Kalata Yopita kwa Aheberi
5 Mkulu wa ansembe aliyense wotengedwa pakati pa anthu, amaikidwa kuti azigwira ntchito ya Mulungu mʼmalo mwa anthu,+ kuti azipereka mphatso ndi nsembe zophimba machimo.+ 2 Amakhala woleza mtima pochita zinthu ndi anthu osadziwa kanthu komanso olakwa,* chifukwa iyenso ali ndi zofooka. 3 Ndipo chifukwa cha zimenezo, amafunika kupereka nsembe za machimo ake, ngati mmenenso amaperekera nsembe za machimo a anthu ena.+
4 Munthu samalandira ulemu umenewu mwa kufuna kwake, koma amachita kupatsidwa ndi Mulungu ngati mmene anachitira Aroni.+ 5 Zilinso chimodzimodzi ndi Khristu. Iye sanadzipatse yekha ulemerero+ podziika yekha kukhala mkulu wa ansembe. Koma amene anamupatsa ulemerero umenewo ndi amene anamuuza kuti: “Iwe ndiwe mwana wanga. Lero ine ndakhala bambo ako.”+ 6 Ngatinso mmene akunenera penapake kuti: “Iwe ndiwe wansembe mpaka kalekale, mofanana ndi unsembe wa Melekizedeki.”+
7 Pamene Khristu anali padzikoli,* anapereka mapemphero ochonderera ndiponso opempha, kwa amene akanatha kumupulumutsa ku imfa. Anapereka mapempherowa mofuula komanso akugwetsa misozi,+ ndipo anamumvera chifukwa ankaopa Mulungu. 8 Ngakhale kuti anali Mwana wa Mulungu, anaphunzira kumvera chifukwa cha mavuto amene anakumana nawo.+ 9 Ndipo atakhala wangwiro,+ anali ndi udindo wopulumutsa kwamuyaya anthu onse amene amamumvera,+ 10 chifukwa wasankhidwa ndi Mulungu kuti akhale mkulu wa ansembe mofanana ndi unsembe wa Melekizedeki.+
11 Tili ndi zambiri zoti tinene zokhudza iyeyu, koma zikuvuta kuzifotokoza chifukwa chakuti inu mumachedwa kumvetsa zinthu. 12 Pofika pano munayenera kukhala aphunzitsi. Koma sizili choncho, ndipo mukufunikanso wina woti akuphunzitseni mfundo zoyambirira+ za mʼmawu opatulika a Mulungu, kuyambira pachiyambi. Inu mwayambanso kufuna mkaka, osati chakudya chotafuna. 13 Aliyense amene amangomwabe mkaka sadziwa mawu a chilungamo ndipo adakali kamwana.+ 14 Koma chakudya chotafuna ndi cha anthu aakulu mwauzimu, amene amatha kusiyanitsa zoyenera ndi zosayenera chifukwa choti amagwiritsa ntchito luso lawo la kuganiza.*