Kuchita Chifuniro cha Mulungu Masiku Ano
“[Khristu] anaferanso onse kuti amoyo asadzikhalire moyo wa iwo eni.”—2 AKORINTO 5:15.
1. Fotokozani zimene mmishonale wina anakumana nazo kudera limene anatumizidwa.
“MMISHONALE wina dzina lake Aarona anati: “Itatha nkhondo yapachiweniweni, galimoto ya anthu wamba yoyamba kufika kumudzi wina wa ku Africa, inali yathu. Panthawi ya nkhondoyo, zinali zovuta kuti tilankhulane ndi abale a mumpingo wina waung’ono m’mudzi umenewo, ndipo tinafunika kuwathandiza. Kuwonjezera pa chakudya, zovala, ndi mabuku ofotokoza za m’Baibulo, tinawatengera vidiyo yofotokoza za ntchito imene Mboni za Yehova zikuchita. (Jehovah’s Witnesses—The Organization Behind the Name)b Vidiyoyi tinaionetsera, m’nyumba ina yaikulu ya udzu, ndipo anthu ambiri achidwi anabwera kudzaionera, moti tinayenera kuionetsa kawiri. Anthu ambiri anayamba kuphunzira Baibulo pambuyo poonera vidiyoyi. Apatu, khama lathu lonse linapindula kwambiri.”
2. (a) N’chifukwa chiyani Akhristu amasankha kutumikira Mulungu pamoyo wawo? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?
2 N’chifukwa chiyani Aaron ndi anzakewo anachita ntchito yovutayi? Chifukwa chakuti amayamikira nsembe ya dipo ya Yesu Khristu, iwo anadzipereka kwa Mulungu ndipo akufuna kuchita zinthu mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Mofanana ndi iwo, Akhristu onse odzipereka asankha kuti “asadzikhalire moyo wa iwo eni” koma kuti achite zonse zomwe angathe “kaamba ka uthenga wabwino.” (2 Akorinto 5:15; 1 Akorinto 9:23) Iwo akudziwa kuti pamapeto a dongosolo la zinthu ili, ndalama zonse ndiponso ulemu wa m’dzikoli zidzakhala zopanda ntchito. Choncho, popeza kuti ali ndi moyo komanso thanzi labwino, amafuna kuyesetsa kuchita chifuniro cha Mulungu. (Mlaliki 12:1) Kodi ife tingachite bwanji zimenezi? Kodi tingapeze kuti mphamvu zotilimbikitsa kuchita chifuniro cha Mulungu? Ndipo tili ndi mwayi wochita utumiki uti?
Kuchita Zinthu Zothandiza Kupita Patsogolo
3. Kodi munthu wofuna kuchita chifuniro cha Mulungu amachita zofunikira kwambiri ziti?
3 Kwa Akhristu oona, kuchita chifuniro cha Mulungu ndi ntchito ya moyo wonse. Kawirikawiri, ntchitoyi imayamba ndi kuchita zinthu zofunikira kwambiri monga kuwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku, kulembetsa m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, kulalikira, kenako n’kubatizidwa. Choncho, tikamapita patsogolo, timakumbukira mawu a mtumwi Paulo akuti: “Sinkhasinkha zinthu zimenezi mozama. Kangalika nazo, kuti kupita kwako patsogolo kuonekere kwa anthu onse.” (1 Timoteyo 4:15) Kupita patsogolo kumeneku si kudzitama koma ndi umboni wakuti tikufunitsitsa kuchita chifuniro cha Mulungu mopanda dyera. Tikatero, timasonyeza kuti tikulola Mulungu kutitsogolera m’mbali zonse za moyo wathu, ndipo iye amachita bwino kwambiri zimenezi kuposa eni akefe.—Salmo 32:8.
4. Kodi tingatani kuti tithetse mantha osayenera?
4 Komabe, kudzikayikira kwambiri kungalepheretse munthu kupita patsogolo potumikira Mulungu. (Mlaliki 11:4) Choncho, tisanayambe kusangalala chifukwa chotumikira Mulungu ndiponso anthu ena, tiyenera kuthetsa mantha. Mwachitsanzo, Erik ankaganiza zokatumikira ku mpingo wachinenero china. Koma anali ndi mantha ndipo ankadzifunsa kuti: ‘Kodi abale akandilandira? Kodi ndikatha kugwirizana ndi abale kumeneko?’ Iye anati: “Kenako, ndinazindikira kuti ndinkafunikira kudera nkhawa kwambiri abalewo m’malo modzidera nkhawa ndekha. Ndinaganiza zosiya kuda nkhawa n’kuyamba kuona mmene ndingathandizire abalewo. Ndinapemphera kuti Mulungu andithandize ndipo sindinabwerere m’mbuyo. Tsopano, ndi kutumikira mosangalala kwambiri kumeneko.” (Aroma 4:20) N’zoonadi, tikamayesetsa kutumikira Mulungu ndiponso anthu ena mopanda dyera, timakhala achimwemwe ndiponso okhutira ndi moyo.
5. N’chifukwa chiyani tiyenera kukonzekera bwino pofuna kuchita chifuniro cha Mulungu? Perekani chitsanzo.
5 Kuti tichite bwino chifuniro cha Mulungu, timafunikanso kukonzekera bwino. Tingachite bwino kupewa kutenga ngongole zambirimbiri zomwe zingatipangitse kukhala akapolo a dzikoli, n’kutilepheretsa kugwira ntchito ya Mulungu momasuka. Baibulo limatikumbutsa kuti: “Wokongola ndiye kapolo wa wom’kongoletsa.” (Miyambo 22:7) Kukhulupirira Yehova ndiponso kuika patsogolo zinthu zauzimu kungatithandize kuti tiziona zinthu moyenera. Mwachitsanzo, Guoming ndi achemwali ake awiri amakhala ndi mayi awo kudera lina komwe nyumba ndi zokwera mtengo ndiponso n’kovuta kupeza ntchito zodalirika. Mwa kugwiritsa ntchito ndalama mosamala ndi kusonkherana ndalama zoti agwiritsire ntchito, iwo amapeza zofunika pamoyo ngakhale pamene wina ali pa ulova. Guoming anati: “Nthawi zina, enafe timakhala tilibe ndalama. Komabe, tikupitiriza kuchita upainiya ndiponso kusamalira bwino mayi athu. Timayamikira kuti iwo safuna kuti tisiye kuchita upainiya n’cholinga choti tiziwapezera zinthu zimene amalakalaka.”—2 Akorinto 12:14; Aheberi 13:5.
6. Perekani chitsanzo chosonyeza mmene tingasinthire kuti tichite zinthu mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu
6 Ngati mumatanganidwa kwambiri ndi kupeza zinthu zakuthupi, kaya ndi chuma kapena zinthu zina, ndiye kuti mufunika kusintha kwambiri kuti muike patsogolo chifuniro cha Mulungu. Koma kusinthako kungatenge nthawi, ndipo ngati poyamba mwalakwitsa penapake, musaone ngati mwalephera. Taganizirani za Koichi, yemwe anali ndi vuto lothera nthawi yambiri pa zosangalatsa. Koichi anaphunzirapo Baibulo ali m’nyamata koma kwa zaka zambiri ankangokhalira kuchita masewera a pakompyuta. Tsiku lina, Koichi anadzifunsa kuti: ‘Kodi ndikuchita chiyani? Ndili ndi zaka zoposa 30, koma sindikuchita chilichonse chaphindu pamoyo wanga!’ Koichi anayambanso kuphunzira Baibulo ndipo anavomera kuti mpingo umuthandize. Ngakhale kuti ankasintha pang’onopang’ono, iye sanabwerere m’mbuyo. Chifukwa chopemphera mwakhama ndiponso thandizo la anthu ena, anasiya chizolowezi chakecho. (Luka 11:9) Panopo, Koichi ndi mtumiki wothandiza ndipo akusangalala ndi utumiki umenewu.
Phunzirani Kuchita Zinthu Mosapyola Malire
7. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuchita zinthu mopyola malire potumikira Mulungu?
7 Kuti tichite chifuniro cha Mulungu tiyenera kudzipereka ndi mtima wonse ndi kupewa kukhala aulesi. (Aheberi 6:11, 12) Komabe, Yehova safuna kuti tizichita zinthu zomwe sitingakwanitse. Tikamavomereza kuti sitingachite ntchito ya Mulungu ndi mphamvu zathu, timalemekeza Mulungu ndipo timasonyeza kuti ndife oganiza bwino. (1 Petulo 4:11) Yehova akulonjeza kuti adzatipatsa mphamvu zoyenera kuti tichite chifuniro chake. Koma sitiyenera kuchita zinthu mopyola malire, n’kumayesetsa kuchita zinthu zimene iye akudziwa kuti sitingathe. (2 Akorinto 4:7) Kuti tipitirize kutumikira Mulungu koma osatopa, tifunikira kuona mmene tingagwiritsire ntchito bwino mphamvu zathu.
8. Kodi chinachitika n’chiyani pamene Mkhristu wina wachinyamata anayesetsa kutumikira Yehova pamene ankagwira ntchito, ndipo anasintha zinthu zotani?
8 Mwachitsanzo, taonani za mlongo wina dzina lake Ji Hye, yemwe amakhala kum’mawa kwa Asia. Kwa zaka ziwiri, iye anagwira ntchito ina yomwe inkafuna nthawi yambiri pamene ankachita upainiya. Iye anati: “Ndinkayesetsa kuchita khama kutumikira Yehova komanso kugwira ntchito, moti ndinkangogona maola asanu okha basi. Kenako, ndinasiya kuganiza za choonadi, ndipo ndinasiyanso kukonda zinthu zauzimu.” Kuti atumikire Yehova ndi ‘mtima wake wonse, ndi moyo wake wonse, ndi maganizo ake onse, ndi mphamvu zake zonse,’ Ji Hye anafuna ntchito ina yosafuna nthawi yambiri. (Maliko 12:30) Iye anati: “Ngakhale kuti banja langa linkandilimbikitsa kuti ndizigwira ntchito ya ndalama zambiri, ndinayesetsa kuika chifuniro cha Mulungu patsogolo. Ndalama zomwe ndimalandira n’zokwanira kugulira zinthu zofunika, monga zovala zabwino. Ndipo ndikusangalala kwambiri chifukwa ndimagona mokwanira. Tsopano ndikutumikira mosangalala, ndiponso ubwenzi wanga ndi Yehova n’ngolimba. Zimenezi zatheka chifukwa choti sindikhala ndi nthawi yambiri yochita zinthu zakuthupi zomwe zingandikope kapena kundisokonezeka.”—Mlaliki 4:6; Mateyo 6:24, 28-30.
9. Kodi utumiki wathu ungakhudze bwanji anthu amene timawalalikira?
9 Si aliyense amene angachite utumiki wa nthawi zonse. Ngati mukulimbana ndi ukalamba, matenda, kapena mavuto ena, dziwani kuti Yehova amayamikira kukhulupirika kwanu ndiponso zilizonse zomwe mukuchita pom’tumikira ndi mtima wonse. (Luka 21:2, 3) Ndipo palibe amene ayenera kupeputsa mmene ena amapindulira ndi utumiki wathu ngakhale tikuchita zochepa. Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti tapita pa nyumba zingapo ndipo sitinapeze munthu aliyense wachidwi ndi uthenga wathu. Titachoka, n’kutheka kuti eninyumbawo angakambirane za ife kwa maola angapo kapenanso masiku ambiri, ngakhale kuti palibe aliyense amene anatilandira. Sitiyembekezera kuti aliyense amene wamva uthenga wabwino angasangalale nawo, koma ena angatero. (Mateyo 13:19-23) N’kutheka kuti ena angadzasangalale ndi uthengawu zinthu zitasintha m’dzikoli kapena pamoyo wawo. Kaya anthu asangalale nawo uthengawu kapena ayi, ife tikamachita zomwe tingathe polalikira, timakhala tikugwira ntchito ya Mulungu. “Ndife antchito anzake a Mulungu.”—1 Akorinto 3:9.
10. Kodi tonse mumpingo tili ndi mwayi wochita chiyani?
10 Kuwonjezera pamenepo, tonsefe tingathe kuthandiza achibale athu ndiponso abale ndi alongo a mumpingo mwathu. (Agalatiya 6:10) Zochita zathu zabwino zingalimbikitse kwambiri anthu ena mpaka kalekale. (Mlaliki 11:1, 6) Akulu ndi atumiki othandiza akamadzipereka pa ntchito zawo, amathandiza kuti mpingo ukhale wokonda zinthu zauzimu ndiponso wolimba, komanso ntchito za Ufumu zimapita patsogolo. Sitikayikira kuti tikakhala ndi “zochita zochuluka m’ntchito ya Ambuye,” ntchito yathu “sikupita pachabe.”—1 Akorinto 15:58.
Kuchita Chifuniro cha Mulungu Monga Ntchito Yathu
11. Kodi tingakhale ndi mwayi wochita utumiki wina uti kuwonjezera pa zomwe tikuchita pa mpingo?
11 Akhristufe timasangalala ndi moyo, ndipo timafuna kutamanda Mulungu pa chilichonse chomwe tikuchita. (1 Akorinto 10:31) Tikamalalikira mokhulupirika uthenga wabwino wa Ufumu ndi kuphunzitsa ena kuti asunge zinthu zonse zimene Yesu anatilamula, tidzapeza mwayi wotumikira Mulungu m’njira zosiyanasiyana. (Mateyo 24:14; 28:19, 20) Kuwonjezera pa kutumikira mu mpingo wanu, mungakhale ndi mwayi wokatumikira kumene kulibe olalikira okwanira, kaya ndi kudera lina, mu mpingo wachinenero china, kapena ku dziko lina. Akulu ndi atumiki othandiza oyenerera amene sanakwatire, angaitanidwe ku Sukulu Yophunzitsa Utumiki, ndipo akamaliza sukuluyo amakatumikira m’mipingo imene ikufunika thandizo la Akhristu okhwima mwauzimu, m’dziko lawo lomwelo kapena m’mayiko ena. Mabanja omwe ali mu utumiki wa nthawi zonse angathe kupita ku sukulu ya Gileadi yophunzitsa umishonale ndi kukatumikira ku mayiko ena. Komanso, nthawi zonse pamafunika anthu odzipereka oti agwire ntchito zosiyanasiyana pa Beteli, ndiponso kumanga malo a misonkhano ndi maofesi a nthambi.
12, 13. (a) N’chiyani chingakuthandizeni kudziwa utumiki woti muchite? (b) Perekani chitsanzo chosonyeza kuti luso limene tingaphunzire mu utumiki wina lingathandize mu utumiki winanso.
12 Kodi inuyo mungachite utumiki uti? Monga mtumiki wodzipereka, muyenera kudalira thandizo la Yehova ndi gulu lake. ‘Mzimu wake wokoma’ udzakuthandizani kuti musankhe mwanzeru. (Nehemiya 9:20) Nthawi zambiri utumiki wina umapereka mwayi wochitira utumiki wina, ndipo luso limene mungapeze mu utumiki wina lingakuthandizeni mu utumiki winanso.
13 Mwachitsanzo, Dennis ndi mkazi wake Jenny, nthawi ndi nthawi amathandiza ntchito zomanga Nyumba za Ufumu. Mphepo ya mkuntho yotchedwa Katrina itawomba kum’mwera kwa dziko la United States, iwo anadzipereka kukathandiza anthu omwe anakhudzidwa ndi tsokalo. Dennis anati: “Tikusangalala kwambiri kugwiritsa ntchito luso limene tinaphunzira pomanga Nyumba za Ufumu, kuthandiza abale athu amene anakhudzidwa ndi tsokali. Zimatikhudza mtima kwambiri kuona anthu amene tinawathandiza akuyamikira zimene tinachita. Ntchito yothandiza anthu m’derali imene magulu ena ambiri akuchita, sikuwayendera bwino kwenikweni. Koma tikunena pano, Mboni za Yehova zakonza kapena kumanganso nyumba zoposa 5,300 ndiponso Nyumba za Ufumu zambiri. Anthu ena akuona zimenezi ndipo tsopano akuchita chidwi kwambiri ndi uthenga wathu.”
14. Kodi mungatani ngati mukufuna kuyamba utumiki wa nthawi zonse?
14 Ndi bwino kwambiri kukonza zochita utumiki wa nthawi zonse pamene mukuchita chifuniro cha Mulungu. Mukatero mudzapeza madalitso ambiri. Ngati panopa simungakwanitse kuchita utumiki wa nthawi zonse, yesani kusintha zinthu zina pamoyo wanu. Pempherani monga mmene Nehemiya anachitira pamene ankafuna kuchita utumiki wofunika kwambiri. Iye anapemphera kuti: “Yehova, . . . mulemereze kapolo wanu.” (Nehemiya 1:11) Mukatero, khulupirirani “Wakumva pemphero,” ndipo chitani zinthu mogwirizana ndi pemphero lanu. (Salmo 65:2) Muyenera kusonyeza khama lofuna kutumikira Yehova ndi mtima wonse ndipo iye adzadalitsa khama lanulo. Ngati mwaganiza zochita utumiki wa nthawi zonse, chitani zimene mukuganizazo ndi mtima wonse. M’kupita kwa nthawi, luso lanu limakula, ndipo mumayamba kusangalala kwambiri.
Moyo Watanthauzo Lenileni
15. (a) Kodi timapindula bwanji tikamalankhula ndi anthu amene akhala akutumikira Mulungu kwa nthawi yaitali ndiponso kuwerenga nkhani zawo? (b) Tchulani nkhani ya moyo wa munthu imene inakulimbikitsani kwambiri.
15 Kodi mungayembekezere zotani ngati mukufuna kuchita chifuniro cha Mulungu? Lankhulani ndi anthu omwe atumikira Yehova nthawi yaitali, makamaka amene akhala akuchita utumiki wa nthawi zonse kwa zaka zambiri. Iwotu ali ndi moyo watanthauzo lenileni. (Miyambo 10:22) Adzakuuzani kuti Yehova wakhala akuwathandiza kupeza zosowa zawo zikuluzikulu ndiponso zinthu zina zambiri ngakhale panthawi yovuta. (Afilipi 4:11-13) Kwa zaka zambiri, Nsanja ya Olonda yakhala ikutulutsa nkhani zofotokoza moyo wa atumiki osiyanasiyana. Nkhani iliyonse imatilimbikitsa kukhala achangu ndiponso osangalala, moti imatikumbutsa zochitika za m’buku la Machitidwe. Tikamawerenga nkhani zosangalatsa zimenezi timalimbikitsidwa kunena kuti, ‘Uwu ndiye moyo womwe ndikufuna!’
16. N’chiyani chimachititsa Mkhristu kukhala ndi moyo watanthauzo ndiponso wosangalala?
16 Aaron amene tam’tchula kumayambiriro uja anati: “Ku Africa kuno ndakhala ndikukumana ndi achinyamata amene amangoyendayenda pofufuza moyo watanthauzo lenileni, koma ambiri sanaupeze. Koma ife tikuchita chifuniro cha Mulungu mwa kupititsa patsogolo uthenga wabwino wa Ufumu, ndipo tasangalala ndi moyo wokhala ndi zochita zambiri ndiponso watanthauzo. Tadzionera tokha kuti kupatsa kumabweretsa chisangalalo chochuluka kuposa kulandira.”—Machitidwe 20:35.
17. N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita chifuniro cha Mulungu panopa?
17 Nanga bwanji inuyo? Kodi muli ndi cholinga chotani? Ngati mulibe cholinga chenicheni cha zinthu zauzimu, padzapezeka zolinga zina zimene zingalowe m’malo. Pewani kugwiritsa ntchito moyo wanu wamtengo wapatali molakwika pofunafuna zinthu zimene zimaoneka ngati zofunika m’dongosolo la Satanali. Posachedwapa, “chisautso chachikulu” chikadzayamba, chuma chakuthupi ndi maudindo amene anthu ali nawo m’dzikoli, zidzakhala zopanda ntchito. Ubwenzi wathu ndi Yehova ndi umene udzakhala wofunika kwambiri. Tidzasangalala kwambiri chifukwa choti tatumikira Mulungu ndiponso anthu ena komanso kuti takhala tikuchita chifuniro cha Mulungu ndi mtima wathu wonse.—Mateyo 24:21; Chivumbulutso 7:14, 15.
[Mawu a M’munsi]
a Mayina ena tawasintha.
b Yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
Kodi Mungafotokoze?
• Kodi Yehova amaona bwanji utumiki wathu?
• Kodi kuganiza ndi kuchita zinthu mwanzeru kungatithandize bwanji kutumikira Mulungu ndiponso anthu ena?
• Kodi pali mwayi wotumikira Mulungu m’njira zosiyanasiyana ziti?
• Kodi tingatani kuti tikhale ndi moyo watanthauzo lenileni panopa?
[Zithunzi patsamba 23]
Tifunika kuchita zinthu mwanzeru kuti tipitirize kutumikira Yehova ndi mtima wonse
[Zithunzi patsamba 24]
Tingatumikire Mulungu m’njira zosiyanasiyana