Kulalikira m’Maputo—Likulu la Mozambique Lochititsa Chidwi!
Mu 1991, Mboni za Yehova zinavomerezedwa mwalamulo m’Mozambique. Kuyambira pamenepo kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu kwakhala kukupita patsogolo mwapadera m’dziko lotentha limeneli lopezeka kugombe lakumwera koma chakummaŵa kwa Afirika. Nkhani yotsatirayi ikusimba mmene Mboni za Yehova zikuchitira ntchito yawo yakuphunzitsa Baibulo m’Mozambique, makamaka m’Maputo, likulu lake.
MOZAMBIQUE ali ndi mkhalidwe wakunja wabwino chifukwa cha mphepo yochokera ku nyanja yanchere yofunda ya Indian Ocean. Gombe lake nlodzala ndi madoko okongoletsedwa ndi mingwalangwa ndi mitandadza ya korali. Dziŵe lalikulu lamadzi otsekerezedwa lipezeka kumwera kwa dzikolo—malo oyenerera a likulu lake, Maputo.
Komabe, kukongola ndi bata la dzikoli, zimapereka chithunzi chosiyana ndi mbiri yake yachiwawa. Kwa zaka mazana ambiri linavutika ndi ulamuliro wa maiko akunja, choyamba Aluya ndiyeno Apwitikizi. Otsiriziraŵa obwera mwachivomerezo cha Tchalitchi cha Katolika anadzafunkha chuma cha dzikoli—minyanga, golidi, ndi akapolo. Pomalizira, pambuyo pa zaka mazana ambiri za kutsenderezedwa ndi atsamunda, munaulika nkhondo yowopsa m’dzikomo imene inatsogolera ku ufulu wodzilamulira mu 1975. Mwachisoni, kusinthako sikunapangitse moyo kukhala wotetezereka kwambiri, popeza kuti dzikolo linagwera m’chipwirikiti cha nkhondo yachiweniweni, ikumachititsa kuvutika kwakukulu kwa anthuwo, makamaka anthu akumidzi osalakwa.
M’Maputo, Likululo
M’zaka khumi zapitazo, zikwi zambiri za Amozambique athaŵira ku malo otetezereka pang’ono a matauni ndi mizinda. Zimenezi makamaka zimawoneka m’Maputo, kumene kusanganikirana kwa nyumba Zachipwitikizi zomangidwa mwaukatswiri ndi Afirika wokongola zimapereka mawonekedwe okongola ku mzindawo. Ngati mukuyenda mowongola miyendo m’makwalala otakata okhala ndi mizera ya mitengo m’mbali mwake m’Maputo lerolino, chinthu choyamba chimene mudzawona ndicho makamu a anthu oyenda piringupiringu otanganitsidwa m’zochita zawo za tsiku ndi tsiku. Koma pali kusiyana. “Mosasamala kanthu za kuchuluka kwawo ndi zovuta za moyo wamasiku onse, anthuwo amakhala aubwenzi nthaŵi zonse,” akutero Rodrigo, mmishonale m’Maputo. “Sumapeza konse anthu amwano!” Inde, Amozambique amadziŵika kukhala anthu achisangalalo ndi aubwenzi.
Ndithudi, mofanana ndi mbali zambiri za Afirika, malo ozoloŵereka opezako anthu ndiwo pamsika wakumalowo. Kupita kumeneko mukhoza kukwera Chapa 100, dzina lakumaloko la magalimoto a vani ambiri amene amagwiritsiridwa ntchito monga zoyendera za anthu onse. Mwachizoloŵezi, anthu ochuluka amawonekera kukhala ogwiririra kunja kwa galimoto kuposa okwera mkati. Mwina kuyenda pansi kuli bwinopo.
Amozambique ali osaletseka m’malonda. Mlendo m’Mozambique sangalephere kuwona mmene ambiri amadzipezera ntchito mwakuimika malo a msika aang’ono m’mbali mwamsewu ndi m’magulayi amakwalala. Kodi mukakonda kugula zipatso zosafota, ndiwo zamasamba, mankhwala amthengo, kapena zokoreretsa? Pali zogulitsa zochuluka kwambiri. Bwanji za nkhuku yamoyo, mtedza, kapena mabango omangira nyumba yanu? Palibe chimene chimadodometsa aliyense, ndipo zonse zimachitidwa ndi mzimu waubwenzi. Mautumiki onga kuikitsa polishi kunsapato zanu kapena kutsukitsa galimoto lanu aliponso. Mwakugwiritsira ntchito chitsulo chotentha ndi pepala lapulasitiki, mnyamata wachichepere adzakuikirani m’mapulasitiki zikalata zanu zofunikazo.
Kwenikweni, simalonda onse a m’khwalala amene amaloledwa ndi lamulo. Komabe amachitidwa. Ogulitsa mosaloledwa ndi lamulo amatchedwa dumba nenge, limene limatanthauza kuti “dalira mapazi ako.” Zimenezi nzowona chifukwa chakuti pamene apolisi abwera kudzayendera, liŵiro limakhala lofunika kupulumutsa malonda awo okhala paupandu.
Mwakumva fungo, tiyenera kukhala tikuyandikira msika wa nsomba! Madzulo tsiku lirilonse, pamadoko a Costa do Sol, pamakhala piringupiringu pamabwato ansomba pamene akubweretsa nsomba zogwidwa patsikulo. Kuwonjezera pansomba zamitundumitundu, zazikulu ndi zazing’ono, pamakhalanso nkhanu, malobster, ndi akamalawo otchuka a ku Mozambique. Komabe, mwina mungakonde kudziŵa za mtundu wina wakusodza umene ukuchitika m’Maputo ndi malo ozungulira.
“Asodzi a Anthu”
Kuyambira pamene zinapatsidwa chilolezo chalamulo m’Mozambique, Mboni za Yehova zapeza kulabadira kwabwino kwa anthu. Mwamuna wina anasonyeza chiyamikiro chake mwakunena kuti: “M’London ndinali kuwona anthu anu ochuluka pamakwalala. Kwenikweni, kuli konse kumene ndakhala, ndimawona Mboni za Yehova. Tsopano ndiri wokondwa kukuwonani kunonso.”
Ngati kuvomereza Mabaibulo ndi mabuku ofotokoza Baibulo m’Chipwitikizi ndi Chitsonga, zinenero zakumaloko, kuli chizindikiro chirichonse, ndithudi ndicho chakuti anthuŵa amakonda zinthu zauzimu. Paula, mmishonale wina, akusimba kuti panthaŵi yakummaŵa pa Loŵeruka, nkotheka kugaŵira magazini oposa 50 pamasitolo, kapena pamsika waukulu. Bukhu la Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Othandiza likukhaladi lotchuka kwambiri. Achichepere ambiri akambululudwa kapena kusiidwa amasiye ndi nkhondo, ndipo akuwonekera kuti amayamikira mapindu ndi malangizo amene bukhuli limapereka.
Mumkhalidwe weniweni wa mu Afirika, magulu aakulu a okondwerera amazinga mmishonale kuti amvetsere zimene akunena. Kusonkhana kwapakhwalala koteroko kaŵirikaŵiri kumafikira kukhala kukambitsirana za m’Malemba kosangalatsa. Mlongo wina akukumbukira chokumana nacho chokondweretsa.
“Nthaŵi ina pamene ndinkachitira umboni m’khwalala, ndinachita mantha kwambiri pamene galimoto la jipi la asilikali linadzaima pafupi nane. Msilikali wachichepere anafuula kwa oima pambali ena kuti: ‘Inu apo, uzani donayo abwere kuno.’ Pamene ndinapita kwa iye, msilikaliyo anamwetulira nati: ‘Inu ndinu anthu abwino kwabasi. Timakondwa kukuwonani kunoko. Ndikhulupirira muli nalo bukhu lija lonena za achichepere. Ndikulifuna nanenso.’ Ndinayankha kuti ndinalibe lirilonse, koma ndinamtsimikizira kuti atangobwera m’sitoko, ndidzamperekera kunyumba kwake.”
Mitokoma ku Depo
Kukwaniritsa kufunika komakulakula kwa mabuku, ofesi yanthambi ya Watch Tower Society ya South Africa imatumiza mitokoma yamabuku ku depo m’Maputo pamilungu iŵiri iriyonse. Manuel, yemwe ndimishonale, amayang’anira depo ndipo ali ndi thayo la kugaŵiridwa kwa mabuku.
Tsiku lina m’mawa, mwamuna wachichepere analoŵa akuwunguzawunguza nafunsa kuti maloŵa anali achiyani. Manuel anayankha kuti ndidepo la mabuku ofotokoza Baibulo. Mwamunayo anatuluka, koma pambuyo pa mphindi imodzi yokha anabwerera.
“Mwanena kuti aŵa ndimabuku ofotokoza Baibulo, eti? anafunsa motero.
“Inde, ndatero,” anayankha Manuel.
“Kodi ali a gulu liti?” anafunsa mwamunayo.
“Mboni za Yehova,” anayankha Manuel, nawonjezera kuti, “timagaŵira mabuku ameneŵa ku mipingo yathu.”
“Eya, Mboni za Yehova!” Mwamunayo anamwetulira. “Pali zinthu zambiri zimene ndimakukonderani anthu inu. Komano, palinso chinthu chimodzi chimene sindimakukonderani.”
“Eya, kodi nchiyani chimene mumatikondera?” anafunsa mochenjera Manuel.
“Ndimakonda mabuku okondweretsa ndi ophunzitsa amene mumalemba,” anafotokoza motero mwamunayo. “Chimene sindimakonda nchakuti sindimapeza okwanira. Simungakhulupirire njala yaikulu ya mabuku onga anu imene tirinayo muno m’Maputo.” Ndiyeno anatulutsa ndandanda yolembedwa ya mabuku a Watch Tower Society, kuphatikizapo makope akumbuyo a magazini a Nsanja ya Olonda ndi Awake! amene sanapeze.
“Ndimanyamula ndandandayi kulikonse kumene ndimapita,” anatero kwa Manuel. “Nthaŵi zonse pamene ndikumana ndi Mboni za Yehova, ndimayesa kutenga mabuku alionse amene zirinawo. Ngati mungandithandize kupeza amene ndiri nawo pandandanda yangayi, ndiri wofunitsitsa kulipira mtengo uliwonse.”
Kukambitsirana kunayambika. Manuel anamva kuti mwamunayo anayamba kukambitsirana ndi Mboni za Yehova m’ma 1950 pamene anaŵerenga bukhu la Creation. Koma popeza kuti ntchito ya Mboni za Yehova inali yoletsedwa m’boma la Apwitikizi, anapita patsogolo pang’ono chabe.
Pamene mkupita kwanthaŵi anachezera mwamunayo ku ofesi kwake, Manuel anawona kuti mabuku onse a Watch Tower amene anali nawo anakutidwa bwino lomwe ndi pulasitiki ndi kuikidwa pafaelo. Manuel anakhoza kupereka mabuku amene mwamunayo anafuna kukwaniritsa ndandanda yake, ndipo anapanga makonzedwe akuchita phunziro Labaibulo ndi mwamunayo ndi banja lake.
Kuwoka kwauzimu ndi kuthirira konseku kukuyamba kubala zipatso zochukula pamene Mulungu akupitiriza ‘kukulitsa.’ Pali umboni wamphamvu wakuti kututa kwa anthu owongoka mtima kudzafikira pakudzaza nkhokwe pha, m’Mozambique!—1 Akorinto 3:6; Yohane 4:36.
Kupita Patsogolo Kwateokratiki Mosasamala Kanthu za Zopinga
Lerolino, pali mipingo yoposa 50 mkati ndi kuzungulira mzinda wa Maputo. Komabe, mulibe Nyumba Yaufumu ya Mboni za Yehova iriyonse. Nchifukwa ninji ziri choncho? Chifukwa cha mikhalidwe yakusoŵa ndalama, mipingo sinathe kumanga ngakhale kuti ina yakhala ndi malo awoawo kwa zaka zingapo.a
Komabe, zopinga zoterozo sizimalepheretsa kupita patsogolo. Pakali pano, maphunziro Abaibulo apanyumba oposa 5,000 amachititsidwa m’chigawo chakumwera kwa Mozambique. Ofuna maphunziro ngochuluka kwambiri kwakuti pafunikira kukhazikitsa zofunika zoyambirira: Ngati munthu apempha phunziro, kaŵirikaŵiri amalingaliridwa pomwepo kuti adzafika pamisonkhano yonse yampingo.
Mpingo wina wokhala m’shantikompaundi posachedwapa unali ndi 189 ofikapo pamisonkhano ya pa Sande ngakhale kuti unali ndi ofalitsa mbiri yabwino 71 okha. Gulu lalikulu limeneli limasonkhana poyera m’bwalo la nyumba ina. Malowo amachingidwa ndi malata ndi mpanda wamabango. Msonkhano uliwonse usanayambe, malowo amasesedwa bwino, ndipo mbali yaikulu ya omvetsera, kuphatikizapo achikulire ambiri, amakhala pamphasa. Amatchera khutu mosamalitsa chotani nanga! Popeza kuti atsopano ambiri samakhala ndi kope la Nsanja ya Olonda kuti atsatire phunzirolo, amaphunzira kutchera khutu kwambiri pamene ndime zikuŵerengedwa, ndipo ambiri amatukula manja pamene wochititsa afunsa mafunso.
Mpingo wina wa ofalitsa 59 mokhazikika umakhala ndi ofikapo oposa 140. Iwo amasonkhana nthaŵi zonse pabwalo lotsetsereka pang’ono. Koma m’nyengo yadzinja, mpingowo umapanikizana m’zipinda ziŵiri za nyumba yaing’ono. Omvetsera ochulukawo amasefukira m’likole, m’kitchini, ndi pakhonde. Apanso, munthu sangalephere kuwona chiyamikiro ndi kutchera khutu pamene aliyense, kuphatikizapo achichepere ambiri, akumvetsera programuyo mwachidwi.
Kulibe malo ena amene kuthekera kwa chiwonjezeko chamtsogolo m’Mozambique kumawonekera kwambiri kuposa pamisonkhano yadera. Posachedwapa msonkhano wadera unachitidwa m’bwalo lakale lomenyanira nkhunzi chapakati pa mzindawo. Kodi mungayerekezere kudabwa kwa ofalitsawo pafupifupi 3,000 pamene oposa 10,000 anapezeka pamaprogramuwo?
‘Zotuta Nzochulukadi’
Zokumana nazo zoterozo zimasonyeza bwino lomwe kuti padakali ntchito yochuluka yoichita m’Mozambique. Mipingo ina posachedwapa inachezeredwa kwanthaŵi yoyamba ndi woyang’anira woyendayenda wotumizidwa ndi ofesi yanthambi. Iyo imalandira chithandizo chofunikira kwambiri chakuwathandiza kugwiritsira ntchito njira zoyenera za gulu m’mipingoyo.
Mipingoyo imayamikiranso kwambiri kufika kwaposachedwapa kwa amishonale a ku Gileadi. Francisco, mkulu m’Maputo, ananena kuti: “Ili ndisitepe lalikulu kwa ife lakupita patsogolo. Tinali ndi changu. Tinali ndi chikondi. Komabe, tinalibe chidziŵitso cha njira zatsopano za gulu zakuyendetsa zinthu. Chimene timafuna kwenikweni ndimunthu amene ali ndi chidziŵitso chakutiphunzitsa mmene zinthu ziyenera kuchitidwira. Tsopano, ndife okondwa kwambiri kukhala ndi amishonale.”
Amishonalewo ali okondwa kukhala othandiza abale awo. Hans, amene anagaŵiridwa ku Mozambique posachedwapa pambuyo potumikira kwazaka 20 m’Brazil, akunena mwachidule motere: “Kugwirira ntchito m’munda wa Mozambique kuli mwaŵi waukulu! Tikuwona kuti tiri pafupi kwambiri ndi kuwonjezereka kwakukulu kunoko. Pali ntchito yaikulu yofunika kuchita. Tikhoza kugwiritsira ntchito amishonale ena 10 kapena 20 m’Maputo mokha.”
Kuwonjezereka kwa ntchito yateokratiki kumene kukupita patsogolo tsopano m’Mozambique kumatikumbutsa mawu ena a Yesu ofulumiza akuti: “Zotuta zichulukadi koma antchito ali oŵerengeka. Chifukwa chake pempherani Mwini zotuta kuti akokose antchito kukututa kwake.” (Mateyu 9:37, 38) Pali zifukwa zabwino zokhulupirira kuti Yehova adzayankha pemphero lofulumira limenelo la atumiki ake m’Mozambique.
Zikwi zambiri za Mboni za Yehova zinathera zaka 12 kapena kuposapo m’misasa ya andende ya kumpoto koma chakumadzulo kwa Mozambique. Pamene ena a iwo anabwerera ku Maputo posachedwapa, chuma chakuthupi chokha chimene anali nacho chinali nsalu yokha yofunda m’chiuno. Chimene anali nacho chochuluka chinali chikhulupiriro! Zakudya ndi zovala zoperekedwa mowoloŵa manja ndi Mboni zinzawo za m’maiko apafupi zinawathandiza kupeza poyambiranso m’moyo.
[Mawu a M’munsi]
a Ngati mwamuna achita mwaŵi wakupeza ntchito kunoko, malipiro apamwezi achikatikati amalingana ndi kuchokera pa US$20 kufikira US$30 pamwezi.
[Chithunzi patsamba 23]
Mipingo imakhala ndi ochuluka otulukira muumboni Wachikristu pa Loŵeruka m’maŵa
[Zithunzi patsamba 24]
Tamverani za Jaimito, mnyamata wazaka 5 zakubadwa. Iye anabadwira mumsasa wa andende. Lerolino, makolo a Jaimito ngokodwa kuti anabwerera ku Maputo. Mlungu uliwonse a Francisco, abambo a Jaimito, amakhala pansi ndi banja lonse kuchita phunziro la Baibulo. Makolo aŵiri onsewo amathera nthaŵi yochuluka kuphunzitsa ana awo kukhala aphunzitsi ogwira mtima muutumiki wakumunda. Jaimito amakonda kugaŵira mabuku pamsika waukulu
[Chithunzi patsamba 25]
Kusoŵa Nyumba Zaufumu zogwiritsira ntchito kwa mipingoyo sikumalepheretsa kupita patsogolo kwawo. Kaŵirikaŵiri, chiŵerengero choposa kuŵirikiza kaŵiri chimafika pamisokhano