numeri 15:14-16; Machitidwe 8:27.a
11, 12. (a) Kodi Aisrayeli anayenera kuwachitira motani olambira achilendo? (b) Kodi nchifukwa ninji tingafunikire kuwongokera m’kutsatira chitsanzo cha Yehova?
11 Mulungu analangiza Aisrayeli kutsanzira mtima wake kulinga kwa olambira akunja: ‘Mlendo wakugonera kwa inu mumyese pakati pa inu monga wa m’dziko momwemo; umkonde monga udzikonda wekha; popeza munali alendo m’dziko la Aigupto.’ (Levitiko 19:33, 34; Deuteronomo 1:16; 10:12-19) Apatu timatengapo phunziro, ngakhale kuti sitiri pansi pa Chilamulo. Nkosavuta kugwa mumsampha wa tsankho ndi udani kulinga kwa fuko, mtundu, kapena mwambo wina. Choncho ndibwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndikuyesayesa kutaya tsankho, ndikulondola chitsanzo cha Yehova?’
12 Aisrayeli anadziwonera okha mmene Mulungu amalandirira anthu. Mfumu Solomo anapemphera kuti: ‘Kunena za mlendo, wosati wa anthu anu a Israyeli, koma wakufumira m’dziko lakutali chifukwa cha dzina lanu . . . akabwera iyeyo nadzapemphera molunjika ku nyumba ino; mverani inu m’mwamba mokhala inu . . . kuti anthu onse a dziko lapansi adziŵe dzina lanu, kuwopa inu.’—1 Mafumu 8:41-43; 2 Mbiri 6:32, 33.
13. Kodi nchifukwa ninji Mulungu anapanga makonzedwe akusintha kachitidwe kake ndi Israyeli?
13 Pamene kuli kwakuti Yehova ankagwiritsirabe mtundu wa Israyeli monga anthu ake ndipo motero kutetezera mzera wobadwira wa Mesiya, Mulungu ananeneratu masinthidwe aakulu. Poyambirira, pamene Israyeli anavomereza kukhala m’pangano la Chilamulo, Mulungu anawauza kuti akakhala magwero a ‘ufumu wa ansembe, ndi mtundu wopatulika.’ (Eksodo 19:5, 6) Koma Israyeli anasonyeza kusakhulupirika kwa zaka mazana ambiri. Chotero Yehova ananeneratu kuti akapanga pangano latsopano mwalimene awo okhala “nyumba ya Israyeli” adzakhululukidwa mphulupulu ndi machimo awo. (Yeremiya 31:33, 34) Pangano latsopano limenelo linayembekezera Mesiya, amene nsembe yake ikayeretsadi ambiri ku machimo awo.—Yesaya 53:5-7, 10-12.
Aisrayeli Kumwamba
14. Kodi ndi “Israyeli” watsopano wotani amene Yehova analandira, ndipo motani?
14 Malemba Achikristu Achigiriki amatithandiza kumvetsetsa mmene zonsezi zinachitikira. Yesu anali Mesiyayo, amene imfa yake inakwaniritsa Chilamulo ndi kuyala maziko achikhululukiro chotheratu cha machimo. Kuti apeze phindu limenelo, munthu sanafunikire kukhala Myuda wodulidwa mwakuthupi. Ayi. Mtumwi Paulo analemba m’pangano latsopano kuti, “iye ali Myuda amene ali mkati ndipo mdulidwe wake ndiwo uja wa mtima mwa mzimu, ndipo osati mwa malamulo olembedwa.” (Aroma 2:28, 29; 7:6, NW) Amene anakhulupirira nsembe ya Yesu anachipeza chikhululukiro, ndipo Mulungu anawavomereza monga ‘Ayuda mwa mzimu,’ amene amapanga mtundu wauzimu wotchedwa “Israyeli wa Mulungu.”—Agalatiya 6:16.
15. Kodi nchifukwa ninji kukhala wa mtundu wakutiwakuti sindiko maziko akukhalira mbali ya Israyeli wauzimu?
15 Inde, kulandiridwa mu Israyeli wauzimu sikunadalire pakukhala wa mtundu kapena wa fuko lakutilakuti. Ena, monga atumwi a Yesu, anali Ayuda akuthupi. Ena, monga kazembe Wachiroma Korneliyo, anali Akunja osadulidwa. (Machitidwe 10:34, 35, 44-48) Ponena za Israyeli wauzimu, Paulo ananena molondola kuti: ‘Palibe Mhelene ndi Ayuda, mdulidwe ndi kusadulidwa, wotchedwa wakunja, Mskuti, kapolo, mfulu.’ (Akolose 3:11) Awo odzozedwa ndi mzimu wa Mulungu anakhala ‘mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu amwini wake.’—1 Petro 2:9; yerekezerani ndi Eksodo 19:5, 6.
16, 17. (a) Kodi Aisrayeli auzimu ali ndi mbali yanji m’chifuniro cha Mulungu? (b) Kodi nchifukwa ninji kuli koyenera kulingalira awo osakhala a Israyeli wa Mulungu?
16 Kodi ndimtsogolo motani mmene Aisrayeli auzimu ali namo m’chifuniro cha Mulungu? Yesu anayankha kuti: ‘Musawopa, kagulu ka nkhosa inu; chifukwa Atate wanu akonda kukupatsani ufumu.’ (Luka 12:32) Ozodzedwa, amene ‘unzika [wawo] uli kumwamba,’ adzakhala oloŵa nyumba ndi Mwanawankhosa muulamuliro wa Ufumu. (Afilipi 3:20; Yohane 14:2, 3; Chivumbulutso 5:9, 10) Baibulo limasonyeza kuti iwoŵa ‘anasindikizidwa chizindikiro mwa ana a Israyeli’ ndi ‘kugulidwa mwa anthu, zipatso zoundukula kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa.’ Chiŵerengero chawo ndi 144,000. Komabe, pambuyo pakufotokoza zakusindikizidwa kwa chiŵerengero chimenechi, Yohane akusonyeza gulu losiyana—‘khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliŵerenga, ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi manenedwe.’—Chivumbulutso 7:4, 9; 14:1-4.
17 Ena angafunse kuti: ‘Koma bwanji ponena za mamiliyoni amene sali mbali ya Israyeli, monga awo amene angapulumuke chisautso chachikulu monga khamu lalikulu? Kodi iwo ali ndi mbali yanji lerolino kulinga kwa otsalira ochepa a Israyeli wauzimu?’b
Alendo Onenedwa mu Ulosi
18. Kodi nchiyani chinachititsa kuti Israyeli abwereko ku ukapolo wa ku Babulo?
18 Titayang’ana kunthaŵi pamene Israyeli anali pansi pa pangano la Chilamulo koma osalisunga, timapeza kuti Mulungu analola Ababulo kugwetsa Israyeli. Mu 607 B.C.E., Israyeli anatengedwa kuukapolo kwa zaka 70. Ndiyeno Mulungu anauwombolanso mtunduwo. Motsogozedwa ndi Kazembe Zerubabele, otsalira a Israyeli wakuthupi anabwerera ku dziko lakwawo. Olamulira a Amedi ndi Aperisi, omwe adagwetsa Babulo, anathandiziradi otuluka muukapolowo mwakuwapatsa zinthu zambiri. Bukhu la Yesaya linaneneratu zochitika zimenezi. (Yesaya 1:1-9; 3:1-26; 14:1-5; 44:21-28; 47:1-4) Ndipo Ezara akutipatsa tsatanetsatane wa mbiri ya kubwerera kumeneko.—Ezara 1:1-11; 2:1, 2.
19. Ponena za kubwerera kwa Israyeli, kodi panali chisonyezero chaulosi chotani chakuti alendo akaphatikizidwapo?
19 Chikhalirechobe, ponena za kuwomboledwanso ndi kubwerera kwa anthu a Mulungu, Yesaya anapereka ulosi wodabwitsawu: ‘Ndipo amitundu adzafika kwa kuunika kwako, ndi mafumu kwa kuyera kwa kutuluka kwako.’ (Yesaya 59:20; 60:3) Izi zimatanthauza zoposa kulandiridwa kwa akunja, mogwirizana ndi pemphero la Solomo. Yesaya anali kuloza ku masinthidwe achilendo a malo a munthu. “Mitundu” ikatumikira pamodzi ndi ana a Israyeli: ‘Alendo adzamanga malinga ako, ndi mafumu awo adzakutumikira; pakuti m’kukwiya kwanga ndinakantha, koma mokomera mtima ndidakuchitira iwe chifundo.’—Yesaya 60:10.
20, 21. (a) Kodi ndikufanana kotani kumene timawona lerolino ndi kubwerako kwa Israyeli ku ukapolo? (b) Kodi ndimotani mmene ‘ana aamuna ndi aakazi’ pambuyo pake anawonjezeredwa ku Israyeli wauzimu?
20 M’mbali zambiri, kupita kwa Israyeli ndi kubwerako ku ukapolo kuli ndi zofanana nazo m’nthaŵi zamakono ndi Israyeli wauzimu. Nkhondo ya Dziko ya I isanachitike, otsalira a Akristu odzozedwa sanatsatire kwenikweni chifuniro cha Mulungu; anatsatirabe malingaliro ena ndi machitachita otengedwa ku matchalitchi a Chikristu Chadziko. Ndiyeno, m’chipwirikiti cha nthaŵi ya nkhondo ndi kusonkhezera kwa atsogoleri achipembedzo, otsogolera ena pakati pa otsalira a Israyeli wauzimu anaponyedwa m’ndende popanda chifukwa choyenera. Pambuyo pa nkhondo, mu 1919 C.E., odzozedwa amenewo okhala m’ndende zenizenizo anamasulidwa ndi kuchotseredwa milandu. Izi zinali umboni wakuti anthu a Mulungu anamasulidwa ku ukapolo wa Babulo Wamkulu, ulamuliro wadziko lonse wa chipembedzo chonyenga. Anthu ake anapita patsogolo kumanga paradaiso wauzimu ndi kukhalamo.—Yesaya 35:1-7; 65:13, 14.
21 Izi zinasonyezedwa m’malongosoledwe a Yesaya akuti: ‘Iwo onse asonkhana pamodzi, adza kwa iwe; ana ako aamuna adzachokera kutali, ndi ana ako aakazi adzaleredwa pambali. Pamenepo udzawona ndi kuunikidwa, ndipo mtima wako udzanthunthumira ndi kukuzidwa; pakuti unyinji wa nyanja udzakutembenukira, chuma cha amitundu chidzafika kwa iwe.’ (Yesaya 60:4, 5) M’zaka makumi otsatira, ‘ana aamuna ndi aakazi’ anapitiriza kubwera, nadzozedwa ndi mzimu kudzatenga malo omalizira mu Israyeli wauzimu.
22. Kodi ndimotani mmene “alendo” amabwerera kudzagwira ntchito pamodzi ndi Aisrayeli auzimu?
22 Bwanji ponena za ‘alendo omwe adzamangadi malinga ako’? Izinso zachitika m’nthaŵi yathu. Pamene chiitano cha a 144,000 chinali kufika kumapeto, khamu lalikulu lochokera m’mitundu yonse linayamba kudza m’maunyinji kudzalambira ndi Israyeli wauzimu. Achatsopano ameneŵa ali ndi chiyembekezo chozikidwa pa Baibulo cha moyo wosatha padziko lapansi laparadaiso. Ngakhale kuti malo awo autumiki wokhulupirika akakhala osiyana, anali osangalala kuthandiza otsalira odzozedwa kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu.—Mateyu 24:14.
23. Kodi “alendo” akhala akuthandiza odzozedwa kuukulu wotani?
23 Lerolino, ‘alendo’ oposa 4,000,000, pamodzi ndi otsalira a amene ‘unzika wawo uli kumwamba,’ akupereka umboni wa kudzipereka kwawo kwa Yehova. Ambiri a iwo, amuna ndi akazi, achichepere ndi nkhalamba, akutumikira muutumiki wanthaŵi zonse monga apainiya. M’yambiri ya mipingo yoposa 66,000, alendo oterowo akusenza mathayo monga akulu ndi atumiki otumikira. Otsalira akukondwera ndi zimenezi, powona kukwaniritsidwa kwa mawu a Yesaya akuti: ‘Ndipo alendo adzaimirira ndi kudyetsa magulu ako, ndi anthu akunja adzakhala olima ako, ndi kukukonzera minda yampesa.’—Yesaya 61:5.
24. Kodi nchifukwa ninji tingalimbikitsidwe ndi zochita za Mulungu ndi Israyeli ndi ena m’nthaŵi zakale?
24 Chotero, m’dziko lirilonse limene mungakhale nzika, wodzakhala m’dziko, kapena wothaŵa kwawo, muli ndi mwaŵi waukulu wakukhala mlendo wauzimu amene Wamphwamvuyonse amamlandira ndi mtima wonse. Kukulandirani kwake kumaphatikizapo kuthekera kwa kusangalala ndi mwaŵi wa mautumiki tsopano ndi mtsogolo mosatha.
[Mawu a M’munsi]
a Ponena zakusiyana kwa mawu akuti “wogonera” (alien resident), “wodzakhala m’dziko” (settler), “mlendo” (stranger), ndi “wakunja” (foreigner), onani Insight on the Scriptures, Volyumu 1, masamba 72-5, 849-51, yofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
b Oposa 10,600,000 anapezeka pachikumbutso cha chaka ndi chaka cha Mgonero wa Ambuye chochitidwa ndi Mboni za Yehova mu 1991, koma 8,850 okha ndiwo anadzisonyeza kukhala otsalira a Israyeli wauzimu.
Kodi Mwadziŵa Izi?
◻ Kodi ndimotani mmene Mulungu anaperekera chiyembekezo chakuti Iye akalandira anthu amitundu yonse?
◻ Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti anthu ena, pambali pa Israyeli, anthu apadera a Mulungu, anakhoza kumfikira Iye?
◻ Malinga ndi ulosi, kodi ndimotani mmene Mulungu anasonyezera kuti alendo akaphatikana ndi Israyeli?
◻ Kodi nchiyani chimene chafanana ndi kubwerako kwa Israyeli ku ukapolo m’Babulo, ndipo kodi ndimotani mmene “alendo” aloŵetsedweramo?
[Chithunzi patsamba 9]
Mfumu Solomo anapemphera ponena za alendo omwe akabwera kudzalambira Yehova