Miyambo
Mwana wanzeru amasangalatsa bambo ake,+
Koma mwana wopusa amamvetsa chisoni mayi ake.
2 Chuma chimene munthu wapeza chifukwa chochita zoipa chidzakhala chopanda phindu,
Koma chilungamo nʼchimene chimapulumutsa munthu ku imfa.+
3 Yehova sadzachititsa kuti munthu wolungama akhale ndi njala,+
Koma anthu oipa sadzawapatsa zimene amalakalaka.
5 Mwana wochita zinthu mozindikira amatuta zokolola mʼchilimwe,
Koma mwana wochititsa manyazi amakhala ali mʼtulo tofa nato pa nthawi yokolola.+
7 Zabwino zimene munthu wolungama ankachita zikakumbukiridwa* amadalitsidwa,+
Koma dzina la anthu oipa lidzawola.+
9 Munthu wochita zinthu mokhulupirika adzakhala wotetezeka,+
Koma munthu wochita zinthu mwachinyengo adzadziwika.+
10 Munthu amene amatsinzinira ena diso amachititsa ena kumva chisoni,+
Ndipo amene amalankhula mopusa adzapeza mavuto.+
13 Nzeru imapezeka pamilomo ya munthu wozindikira,+
Koma ndodo amakwapulira msana wa munthu wopanda nzeru.+
14 Anzeru ndi amene amapitiriza kuphunzira zinthu zamtengo wapatali,+
Koma pakamwa pa wopusa pamachititsa kuti awonongedwe.+
15 Munthu wolemera amaona kuti chuma chake chili* ngati mzinda wokhala ndi mpanda wolimba.
Koma anthu osauka amavutika chifukwa cha umphawi wawo.+
17 Amene amamvera malangizo* amathandiza ena kukapeza moyo,*
Koma amene amanyalanyaza chidzudzulo amasocheretsa ena.
18 Munthu amene amabisa chidani mumtima mwake amalankhula mabodza,+
Ndipo amene amafalitsa mphekesera zoipa ndi wopusa.
19 Mawu akachuluka sipalephera kukhala zolakwika,+
Koma amene amalamulira milomo yake amachita zinthu mwanzeru.+
22 Madalitso a Yehova ndi amene amalemeretsa munthu,+
Ndipo popereka madalitsowa Mulungu sawonjezerapo ululu.*
23 Kwa munthu wopusa, kuchita khalidwe lochititsa manyazi kuli ngati masewera,
Koma munthu wozindikira amakhala ndi nzeru.+
24 Chinthu chimene munthu woipa amaopa nʼchimene chidzamuchitikire,
Koma anthu olungama adzapatsidwa zimene amalakalaka.+
26 Viniga* amachititsa kuti mano ayezimire ndipo utsi umapweteka mʼmaso,
Izi nʼzimene munthu waulesi amachita kwa munthu amene wamutuma.*
28 Zimene anthu olungama akuyembekezera zimasangalatsa,*+
Koma chiyembekezo cha anthu oipa sichidzakwaniritsidwa.+
29 Njira ya Yehova ndi malo achitetezo kwa munthu wopanda cholakwa,+
Koma anthu ochita zoipa amawonongedwa mʼnjira imeneyi.+
31 Pakamwa pa munthu wolungama pamalankhula* zanzeru,
Koma lilime lolankhula zinthu zopotoka lidzadulidwa.
32 Milomo ya munthu wolungama imadziwa zinthu zosangalatsa,
Koma pakamwa pa anthu oipa mʼpachinyengo.