Nthaŵi ndi Nyengo Zili m’Manja mwa Yehova
“Sikuli kwa inu kudziŵa nthaŵi kapena nyengo, zimene Atate anaziika m’ulamuliro wake wa Iye yekha.”—MACHITIDWE 1:7.
1. Kodi Yesu anawayankha motani mafunso a atumwi ake ofuna kudziŵa za nthaŵi?
KODI awo amene “akuusa moyo ndi kulira chifukwa cha zonyansa zonse zichitidwa” m’Dziko Lachikristu ndiponso padziko lonse lapansi angachitenso zina mwachibadwa zoposa kufuna kudziŵa nthaŵi imene dongosolo loipali lidzatha ndi kuloŵedwa m’malo ndi dziko lolungama la Mulungu? (Ezekieli 9:4; 2 Petro 3:13) Imfa ya Yesu ili pafupi ndiponso ataukitsidwa, atumwi ake anamfunsa mafunso ofuna kudziŵa za nthaŵi. (Mateyu 24:3; Machitidwe 1:6) Koma powayankha, Yesu sanawauze mmene angaŵerengere masiku. Panthaŵi ina anawapatsa chizindikiro chokhala ndi mbali zambiri, ndiponso nthaŵi inayake ananena kuti ‘sikunali kwa iwo kudziŵa nthaŵi kapena nyengo, zimene Atate anaziika m’ulamuliro wake wa Iye yekha.’—Machitidwe 1:7.
2. Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti si nthaŵi zonse pamene Yesu wadziŵa ndondomeko ya Atate wake ya zinthu zoyenera kuchitika m’nthaŵi yamapeto?
2 Ngakhale kuti Yesu ndiye Mwana wobadwa yekha wa Yehova, si nthaŵi zonse pamene wadziŵa ndondomeko ya Atate wake ya zochitika. Polosera za masiku otsiriza, Yesu anavomereza modzichepetsa kuti: “Koma za tsiku ilo ndi nthaŵi yake sadziŵa munthu aliyense, angakhale angelo a Kumwamba, kapena Mwana, koma Atate yekha.” (Mateyu 24:36) Yesu anali wofunitsitsa kuyembekezera moleza mtima kuti Atate wake amuuze nthaŵi yeniyeni yowonongera dongosolo la zinthu loipali.a
3. Kodi tikuphunzirapo chiyani pakayankhidwe ka Yesu ka mafunso okhudza cholinga cha Mulungu?
3 Tikuphunzirapo zinthu ziŵiri pakayankhidwe ka Yesu ka mafunso okhudza nthaŵi imene zinthu zidzachitika pokwaniritsa cholinga cha Mulungu. Choyamba, tikuphunzirapo kuti Yehova ali ndi ndondomeko ya zochita; ndiponso chachiŵiri, amaika yekha nthaŵi, ndipo atumiki ake sayenera kuyembekezera kuti adzapatsidwa chidziŵitso chonse chokhudza nthaŵi kapena nyengo zake pasadakhale.
Nthaŵi ndi Nyengo za Yehova
4. Kodi mawu achigiriki otembenuzidwa kuti “nthaŵi” ndi “nyengo” pa Machitidwe 1:7 amatanthauzanji?
4 Kodi mawuwo “nthaŵi” ndi “nyengo” akutanthauzanji? Mawu a Yesu olembedwa pa Machitidwe 1:7 ali ndi matanthauzo aŵiri a nthaŵi. Liwu lachigiriki lotembenuzidwa kuti “nthaŵi” limatanthauza “utali wa nthaŵi,” nthaŵi yoyambira pakutipakuti kutheranso pakutipakuti (yaitali kapena yaifupi). Liwu lakuti “nyengo” latembenuzidwa ku liwu lotanthauza nthaŵi yeniyeni kapena kuti nthaŵi yoikika, nyengo yakutiyakuti, pamene zinthu zakutizakuti zimachitika. Ponena za mawu ake enieni aŵiri ameneŵa, W. E. Vine anati: “Pa Machitidwe 1:7, ‘Atate waika mu ulamuliro Wake’ zonse ziŵiri nthaŵi (chronos), utali wa nthaŵi, ndi nyengo (kairos), nthaŵi imene zinthu zina zosaiŵalika zidzachitika.”
5. Kodi Yehova anamuuza liti Nowa za cholinga Chake cha kuwononga dziko loipalo, ndipo ndi ntchito ziŵiri ziti zimene Nowa anachita?
5 Chigumula chisanachitike, Mulungu anaikiratu nthaŵi ya zaka 120 ya dziko limene anthu ndi angelo opanduka ovala matupi a anthu anaipitsa. (Genesis 6:1-3) Nowa woopa Mulunguyo anali ndi zaka 480 panthaŵiyo. (Genesis 7:6) Analibe ana ndipo anakhalabe wopanda ana kwa zaka zinanso 20. (Genesis 5:32) Patapita zaka zambiri, ana aamuna a Nowa atakula ndi kukwatira, Mulungu anauza Nowa za cholinga Chake chochotsa kuipa padziko lapansi. (Genesis 6:9-13, 18) Ngakhale kuti panthaŵiyo Nowa anapatsidwa ntchito ziŵiri, yomanga chingalawa ndiponso yolalikira kwa anthu ena, Yehova sanamuuze nthaŵi imene adzachotsa kuipako.—Genesis 6:14; 2 Petro 2:5.
6. (a) Kodi Nowa anasonyeza motani kuti nthaŵi anazisiya m’manja mwa Yehova? (b) Kodi tingachitsanzire motani chitsanzo cha Nowa?
6 Kwa zaka zambirimbiri—mwinamwake theka la zaka zana—“anachita Nowa, monga mwa zonse anamlamulira iye Mulungu.” Nowa anachita zimenezo “ndi chikhulupiriro,” mosadziŵa tsiku lake lenileni. (Genesis 6:22; Ahebri 11:7) Yehova sanamuuze nthaŵi yeniyeni imene zinthuzo zidzachitika mpaka kutatsala mlungu umodzi kuti Chigumula chiyambe. (Genesis 7:1-5) Chifukwa chakuti Nowa anadalira ndi kukhulupirira Yehova ndi mtima wonse, za nthaŵi anazisiya m’manja mwa Mulungu. Choncho Nowa ayenera kuti anayamikira chotani nanga ataona chitetezo cha Yehova pa Chigumula, kenako kutuluka m’chingalawa ndi kuponda padziko lapansi loyeretsedwa! Popeza tikuyembekezera chilanditso ngati chimenecho, kodi sitiyenera kusonyeza chikhulupiriro chofananacho mwa Mulungu?
7, 8. (a) Kodi mitundu ndi maulamuliro a dziko lonse zinakhalapo motani? (b) Kodi ndi motani mmene Yehova ‘anapangiratu nyengo, ndi malekezero a pokhala pa anthu’?
7 Chigumula chitapita, mbadwa zambiri za Nowa zinasiya kulambira koona kwa Yehova. Posafuna kubalalika padziko lonse, iwo anayamba kumanga mudzi ndi nsanja ya kulambira konyenga. Yehova anaona kuti ndi nthaŵi yoti aloŵererepo. Iye anasokoneza chinenero chawo ndipo “anabalalitsa iwo padziko lonse lapansi [kuchokera pa Babele].” (Genesis 11:4, 8, 9) Pambuyo pake, anthu olankhula chinenero chimodzi anakhala mtundu umodzi, ndipo mitundu ina inatenganso mitundu ina nikhala mitundu yamphamvu m’deralo, nikhalanso ngakhale maulamuliro a dziko lonse.—Genesis 10:32.
8 Pofuna kukwaniritsa zolinga zake, nthaŵi zina Mulungu ndiye ankalemba malire a maiko ndi kuika nthaŵi imene mtundu wakutiwakuti udzakhala ulamuliro wamphamvu kuderalo kapena padziko lonse. (Genesis 15:13, 14, 18-21; Eksodo 23:31; Deuteronomo 2:17-22; Danieli 8:5-7, 20, 21) Mtumwi Paulo ankanena za tanthauzo limeneli la nthaŵi ndi nyengo za Yehova pamene anauza Agiriki amaphunziro apamwamba ku Atene kuti: “Mulungu amene analenga dziko lapansi ndi zonse zili momwemo, . . . ndi mmodzi analenga mitundu yonse ya anthu, kuti akhale ponse pankhope ya dziko lapansi, atapangiratu nyengo zawo, ndi malekezero a pokhala pawo.”—Machitidwe 17:24, 26.
9. Kodi ndi motani mmene Yehova ‘wasinthira nthaŵi ndi nyengo’ za mafumu?
9 Zimenezi sizikutanthauza kuti Yehova ndiye amachititsa zipambano zonse ndi kusintha konse kwa zandale m’mitundu yosiyanasiyana. Komabe, ngati wasankha kuloŵererapo kuti akwaniritse cholinga chake, akhozadi kutero. Ndiye chifukwa chake mneneri Danieli, amene anali kudzaona kugwa kwa Ulamuliro Wadziko Lonse wa Babulo ndi kuloŵedwa m’malo kwake ndi Amedi ndi Aperisi, anati ponena za Yehova: “Amasanduliza nthaŵi ndi nyengo, achotsa mafumu, nalonga mafumu, apatsa anzeru nzeru, ndi chidziŵitso kwa iwo okhoza kuzindikira.”—Danieli 2:21; Yesaya 44:24–45:7.
“Inayandikira Nthaŵi”
10, 11. (a) Kodi Yehova anaikiratu kwautali wotani nthaŵi imene adzalanditsa mbadwa za Abrahamu mu ukapolo? (b) Kodi nchiyani chikusonyeza kuti Aisrayeli sanadziŵe nthaŵi yeniyeni imene adzalanditsidwa?
10 Zaka zoposa mazana anayi pasadakhale, Yehova anaikiratu chaka chenicheni chimene adzanyazitsa mfumu ya Ulamuliro Wadziko Lonse, Igupto, ndi kumasula mbadwa za Abrahamu kuukapolo. Povumbula cholinga chake kwa Abrahamu, Mulungu analonjeza kuti: “Dziŵitsa ndithu kuti mbewu zako zidzakhala alendo m’dziko la eni, nizidzatumikira iwo, ndipo iwo adzasautsa izo zaka mazana anayi; ndiponso mtunduwo adzautumikira, Ine ndidzauweruza: ndiponso pambuyo pake adzatuluka ndi chuma chambiri.” (Genesis 15:13, 14) Posimbira Sanihedrini za mbiri ya Israyeli mwachidule, Stefano anatchulapo za nthaŵi ya zaka 400 imeneyi nati: “Koma mmene inayandikira nthaŵi ya lonjezo limene Mulungu adalonjezana ndi Abrahamu, anthuwo anakula nachuluka m’Aigupto, kufikira inauka mfumu ina pa Aigupto, imene siinamdziŵa Yosefe.”—Machitidwe 7:6, 17, 18.
11 Farao watsopano ameneyu anangosandutsa Aisrayeliwo kukhala akapolo. Buku la Genesis linali lisanalembedwebe ndi Mose, ngakhale kuti malonjezo a Yehova kwa Abrahamu ayenera kuti anangonenedwa pakamwa kapena analembedwa. Ngakhale zili choncho, zikuoneka kuti malinga ndi chidziŵitso chimene Aisrayeli anali nacho, iwo sanathe kuŵerengera tsiku lenileni limene anali kudzalanditsidwa pachitsenderezo. Mulungu anali kudziŵa nthaŵi imene adzawalanditsa, koma mwachionekere Aisrayeli osautsidwawo sanauzidwe. Timaŵerenga kuti: “Kunali pakupita masiku ambiri aja, idafa mfumu ya Aigupto; ndi ana a Israyeli anatsitsa moyo chifukwa cha ukapolo wawo, nalira, ndi kulira kwawo kunakwera kwa Mulungu chifukwa cha ukapolowo. Ndipo Mulungu anamva kubuula kwawo, ndi Mulungu anakumbukira chipangano chake ndi Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo. Ndipo Mulungu anapenya Aisrayeli, ndi Mulungu anadziŵa.”—Eksodo 2:23-25.
12. Kodi Stefano anasonyeza motani kuti Mose anafulumirira nthaŵi ya Yehova?
12 Tingaonenso kuti Aisrayeli sanadziŵe nthaŵi yeniyeni ya kulanditsidwa kwawo m’mawu achidule a Stefano. Ponena za Mose, iye anati: ‘Pamene zaka zake zinafikira ngati makumi anayi, kunaloŵa mumtima mwake kuzonda abale ake ana a Israyeli. Ndipo pakuona wina woti alikumchitira choipa, iye anamchinjiriza, nambwezera chilango wozunzayo, nakantha Mwaigupto. Ndipo anayesa kuti abale ake akazindikira kuti Mulungu alikuwapatsa chipulumutso mwa dzanja lake; koma sanazindikira.’ (Machitidwe 7:23-25) Panopo Mose anachita zinthu zaka 40 nthaŵi ya Mulungu isanakwane. Stefano anafotokoza kuti Mose anayembekezera zaka zinanso 40 Mulungu ‘asanapatse Aisrayeli chipulumutso mwa dzanja lake.’—Machitidwe 7:30-36.
13. Kodi mkhalidwe wathu wafanana motani ndi wa Aisrayeli asanalanditsidwe ku Igupto?
13 Ngakhale kuti “inayandikira nthaŵi ya lonjezo” ndiponso Mulungu anali ataikiratu chaka chake chenicheni, Mose ndi Aisrayeli onse anafunikira kusonyeza chikhulupiriro. Anayenera kuyembekezera nthaŵi yoikidwiratu ya Yehova, mwachionekere mosatha kuiŵerengera isanafike. Ifenso tikudziŵa kuti chilanditso chathu m’dongosolo loipa lilipoli chikuyandikira. Tikudziŵa kuti tikukhala mu “masiku otsiriza.” (2 Timoteo 3:1-5) Chotero kodi sitiyenera kukhala ofunitsitsa kusonyeza chikhulupiriro chathu ndi kuyembekezera nthaŵi yoikidwiratu ya Yehova ya tsiku lake lalikulu? (2 Petro 3:11-13) Kenako, monga Mose ndi Aisrayeli, tidzaimbanso nyimbo yachilanditso yaulemerero, kutamanda Yehova.—Eksodo 15:1-19.
‘Itakwanira Nthaŵi’
14, 15. Kodi tikudziŵa motani kuti Mulungu anali ataikiratu nthaŵi yoti Mwana wake adze padziko lapansi, ndipo kodi aneneri ndi angelo ankadikira chiyani?
14 Yehova anali ataikiratu nthaŵi yeniyeni yoti Mwana wake wobadwa yekha adze padziko lapansi monga Mesiya. Paulo analemba kuti: “Pokwaniridwa nthaŵi, Mulungu anatuma Mwana wake, wobadwa ndi mkazi, wobadwa wakumvera lamulo.” (Agalatiya 4:4) Zimenezi zinakwaniritsa lonjezo la Mulungu lakuti adzatumiza Mbewu—‘Silo; amene anthu anali kudzamvera iye.’—Genesis 3:15; 49:10.
15 Aneneri a Mulungu—ngakhale angelo—anadikira “nthaŵi” imene Mesiya anali kudzaonekera padziko lapansi imenenso anthu ochimwa anali kudzapeza chipulumutso. “Kunena za chipulumutso ichi,” anatero Petro, “anafunafuna nasanthula aneneri, pakunenera za chisomo chikudzerani; ndi kusanthula nthaŵi iti, kapena nthaŵi yanji Mzimu wa Kristu wokhala mwa iwo analozera [mzimu wokhala mwa iwo unawalozera ponena za Kristu, NW], pakuchitiratu umboni wa masautso a Kristu, ndi ulemerero wotsatana nawo. . . . Zinthu izi angelo alakalaka kusuzumiramo.”—1 Petro 1:1-5, 10-12.
16, 17. (a) Kodi Yehova anagwiritsira ntchito ulosi uti pothandiza Ayuda a m’zaka za zana loyamba kuyembekezera Mesiya? (b) Kodi ulosi wa Danieli unakhudza motani kuyembekezera Mesiya kwa Ayuda?
16 Mwa mneneri wake Danieli—mwamuna wachikhulupiriro chosagwedera—Yehova anapereka ulosi wonena za “masabata makumi asanu ndi aŵiri.” Ulosi umenewo unali kudzadziŵitsa Ayuda a m’zaka za zana loyamba kuti Mesiya wolonjezedwayo wakhala pang’ono kuonekera. Mbali ina ya ulosiwo imati: “Kuyambira kutuluka lamulo lakukonzanso, ndi kummanga Yerusalemu, kufikira wodzozedwayo, ndiye kalonga, kudzakhala masabata asanu ndi aŵiri; ndi masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu aŵiri.” (Danieli 9:24, 25) Akatswiri ambiri achiyuda, achikatolika, ndi achiprotesitanti amavomereza kuti “masabata” otchulidwa pano amatanthauza masabata a zaka. “Masabata” 69 (zaka 483) otchulidwa pa Danieli 9:25 anayamba mu 455 B.C.E., pamene Mfumu Aritasasta ya Perisiya inalamula Nehemiya “kukonzanso, ndi kummanga Yerusalemu.” (Nehemiya 2:1-8) Masabatawo anatha patapita zaka 483—mu 29 C.E., pamene Yesu anabatizidwa ndi kudzozedwa ndi mzimu woyera, nakhala Mesiya, kapena kuti Kristu.—Mateyu 3:13-17.
17 Sitikudziŵa ngati Ayuda a m’zaka za zana loyamba anadziŵa nthaŵi yeniyeni pamene zaka 483 zimenezo zinayamba. Koma pamene Yohane Mbatizi anayamba utumiki wake, “anthu anali kuyembekezera, ndipo onse anaganizaganiza m’mitima yawo za Yohane, ngati kapena iye ali Kristu.” (Luka 3:15) Akatswiri ena a Baibulo amanena kuti anthu anali ndi chiyembekezo chimenechi chifukwa cha ulosi wa Danieli. Pothirira ndemanga vesili, Matthew Henry analemba kuti: “Panopo tikuuzidwa . . . mmene anthu anayambira kuganiza za Mesiya chifukwa cha utumiki ndi ubatizo wa Yohane, ndi kuganiza kuti Mesiyayo ali pakhomo. . . . Masabata makumi asanu ndi aŵiri a Danieli anali kutha tsopano.” Manuel Biblique yachifalansa, yolembedwa ndi Vigouroux, Bacuez, ndi Brassac imati: “Anthu anadziŵa kuti masabata makumi asanu ndi aŵiri a zaka otchulidwa ndi Danieli anali kutha; panalibe amene anadabwa kumva Yohane Mbatizi akulengeza kuti ufumu wa Mulungu wayandikira.” Katswiri wamaphunziro wachiyuda Abba Hillel Silver analemba kuti malinga ndi “kuŵerengera nthaŵi kodziŵika bwino” m’masikuwo, “anthu anali kuyembekezera Mesiya chapakati pa zaka za zana loyamba C.E.”
Zochitika—Osati Kuŵerengera Nthaŵi
18. Pamene kuli kwakuti ulosi wa Danieli unathandiza Ayuda kudziŵa nthaŵi imene anayenera kuyembekezera Mesiya, kodi umboni wokhutiritsa kwambiri wakuti Yesu ndiye Mesiya unali chiyani?
18 Ngakhale zikuoneka kuti kuŵerengera nthaŵi kunathandiza Ayuda kudziŵa nthaŵi yachisawawa imene Mesiya anali kudzaonekera, zochitika zotsatira zikusonyeza kuti ambiri a iwo sikunawathandize kukhulupirira kuti Yesu ndiye Mesiya. Kutatsala nthaŵi yosakwanira chaka kuti afe, Yesu anafunsa ophunzira ake kuti: “Makamuwo a anthu anena kuti Ine ndine yani?” Iwo anayankha kuti: “Yohane Mbatizi; koma ena, Eliya; ndi ena, kuti anauka mmodzi wa aneneri akale.” (Luka 9:18, 19) Tilibe zolembedwa zilizonse zosonyeza kuti Yesu anagwirapo mawu ulosi wa masabata ophiphiritsawo pofuna kusonyeza kuti ndiye Mesiya. Koma panthaŵi ina, iye anati: “Ine ndili nawo umboni woposa wa Yohane; pakuti ntchito zimene Atate anandipatsa ndizitsirize, ntchito zomwezo ndizichita zindichitira umboni, kuti Atate anandituma Ine.” (Yohane 5:36) Nthaŵi iliyonse imene inavumbulidwa sinapereke umboni wakuti Yesu ndiye Mesiya wotumizidwa ndi Mulungu. M’malo mwake, kulalikira kwake, zozizwitsa zake, ndi zinthu zimene zinachitika pa imfa yake (mdima wozizwitsa, kung’ambika kwa chinsalu chotchinga cha m’kachisi, ndi chivomezi) nzimene zinapereka umboniwo.—Mateyu 27:45, 51, 54; Yohane 7:31; Machitidwe 2:22.
19. (a) Kodi Akristu anali kudzadziŵa motani kuti chiwonongeko cha Yerusalemu chayandikira? (b) Kodi nchifukwa chiyani Akristu oyambirira othaŵa ku Yerusalemu anafunikirabe chikhulupiriro chachikulu?
19 Mofananamo, imfa ya Yesu itapita, Akristu oyambirirawo sanauzidwe mmene angaŵerengere nthaŵi ya mapeto a dongosolo la zinthu lachiyuda amene anali kudza. Nzoona kuti ulosi wa Danieli wa masabata ophiphiritsa unatchulapo za kuwonongedwa kwa dongosolo limenelo. (Danieli 9:26b, 27b) Koma zimenezi zinali kudzachitika “masabata makumi asanu ndi aŵiri” atatha (455 B.C.E.–36 C.E.). M’mawu ena, Akunja oyamba atakhala otsatira a Yesu mu 36 C.E., Akristu anali atadutsa nthaŵi zotchulidwa pa Danieli chaputala 9. Kwa iwo, zochitika nzimene zinali kudzawasonyeza kuti dongosolo lachiyuda lakhala pang’ono kutha, osati kuŵerengera nthaŵi. Zochitika zimenezo, zoloseredwa ndi Yesu, zinayamba kufika pachimake kuyambira mu 66 C.E., pamene asilikali a Roma anaukira Yerusalemu kenako nkubwerera. Zimenezi zinapatsa Akristu okhulupirika ndi atcheru a m’Yerusalemu ndi m’Yudeya mpata ‘wothaŵira kumapiri.’ (Luka 21:20-22) Popeza sanauzidwe nthaŵi iliyonse, Akristu oyambirira amenewo sanadziŵe nthaŵi imene Yerusalemu adzawonongedwa. Anafunikira chikhulupiriro chachikulu chotani nanga kuti asiye nyumba zawo, minda yawo, ndi ntchito zawo kukakhala kunja kwa Yerusalemu zaka pafupifupi zinayi mpaka pamene gulu lankhondo la Roma linabweranso mu 70 C.E. ndi kuthetsa dongosolo lachiyudalo!—Luka 19:41-44.
20. (a) Kodi tingapindule motani ndi zitsanzo za Nowa, Mose, ndi Akristu a ku Yudeya a m’zaka za zana loyamba? (b) Kodi tidzakambitsirana za chiyani m’nkhani yotsatira?
20 Mwachidaliro, monga Nowa, Mose, ndi Akristu a m’zaka za zana loyamba m’Yudeya, ifeyo lerolino tingasiye nthaŵi ndi nyengo m’manja mwa Yehova. Chikhulupiriro chathu chakuti tikukhala m’nthaŵi yamapeto ndi kuti chilanditso chathu chili pafupi, sichikudalira pa kuŵerengera nthaŵi, koma pa zochitika zenizeni zimene zikukwaniritsa maulosi a Baibulo. Ndiponso, ngakhale kuti tikukhala m’nthaŵi ya kukhalapo kwa Kristu, sikuti tiyenera kukhala opanda chikhulupiriro ndi kukhala osadikira. Tiyenera kupitirizabe kuyembekezera mwachidwi zochitika zosangalatsa zonenedweratu m’Malemba. Izi nzimene tidzakambitsirana m’nkhani yotsatira.
[Mawu a M’munsi]
Kubwereza
◻ Ponena za nthaŵi ndi nyengo za Yehova, kodi Yesu anawauzanji atumwi ake?
◻ Kodi Nowa anadziŵiratu kwautali wotani za nthaŵi imene Chigumula chidzayamba?
◻ Kodi nchiyani chikusonyeza kuti Mose ndi Aisrayeli sanadziŵe nthaŵi yeniyeni imene adzalanditsidwa ku Igupto?
◻ Kodi tingapindule motani ndi zitsanzo za m’Baibulo zokhudza nthaŵi ndi nyengo za Yehova?
[Chithunzi patsamba 11]
Chifukwa cha chikhulupiriro chake, Nowa anasiya za nthaŵi m’manja mwa Yehova