Mtsogoleri Wathu Akuchita Zambiri Masiku Ano
“Anapita kukagonjetsa ndi kukatsiriza kugonjetsa kwake.”—CHIV. 6:2.
1, 2. (a) Kodi Baibulo limamufotokoza bwanji Khristu monga mfumu kuyambira mu 1914? (b) Kodi ndi zinthu ziti zimene Khristu wachita kuyambira pamene anaikidwa kukhala Mfumu?
MU 1914 Khristu anaikidwa kukhala Mfumu ya Ufumu wa Yehova wolamulidwa ndi Mesiya. Kodi tikuganiza kuti panopa iye akuchita chiyani? Kodi iye ndi mfumu yomwe yakhala pampando wake phee, n’kumangoyang’ana padziko lapansi mmene zinthu zikuyendera mu mpingo wake? Ngati tikuganiza choncho tiyenera kusintha maganizo athu. Buku la Masalmo ndi la Chivumbulutso limafotokoza kuti Khristu ndi mfumu yamphamvu ndipo wakwera pa kavalo kupita “kukagonjetsa ndi kukatsiriza kugonjetsa kwake” mpaka kupambana.—Chiv. 6:2; Sal. 2:6-9; 45:1-4.
2 Chinthu choyamba chimene Khristu anachita atangoikidwa kukhala mfumu, chinali kugonjetsa “chinjoka ndi angelo ake.” Khristu monga Mikayeli, mkulu wa angelo, anatsogolera angelo ake kugwetsa Satana ndi ziwanda zake kuchoka kumwamba n’kuwaponyera padziko lapansi. (Chiv. 12:7-9) Kenako monga “mthenga wa chipangano” wa Yehova, iye anabwera ndi Atate wake kudzayendera kachisi wauzimu. (Mal. 3:1) Iye anaweruza Matchalitchi Achikhristu omwe ndi mbali yoipa kwambiri ya “Babulo wamkulu” kuti ali ndi mlandu wakupha anthu ndiponso wochita chiwerewere mwauzimu ndi dongosolo la ndale la dzikoli.—Chiv. 18:2, 3, 24.
Khristu Ayeretsa Kapolo Wake Wapadziko Lapansi
3, 4. (a) Kodi ndi ntchito iti imene Khristu anagwira monga “mthenga” wa Yehova? (b) Kodi zotsatira za kuyendera kachisi zinali zotani, nanga kodi Yesu monga Mutu wa mpingo anapereka udindo wotani kwa kapolo wokhulupirika?
3 Kuyendera kumene Yehova ndi “mthenga” wake anachita kunasonyezanso kuti m’bwalo la padziko lapansi la kachisi wauzimu ameneyu muli gulu la Akhristu oona amene sali mbali ya Matchalitchi Achikhristu. Komabe, ngakhale Akhristu odzozedwa amenewa, kapena kuti “ana a Levi” anayenera kuyeretsedwa. Zimenezi n’zogwirizana ndi zimene mneneri Malaki analosera kuti: “[Yehova] adzakhala pansi ndi kuyenga ndi kuyeretsa siliva, nadzayeretsa ana a Levi, nadzawayengetsa ngati golidi ndi siliva; pamenepo iwo adzapereka kwa Yehova zopereka m’chilungamo.” (Mal. 3:3) Yehova anagwiritsa ntchito “mthenga wa chipangano,” Khristu Yesu kuyeretsa Aisiraeli auzimu amenewa.
4 Koma Khristu anapeza Akhristu odzozedwa okhulupirikawa akuyesetsa mmene angathere kupereka chakudya chauzimu cha pa nthawi yake kwa Akhristu anzawo. Kuyambira m’chaka cha 1879, gululi linkafalitsa mfundo za choonadi cha m’Baibulo chonena za Ufumu wa Mulungu m’magazini a Nsanja ya Olonda ndipo linkachita zimenezi ngakhale kuti panali mavuto ambirimbiri. Yesu analosera kuti “pobwera” kudzayendera antchito ake a pakhomo nthawi ya “mapeto a dongosolo lino la zinthu,” adzapeza kapoloyu akupereka “chakudya chawo panthawi yoyenera.” Iye anali kudzatcha kapoloyu kuti ndi wosangalala, ‘n’kumuika kukhala woyang’anira zinthu zake zonse.’ (Mat. 24:3, 45-47) Monga Mutu wa Mpingo, Khristu akugwiritsa ntchito “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ameneyu kuyang’anira zinthu Zake zokhudza Ufumu padziko lapansi. Iye amapereka malangizo kwa odzozedwa omwe ndi “antchito ake a pakhomo” ndiponso kwa anzawo a “nkhosa zina” kudzera m’Bungwe Lolamulira.—Yoh. 10:16.
Ntchito Yokolola Padziko Lapansi
5. M’masomphenya, kodi mtumwi Yohane anaona mfumu ikuchita chiyani?
5 Mtumwi Yohane anaona masomphenya a zinthu zinanso zimene Mfumu Mesiya inali kudzachita “m’tsiku la Ambuye” ataikidwa kukhala Mfumu mu 1914. Yohane analemba kuti: “Nditayang’ana, ndinaona mtambo woyera. Pamtambopo panakhala winawake ngati mwana wa munthu, atavala kolona wachifumu wa golide kumutu kwake, ndi chikwakwa chakuthwa chili m’dzanja lake.” (Chiv. 1:10; 14:14) Yohane anamva mngelo wochokera kwa Yehova akuuza Wokolola kuti atsitse chikwakwa chake chifukwa zokolola “za dziko lapansi zapsa bwino ndithu.”—Chiv. 14:15, 16.
6. Kodi Yesu ananena kuti chidzachitike n’chiyani m’munda isanafike nthawi yokolola?
6 Ntchito yokhudza “zokolola za dziko lapansi” imeneyi ikutikumbutsa fanizo la Yesu la tirigu ndi namsongole. Yesu anadziyerekezera ndi munthu amene anafesa tirigu m’munda wake n’kumayembekezera kuti adzakolole tirigu wabwino. Tirigu akuimira “ana a ufumu” omwe ndi Akhristu odzozedwa amene adzalamulire ndi Yesu mu Ufumu wake. Koma pakati pa usiku mdani yemwe ndi “Mdyerekezi” anafesanso namsongole amene akuimira “ana a woipayo.” Wofesayo anauza antchito ake kuti asiye tirigu ndi namsongole kuti zikulire limodzi mpaka nthawi yokolola imene ndi “mapeto a dongosolo lino la zinthu.” Pa nthawi imeneyo iye adzatumiza angelo ake kuti asiyanitse tirigu ndi namsongole.—Mat. 13:24-30, 36-41.
7. Kodi Khristu akutsogolera bwanji ntchito ‘yokolola padziko lapansi’?
7 Pokwaniritsa masomphenya amene Yohane anaona, Yesu wakhala akutsogolera ntchito yokolola padziko lonse. Ntchito ‘yokolola padziko lapansi’ inayamba ndi kusonkhanitsidwa kwa otsalira odzozedwa a 144,000. Amenewa ndi “ana a ufumu” ndiponso “tirigu” wa m’fanizo la Yesu. Kusiyana pakati pa Akhristu oona ndi Akhristu onama kunayamba kuonekera bwino kwambiri nkhondo yoyamba ya padziko lonse itatha. Zimenezi zachititsa kuti mbali yachiwiri ya ntchito ‘yokolola padziko lapansi,’ yomwe ndi kusonkhanitsa a nkhosa zina, iyambike. A nkhosa zina si “ana a ufumu” koma ndi “khamu lalikulu” la anthu omwe ndi nzika za Ufumuwo. Iwo akusonkhanitsidwa kuchokera pakati pa “anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse.” Iwo amagonjera Ufumu wa Mesiya womwe olamulira ake ndi Khristu Yesu ndi a 144,000. Anthu 144,000 amenewa ndi “opatulika” ndipo adzalamulira naye m’boma lakumwamba limeneli.—Chiv. 7:9, 10; Dan. 7:13, 14, 18.
Kodi Khristu Amatsogolera Bwanji Mipingo?
8, 9. (a) Kodi tikudziwa bwanji kuti Khristu samangoyang’ana khalidwe la mpingo koma amadziwanso khalidwe la Mkhristu aliyense payekha? (b) Mogwirizana ndi chithunzi chomwe chili patsamba 26, ndi “zinthu zozama za Satana” ziti zimene tiyenera kuzipewa?
8 M’nkhani yapitayi tinaona kuti m’nthawi ya atumwi, Khristu ankaona moyo wauzimu wa mpingo uliwonse. Masiku ano, Mfumu Khristu wapatsidwa “ulamuliro wonse . . . kumwamba ndi padziko lapansi.” Mtsogoleri wathuyu akuchita zambiri potsogolera mipingo ya padziko lonse lapansi komanso oyang’anira ake. (Mat. 28:18; Akol. 1:18) Yehova wamuika kukhala “mutu wa zinthu zonse kaamba ka mpingo” wa odzozedwa. (Aef. 1:22) Choncho, palibe chimene chimachitika mu uliwonse wa mipingo 100,000 ya Mboni za Yehova, chomwe Yesu sachiona.
9 Yesu anauza mpingo wakale wa ku Tiyatira kuti: “Nazi zimene Mwana wa Mulungu akunena, iye amene maso ake ali ngati lawi lamoto, . . . ‘Ndikudziwa ntchito zako.’” (Chiv. 2:18, 19) Iye anadzudzula anthu a mumpingo umenewo chifukwa cha khalidwe lawo lachiwerewere ndiponso longofuna kudzisangalatsa. Iye anawauza kuti: “Ineyo ndiye amene ndimafufuza impso ndi mitima, ndipo ndidzabwezera mmodzimmodzi wa inu malinga ndi ntchito zanu.” (Chiv. 2:23) Mawu amenewa akusonyeza kuti Khristu samangoona khalidwe la mpingo uliwonse, koma amaonanso zimene Mkhristu aliyense payekha amachita. Yesu anayamikira Akhristu a ku Tiyatira ‘amene sanadziwe “zinthu zozama za Satana.”’ (Chiv. 2:24) Masiku anonso iye amasangalala ndi achinyamata kapena achikulire amene amapewa kulowerera mu “zinthu zozama za Satana” kudzera pa Intaneti, masewera achiwawa a pakompyuta kapena kutsatira maganizo a anthu otayirira. Iye amasangalala kwambiri akamaona Akhristu akuchita khama kutsatira malangizo ake pamoyo wawo.
10. Kodi Baibulo limasonyeza bwanji kuti Khristu amatsogolera akulu m’mipingo, nanga ndi dongosolo liti limene sitiyenera kuiwala?
10 Khristu amayang’anira mipingo yake ya padziko lapansi mwachikondi kudzera mwa akulu. (Aef. 4:8, 11, 12) Mu nthawi ya atumwi akulu onse anali odzozedwa ndi mzimu. Buku la Chivumbulutso limati iwo ndi nyenyezi m’dzanja lamanja la Khristu. (Chiv. 1:16, 20) Masiku ano, akulu m’mipingo yambiri ndi a nkhosa zina. Akulu amenewa amaikidwa motsogoleredwa ndi mzimu pambuyo pa pemphero, choncho iwonso akutsogoleredwa ndi Khristu, kapena kuti ndi dzanja lake. (Mac. 20:28) Komabe iwo amadziwa kuti Khristu akugwiritsa ntchito kagulu ka Akhristu odzozedwa monga Bungwe Lolamulira potsogolera ndiponso popereka malangizo kwa ophunzira ake padziko lapansi.—Werengani Machitidwe 15:6, 28-30.
“Bwerani, Ambuye Yesu”
11. N’chifukwa chiyani tikufunitsitsa kuti Mtsogoleri wathu abwere mwamsanga?
11 M’masomphenya amene Yohane anaona, Yesu ananena mobwerezabwereza kuti akubwera mofulumira. (Chiv. 2:16; 3:11; 22:7, 20) Mosakayikira, iye ankanena za kubwera kwake kudzapereka chiweruzo kwa Babulo Wamkulu ndiponso mbali yonse ya dongosolo loipa la Satanali. (2 Ates. 1:7, 8) Chifukwa chakuti ankafunitsitsa kuona kukwaniritsidwa kwa zinthu zochititsa chidwizi, mtumwi wokalamba Yohane anafuula kuti: “Amen! Bwerani, Ambuye Yesu.” Ifenso amene tikukhala m’nthawi yamapeto a dongosolo loipa lino la zinthu, tikufunitsitsa kuona Mtsogoleri ndiponso Mfumu yathu ikubwera kudzayeretsa dzina la Atate wake ndi kudzatsimikizira kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira.
12. Kodi ndi ntchito iti imene Khristu ayenera kumaliza angelo asanasiye mphepo zowononga dziko?
12 Yesu akamadzabwera kudzawononga dongosolo la Satanali, anthu onse a m’gulu la 144,000, omwe ndi Isiraeli wauzimu, adzakhala atalandira chisindikizo chomaliza. Baibulo limanena momveka bwino kuti mphepo zowononga dongosolo la Satanali sizidzasiyidwa kuti ziwononge dzikoli anthu ena a m’gulu la 144, 000 asanasindikizidwe.—Chiv. 7:1-4.
13. Kodi kukhalapo kwa Khristu kudzaonekera bwanji kumayambiriro kwa “chisautso chachikulu”?
13 Anthu ambiri m’dzikoli sadziwa kuti nthawi ya “kukhalapo” kwa Khristu inayamba mu 1914. (2 Pet. 3:3, 4) Koma posachedwapa kukhalapo kwake kudzaonekera akamadzapereka ziweruzo za Yehova pa mbali zosiyanasiyana za dongosolo la Satanali. Kuwonongedwa kwa “munthu wosamvera malamulo” amene ndi atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu, kudzakhala umboni ‘woonekeratu wa kukhalapo kwake.’ (Werengani 2 Atesalonika 2:3, 8.) Zimenezi zidzapereka umboni wosatsutsika wakuti Khristu akugwira ntchito monga Woweruza wosankhidwa ndi Yehova. (Werengani 2 Timoteyo 4:1.) Kuwonongedwa kwa mbali yoipa kwambiri ya Babulo Wamkulu, kudzakhala kalambula bwalo wa chiwonongeko cha ufumu wa padziko lonse wa chipembedzo chonyenga. Yehova adzaika maganizo ake mumtima wa atsogoleri a ndale kuti awononge mkazi wachiwerewere. (Chiv. 17:15-18) Kumeneku kudzakhala kuyamba kwa “chisautso chachikulu.”—Mat. 24:21.
14. (a) N’chifukwa chiyani mbali yoyambirira ya chisautso chachikulu idzafupikitsidwa? (b) Kodi “chizindikiro cha mwana wa munthu” chikadzaonekera zidzatanthauza chiyani kwa anthu a Yehova?
14 Yesu ananena kuti masiku a chisautso amenewo adzafupikitsidwa “chifukwa cha osankhikawo” amene ndi Akhristu odzozedwa omwe adakali padziko lapansi. (Mat. 24:22) Yehova sadzalola kuti Akhristu odzozedwa ndi anzawo a nkhosa zina awonongedwe pa nthawi imeneyi pamene chipembedzo chonyenga chidzaukiridwa. Yesu anawonjezera kuti, “chisautso cha masiku amenewo chikadzangotha” padzakhala zizindikiro padzuwa, mwezi ndi nyenyezi, ndipo kenako “chizindikiro cha Mwana wa munthu chidzaonekera kumwamba.” Zimenezi zidzachititsa mitundu ya padziko lapansi ‘kudziguguda pachifuwa chifukwa cha chisoni.’ Koma sizidzakhala choncho ndi Akhristu odzozedwa amene ali ndi chiyembekezo chodzapita kumwamba komanso anzawo a nkhosa zina amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi. Iwo ‘adzaimilira chilili ndi kutukula mitu yawo, chifukwa chipulumutso chawo chidzakhala chitayandikira.’—Mat. 24:29, 30; Luka 21:25-28.
15. Kodi Khristu akadzabwera adzagwira ntchito yotani?
15 Asanatsirize kugonjetsa, Mwana wa munthu adzabweranso m’njira ina. Iye analosera kuti: “Mwana wa munthu akadzafika mu ulemerero wake, limodzi ndi angelo ake, pamenepo adzakhala pa mpando wake wachifumu waulemerero. Ndipo mitundu yonse ya anthu idzasonkhanitsidwa kwa iye, ndipo adzalekanitsa anthu, mmene m’busa amalekanitsira nkhosa ndi mbuzi. Ndipo adzaika nkhosa ku dzanja lake lamanja, koma mbuzi adzaziika kumanzere kwake.” (Mat. 25:31-33) Lembali likunena za kubwera kwa Yesu monga Woweruza kudzasiyanitsa anthu a “mitundu yonse” m’magulu awiri. Gulu loyamba ndi la “nkhosa” zomwe zikuimira anthu amene amachirikiza abale auzimu a Khristu (Akhristu odzozedwa amene ali padziko lapansi). Gulu lachiwiri ndi la “mbuzi” zomwe zikuimira anthu “osamvera uthenga wabwino wonena za Ambuye wathu Yesu.” (2 Ates. 1:7, 8) Nkhosa zimene azifokoza kuti ndi anthu “olungama,” zidzalandira ‘moyo wosatha,’ koma mbuzi zidzapita “ku chiwonongeko chotheratu.”—Mat. 25:34, 40, 41, 45, 46.
Yesu Akukatsiriza Kugonjetsa Kwake
16. Kodi mtsogoleri wathu Khristu adzatsiriza bwanji kugonjetsa kwake?
16 Ansembe achifumu onse akadzasindikizidwa chisindikizo, ndiponso nkhosa zikadzadziwika n’kuikidwa kudzanja lamanja la Khristu, Khristuyo adzapita “kukatsiriza kugonjetsa kwake.” (Chiv. 5:9, 10; 6:2) Iye adzatsogolera gulu la nkhondo la angelo amphamvu, ndiponso mwina abale ake oukitsidwa, kuwononga dongosolo lonse la Satana la ndale, nkhondo ndiponso la malonda padziko lapansi. (Chiv. 2:26, 27; 19:11-21) Khristu adzatsiriza kugonjetsa akadzawononga dongosolo loipa la Satanali. Kenako adzaponya Satana ndi ziwanda zake kuphompho kwa zaka 1,000.—Chiv. 20:1-3.
17. Mu Ulamuliro wa Zaka 1,000, kodi Khristu adzatsogolera a nkhosa zina kuti, ndipo kodi tiyenera kutsimikiza mtima za chiyani?
17 Ponena za “khamu lalikulu” la a nkhosa zina amene adzapulumuke chisautso chachikulu, mtumwi Yohane analosera kuti: “Mwanawankhosa, amene ali pambali pa mpando wachifumu, adzawaweta ndi kuwatsogolera ku akasupe a madzi a moyo.” (Chiv. 7:9, 17) Ndithudi, mu Ulamuliro wa Zaka 1000, Khristu adzapitiriza kuthandiza a nkhosa zina, amene amamvera mawu ake, ndipo adzawatsogolera ku moyo wosatha. (Werengani Yohane 10:16, 26-28.) Choncho tiyeni tipitirize kutsatira mokhulupirika Mtsogoleri wathu wokhulupirika mpaka m’dziko lapansi latsopano limene Yehova walonjeza.
Kubwereza
• Fotokozani zimene Khristu anachita ataikidwa kukhala mfumu.
• Kodi Khristu akugwiritsa ntchito ndani potsogolera mpingo?
• Kodi Khristu yemwe ndi Mtsogoleri wathu, adzabweranso m’njira ziti?
• Kodi Khristu adzapitiriza bwanji kutitsogolera m’dziko latsopano?
[Chithunzi patsamba 29]
Kukhalapo kwa Khristu kudzaonekera akamadzawononga dongosolo loipa la Satanali