Kalata Yopita kwa Aroma
14 Landirani munthu amene ali ndi chikhulupiriro chofooka,+ koma musamaweruze amene ali ndi maganizo osiyana ndi anu. 2 Wina ali ndi chikhulupiriro chakuti angadye china chilichonse, koma munthu wofooka amangodya zamasamba. 3 Amene amadya chilichonse, asamanyoze amene sadya, ndipo wosadyayo asamaweruze amene amadya chilichonse,+ popeza iye analandiridwa ndi Mulungu. 4 Ndiwe ndani kuti uweruze wantchito wa mnzako?+ Ndi udindo wa bwana wake kumuweruza kuti ndi wolakwa kapena wosalakwa+ chifukwa Yehova* akhoza kumuthandiza kuti zimuyendere bwino.
5 Wina amaona tsiku lina ngati loposa linzake,+ koma wina amaona kuti masiku onse ndi ofanana.+ Munthu aliyense azitsimikiza kuti zimene akukhulupirira nʼzolondola. 6 Amene amaona kuti tsiku lina ndi lofunika amachita zimenezo pofuna kulemekeza Yehova.* Amene amadya chakudya chilichonse, amadya kuti alemekeze Yehova,*+ chifukwa amayamika Mulungu. Amene sadya, nayenso sadya pofuna kulemekeza Yehova,* chifukwa amayamikanso Mulungu.+ 7 Kunena zoona, palibe aliyense wa ife amene amakhala ndi moyo kuti adzilemekeze yekha,+ ndipo palibe amene amafa kuti adzilemekeze yekha. 8 Tikakhala ndi moyo, timakhalira moyo Yehova,*+ ndipo tikafa, timafera Yehova.* Choncho kaya tikhale ndi moyo kapena tife, ndife a Yehova.*+ 9 Nʼchifukwa chake Khristu anafa nʼkukhalanso ndi moyo, kuti akhale Ambuye wa akufa ndiponso wa amoyo.+
10 Nanga nʼchifukwa chiyani umaweruza mʼbale wako?+ Kapenanso nʼchifukwa chiyani umanyoza mʼbale wako? Popeza tonse tidzaima patsogolo pa mpando woweruzira wa Mulungu.+ 11 Malembatu amati: “‘Pali ine Mulungu wamoyo,’+ watero Yehova,* ‘bondo lililonse lidzandigwadira, ndipo lilime lililonse lidzavomereza poyera kuti ndine Mulungu.’”+ 12 Choncho aliyense wa ife adzayankha yekha kwa Mulungu.+
13 Ndiye tisamaweruzane,+ koma mʼmalomwake tsimikizani mtima kuti simukuchita chilichonse chimene chingakhumudwitse kapena kupunthwitsa mʼbale wanu.+ 14 Ndikudziwa ndipo ndikukhulupirira mwa Ambuye Yesu kuti palibe chakudya chimene pachokha ndi chodetsedwa.+ Koma ngati munthu akuona kuti chinachake nʼchodetsedwa, kwa iyeyo ndi chodetsedwa. 15 Chifukwa ngati mʼbale wanu akukhumudwa chifukwa cha chakudya, ndiye kuti simukusonyezanso chikondi.+ Musawononge* munthu amene Khristu anamufera chifukwa cha zakudya zanu.+ 16 Choncho musalole kuti anthu azinena zoipa pa zabwino zimene mukuchita. 17 Chifukwa pa nkhani ya Ufumu wa Mulungu chofunika kwambiri si kudya ndi kumwa ayi,+ koma chilungamo, mtendere ndi chimwemwe zimene zimabwera ndi mzimu woyera. 18 Aliyense amene amatumikira Khristu mʼnjira imeneyi ndi wovomerezeka kwa Mulungu ndipo anthu amasangalala naye.
19 Choncho tiyeni tiziyesetsa kukhala mwamtendere+ ndiponso kulimbikitsana.+ 20 Siyani kuwononga ntchito ya Mulungu chifukwa cha zakudya basi.+ Zoonadi, zinthu zonse nʼzoyera, koma nʼkulakwa kudya zinthuzo ngati wina akukhumudwa nazo.+ 21 Ndi bwino kusadya nyama kapena kusamwa vinyo kapena kusachita chilichonse chimene chimakhumudwitsa mʼbale wako.+ 22 Chikhulupiriro chimene uli nacho, ukhale nacho pakati pa iweyo ndi Mulungu. Munthu amakhala wosangalala ngati sakudziimba mlandu pa zinthu zimene wasankha. 23 Koma ngati akudya kwinaku akukayikira, ameneyo watsutsidwa kale, chifukwa sakudya mogwirizana ndi chikhulupiriro. Ndithu, chilichonse chochitidwa mosemphana ndi chikhulupiriro ndi tchimo.