Yendani Mogwirizana ndi Mzimu Kuti Mupeze Moyo ndi Mtendere
‘Yendani motsatira za mzimu, osati motsatira zofuna za thupi.’—AROMA 8:4.
1, 2. (a) Kodi ndi mavuto otani amene amakhalapo munthu akamayendetsa galimoto uku akuchita zinthu zina? (b) Kodi ndi ngozi yotani imene ingakhalepo munthu akamasokonezedwa mwauzimu?
MKULU wina wa boma ku United States ananena kuti: “Vuto lopanga zinthu zina uku ukuyendetsa galimoto likuwonjezeka chaka ndi chaka.” Anthu ambiri amagwiritsa ntchito foni ya m’manja uku akuyendetsa galimoto. Pa kafukufuku wina, anapeza kuti munthu mmodzi pa anthu atatu amene anafunsidwa ananena kuti anagundidwa kapena kutsala pang’onong’ono kugundidwa ndi galimoto yomwe woyendetsa wake ankalankhula pa foni ya m’manja. Munthu amene amachita zinthu zina uku akuyendetsa galimoto amaoneka ngati katswiri koma zotsatira zake zimakhala zangozi.
2 Woyendetsa galimoto amene akuchita zinthu zina, sangaone zinthu zimene zingachititse ngozi pamsewu. Mofanana ndi zimenezi, nafenso tikhoza kusokonezeka mwauzimu. Tikalola kuti tisiye kuchita zinthu monga Akhristu, zotsatira zake n’zakuti chikhulupiriro chathu chikhoza kusweka ngati ngalawa. (1 Timoteyo 1:18, 19) Mtumwi Paulo anachenjeza Akhristu anzake ku Roma za vuto limeneli. Iye anati: “Pakuti kuika maganizo pa zinthu za thupi kumabweretsa imfa, koma kuika maganizo pa zinthu za mzimu kumabweretsa moyo ndi mtendere.” (Aroma 8:6) Kodi Paulo ankatanthauza chiyani pamenepa? Kodi tingapewe bwanji “kuika maganizo pa zinthu za thupi” koma ‘n’kumaika maganizo pa zinthu za mzimu’?
“Ogwirizana ndi Khristu Yesu Alibe Mlandu”
3, 4. (a) Kodi Paulo analemba zinthu ziti zomwe ankalimbana nazo pa moyo wake? (b) Kodi zimene Paulo anakumana nazo zikutikhudza bwanji?
3 M’kalata yake yopita kwa Akhristu a ku Roma, Paulo analemba zinthu zina zimene ankalimbana nazo. Panali kumenyana pakati pa ziwalo zake ndi maganizo ake. (Werengani Aroma 7:21-23.) Paulo sankanena zimenezi ndi mtima wodzikhululukira ayi. Komanso sikuti ankalankhula poona kuti wasowa mtengo wogwira chifukwa cha uchimo. Ndipotu iye anali Mkhristu wodziwa zinthu ndiponso wodzozedwa ndi mzimu. Iye anatumidwanso kukalalikira “kwa mitundu ina.” (Aroma 1:1; 11:13) Ndiyeno n’chifukwa chiyani Paulo analemba za nkhondo imeneyi?
4 Paulo ankavomereza kuti payekha sakanatha kuchita zonse zimene ankalakalaka pa nkhani yochita chifuniro cha Mulungu. N’chifukwa chiyani anavomereza? Iye anati: “Pakuti onse ndi ochimwa ndipo ndi operewera pa ulemerero wa Mulungu.” (Aroma 3:23) Popeza anali mbadwa ya Adamu, Paulo ankavutika ndi zotsatira za uchimo ndiponso kupanda ungwiro. Tikhoza kumvetsa bwino vuto lakeli chifukwa chakuti nafenso ndife opanda ungwiro ndipo timakhala pa nkhondo imeneyi tsiku lililonse. Komanso pali zinthu zambiri zimene zingatisokoneze n’kutipatutsa pa ‘msewu wolowera kumoyo womwe ndi wopanikiza.’ (Mat. 7:14) Ngakhale zinali choncho, sikuti iye analibe mtengo wogwira. Ifenso sikuti tikusoweratu chochita.
5. Kodi Paulo ananena kuti adzapulumutsidwa ndi ndani?
5 Paulo analemba kuti: “Ndani adzandipulumutse . . . ? Mulungu adzatero kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye wathu.” (Aroma 7:24, 25) Kenako anadzalankhula ndi Akhristu odzozedwa omwe ndi “ogwirizana ndi Khristu.” (Werengani Aroma 8:1, 2.) Yehova amawatenga kukhala ana ake pogwiritsa ntchito mzimu wake woyera ndipo amawaitana kukakhala “olandira cholowa anzake a Khristu.” (Aroma 8:14-17) Mzimu wa Mulungu ndiponso kukhulupirira nsembe ya dipo ya Khristu zimawathandiza kupambana pa nkhondo imene Paulo anaitchula. Choncho iwo “alibe mlandu.” Anamasulidwa ku “chilamulo cha uchimo ndi cha imfa.”
6. N’chifukwa chiyani atumiki onse a Mulungu ayenera kumvetsa tanthauzo la mawu a Paulo?
6 Mawu a Paulowa ankapita kwa Akhristu odzozedwa. Koma zimene ananena pa nkhani ya mzimu wa Mulungu ndiponso za nsembe ya dipo ya Khristu n’zothandiza kwa atumiki onse a Yehova, kaya ali ndi chiyembekezo chopita kumwamba kapena chodzakhala pano padziko lapansi. Ngakhale kuti Paulo anauziridwa kulembera Akhristu odzozedwa malangizo amenewa, m’pofunika kuti atumiki a Mulungu onse adziwe tanthauzo la zimene analemba ndi kuyesetsa kupindula nazo.
Mulungu Anagwiritsira Ntchito Thupi Kuti Atsutse Uchimo
7, 8. (a) Kodi chilamulo chinali “chofooka chifukwa cha thupi” m’njira yotani? (b) Kodi Mulungu wakwanitsa kuchita chiyani pogwiritsa ntchito mzimu wake komanso dipo?
7 Mu chaputala 7 cha buku la Aroma, Paulo anavomereza kuti uchimo ndi wamphamvu kwambiri m’matupi a anthu opanda ungwiro. Koma mu chaputala 8, anafotokoza za mphamvu ya mzimu woyera. Mtumwiyu anafotokoza mmene mzimu wa Mulungu umathandizira Akhristu kulimbana ndi uchimo. Mzimuwo umawathandiza kuti azichita zinthu mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu n’kukhala naye pa ubwenzi wabwino. Paulo ananena kuti pogwiritsira ntchito mzimu wa Mulungu ndi nsembe ya dipo ya Mwana wake, Mulungu wakwanitsa kuchita zimene Chilamulo cha Mose sichikanatha kuchita.
8 Chilamulo, chomwe chinali ndi malamulo ambirimbiri, chinkaimba mlandu anthu ochimwa. Komanso mkulu wa ansembe wa Isiraeli amene ankatumikira motsatira Chilamulo ankakhala wopanda ungwiro, choncho nsembe zauchimo zimene ankapereka zinkakhala zoperewera. Chifukwa cha zimenezi, tingati Chilamulo chinali “chofooka chifukwa cha thupi.” Koma “potumiza Mwana wake m’thupi lofanana ndi lauchimo” n’kumupereka monga dipo “anatsutsa uchimo mwa kugwiritsa ntchito thupi” ndipo pamenepa anachita zinthu zimene “Chilamulo sichinathe kuchita.” Chifukwa cha zimenezi, Akhristu odzozedwa amaonedwa kuti ndi olungama ngati amakhulupirira nsembe ya dipo ya Yesu. Iwo amalimbikitsidwa ‘kuyenda motsatira za mzimu, osati motsatira zofuna za thupi.’ (Werengani Aroma 8:3, 4.) Iwo ayenera kuchita zimenezi mokhulupirika mpaka mapeto a moyo wawo padziko lapansi n’cholinga choti apatsidwe “mphoto ya moyo.”—Chiv. 2:10.
9. Kodi mawu akuti “chilamulo” amene ali pa Aroma 8:2 amatanthauza chiyani?
9 Kuwonjezera pa “Chilamulo,” Paulo ananenanso za “chilamulo cha mzimu” komanso “chilamulo cha uchimo ndi cha imfa.” (Aroma 8:2) Kodi mawu oti “chilamulo” amenewa akutanthauza chiyani? Mawu akuti “chilamulo” m’lembali sakutanthauza malamulo ngati amene anali m’Chilamulo cha Mose. Buku lina linanena kuti: “Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti chilamulo m’lembali amatanthauza zinthu zabwino kapena zoipa zimene anthu amachita ndipo zimakhala ngati lamulo. Lamulo limeneli ndi limene limachititsa kuti munthu azikhala ndi moyo umene ali nawo.”
10. Kodi tinakhala bwanji pansi pa chilamulo cha uchimo ndi imfa?
10 Mtumwi Paulo analemba kuti: “Uchimo unalowera m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzera mwa uchimo, imfayo n’kufalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.” (Aroma 5:12) Popeza tonsefe ndi ana a Adamu, tili pansi pa chilamulo cha uchimo ndi imfa. Nthawi zonse thupi lathu lochimwali limatilimbikitsa kuchita zinthu zimene Mulungu amadana nazo ndipo zotsatira zake ndi imfa basi. M’kalata yake yopita kwa Agalatiya, Paulo ananena kuti zinthu zimenezi ndi “ntchito za thupi.” Kenako anati: “Anthu amene amachita zimenezi sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.” (Agal. 5:19-21) Anthu oterewa akufanana ndi anthu oyenda motsatira zofuna za thupi. (Aroma 8:4) Iwo amangotsogoleredwa ndi thupi lawo lochimwa. Kodi anthu amene amayenda motsatira zofuna za thupi ndi okhawo amene amachita machimo akuluakulu monga dama, kupembedza mafano ndi kukhulupirira mizimu? Ayi. Zili choncho chifukwa chakuti zinthu zina zimene anthu amati ndi mavuto ang’onoang’ono zili m’gulu la ntchito za thupi. Zinthu zake ndi monga nsanje, kupsa mtima, mikangano ndi kaduka. Ndiye ndi ndani amene anganene kuti satsatira zofuna za thupi ngakhale pang’ono?
11, 12. Kodi Yehova wachita chiyani kuti tisakhalenso pansi pa chilamulo cha uchimo ndi imfa, ndipo tingachite chiyani kuti tikhale pa ubwenzi wabwino ndi Iye?
11 N’zosangalatsa kwambiri kuti Yehova wakonza njira yotithandiza kuthana ndi chilamulo cha uchimo ndi imfa. Yesu ananena kuti: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.” Tikamavomereza chikondi cha Mulungu ndiponso kukhulupirira nsembe ya dipo ya Yesu Khristu, tikhoza kumasuka ku mlandu umene tili nawo chifukwa cha uchimo umene tinatengera. (Yoh. 3:16-18) Mofanana ndi Paulo, nafenso tingayamikire ‘Mulungu amene wachita zimenezi kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye wathu.’
12 Zimene zachitikazi zikufanana ndi munthu amene wachiritsidwa matenda oopsa amene akanafa nawo. Kuti tichire bwinobwino tiyenera kuchita zonse zimene dokotala watiuza. Ngakhale kuti kukhulupirira dipo kumatimasula ku chilamulo cha uchimo ndi imfa, anthufe tidakali opanda ungwiro ndipo timachimwa. Pali zinthu zinanso zimene zikufunika kuti tikhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova n’kulandira madalitso ake. Pofotokoza za kukwaniritsa “miyezo yolungama ya Chilamulo,” Paulo ananena za kuyenda motsatira za mzimu.
Kodi Tingayende Bwanji Motsatira za Mzimu?
13. Kodi kuyenda motsatira za mzimu kumatanthauza chiyani?
13 Munthu amene akuyenda, amakhala kuti akulowera kwinakwake ndiponso amakhala ali ndi cholinga. Choncho munthu amene akuyenda motsatira za mzimu amapita patsogolo mwauzimu koma sikuti amakhala wangwiro. (1 Tim. 4:15) Tsiku lililonse tiyenera kuyesetsa mmene tingathere kuyenda kapena kuti kuchita zinthu motsogoleredwa ndi mzimu. Mulungu amakonda kwambiri anthu amene ‘amayenda mwa mzimu.’—Agal. 5:16.
14. Kodi anthu oyenda motsatira “zofuna za thupi” amakhala otani?
14 M’kalata yake yopita kwa Akhristu a ku Roma, Paulo ananenanso za magulu awiri a anthu oganiza mosiyana. (Werengani Aroma 8:5.) Pa lembali mawu akuti thupi sakutanthauza thupi lenilenilo. M’Baibulo mawu akuti “thupi” nthawi zina amagwiritsidwa ntchito potanthauza zilakolako za thupi lathu lochimwa. Thupi lathu lochimwali ndi limene limachititsa kuti pakhale nkhondo imene Paulo ananena ya pakati pa ziwalo zathu ndi maganizo athu. Mosiyana ndi Paulo, anthu amene amayenda “motsatira zofuna za thupi” samenya n’komwe nkhondo imeneyi. M’malo moganizira zimene Mulungu amafuna ndiponso kulandira thandizo limene amapereka, iwo nthawi zambiri “amaika maganizo awo pa zinthu za thupi.” Iwo amangofuna kuchita zofuna za thupi lawo. Koma anthu “otsatira za mzimu” amaika maganizo awo pa “zinthu za mzimu” kapena kuti amalola Yehova kuwatsogolera.
15, 16. (a) Kodi kuika maganizo pa zinthu zabwino kapena zoipa kungakhudze bwanji mmene timaganizira? (b) Kodi anthu ambiri masiku ano amaganiza za chiyani?
15 (Werengani Aroma 8:6.) Munthu asanachite chilichonse kaya chabwino kapena choipa amayamba wachiganizira kaye. Anthu amene amangoganizira zofuna za thupi amayamba kusintha n’kumangoika maganizo awo pa zinthu zathupi. Zolankhula zawo ndiponso zokonda zawo zimangokhala za thupi basi.
16 Kodi anthu ambiri masiku ano amaganizira kwambiri zinthu ziti? Mtumwi Yohane analemba kuti: “Chilichonse cha m’dziko, monga chilakolako cha thupi, chilakolako cha maso ndi kudzionetsera ndi zimene munthu ali nazo pa moyo wake, sizichokera kwa Atate, koma kudziko.” (1 Yoh. 2:16) Zilakolako zimenezi ndi zinthu monga chiwerewere, kufuna kutchuka ndiponso kufuna kukhala ndi zinthu zambiri. Masiku ano, zinthu zimenezi n’zofala kwambiri m’mabuku, m’magazini, m’nyuzipepala, m’mafilimu, m’mapulogalamu a pa TV ndiponso pa Intaneti. Zili choncho chifukwa chakuti zimenezi n’zimene anthu ambiri amakonda kuganizira komanso amazilakalaka. Komatu “kuika maganizo pa zinthu za thupi kumabweretsa imfa” yauzimu panopa komanso imfa yeniyeni m’tsogolomu. N’chifukwa chiyani tikutero? N’chifukwa chakuti “kuika maganizo pa zinthu za thupi ndiko udani ndi Mulungu, popeza thupi siligonjera chilamulo cha Mulungu, ndipotu kunena zoona, silingachigonjere. Choncho, otsatira zofuna za thupi sangakondweretse Mulungu.”—Aroma 8:7, 8.
17, 18. Kodi tingatani kuti tiziyenda motsatira za mzimu, ndipo tikatero tidzapeza madalitso otani?
17 Koma “kuika maganizo pa zinthu za mzimu kumabweretsa moyo ndi mtendere.” Munthu amene amachita zimenezi adzapeza moyo wosatha m’tsogolo ndipo panopa amapeza mtendere wa mumtima komanso amakhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. Kodi tingasonyeze bwanji kuti ‘tikuika maganizo pa zinthu za mzimu?’ Tikamalola Mulungu ndiponso mzimu wake kutitsogolera, maganizo athu amasintha n’kukhala ogwirizana ndi a Mulungu. Tikamatero, tidzakhala ndi maganizo “ogonjera chilamulo cha Mulungu” ndipo ‘tizitsatira’ maganizo ake. Tikakumana ndi mayesero sitidzavutika kusankha zochita. Tidzasankha zinthu mwanzeru ndiponso mogwirizana ndi mzimu.
18 Choncho tiyenera kuyesetsa kuti tiziika maganizo athu pa zinthu za mzimu. Kuti tichite zimenezi tiyenera ‘kukonzekeretsa maganizo athu kuti tigwire ntchito mwamphamvu.’ Tiyeneranso kukhala ndi chizolowezi chochita zinthu zauzimu monga kupemphera, kuwerenga ndi kuphunzira Baibulo, kupezeka pa misonkhano ndiponso kulowa mu utumiki. (1 Pet. 1:13) M’malo molola kuti zinthu za thupi zitisokoneze, tiyenera kuika maganizo athu pa zinthu za mzimu. Tikatero, tidzapitiriza kuyenda motsatira za mzimu. Zotsatira zake n’zakuti tidzapeza madalitso, chifukwa kuika maganizo pa zinthu za mzimu kumabweretsa moyo ndi mtendere.—Agal. 6:7, 8.
Kodi Mungafotokoze?
• Kodi chilamulo chinali cholephera m’njira yotani, nanga Mulungu anachita chiyani?
• Kodi “chilamulo cha uchimo ndi cha imfa” n’chiyani, ndipo tingatani kuti timasuke ku chilamulo chimenechi?
• Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tiziika maganizo pa zinthu za mzimu?
[Zithunzi pamasamba 12, 13]
Kodi mumayenda motsatira zofuna za thupi, kapena motsatira za mzimu?