“Thandizo Langa Lidzera kwa Yehova”
Osakwatira Koma Osangalala Potumikira Yehova
“AMBIRIFE ndife osangalala kwambiri ngakhale sitili pabanja,” anatero mayi wina wachikristu ku Spain. N’chifukwa chiyani mayiyu ali wosangalala? Iye anati: “Popeza sitikhala ndi zotangwanitsa zambiri, ndife osangalala chifukwa tikuchita zambiri potumikira Mulungu wathu Yehova.”
Mawu amenewo akugwirizana ndi zimene Mawu a Mulungu amanena za kukhala wosakwatira. Pamene mtumwi Paulo anali kufotokoza nkhani zina za ukwati, ananena mawu anzeru ouziridwa awa: “Ndinena kwa osakwatira, ndi kwa akazi amasiye, kuti kuli bwino kwa iwo ngati akhala monganso ine.” Paulo anali wosakwatira. Koma kodi n’chifukwa chiyani analimbikitsa ena kukhalanso osakwatira? Iye anati munthu wokwatira amakhala wogawanika, koma mwamuna kapena mkazi wosakwatira “alabadira zinthu za Ambuye.” (1 Akorinto 7:8, 32-34) Kutumikira Yehova ndiko chinthu chachikulu chimene chimachititsa munthu wosakwatira kukhala wosangalala ndiponso kukhala wokhutira m’moyo.
Kukhala Osakwatira ndi Cholinga Chapadera
Mawu a Paulowa angakhale odabwitsa kwa anthu amene chikhalidwe chawo chimawalimbikitsa kukwatira ndi kukhala ndi ana. Komabe, Yesu Kristu, yemwe anali wosakwatira koma wosangalala ndi wokhutira ndi moyo, anatchula cholinga chapadera chimene Akristu angakhalire osakwatira. Iye anati: “Ena anaukana ukwati chifukwa cha Ufumu wa Kumwamba. Iye amene angalandire ichi alandire.”—Mateyu 19:12, Chipangano Chatsopano Mu Chichewa Cha Lero.
Mogwirizana ndi mawu amenewa, anthu ambiri aonadi kuti kukhala wosakwatira kumawapatsa mwayi wotumikira Mulungu popanda zododometsa zimene zimakhala m’banja.(1 Akorinto 7:35) Akristu zikwizikwi osakwatira akupembedza Yehova mosangalala, ndipo amakhala achimwemwe pothandiza anthu ena mokangalika.a
Akristu ambiri osakwatira amadziwa kuti si anthu okwatira okha amene amakhala osangalala, komanso kuti si onse osakwatira amene amakhala osasangalala. Onse okwatira ndi osakwatira omwe nthawi zina amakhala osangalala, ndipo nthawi zinanso amakhala achisoni. Ndipotu Baibulo limachita kuneneratu kuti ukwati umabweretsera munthu “chisautso m’thupi.”—1 Akorinto 7:28.
Kukhala Osakwatira Chifukwa cha Mavuto Ena
Ambiri sanakwatire chifukwa cha mavuto ena osati mwa kufuna kwawo. Amafuna chikondi ndi mgwirizano umene umapezeka m’banja. Koma chifukwa cha mavuto a zachuma ndi mavuto ena, anthu ena sangathe kukwatira pakali pano. Akristu ena, ambiri mwa iwo alongo athu okonda zinthu zauzimu, sanakwatire chifukwa chakuti anatsimikiza mtima kumvera uphungu wa m’Baibulo wa kukwatira “mwa Ambuye.” (1 Akorinto 7:39) Amenewa, mokhulupirika akufunafuna munthu woti amange naye banja pakati pa anthu odzipereka ndi obatizidwa opembedza Yehova.
Nthawi zina ena mwa iwo amasukidwa. Mkristu wina wosakwatiwa anavomereza kuti amasukidwa, koma kenako anati: “Tikudziwa lamulo la Yehova ndipo sitifuna kumukhumudwitsa mwa njira iliyonse. Nthawi zina timalakalaka titakhala pabanja, koma ngakhale kuti kawirikawiri anthu m’dzikoli amatikankhizira kwa anthu oti atifunsire, ife sitilolera. Sitifuna n’komwe kukhala m’gulu la amuna kapena akazi osakhulupirira.” Akristu otere tiyenera kuwayamikira chifukwa chotsatira uphungu wa m’Baibulo ndi kukhalabe ndi khalidwe labwino kuti akondweretse Yehova ngakhale pamene ali ndi nkhawa.
Mulungu Amawathandiza Kwambiri
Yehova ndi wokhulupirika kwa anthu amene amaonetsa kuti ndi okhulupirika kwa iye mwa kukana kukwatirana ndi anthu amene samutumikira. Malinga ndi zimene Mfumu Davide inakumana nazo, inatsimikizira zimenezi pamene inanena kuti: “Kwa munthu wokhulupirika inu [Yehova] mudzakhala wokhulupirika.” (Salmo 18:25, NW) Mulungu akulonjeza onse amene amamumvera mokhulupirika kuti: “Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.” (Ahebri 13:5) Potsanzira Yehova, tiwayamikire ndi mtima wonse Akristu osakwatira amisinkhu yonse amene amatsatira Mawu a Mulungu mokhulupirika. Tingawapemphererenso kuti Yehova awapatse mphamvu kuti athe kulimbana ndi mavuto awo.—Oweruza 11:30-40.
Akristu ambiri osakwatira aona kuti kugwira ntchito yophunzitsa Baibulo ndi mtima wonse kumakhutiritsa moyo wawo. Mwachitsanzo, tamvani zimene ananena mayi wina wosakwatiwa wazaka pafupifupi 35 dzina lake Patricia, amene ndi mpainiya, kapena kuti mlaliki wa nthawi zonse. Iye anati: “Ngakhale kuti ukakhala wosakwatiwa umakumana ndi mayesero ambiri, kukhala wosakwatiwa kwandipatsa mpata wokhala mpainiya wokhazikika. Popeza ndili ndekha, ndimatha kusintha zochita zanga mosavuta ndipo zimenezi zimandipatsa nthawi yochuluka yophunzira Baibulo. Ndaphunzira kudalira Yehova ndi mtima wonse, makamaka ndikakumana ndi mayesero.”
Maganizo amenewa akugwirizana ndi zimene Baibulo limatilimbikitsa kuchita kuti: “Pereka njira yako kwa Yehova; khulupiriranso Iye, adzachichita.” (Salmo 37:5) Anthu onse opembedza Yehova mokhulupirika, okwatira kapena osakwatira, angalimbikitsidwe ndi kupeza mphamvu ndi mawu ouziridwa awa akuti: “Thandizo langa lidzera kwa Yehova.”—Salmo 121:2.
[Mawu a M’munsi]
a Onani Kalendala ya 2005 ya Mboni za Yehova, pa mwezi wa July ndi August.
[Mawu Otsindika patsamba 9]
“Wosakwatira alabadira zinthu za Ambuye, kuti akondweretse Ambuye.”—1 AKORINTO 7:32
[Bokosi patsamba 8]
ZIMENE MUNTHU ANGACHITE KUTI APINDULE POKHALA WOSAKWATIRA
Yesu, yemwe sanakwatirepo anati: “Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha Iye amene anandituma Ine, ndi kutsiriza ntchito yake.”—Yohane 4:34.
Ana aakazi anayi a Filipo omwe anali osakwatiwa anali otanganidwa ndi ‘kunenera.’—Machitidwe 21:8, 9.
Alongo achikristu osakwatiwa amene amalalikira uthenga wa Ufumu ali m’gulu la ‘khamu lalikulu la akazi olalikira uthengawo.’—Salmo 68:11.