Yehova Amaona Mavuto Athu N’kutithandiza
“Maso a Yehova ali paliponse. Amayang’ana anthu oipa ndi abwino omwe.”—MIY. 15:3.
1, 2. Kodi mmene Yehova amatiyang’anira ndi zosiyana bwanji ndi makamera amene anthu amaika m’malo osiyanasiyana?
M’MAYIKO ambiri, muli makamera amene amathandiza kuona zimene zikuchitika. Ngati wina wachita ngozi pamsewu n’kuthawa, makamerawa amajambula zonse ndipo zimenezi zimathandiza kuti munthuyo agwidwe. Chifukwa cha makamerawa, zimakhala zovuta kuti munthu amene wapalamula athawe.
2 Koma kodi makamera amenewa akutikumbutsa chiyani za Atate wathu wachikondi Yehova? Baibulo limanena kuti maso a Yehova “ali paliponse.” (Miy. 15:3) Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti iye nthawi zonse amafufuza zimene tikuchita? Kodi Mulungu amatiyang’anitsitsa n’cholinga choti aone zomwe tikulakwitsa n’kutilanga? (Yer. 16:17; Aheb. 4:13) Ayi si choncho. Yehova amatiyang’ana chifukwa amatikonda ndipo amafuna kuti zinthu zizitiyendera bwino.—1 Pet. 3:12.
3. Kodi tikambirana njira 5 ziti zimene Mulungu amasonyezera kuti amatikonda?
3 N’chiyani chingatithandize kumvetsa kuti Yehova amatiyang’ana chifukwa choti amatikonda? Tingamvetse tikaona mmene amachitira zimenezi. Iye amachita zimenezi m’njira izi: (1) Amatichenjeza akaona kuti tayamba kuganiza zinthu zolakwika. (2) Amatipatsa malangizo akaona kuti tayamba kuchita zoipa. (3) Amatitsogolera pogwiritsa ntchito mfundo zopezeka m’Mawu ake. (4) Amatithandiza tikakumana ndi mavuto osiyanasiyana. (5) Komanso amatipatsa madalitso tikamachita zabwino.
MULUNGU WATHU AMATICHENJEZA
4. N’chifukwa chiyani Yehova anachenjeza Kaini kuti ‘uchimo wamyata pakhomo kumudikirira’?
4 Choyamba, tiyeni tione mmene Mulungu amatichenjezera akaona kuti tayamba kuganiza zinthu zolakwika. (1 Mbiri 28:9) Kuti timvetse zimenezi, taganizirani mmene Mulungu anachitira ndi Kaini amene “anapsa mtima kwambiri” ataona kuti Yehova sakusangalala naye. (Werengani Genesis 4:3-7.) Yehova analimbikitsa Kaini kuti ‘asinthe n’kuchita zabwino.’ Iye anamuchenjeza kuti ngati sasintha, ‘uchimo wamyata pakhomo kumudikirira.’ Ndiyeno anamufunsa kuti: “Kodi iweyo suugonjetsa?” Mulungu ankafuna kuti Kaini amvere malangizowa kuti ayambenso kusangalala naye. Iye akanamvera chenjezoli, akanakhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu.
5. Kodi Yehova amatichenjeza bwanji tikayamba kuganiza kapena kulakalaka zinthu zolakwika?
5 Kodi Mulungu amatichenjeza bwanji masiku ano? Yehova amaona zimene zili mumtima mwathu ndipo sitingamubisire zimene tikuganiza komanso kulakalaka. Atate wathu wachikondi amafuna kuti tizichita zinthu zoyenera koma satikakamiza kuti tizichita zimene iye akufuna. Akaona kuti tatenga njira yolakwika amatichenjeza. Kodi amachita bwanji zimenezi? Tikamawerenga Baibulo tsiku ndi tsiku timapeza mfundo zina zomwe zingatithandize kusintha zochita komanso maganizo olakwika. Mabuku athu angafotokozenso za vuto lina limene takhala tikulimbana nalo komanso njira zothetsera vutolo. Ndiponso pa misonkhano ya mpingo, timalandira malangizo a pa nthawi yake.
6, 7. (a) Kodi pali umboni wotani wosonyeza kuti Yehova amakonda mtumiki wake aliyense? (b) Kodi tingatani kuti tipindule ndi chikondi chimene Yehova amatisonyeza?
6 Machenjezo onse amene Yehova amatipatsa ndi umboni woti amakonda Mkhristu aliyense. N’zoona kuti Baibulo, mabuku athu ndiponso malangizo amene timalandira pa misonkhano zimathandiza anthu ambirimbiri. Koma Yehova amafuna kuti mtumiki wake aliyense amvetsere machenjezo amenewa n’cholinga choti azichita zoyenera. Choncho tinganene kuti zonsezi ndi umboni woti Yehova amatikonda.
7 Machenjezo a Yehova angatithandize ngati choyamba titazindikira kuti iye amafuna kuti zinthu zitiyendere bwino. Choncho tiyenera kumvera Mawu ake, n’kusiya kuganizira zimene amadana nazo. (Werengani Yesaya 55:6, 7.) Tikamamvera machenjezo amene amatipatsa, timapewa mavuto osiyanasiyana. Koma kodi Atate wathu wachikondi amatithandiza bwanji tikalakwitsa?
ATATE WATHU WACHIKONDI AMATIPATSA MALANGIZO
8, 9. Kodi malangizo amene Yehova amatipatsa kudzera mwa atumiki ake amasonyeza bwanji kuti amafuna kuti zinthu zizitiyendera bwino? Perekani chitsanzo.
8 Tikadzudzulidwa m’pamene timazindikira kuti Yehova akufuna kuti zinthu zizitiyendera bwino. (Werengani Aheberi 12:5, 6.) N’zoona kuti palibe amene amasangalala akamadzudzulidwa. (Aheb. 12:11) Koma taganizirani zimene wopereka malangizoyo amayamba waganizira. Choyamba, ayenera kudziwa zochita zathu, zomwe zingawononge ubwenzi wathu ndi Yehova Mulungu. Kenako ayenera kuganizira mmene tikumvera, komanso ayenera kukhala wofunitsitsa kutithandiza pogwiritsa ntchito Baibulo kuti tisinthe n’kuyamba kuchita zinthu zokondweretsa Mulungu. Timalemekeza malangizo amenewo chifukwa akuchokera kwa Yehova.
9 Tiyeni tione chitsanzo chosonyeza kuti munthu akamatipatsa malangizo ndi umboni woti Mulungu akutifunira zabwino. M’bale wina asanayambe kutumikira Mulungu ankakonda kuonera zolaula, koma kenako anasiya. Koma ankalimbanabe ndi mtima wofuna kuonera zolaulazo. Izi zinaonekera kwambiri atagula foni yatsopano. (Yak. 1:14, 15) Pogwiritsa ntchito foniyi, ankatsegula malo omwe amaonetsa zolaula pa Intaneti. Tsiku lina akuchita ulaliki wa pa telefoni, anapereka foni yakeyo kwa mkulu wina kuti amuthandize kufufuza maadiresi a anthu. Mkuluyo atayamba kugwiritsa ntchito foniyo, anaona kuti m’baleyo ankatsegula malo oonetsa zolaula. Umenewu unali mwayi woti m’baleyo athandizidwe. Choncho nthawi yomweyo mkuluyo anamulangiza ndipo m’baleyo anamvera malangizowo n’kusiya kuonera zolaulazo. Timathokoza Atate wathu wakumwamba, amene amaona machimo athu obisika ndipo amatithandiza zinthu zisanafike poipa kwambiri.
MFUNDO ZA M’BAIBULO ZIMATITHANDIZA
10, 11. (a) Kodi tingatani kuti tizitsatira malangizo a Mulungu? (b) Kodi banja lina linaona bwanji phindu lotsatira malangizo a Yehova?
10 Wolemba masalimo anaimbira Yehova kuti: “Mudzanditsogolera ndi malangizo anu.” (Sal. 73:24) Nthawi zonse tikafuna malangizo, tiyenera ‘kukumbukira’ Yehova. Tingachite zimenezi pofufuza m’Mawu ake kuti tidziwe maganizo ake pa nkhani zosiyanasiyana. Kutsatira mfundo za m’Baibulo kumatithandiza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu komanso kumatithandiza pa moyo wathu wa tsiku ndi tsiku.—Miy. 3:6.
11 Zimene zinachitikira m’bale wina zimasonyeza kuti Yehova amatitsogolera ndi mfundo zake. M’baleyu ankakhala m’dera lina la mapiri lotchedwa Masbate ku Philippines. Iye ndi mkazi wake ankachita upainiya wokhazikika ngakhale kuti anali ndi banja lalikulu. Kuti azipeza zofunika pa moyo, ankadalira ulimi. Koma munda womwe ankalima unali walendi. Tsiku lina anangodabwa mwiniwake wa malowo akuwauza kuti achoke ndipo asalimenso mundawo. N’chifukwa chiyani anachita zimenezi? Anthu ena anali atawanenera zoipa kwa mwiniwake wa malowo. Koma m’malo modera nkhawa kwambiri za mmene angapezerenso malo ena, m’baleyu anati: “Yehova atipatsa malo. Nthawi zonse amatithandiza.” Ndi zimenedi zinachitika. Patangodutsa masiku ochepa, mwini malo uja anawauza kuti asachoke. Chifukwa chiyani? Iye anaona kuti banjali limatsatira mfundo za m’Baibulo zimene zimawathandiza kuti akhale anthu aulemu komanso kuti azikhala mwamtendere ndi ena. Zimenezi zinamusangalatsa kwambiri ndipo anawawonjezera munda wina. (Werengani 1 Petulo 2:12.) Ndithudi, Yehova amatitsogolera kudzera m’Mawu ake ndipo amatithandiza kupirira tikakumana ndi mavuto.
MULUNGU AMATITHANDIZA KUPIRIRA MAVUTO
12, 13. Kodi n’chiyani chimene chimapangitsa ena kuona ngati Mulungu sakudziwa mavuto awo?
12 Nthawi zina tingakumane ndi mavuto aakulu. Mwina tikuvutika chifukwa cha matenda aakulu, kuzunzidwa kapena kutsutsidwa kwa nthawi yaitali ndi achibale. Enanso sasangalala chifukwa cha zochita za anthu ena mumpingo.
13 Mwachitsanzo, n’kutheka kuti munakhumudwapo ndi mawu amene Mkhristu mnzanu anakulankhulani. Mwina munafika ponena kuti: ‘Zimenezi siziyenera kuchitika m’gulu la Mulungu.’ Komabe mukuona kuti m’bale amene anakukhumudwitsaniyo akupatsidwa maudindo mumpingo ndipo anthu ena amamuona kuti ndi munthu wabwino. Mwina mungamadabwe kuti, ‘zikutheka bwanji zimenezi? Kodi Yehova sakuona? Ngati akuona, bwanji sakuchitapo kanthu?’—Sal. 13:1, 2; Hab. 1:2, 3.
14. Kodi n’chifukwa chiyani nthawi zina tingaone ngati Mulungu sakutithandiza kuthetsa mavuto athu?
14 Yehova ali ndi zifukwa zokwanira zomwe zingamuchititse kuti asachitepo kanthu pa zinthu zina. Mwachitsanzo, inuyo mukhoza kumaganiza kuti mnzanuyo wakulakwirani kwambiri pamene Mulungu sakuona choncho. Iye akhoza kuona kuti muli ndi vuto ndi inuyo. N’kutheka kuti mawu amene munakhumudwa nawowo anali malangizo oti akuthandizeni. M’nkhani imene inafotokoza mbiri ya moyo wa M’bale Karl Klein, yemwe anali wa m’Bungwe Lolamulira, anafotokoza kuti nthawi ina anapatsidwa uphungu ndi M’bale J. F. Rutherford. Tsiku lina, M’bale Rutherford anapatsa M’bale Klein moni wansangala kuti, “Muli bwanji M’bale Klein?” Koma popeza M’bale Klein anakhumudwa chifukwa cha uphunguwo, sanayankhe mosangalala. M’bale Rutherford anadziwa kuti M’bale Klein wakhumudwa, ndipo anamuchenjeza kuti asam’patse malo Mdyerekezi. Kenako M’bale Klein anadzalemba kuti: “Tikasungira chakukhosi m’bale, makamaka amene watipatsa malangizo chifukwa cha udindo umene ali nawo, timam’patsa malo Mdyerekezi.”a
15. Kodi n’chiyani chimene chingatithandize kukhalabe oleza mtima tikakumana ndi mayesero?
15 Koma nthawi zina timataya mtima makamaka tikaona kuti mavuto athu sakutha. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tipirire? Tiyerekeze kuti mukuyendetsa galimoto ndiyeno mwaima chifukwa choti mumsewu muli magalimoto ambiri. Simukudziwa kuti muima nthawi yaitali bwanji. Ngati mungapupulume n’kuganiza zodzera njira ina, mukhoza kusochera n’kukafika mochedwa kusiyana ndi mmene zikanakhalira mukanangodikira pang’ono. N’chimodzimodzinso tikakumana ndi mayesero. Tikaleza mtima n’kutsatira mfundo za m’Baibulo, Yehova adzatithandiza kuti tipirire.
16. Tchulani chifukwa chinanso chimene chingachititse Yehova kuti asachitepo kanthu tikakumana ndi mayesero.
16 Nthawi zina Yehova sangachitepo kanthu tikakumana ndi mayesero chifukwa choti akufuna kuti tiphunzirepo kenakake. (Werengani 1 Petulo 5:6-10.) Koma tisaganize kuti Mulungu ndi amene amachititsa kuti tikumane ndi mayesero. (Yak. 1:13) Mavuto ambiriwa amayambitsa ndi ‘mdani wathu Mdyerekezi.’ Komabe nthawi zina Mulungu angagwiritse ntchito mavuto amene tikukumana nawo potithandiza kuti tikule mwauzimu. Mulungu amaona tikamavutika ndipo ‘amatidera nkhawa.’ Choncho amaonetsetsa kuti mayeserowo angokhalapo “kwa kanthawi” kochepa. Dziwani kuti Yehova amakuderani nkhawa ndipo adzakupatsani mphamvu kuti mupirire mpaka mapeto.—2 Akor. 4:7-9.
MUZIKONDWERETSA MULUNGU KUTI AKUDALITSENI
17. N’chifukwa chiyani Yehova amafufuza mtima wa munthu aliyense?
17 Pali chifukwa chinanso chabwino chimene chimachititsa kuti Mulungu azionetsetsa zimene zikuchitika pa moyo wathu. Kudzera mwa mneneri Haneni, Mulungu anauza Mfumu Asa kuti: “Maso a Yehova akuyendayenda padziko lonse lapansi kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo uli wathunthu kwa iye.” (2 Mbiri 16:9) Mulungu anaona kuti Asa sanali wokhulupirika. Koma inuyo mukapitiriza kuchita zabwino, Yehova ‘adzaonetsa mphamvu zake’ kwa inu.
18. Kodi tizikumbukira chiyani tikamaona ngati palibe amene akuona zabwino zimene tikuchita? (Onani chithunzi patsamba 27.)
18 Mulungu akufuna kuti ‘tiziyesetsa kuchita zabwino’ komanso kuti ‘tizikonda chabwino.’ Tikatero iye ‘adzatikomera mtima.’ (Amosi 5:14, 15; 1 Pet. 3:11, 12) Yehova amaona anthu olungama ndipo amawadalitsa. (Sal. 34:15) Mwachitsanzo, ganizirani za Sifira ndi Puwa omwe anali azamba achiheberi. Pamene Aisiraeli anali ku ukapolo ku Iguputo, azimayi awiriwa anasonyeza kuti ankaopa kwambiri Mulungu osati Farao. Iwo anakana kumvera lamulo la Farao lakuti azipha mwana wamwamuna aliyense wachiheberi akangobadwa. Zikuoneka kuti chifukwa cha chikumbumtima chawo iwo sanaphe anawo. Patapita nthawi, Mulungu anadalitsa Sifira ndi Puwa powapatsa mabanja awoawo. (Eks. 1:15-17, 20, 21) Yehova anaona ntchito zawo zabwino. Nthawi zina tingamaone ngati palibe amene akuona zabwino zimene tikuchita. Koma Yehova amaona ndipo adzatidalitsa.—Mat. 6:4, 6; 1 Tim. 5:25; Aheb. 6:10.
19. Kodi mlongo wina anazindikira bwanji kuti Yehova amaona zabwino zimene tikuchita?
19 Mlongo wina ku Austria anazindikira kuti Mulungu ankaona zabwino zimene ankachita. Popeza kuti mlongoyu anali wa ku Hungary, anapatsidwa mapu a nyumba ya munthu wina wolankhula Chihangare kuti akayambe kuphunzira naye Baibulo. Nthawi yomweyo mlongoyu anapita kwa munthuyo, koma sanam’peze. Anapita mobwerezabwereza kwa chaka ndi hafu, ndipo nthawi zina ankaona kuti m’nyumbamo muli anthu koma palibe amene ankayankha. Akapitako, nthawi zonse ankasiya mabuku, makalata ndi nambala yake ya foni. Tsiku lina atapitanso, mayi wina wansangala anatsegula chitseko n’kumuuza kuti: “Lowani. Ndinawerenga mabuku onse amene munandibweretsera aja ndipo ndakhala ndikukuyembekezerani.” Mayiyu ankadwala ndipo pa nthawi imene sankapezekayo sakanatha kuonana ndi anthu. Kenako anayamba kuphunzira Baibulo. Apatu Mulungu anadalitsa mlongoyu chifukwa cha khama lakelo.
20. Kodi timamva bwanji tikaganizira mfundo yakuti Yehova amatiyang’anitsitsa kuti atithandize?
20 M’nkhaniyi taona kuti Yehova amaona zimene aliyense akuchita ndipo amafufuza zimene zili mumtima mwathu. Komatu zimenezi sizikutanthauza kuti amachita zimenezi kuti atipezere zifukwa n’kutipatsa chilango. Iye sali ngati anthu amene amaika makamera m’malo osiyanasiyana aja. Koma umenewu ndi umboni wosonyeza kuti Mulungu amafuna kuti zinthu zizitiyendera bwino. Zimenezi zimatithandiza kuti tikhale naye pa ubwenzi wabwino.
a Nkhani imene ikufotokoza mbiri ya moyo wa M’bale Klein, ikupezeka mu Nsanja ya Olonda ya Chingelezi ya October 1, 1984.