Mungapezedi Chimwemwe
CHIMWEMWE chenicheni ndiponso chokhalitsa, nthawi zina chimavuta kupeza. Zili choncho chifukwa choti anthu ambiri pofunafuna chimwemwe mosalekeza, amachifuna m’malo olakwika. Amalakalaka atakhala ndi mnzawo wodziwa zinthu ndiponso wodalirika amene angawatsogolere njira yoyenera.
Baibulo lili ndi malangizo ofunika oterowo. Taganizirani buku lake limodzi lokha, la Masalmo. Buku limeneli lili ndi nyimbo zopatulika 150 zotamanda Yehova Mulungu, ndipo pafupifupi theka la zimenezi zinalembedwa ndi Mfumu Davide ya ku Israyeli wakale. Koma chofunika kwambiri kuposa kudziwa kuti analilemba ndani ndicho kudziwa kuti buku limeneli linalembedwa mouziridwa ndi Bwenzi lapamtima kwambiri la anthu, Yehova. Choncho tingakhale ndi chikhulupiriro kuti lili ndi malangizo a Mulungu otithandiza ndi kuti limatisonyeza njira yopezera chimwemwe.
Anthu amene analemba Masalmo ankadziwa kuti chimwemwe chimabwera chifukwa chokhala ndi ubwenzi wabwino ndi Mulungu. Wamasalmo analemba kuti: “Wodala [“wachimwemwe,” NW] munthu wakuopa Yehova.” (Salmo 112:1) Palibe ubwenzi ndi munthu wina aliyense, kaya kukhala ndi katundu wotani, kapena kukwanitsa kuchita chinthu chilichonse kumene kungabweretse chimwemwe ngati chimene chimabwera chifukwa chokhala m’gulu la “anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.” (Salmo 144:15) Moyo wa atumiki a Mulungu ambirimbiri masiku ano umasonyeza kuti zimenezi n’zoona.
Susanne, yemwe ali ndi zaka za m’ma 40, ndi chitsanzo chimodzi.a Iye anati: “Masiku ano, anthu ambiri amalowa magulu enaake kuti akwanitse zolinga zofanana zomwe ali nazo, kapena kuti azichitira limodzi zinthu zimene amakonda. Koma nthawi zambiri sizitheka kuti aliyense m’gulumo akhale mnzawo. N’zosiyana ndi anthu a Yehova. Chifukwa tonse timakonda Yehova, timakondananso wina ndi mnzake. Tikakhala pakati pa anthu a Mulungu, timakhala omasuka kulikonse kumene tingakhale. Umodzi umenewu umatithandiza kukhala ndi moyo wachimwemwe kwambiri. Kodi ndaninso amene anganene kuti ali ndi anzake a moyo wosiyanasiyana, opeza mosiyanasiyana, oleredwa mosiyanasiyana, ndiponso ochokera m’mayiko osiyanasiyana ngati ife? Ndi mtima wonse, ndinganene kuti kukhala mmodzi wa anthu a Yehova n’kumene kumabweretsa chimwemwe.”
Maree, yemwe anabadwira ku Scotland, anaonanso kuti kukhala ndi ubwenzi wabwino ndi Yehova n’kofunika kwambiri kuti munthu apeze chimwemwe. Iye anati: “Ndisanaphunzire Baibulo, ndinkakonda kuonerera mafilimu oopsa. Koma usiku sindinkatha kugona ndikapanda kunyamula mtanda m’manja mwanga kuti ndithamangitse mizukwa, imene mafilimu ambiri amene ndinkaonererawo ankasonyeza. Koma nditaphunzira choonadi, ndinasiya kuonerera mafilimu oterowo, ndipo ubwenzi wanga ndi Yehova unandithandiza kuti ndizitha kugona bwinobwino osachita mantha. Ndinali wachimwemwe kutumikira Mulungu wamphamvu kuposa ziwanda ndi mizukwa ija, imene ndinkaganiza kuti ilikodi.”
Kukhulupirira Yehova Kumabweretsa Chimwemwe
Tilibe zifukwa zokayikirira mphamvu ndi nzeru zakuya za Mlengi wathu. Podziwa kuti akhoza kudalira Yehova ndi mtima wonse ndi kuti akhoza kubisala kwa iyeyo, Davide analemba kuti: “Wodala [“wachimwemwe,” NW] munthuyo wakuyesa Yehova wokhulupirika.”—Salmo 40:4.
Maria anati: “Zomwe zinandichitikira ku Spain ndi ku mayiko ena zandisonyeza kuti tikachita zinthu m’njira ya Yehova, ngakhale ngati maganizo ndi mtima wathu ungafune kuti tizichite mwamtundu wina, zinthu zimatiyendera bwino kwambiri. Zimenezi zimabweretsa chimwemwe chifukwa njira ya Yehova nthawi zonse imakhala yabwino kwambiri.”
Andreas, amene ndi mkulu mu mpingo wachikristu ndipo watumikirapo m’mayiko angapo a ku Ulaya, nayenso kudzera m’zomwe zamuchitikira waona kuti tikhoza kuika chikhulupiriro chathu mwa Yehova. Anati: “Ndili mwana, mkulu wanga, amene ali wa chipembedzo china, anandichititsa kwambiri kufuna kudzapeza ntchito ya ndalama zambiri. Anakhumudwa kwambiri n’tayamba utumiki wa nthawi zonse m’malo modalira chitetezo chimene amati chimachokera ku mapenshoni a ntchito zolembedwa. Mu utumiki wanga wa nthawi zonse, sindinasowepo kanthu, ndipo ndapeza madalitso amene anthu ena amangowalota chabe.”
Mu 1993, Felix anapemphedwa kuti akathandize nawo pa ntchito yowonjezera ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Selters, ku Germany. Ntchitoyo itatha, anamupempha kuti akhaliretu pa banja la Beteli kumeneko. Kodi iye anatani? Iye akuti: “Ndinavomera koma kwinaku ndikukayikira. Koma panopa ndakhala kuno kwa zaka pafupifupi 10, ndipo ndikukhulupirira kuti Yehova anayankha mapemphero anga. Akudziwa zinthu zomwe zili zabwino kwambiri kwa ine. Mwakumudalira ndi mtima wonse ndi kumulola kuti anditsogolere, ndimamupatsa mpata woti andionetse zimene akufuna kuti ndichite.”
Susanne, yemwe tinamutchula kale uja, ankafuna kukhala mpainiya, kapena kuti mtumiki wa nthawi zonse, koma ankavutika kupeza ntchito yoti asamagwire masiku onse pamlungu. Atadikirira kwa chaka kuti mwina aipeza, anachita zinthu modalira Yehova. Iye anati: “Ndinapereka fomu yanga yofunsira kuti ndikhale mpainiya wokhazikika. Ndinali n’tasunga ndalama zokwanira kulipirira zosowa zanga kwa mwezi umodzi. Ndipo mwezi umenewo unakhala wodabwitsa kwambiri. Utumiki wanga ndinkasangalala nawo kwambiri, koma ndikaitanidwa kuti akandiyese ngati angandilembe ntchito, sankanditenga. Komabe, monga momwe Yehova analonjezera, sananditaye. Tsiku lomaliza la mweziwo, ndinalembedwa ntchito. Pamenepa ndinadziwa kuti ndikhozadi kumukhulupirira Yehova. Zinthu zimene zinandichitikira koyambirira kwa utumiki wanga wa nthawi zonse zimenezi, zandichititsa kukhala ndi moyo wachimwemwe kwambiri.”
Kutsatira Malangizo a Mulungu Kumabweretsa Chimwemwe
Mfumu Davide analakwitsa zinthu zina zikuluzikulu. Nthawi zina ankafunikira malangizo anzeru. Kodi ndife okonzeka kumvera uphungu ndi malangizo ngati mmene Davide analili?
Aida, wa ku France, nthawi inayake anazindikira kuti wachita cholakwa chachikulu. Iye anati: “Nkhawa yanga yaikulu inali yoti ndibwezeretse ubwenzi wanga ndi Yehova. Zina zonse ndinalibe nazo ntchito.” Anapita kwa akulu a mumpingo kuti amuthandize. Pokhala atatumikira kwa zaka zoposa 14 mu utumiki wa nthawi zonse, iye tsopano akuti: “N’zokhutiritsa kwambiri kudziwa kuti Yehova anandikhululukira tchimo langa.”
Kumvera malangizo a Mulungu kungatiteteze kuti tisachite n’komwe zolakwa. Judith anafotokoza kuti: “Pamene ndinali ndi zaka 20, ndinakopeka ndi mwamuna wina wachijeremani yemwe ndinali kuchita naye bizinesi, amene anachita zotheka kuti andigometse. Anthu ankamulemekeza, anali ndi ntchito yabwino kwambiri, komanso anali wokwatira! Ndinadziwa kuti ndiyenera kusankha pakati pa kumvera malamulo a Yehova kapena kumukaniratu Yehovayo. Ndinafotokozera makolo anga nkhaniyi. Bambo anga sananalankhule mondinyengerera, anandikumbutsa zimene Yehova ankafuna kuti ndichite. Anandilankhula mosapita m’mbali, ndipo zimenezo n’zimene ndinkafunikira! Ngakhale zinali choncho, mtima wanga unapeza njira yodzikhululukira. Kwa milungu yambiri, mayi anga ankalankhula nane madzulo alionse za momwe malamulo a Mulungu alili ofunika ndi opulumutsa moyo. Ndine woyamikira kwambiri kuti m’kupita kwa nthawi mtima wanga pang’ono ndi pang’ono unakopekanso ndi Yehova. Kulangidwa ndi kuphunzitsidwa ndi Yehova kwandibweretsera chimwemwe chachikulu. Ndachita utumiki wa nthawi zonse wokhutiritsa kwa zaka zambiri ndiponso ndinapeza mwamuna wabwino wachikristu amene amandikonda ndiponso amakonda Yehova ndi mtima wake wonse.”
Mwachionekere, nkhani ngati zimenezi zimasonyeza kuti mawu a Davide ndi oona, akuti: “Wodala [“wachimwemwe,” NW] munthuyo wokhululukidwa tchimo lake; wokwiriridwa choipa chake. Wodala [“wachimwemwe,” NW] munthuyu Yehova samuwerengera mphulupulu zake.”—Salmo 32:1, 2.
Kusamalira Ena Kumabweretsa Chimwemwe
Davide analemba kuti: “Wodala [“wachimwemwe,” NW] iye amene asamalira wosauka.” Anapitiriza kuti: “Tsiku la tsoka Yehova adzam’pulumutsa: Yehova adzam’sunga, nadzam’sunga ndi moyo, ndipo [“adzakhala wachimwemwe” NW].” (Salmo 41:1, 2) Chisamaliro chimene Davide anapatsa Mefiboseti, mwana wolumala wa Jonatani, mnzake wapamtima wa Davide, ndi chitsanzo cha mtima woyenera kuuonetsa kwa anthu otsika.—2 Samueli 9:1-13.
Marlies, yemwe wakhala mmishonale kwa zaka 47, ali ndi mwayi wolalikira kwa anthu amene anathawa ku madera oopsa a ku Africa, Asia, ndi kummawa kwa Ulaya. Iye anati: “Anthuwa amakhala ndi mavuto osiyanasiyana, ndipo nthawi zambiri amaona kuti salandiridwa kwenikweni, ndi kuti ena amawasankha. Kuthandiza anthu oterowo nthawi zonse kumabweretsa chimwemwe.”
Marina, yemwe ali ndi zaka za m’ma 40, analemba kuti: “Popeza ndine wosakwatiwa, ndikudziwa mmene zimasangalatsira ukadziwa kuti anthu ena ndi okonzeka kukuthandiza. Zimenezi zimandichititsa kuti ndizilimbikitsa anthu mwa kuwaimbira foni kapena kuwalembera makalata. Ambiri andiuza kuti amayamikira zimenezi. Kuthandiza ena kumandibweretsera chimwemwe.”
Dimitar, yemwe ali ndi zaka za m’ma 20, anati: “Ndinaleredwa ndi mayi anga okha. Pamene ndinali wamng’ono, ndinasangalala kuti mbale wina woyang’anira Phunziro la Buku la Mpingo ankanditenga mu utumiki mlungu uliwonse n’kumandiphunzitsa. Ndimayamikirabe khama lake. Ndikudziwa kuti nthawi zina zinali zovuta kundilimbikitsa kuchita zinthu zinazake.” Chifukwa choyamikira thandizo limene iyeyo analandirapo, Dimitar tsopano amathandiza anthu ena. Iye anati: “Ndimayesetsa kutenga wachinyamata ndi wachikulire mu utumiki wa kumunda kamodzi pa mwezi kapena kuposa pamenepo.”
Buku la Masalmo limatchulanso zinthu zina zimene zimatipatsa chimwemwe. Chimodzi ndicho kudalira mphamvu za Yehova, osati zako. Limati: “Wodala [“wachimwemwe,” NW] munthu amene mphamvu yake ili mwa [Yehova].”—Salmo 84:5.
Corinna akugwirizana ndi mawu amenewa. Iye anasamukira ku dziko limene linali kufunikira thandizo lalikulu mu utumiki. Anati: “Ndinakumana ndi chinenero chatsopano, chikhalidwe chatsopano, ndi kaganizidwe katsopano. Ndinkamva ngati sindilinso padziko lapansi pompano. Ndinkachita mantha kwambiri ndikaganizira zolalikira kumalo achilendo. Ndinapempha Yehova kuti andithandize, ndipo mphamvu zimene anandipatsa n’zimene zinandithandiza kuti ndizitha kulalikira tsiku lonse lathunthu kumagawo akumidzi. M’kupita kwanthawi, kuchita zimenezi sikunkandivutanso. Ndinayambitsa maphunziro a Baibulo ambiri, ndipo ndikupindulabe chifukwa cha zimene zinandichitikirazi. Ndinaphunzira kuti ndi mphamvu ya Yehova, tikhoza kugonjetsa ngakhale zopinga zooneka ngati zosagonjetseka.”
Zoonadi, zinthu zosiyanasiyana zimabweretsa chimwemwe. Zinthu zake ndi monga kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu ndi anthu ake, kukhulupirira Yehova ndi mtima wonse, kumvera malangizo ake, ndi kusamalira anthu ena. Mwa kuyenda m’njira za Yehova ndi kumvera malamulo ake, tikhoza kukhala achimwemwe podziwa kuti tikumusangalatsa.—Salmo 89:15; 106:3; 112:1; 128:1, 2.
[Mawu a M’munsi]
a Tasintha mayina ena.
[Chithunzi patsamba 12]
Maria
[Chithunzi patsamba 13]
Maree
[Chithunzi patsamba 13]
Susanne ndi Andreas
[Chithunzi patsamba 15]
Corinna
[Chithunzi patsamba 15]
Dimitar