Chenjerani ndi Kudzilungamitsa!
MU ZAKA za zana loyamba, Afarisi anakhala ndi mbiri yabwino ya kukhala alambiri olungama a Mulungu. Anali ophunzira Malemba achangu ndipo anali kupemphera nthaŵi zonse. Anthu ena anawaona kukhala ngati ofatsa ndi ololera. Wolemba mbiri Wachiyuda Josephus analemba kuti: “Afarisi ngachikondi kwa wina ndi mnzake ndipo amakulitsa maunansi ogwirizana ndi anthu onse.” Nchifukwa chake anali anthu olemekezedwa koposa m’chitaganya Chachiyuda panthaŵiyo!
Komabe, lerolino liwu lakuti “Ufarisi” ndi mawu ena ofanana nalo ali onyoza, ofanana ndi kudzipatula kukhala wolungama, kudzilungamitsa, kudzionetsera kukhala woyera kupambana ena, wopembedza kwambiri, ndi wochita utumiki wapakamwa. Kodi nchifukwa ninji Afarisi anataya dzina lawo labwino?
Chinali chifukwa chakuti Yesu Kristu, mosiyana ndi Ayuda ambiri, sananyengedwe ndi kaonekedwe kakunja ka Afarisi. Iye anawayerekezera ndi “manda opaka njereza, amene aonekera okoma kunja kwake, koma adzala mkatimo ndi mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zonse.”—Mateyu 23:27.
Zoonadi, anapereka mapemphero aatali ataima pa malo oonekera, koma anachita zimenezi kungoti aonedwe ndi ena, monga mmene Yesu ananenera. Kupembedza kwawo kunali kwachinyengo chabe. Anali kukonda kwambiri malo aulemu pa chakudya cha madzulo ndi mipando yaulemu kutsogolo m’masunagoge. Pamene kunali kwakuti Ayuda onse analamulidwa kuika mphonje pa zovala zawo, Afarisi anayesa kukondweretsa anthu mwa kuvala mphonje zazitali mopambanitsa. Ananyadira kuonetsera zitando zawo zazikulu kwambiri zovalidwa ngati njirisi. (Mateyu 6:5; 23:5-8) Chinyengo chawo, umbombo wawo, ndi kudziona kwawo kukhala apamwamba zinawadzetsera chitonzo pomalizira pake.
Yesu anamveketsa za kukana Afarisi kwa Mulungu kuti: “Onyenga inu! Yesaya ananenera bwino za inu, ndi kuti, Anthu awa andilemekeza ine ndi milomo yawo; koma mtima wawo uli kutali ndi ine. Koma andilambira ine kwachabe, ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.” (Mateyu 15:7-9) Kulungama kwawo kunalidi kudzilungamitsa. Nchifukwa chake, Yesu anachenjeza ophunzira ake kuti: “Tachenjerani nokha ndi chotupitsa mikate cha Afarisi.” (Luka 12:1) Ifenso lerolino tiyenera ‘kuchenjera’ kapena kudzitetezera pa kukhala onyenga achipembedzo.
Pochita motero, tiyenera kuzindikira kuti munthu samakhala wodzilungamitsa mwadzidzidzi. M’malo mwake, mkhalidwewu umaloŵa pang’onopang’ono m’kupita kwa nthaŵi. Munthu angakhale ndi mikhalidwe yosafunika ya Afarisi ngakhale mosadziŵa.
Mzimu wa Kudzikweza
Kodi ndi mikhalidwe ina iti imene tiyenera ‘kuchenjera’ nayo? Anthu odzilungamitsa nthaŵi zambiri “amalankhula, ndi kudzionetsera, ndi kuoneka ngati kuti sanachitepo cholakwa,” ikufotokoza motero Encyclopædia of Religion and Ethics. Anthu odzilungamitsa alinso odzitamandira ndi odzikweza, zimene zinali vuto lalikulu la Afarisi.
Yesu analongosola mkhalidwe wa Afarisi umenewu ndi fanizo kuti: “Anthu aŵiri anakwera kumka ku kachisi kukapemphera; winayo Mfarisi ndi mnzake wamsonkho. Mfarisiyo anaimirira napemphera izi mwa yekha, Mulungu, ndikuyamikani kuti sindili monga anthu onse ena, opambapamba, osalungama, achigololo, kapenanso monga wamsonkho uyu; ndisala chakudya kaŵiri sabata limodzi; ndipereka limodzi la magawo khumi la zonse ndili nazo.” Mosiyana ndi zimenezo wamsonkho anavomereza zolakwa zake ndipo anaonedwa kukhala wolungama kuposa Mfarisi wodzitamandirayo. Yesu ananena fanizo limeneli kwa awo amene “anadzikhulupirira mwa iwo okha kuti ali olungama, napeputsa onse ena.”—Luka 18:9-14.
Monga anthu opanda ungwiro nthaŵi zina tingadzimve kukhala oposa ena chifukwa cha maluso athu achibadwa. Koma Akristu ayenera kuthamangitsa malingaliro otereŵa mwamsanga. Mwina mungakhale muli ndi chidziŵitso cha zaka zambiri pa umoyo Wachikristu. Mwina mungakhale muli mphunzitsi wa Baibulo wa luso. Kapena mungadzinenere kukhala wosankhidwa kukalamulira ndi Kristu kumwamba. Ena mumpingo ali ndi mwaŵi wapadera monga atumiki anthaŵi yonse, akulu, kapena atumiki otumikira. Dzifunseni kuti, ‘Kodi Yehova adzamva bwanji ngati ndigwiritsira ntchito zimene wandipatsa monga chodzikwezera pa ena?’ Mosakayikira, zimenezi sizingamkondweretse.—Afilipi 2:3, 4.
Pamene Mkristu asonyeza mzimu wa kudzikweza chifukwa cha maluso ake, mwaŵi, kapena thayo zopatsidwa ndi Mulungu, iye kwenikweni akulanda Mulungu ulemerero ndi ulemu umene uyenera kupita kwa Iye yekha. Baibulo limalangiza Mkristu momvekera bwino kuti “asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa.” Limatifulumiza kuti: “Mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake. Musasamalire zinthu zazikulu, koma phatikanani nawo odzichepetsa. Musadziyesere anzeru mwa inu nokha.”—Aroma 12:3, 16.
“Musaweruze”
Malinga ndi insaikulopediya ina ya Baibulo, munthu wodzilungamitsa “mwina amadziyesa wolungama m’mkhalidwe kapena wokhala ndi unansi wabwino ndi Mulungu chifukwa cha kulondola kwake zofunika za lamulo popanda kudziŵa chifukwa chake chenicheni.” Buku lina limafotokoza anthu odzilungamitsa kukhala “anthu omwerekera m’chipembedzo amene amathera nthaŵi yawo yonse pa kufunafuna zoipa za ena.”
Afarisi anali aliwongo ndi zimenezi. M’kupita kwa nthaŵi malamulo awo opangidwa ndi anthu anaoneka kukhala ofunika kuposa malamulo ndi miyezo ya Mulungu. (Mateyu 23:23; Luka 11:41-44) Iwo anadziika kukhala oweruza ndipo anakonda kutsutsa aliyense amene sanafikitse miyezo yawo yodzilungamitsa. Mzimu wawo wa kudzikweza ndi kufuna kuchitiridwa ulemu kopambanitsa unawachititsa kufuna kulamulira ena. Kulephera kwawo kupondereza Yesu kunawakwiyitsa, motero analinganiza kumupha.—Yohane 11:47-53.
Nkosakondweretsa chotani nanga kukhala pamodzi ndi munthu amene amadziika kukhala woweruza, nthaŵi zonse akumafunafuna zolakwa za ena, kufufuza ndi kulamulira aliyense womzinga. Ndithu, palibe ali ndi mphamvu mumpingo ya kukakamiza ena kutsatira malingaliro ake ndi malamulo odzipangira. (Aroma 14:10-13) Akristu olingalira bwino amazindikira kuti mbali zambiri m’moyo watsiku ndi tsiku zimasankhidwa ndi munthu mwini. Makamaka awo amene ali ndi chikhoterero cha kufuna kuona ungwiro ndi kufuna zambiri kwa ena ayenera kupeŵa kuweruza ena.
Zoonadi, mpingo Wachikristu unapatsidwa mphamvu ya kukhala ndi miyezo yothandiza kuyendetsedwa bwino kwa gulu la pa dziko lapansi la Yehova. (Ahebri 13:17) Koma ena asokoneza miyezo imeneyi kapena awonjezerapo malamulo a iwo eni. Kudera lina ophunzira onse mu Sukulu Yautumiki Wateokratiki anafunikira kuvala masuti ndi kumanga mabatani a majekete awo popereka nkhani. Wophunzira amene analephera kuchita zimenezo sanaloledwenso kudzapereka nkhani mtsogolo. M’malo mopanga malamulo olimba otero, kodi sikwanzeru ndi kogwirizana ndi tanthauzo lenileni la Mawu a Mulungu kupereka chitsogozo chaumwini, chokoma mtima chofunikacho?—Yakobo 3:17.
Kudzilungamitsa kungachititsenso lingaliro lolakwika lakuti ngati Mkristu ali ndi mavuto aumwini ambiri, ndiko kuti ali wopereŵera pa mkhalidwe wauzimu. Izi ndizo zimenedi Elifazi, Bilidadi, ndi Zofari odzilungamitsawo analingalira ponena za Yobu wokhulupirikayo. Iwo analibe chithunzi chonse cha nkhaniyo, motero kuimba Yobu mlandu wa tchimo lina kunali kudzikuza. Yehova anaŵalanga kaamba ka kugamula kwawo kokhota pa mayeso a Yobu.—Onani Yobu, machaputala 4, 5, 8, 11, 18, 20.
Changu Chosayenera
Kudzilungamitsa ndi changu kaŵirikaŵiri zimayendera limodzi. Mtumwi Paulo analankhula za Ayuda okonda chipembedzo monga okhala ndi “changu cha kwa Mulungu, koma si monga mwa chidziŵitso. Pakuti pakusadziŵa chilungamo cha Mulungu, ndipo pofuna kukhazikitsa chilungamo cha iwo okha, iwo sanagonja ku chilungamo cha Mulungu.” (Aroma 10:2, 3) Pamene anali Mfarisi, Paulo iye mwini anali wachangu koposa, ngakhale kuti changu chake chinali chosayenera, chosazikidwa pa chilungamo cha Yehova.—Agalatiya 1:13, 14; Afilipi 3:6.
Moyenerera Baibulo limachenjeza kuti: “Usapambanitse kukhala wolungama; usakhale wanzeru koposa; bwanji ufuna kudziononga wekha?” (Mlaliki 7:16) Mkristu angayambe kukhala wosamalitsa zinthu kwambiri mumpingo, komano mkhalidwe wake wa kusamalitsa zinthu kwambiriwo ungasanduke kudzilungamitsa. Potsogozedwa ndi nzeru yaumunthu m’malo mwa chilungamo cha Yehova, changu cha chipembedzo chingavulaze ena. Motani?
Mwachitsanzo, makolo, angakhale otanganitsidwa kwambiri ndi kusamalira zosoŵa zauzimu za ena, ndipo mwakutero anganyalanyaze zosoŵa za banja la iwo eni. Kapena makolo angakhale ndi changu chopambanitsa, akumafuna kuti ana awo achite zambiri koposa zimene angathe kuchita. (Aefeso 6:4; Akolose 3:21) Ana ena, pokhala osakhoza kukwaniritsa zofunika zovuta zimenezo, amakhala ndi moyo wapaŵiri. Kholo lolingalira lidzaganizira zimene banja lake lingathe kuchita ndi kupanga kusintha koyenera.—Yerekezerani ndi Genesis 33:12-14.
Changu chopambanitsa chingatilandenso luso, chifundo, ndi kukoma mtima, zimene zili zofunika kwambiri pa zochita zathu ndi ena. Munthu angagwire ntchito zolimba kuti apititse patsogolo zinthu za Ufumu. Komabe, changu chake chopambanitsa chingavulaze ena pomachisonyeza. Paulo anati: “Ndingakhale ndikhoza kunenera ndipo ndingadziŵe zinsinsi zonse, ndi nzeru zonse, ndipo ndingakhale ndili nacho chikhulupiriro chonse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndilibe chikondi, ndili chabe. Ndipo ndingakhale ndipereka chuma changa chonse kudyetsa osauka, ndipo ndingakhale ndipereka thupi langa alitenthe m’moto, koma ndilibe chikondi, sindipindula kanthu ayi.”—1 Akorinto 13:2, 3.
Mulungu Akonda Odzichepetsa
Monga Akristu tiyenera kudziŵa kuwopsa kwa kudzilungamitsa kusanayambe kukula. Tiyenera kupeŵa mzimu wa kudzikweza, chizoloŵezi cha kuweruza ena, ndi changu chakhungu chozikidwa pa nzeru yaumunthu.
Pamene tikhala ‘ochenjera’ ndi mikhalidwe ya Ufarisi, m’malo mwa kuona ena kukhala odzilungamitsa, kungakhale kwabwino kwambiri kuyang’anitsitsa pa zizoloŵezi ndi zikhoterero za ife eni. Zoonadi, Yesu anaweruza Afarisi ndi kuwatsutsa monga ‘obadwa a mamba’ oyenerera chiwonongeko chosatha. Koma Yesu anali wokhoza kudziŵa mitima ya anthu. Ife sitingathe.—Mateyu 23:33.
Tiyeni tifunefune chilungamo cha Mulungu osati chathu. (Mateyu 6:33) Tidzakhala ndi chiyanjo cha Yehova pokhapokha ngati tichita zimenezi, pakuti Baibulo limatilangiza kuti: “Muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.”—1 Petro 5:5.