Zosangulutsa Pocheza—Sangalalani ndi Mapinduwo, Peŵani Misampha
‘Nkwabwino kuti munthu adye namwe, nawonetse moyo wake zabwino m’ntchito yake.’—MLALIKI 2:24.
1. Kodi ndimwanjira zotani zimene chitsogozo cha Mulungu chimathandizira anthu ake m’zosangulutsa?
CHITSOGOZO cha Yehova chimabweretsera atumiki ake mapindu ambiri. Tingathe kuwona zimenezi m’zosangulutsa. Chitsogozo chake chimathandiza Akristu kupeŵa kapenyedwe ka zinthu konkitsa. Anthu ena opembedza, amene amaumirira pamalamulo ankhokera akavalidwe ndi kudzisungira, amawona pafupifupi kusanguluka kulikonse kukhala tchimo. Kumbali ina, anthu ochuluka amalondola zosangulutsa ngakhale ngati zimenezo ziwombana ndi malamulo a Yehova ndi makhalidwe abwino.—Aroma 1:24-27; 13:13, 14; Aefeso 4:17-19.
2. Kodi nchiyani poyambirira chinasonyeza lingaliro la Mulungu ponena za zosangulutsa?
2 Komabe, bwanji ponena za anthu a Mulungu? Ambiri amene amayamba kuphunzira Baibulo amadabwa kumva kuti kwenikweni Mulungu analenga anthu ndi kuthekera kwa kusangalala ndi moyo. Anapatsa makolo athu oyambirira ntchito yochita—koma osati ntchito yothodwetsa imene kwakukulukulu yalamulira miyoyo ya anthu ochuluka opanda ungwiro. (Genesis 1:28-30) Talingalirani njira zambimbiri zimene onse okhala m’dziko lapansi laparadaiso angapezere chisangalalo. Tayerekezerani chimwemwe chawo powona nyama zakutchire zimene sizingawawopseze ndi zoŵeta zosiyanasiyana zimene zingakhale mbali ya moyo wa tsiku ndi tsiku! Ndi zakudya zimene angapeze ku “mitengo yonse yokoma m’maso ndi yabwino kudya.”—Genesis 2:9; Mlaliki 2:24.
3-5. (a) Kodi nchifuno chotani chimene zosangulutsa ziyenera kutumikira? (b) Kodi nchifukwa ninji tingatsimikizire kuti Mulungu sanaletse Aisrayeli kupeza chisangalalo?
3 Kunena zowona, zochita zimenezo zingatengedwe kukhala zosangulutsa, zimene chifuno chake m’Paradaiso chingakhale chofanana ndi cha leroli: kutsitsimula ndi kulimbitsa nyonga ya munthu kaamba ka zochita (ntchito) zopindulitsa zowonjezereka. Pamene zosangulutsa zikwaniritsa zimenezi, zimapindulitsa. Kodi zimenezo zikutanthauza kuti olambira owona angakhale ndi nthaŵi m’moyo wawo ya zosangulutsa ngakhale kuti sali kale m’Paradaiso? Inde. Insight on the Scriptures imati ponena za zosangulutsa pakati pa anthu a Yehova amakedzana:
4 “Zokondweretsa ndi maseŵera a Aisrayeli sizimasonyezedwa mwapadera m’cholembedwa cha Baibulo. Komabe, chimazisonyeza kukhala zofunika kuwonedwa kukhala ponse paŵiri zoyenera ndi zabwino zitagwirizana ndi malamulo amakhalidwe abwino achipembedzo a mtunduwo. Mipangidwe yaikulu ya maseŵera inali kuimba ndi zoimbira, kuimba nyimbo, kuvina, kukambitsirana, kudzanso maseŵero. Kupherana miyambi ndi mafunso ovuta kunali kwamtengo wapatali.—Ower 14:12.”—Voliyamu 1, tsamba 102.
5 Pamene Davide anabwerera atalakika, akazi Achihebri anaimba ndi zoimbira ndi malingaka pokondwerera (Chihebri, sa·chaqʹ). (1 Samueli 18:6, 7) Liwu Lachihebrilo kwakukulukulu limatanthauza “kuseka,” ndipo matembenuzidwe ena amanena za “akazi osekera.” (Byington, Rotherham, The New English Bible) Pamene Likasa linali kusamutsidwa, “Davide ndi a nyumba yonse ya Israyeli anaseŵera pamaso pa Yehova, ndi zoimbira zamitundumitundu.” Mikala, mkazi wa Davide, anali ndi lingaliro lopambanitsa, pakuti anatsutsa Davide chifukwa chokhala ndi phande m’machitachita osangulutsawo. (2 Samueli 6:5, 14-20) Mulungu analosera kuti andende obwerako ku Babulo akakhala ndi phande m’machitachita osangalatsa ofananawo.—Yeremiya 30:18, 19; 31:4; yerekezerani ndi Salmo 126:2.
6. Kodi ndimotani mmene Malemba Achikristu Achigiriki amatithandizira m’kapenyedwe kathu ka zosangulutsa?
6 Nafenso tiyenera kuyesayesa kukhala achikatikati m’zosangulutsa. Mwachitsanzo, kodi timazindikira kuti Yesu sanali wodzimana mopambanitsa? Iye anapeza nthaŵi ya madyerero otsitsimula, onga ngati “phwando lalikulu” limene Levi anakonza. Ndipo pamene odziyesa olungama anamuimba mlandu chifukwa cha kudya ndi kumwa, Yesu anatsutsa malingaliro ndi njira zawo. (Luka 5:29-31; 7:33-36) Kumbukiraninso kuti, anachita zonse ziŵiri kufika paphwando laukwati ndi kuthandiza pamapwandowo. (Yohane 2:1-10) Mbale wa Yesu wa atate wina Yuda akunena kuti Akristu anali ndi “mapwando achikondano,” mwachiwonekere madyerero amene osoŵa akadyako chakudya ndi kusangalala ndi mayanjano okoma, otsitsimula.—Yuda 12.
Zosangulutsa Pocheza Nthaŵi ndi Malo Ake
7. Kodi ndimotani mmene Mawu a Mulungu amalimbikitsira uchikatikati m’zosangulutsa?
7 Mlaliki 10:19 amanena moyanja ‘mkate wakudya kuti antchito asekere ndi vinyo wokondweretsa moyo.’ Zimenezo sizikumveka ngati kuti zosangulutsa mwa izo zokha ziri zolakwika kapena zoipa, kodi sichoncho? Komabe, lemba limodzimodzilo limati: “Kanthu kalikonse kali ndi nthaŵi yake . . . mphindi yakugwa misozi ndi mphindi yakuseka; mphindi yakulira ndi mphindi yakuvina.” (Mlaliki 3:1, 4) Inde, ngakhale kuti silimatsutsa zosangulutsa zoyenerera, Baibulo limatichenjeza. Machenjezowo amaphatikizapo uphungu wakuika zosangulutsa pocheza m’malo ake ponena za nthaŵi ndi mlingo wake. Limatichenjezanso za mbuna zimene zafalikira kwambiri pamasonkhano aakulu akucheza.—2 Timoteo 3:4.
8, 9. Kodi nchifukwa ninji nthaŵi imene tikukhalamo ndi moyo ndi ntchito yathu yopatsidwa ndi Mulungu ziyenera kuyambukira zosangulutsa?
8 Tawona kale kuti Ayuda obwerako ku Babulo—amene anali ndi ntchito yakalavula gaga yochuluka yochita—akakhala ndi phande m’kupuma kotsitsimula. Komabe, Yeremiya poyambirira ananena kuti ‘sakakhala m’msonkhano wa iwo amene asekerasekera, ndi kusangalala.’ (Yeremiya 15:17) Iye anagaŵiridwa ntchito ndi Mulungu yakulalikira uthenga wa chilango chomayandikira, chotero sinali nthaŵi yoyenerera yakuti iye asekere.
9 Akristu lerolino agaŵiridwa ntchito yolengeza uthenga wa Mulungu wa chiyembekezo limodzi ndi kulengeza ziweruzo zake padongosolo loipa la Satana. (Yesaya 61:1-3; Machitidwe 17:30, 31) Chotero ziyenera kukhala zowonekeratu kuti sitiyenera kulola zosangulutsa kukhala ndi mbali yaikulu m’miyoyo yathu. Tingayerekezere mfundoyi ndi kuika mchere pang’ono kapena chokoleretsa china chapadera chimene chimawonjezera kukoma kwa chakudya. Kodi mungatsire zokoleretsa zochuluka kotero kuti nkuchititsa chakudya kuŵaŵa? Kutalitali. Mogwirizana ndi mawu a Yesu pa Yohane 4:34 ndi Mateyu 6:33, chinthu chachikulu kwa ife—chakudya chathu chenicheni—chiyenera kukhala kuchita chifuniro cha Mulungu. Chotero zosangulutsa zimakhala ngati chokoleretsa. Ziyenera kukhala zotsitsimula ndi zolimbikitsa, osati zolemetsa kapena zothodwetsa.
10. Kodi nchifukwa ninji tonsefe tiyenera kupendanso nthaŵi imene timathera m’zosangulutsa?
10 Taimani kaye ndi kulingalira kuti, Kodi anthu ochuluka sanganene kuti nthaŵi ndi chisamaliro zimene amapereka kuzosangulutsa ziri zachikatikati? Ngati akanalingalira kuti siziri choncho, akanapanga masinthidwe. Kodi zimenezi sizikupereka lingaliro lakuti aliyense wa ife ayenera kuima kaye, ndiyeno kupenda mwamphamvu, ndi mowona mtima malo amene kwenikweni zosangulutsa ziri nawo m’moyo wathu? Kodi mwinamwake mosadziŵa zakhala mbali yaikulu ya moyo wathu? Mwachitsanzo, kodi timangofikira kutsegula TV panthaŵi iriyonse imene tafika panyumba? Kodi takulitsa chizoloŵezi chakupatula nthaŵi yaikulu kaamba ka zosangulutsa mlungu uliwonse, monga ngati Lachisanu kapena Loŵeruka lirilonse usiku? Kodi tingagwiritsidwe mwala ngati nthaŵiyo yafika ndipo tiri panyumba popanda zosangulutsa zolinganizidwa? Mafunso aŵiri owonjezereka ngakuti: “Pambuyo pa tsiku la kucheza kosangulutsa kapena chochitika china chofanana, kodi timapeza kuti tinachedwa kufika panyumba kapena tinayenda mtunda wautali kotero kuti talema, mwinamwake kutoperatu kotero kuti tilephera kukhala ndi phande muunisitala Wachikristu kapena kulephera kugwirira bwino ntchito wotilemba ntchitoyo patsikulo? Ngati panthaŵi zina, kapena kaŵirikaŵiri, zosangulutsa zathu zimakhala ndi chiyambukiro chimenecho, kodi ziridi kusanguluka koyenera ndi kwachikatikati?—Yerekezerani ndi Miyambo 26:17-19.
11. Kodi nchifukwa ninji kupenda mtundu wa zosangulutsa zathu kuli koyenerera?
11 Kungakhalenso bwino kwa ife kupendanso mtundu wa zosangulutsa zathu. Kukhala kwathu atumiki a Mulungu sindiko chitsimikizo chakuti zosangulutsa zathu nzoyenerera. Talingalirani zimene mtumwi Petro analembera Akristu odzozedwa: “Nthaŵi yapitayi idatifikira kuchita chifuno cha amitundu, poyendayenda ife m’kukhumba zonyansa, zilakolako, maledzero, madyerero, mamwaimwa, ndi kupembedza mafano kosaloleka.” (1 Petro 4:3) Iye sanali kuloza chala, titero kunena kwake, akumaimba abale ake mlandu wakutsanzira zimene anthu akudziko anali kuchita. Komabe, kukhala tcheru nkofunika kwa Akristu (panthaŵiyo ndi tsopanoli) chifukwa chakuti munthuwe ungagwidwe mosavuta m’msampha wa zosangulutsa zovulaza.—1 Petro 1:2; 2:1; 4:7; 2 Petro 2:13.
Chenjerani ndi Misampha
12. Kodi 1 Petro 4:3 amagogomezera msampha wotani?
12 Kodi ndimsampha wotani umene tiyenera kuchenjera nawo? Eya, Petro anatchula “maledzero, madyerero, mamwaimwa.” Mjeremani wina wothirira ndemanga anafotokoza kuti mawu Achigiriki ogwiritsiridwa ntchito “kwakukulukulu anasonya kukumwa pocheza paphwando.” Profesa Wachiswiss analemba kuti machitachita amenewo anali ofala kalelo akumati: “Malongosoledwewo ayenera kusonya kumapwando olinganizidwa kapena makalabu anthaŵi zonse kumene zinthu zochititsa manyazi zolongosoledwazo zinachitika.”
13. Kodi ndimotani mmene kumwa zoledzeretsa pamasonkhano ocheza kwakhalira msampha? (Yesaya 5:11, 12)
13 Kukhala ndi zakumwa zoledzeretsa pamapwando ocheza kwatchera ambiri msampha. Sitikunena kuti Baibulo limaletsa kumwa kwachikatikati zoledzeretsa zotero, pakuti silimatero. Monga umboni wa zimenezi, Yesu anapanga vinyo paphwando laukwati ku Kana. Payenera kukhala panalibe kumwa kopambanitsa, pakuti Yesu akanasunga uphungu wa Mulungu wakupeŵa kukhala ndi zidakwa. (Miyambo 23:20, 21) Koma talingalirani mawu aŵa: Woyang’anira phwandolo ananena kuti pamapwando ena vinyo wokoma anayamba kuperekedwa ‘ndipo anthu ataledzera, pamenepo vinyo wosakoma.’ (Yohane 2:10) Choncho kunali kofala kwa Ayuda kuledzera pamaukwati amene vinyo wochuluka anali wopezeka kwa onse.
14. Kodi ndimwanjira zotani zimene Akristu olandira alendo angalakire msampha umene zakumwa zoledzeretsa zingapereke?
14 Chotero, Akristu ena olandira alendo asankha kupereka vinyo, moŵa, ndi zakumwa zina zoledzeretsa kokha pamene iwo eni angayang’anire zimene alendo awo akulandira kapena kumwa. Ngati gululo liri lalikulu kwambiri kuposa limene wocherezayo angayang’anire iye mwini mwachindunji, longa ngati la maukwati Achiyuda otchulidwawo, zoledzeretsa zochuluka zingakhale msampha wowopsa. Pangakhale munthu amene anamenyera nkhondo kulaka vuto lakumwa. Inu mudziŵa kuti kupeza zoledzeretsa kosalamulirika kwa aliyense kungaike munthuyo pachiyeso chakumwa mopambanitsa ndi kuipitsira onse chochitikacho. Woyang’anira wina amenenso ali atate ku Jeremani ananena kuti banja lake limapindula ndi mayanjano abwino ndi okhulupirira anzawo pamapwando ocheza. Komabe, iye anawonjezera kuti kuthekera kwa mavuto kumakhaladi kokulirapo pamene moŵa uperekedwa mosavuta.
15. Kodi ndimotani mmene chitsogozo choyenera pamapwando ocheza chingapezekere?
15 Ukwati wa ku Kana unali ndi ‘mkulu waphwando.’ (Yohane 2:8) Zimenezi sizikutanthauza kuti banja limene laitanira kagulu kuchakudya panyumba yawo kapena lalinganiza mphindi zakucheza liyenera kuika woyang’anira. Mwamunayo ayenera kukhala ndi thayo lakuyang’anira chochitikacho. Koma kaya kaguluko kali kokha mabanja aŵiri kapena kokulirapo, kuyenera kukhala kodziŵika kuti wina ali ndi thayo loyang’anira zochitikazo. Makolo ambiri amapenda zimenezi pamene mwana wawo wamwamuna kapena wamkazi waitanidwa kuphwando lokacheza. Amafunsa wocherezayo ponena za amene adzayang’anira chochitika chonsecho, kuphatikizapo kukhalapo mpaka mapeto. Makolo Achikristu asintha ngakhale programu yawo kuti apezekepo kotero kuti achikulire ndi achichepere omwe akhoze kusangalala pamodzi.
16. Kodi ndizinthu ziti zoyenera kuzilingalira ponena za chiŵerengero cha ofika paphwando?
16 Nthambi ya ku Canada ya Watch Tower Society inalemba kuti: “Uphungu wonena za kuchepetsa chiŵerengero cha ofika pamapwando ocheza wamvedwa ndi akulu angapo kukhala ukutanthauza kuti ziŵerengero zazikulu za anthu ofika pamapwando aukwati zimaswa uphungu. Iwo anena kuti ngati tapatsidwa uphungu wakuchepetsa chiŵerengero cha ofika pamapwando ocheza, kukhala chokhoza kulamulirika, kungakhale kulakwa kukhala ndi anthu 200 kapena 300 paphwando laukwati.”a Mmalo mogogomezera mopambanitsa chiŵerengero choikidwiratu, chisamaliro chachikulu chiyenera kuperekedwa pauyang’aniro woyenera, mosasamala kanthu za unyinji umene udzakhalako. Kuchuluka kwa vinyo amene Yesu anapereka kumasonyeza kuti kagulu kokulirapo kanafika paukwatiwo ku Kana, koma mwachiwonekere kanayang’aniridwa bwino. Mapwando ena kalelo sanatero; kukula kwawo kungakhale kunachititsa uyang’aniro wopeleŵera. Pamene kaguluko kali kokulirapo, mpamenenso chitokoso chimakhala chokulirapo, chifukwa chakuti nkosavuta kwa ofookerapo, okhoterera kukunkitsa, kudzilungamitsa. Pamayanjano osayang’aniridwa iwo angaphatikizidwe m’machitachita okaikiritsa.—1 Akorinto 10:6-8.
17. Kodi ndimotani mmene uchikatikati Wachikristu ungasonyezedwere polinganiza mapwando?
17 Uyang’aniro wabwino pakusonkhana kocheza umaphatikizapo kuulinganiza ndi kuukonzekera. Zimenezi sizimafuna kulinganiza mutu wankhani wokopa wopanga phwandolo kukhala lapadera kapena losaiŵalika koma limene lingafanane ndi mapwando audziko, monga ngati mapwando komwe anthu amavina atavala malaya ovinira kapena mapwando ozimbaiza. Kodi mungayerekezere Aisrayeli okhulupirika m’Dziko Lolonjezedwa akulinganiza phwando limene onse akafunikira kuvala mofanana ndi akunja m’Igupto kapena dziko lina? Kodi iwo akalinganiza kuvina kodzutsa chilakolako kapena nyimbo zaphokoso zimene zingakhale zotchuka pakati pa akunja? Pa Phiri la Sinai, iwo anakodwa m’msampha wa nyimbo ndi kuvina zimene mwinamwake zinali zofala ndi zotchuka m’Igupto. Tidziŵa mmene Mulungu ndi mtumiki wake wokula msinkhu Mose anawonera kusanguluka kumeneko. (Eksodo 32:5, 6, 17-19) Chifukwa chake, wolandira alendoyo kapena woyang’anira chochitika chakucheza ayenera kupenda kuti kaya padzakhala kuimba kulikonse ndi kuvina; ndipo ngati zidzakhalapo, ayenera kutsimikizira kuti ziri zogwirizana ndi malamulo amakhalidwe abwino Achikristu.—2 Akorinto 6:3.
18, 19. Kodi ndichidziŵitso chotani chimene tingapeze m’kuitanidwa kwa Yesu kuukwati, ndipo tingaigwiritsire ntchito motani mfundoyi?
18 Pomaliza, tikukumbukira kuti ‘Yesu ndi ophunzira ake anaitanidwa kuphwando laukwati.’ (Yohane 2:2) Nzowona kuti, Mkristu wina kapena banja lingangocheza kwa ena kaamba ka nthaŵi yabwino yomangirira. Koma ponena za mapwando ocheza olinganizidwa, maumboni amasonyeza kuti kudziŵiratu pasadakhale amene adzapezekako kumathandizira kupeŵa mavuto. Kufunika kwa zimenezi kunagogomezeredwa ndi mkulu wina ku Tennessee, U.S.A., amene walera ana amuna ndi akazi amene ali muuminisitala wanthaŵi yonse. Iye ndi mkazi wake asanavomereze chiitano, kapena kulola ana ake kukapezekako, akafunsa wolandira alendo kuti atsimikizire ngati opezekako anali odziŵika pasadakhale. Banja lake linatetezeredwa kumisampha imene yagwira ena pamayanjano otsegukira onse, kaya akhale madyerero, pikiniki, kapena kulimbitsa thupi, monga ngati kuseŵera mpira.
19 Yesu sanalimbikitse kuitanira kuphwando achibale okha, mabwenzi akale, kapena anthu amsinkhu kapena mkhalidwe wachuma wofanana. (Luka 14:12-14; yerekezerani ndi Yobu 31:16-19; Machitidwe 20:7-9.) Ngati musankha mosamalitsa amene muyenera kuitana, nkosavuta kuphatikizapo Akristu amisinkhu ndi mikhalidwe yosiyanasiyana. (Aroma 12:13; Ahebri 13:2) Ena a iwo angakhale ofooka kuuzimu kapena atsopano amene angapindule ndi kuyanjana ndi Akristu akulu msinkhu.—Miyambo 27:17.
Zosangulutsa m’Malo Ake Oyenera
20, 21. Kodi nchifukwa ninji zosangulutsa moyenerera zingakhale ndi malo m’moyo wathu?
20 Nkoyenera kwa ife monga anthu owopa Mulungu kukhala okondwera ndi zosangulutsa zathu ndi kutsimikizira kuti zimenezo nzoyenera ndi kuti tiri achikatikati panthaŵi imene timathera potero. (Aefeso 2:1-4; 5:15-20) Wolemba Mlaliki wouziridwa analingalira mofananamo kuti: “Ndinatama kusekaseka, pakuti munthu alibe kanthu kabwino pansi pano, koma kudya ndi kumwa, ndi kusekera; ndi kuti zimenezi zikhalebe naye m’vuto lake masiku onse a moyo wake umene Mulungu wampatsa pansi pano.” (Mlaliki 8:15) Zosangulutsa zachikatikati zotero zingatsitsimule thupi ndi kuthandizira kupeŵetsa mavuto ndi zogwiritsa mwala zofala m’dongosolo lamakonoli.
21 Mwachitsanzo, mpainiya wina ku Austria analembera bwenzi lake lakale kuti: “Tinali ndi pikiniki yabwino kwambiri posachedwapa. Ifeyo, pafupifupi 50, tinapita kunyanja ina yaing’ono pafupi ndi Ferlach. Mbale B—— anatinyamula tonse m’galimoto lake, titatenga mbaula zitatu zophikira, mipando yopinda, mathebulo, ndipo ngakhale thebulo la thebotenesi. Tinasangalala kwambiri. Mlongo wina anali ndi akodiyoni, chotero tinaimba nyimbo zambiri Zaufumu. Abale, achichepere ndi achikulire, anasangalala ndi mayanjanowo.” Mpainiyayu anali ndi zikumbukiro zabwino za zosangulutsa zoyang’aniridwa bwino zimene zinalibe misampha yonga ngati kumwa kopambanitsa kapena kudzisungira kosadziletsa.—Yakobo 3:17, 18.
22. Pamene tikusanguluka pocheza, kodi ndichenjezo lotani limene aliyense wa ife ayenera kulikumbukira mosalekeza?
22 Paulo anatifulumiza kukhala osamala kusagonjera zikhumbo za thupi lopanda ungwiro, osati ngakhale kulinganiza zinthu zimene zimatiika pachiyeso. (Aroma 13:11-14) Zimenezo zimaphatikizapo makonzedwe a zosangulutsa pocheza. Pamene tigwiritsira ntchito uphungu wake pazinthu zotero, tidzakhoza kupeŵa mikhalidwe imene yachititsa ena kuwonongeka mwauzimu. (Luka 21:34-36; 1 Timoteo 1:19) Mmalomwake, tidzasankha mwanzeru zosangulutsa zabwino zimene zidzatithandiza kusungitsa unansi wathu ndi Mulungu. Motero tidzapindula ndi zosangulutsa pocheza zimene zingawonedwe kukhala zina za mphatso zabwino za Mulungu.—Mlaliki 5:18.
[Mawu a M’munsi]
a Nsanja ya Olonda ya October 15, 1984, inali ndi uphungu wachikatikati wonena za maukwati ndi mapwando aukwati. Woyembekezera kukhala mkwati ndi mkwatibwi wake, limodzi ndi ena amene adzawathandiza, angapindule mwakupendanso nkhani imeneyo asanalinganize makonzedwe aukwati.
Kodi Taphunziranji?
◻ Kodi ndilingaliro lachikatikati lotani limene timalipeza m’Baibulo lonena za kukhala ndi zosangulutsa pocheza?
◻ Kodi nchifukwa ninji nthaŵi ndi mtundu wa zosangulutsa ziyenera kulingaliridwa?
◻ Kodi ndizinthu zina ziti zimene Mkristu wolandira alendo ayenera kuchita kuti apeŵe msampha?
◻ Ngati ziri zoyenera ndi zachikatikati, kodi nchiyani chimene zosangulutsa zingachitire Akristu?
[Chithunzi patsamba 18]
Wolandira alendo kapena woyang’anira phwando ali ndi thayo lakuwona kuti alendo sakutcheredwa msampha