Yehova Ndi Mulungu Wachikondi
“Mulungu ndiye chikondi.”—1 YOH. 4:8, 16.
1. (a) Kodi khalidwe lalikulu la Mulungu ndi liti? (b) Nanga inuyo mumamva bwanji chifukwa chodziwa zimenezi?
BAIBULO limanena kuti “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yoh. 4:8) N’chifukwa chiyani limanena kuti “Mulungu ndiye chikondi” osati ndi wachikondi? Mawuwa amasonyeza kuti limeneli ndi khalidwe lake lalikulu kwambiri. Iye amachita chilichonse chifukwa cha chikondi. N’zosangalatsa kwambiri kudziwa kuti Mulungu amene analenga zonse ndi wachikondi chachikulu chonchi.
2. Kodi mfundo yoti Yehova amakonda anthu imatitsimikizira chiyani? (Onani chithunzi pamwambapa.)
2 Yehova amakonda kwambiri anthu komanso zinthu zonse zimene analenga. Mfundo imeneyi imatitsimikizira kuti cholinga chake chokhudza anthufe chidzakwaniritsidwa m’njira yabwino kwambiri. Mwachitsanzo, Yehova ‘wakhazikitsa tsiku limene akufuna kudzaweruza m’chilungamo dziko lapansi kumene kuli anthu, kudzera mwa Yesu Khristu amene iye wamuika.’ (Mac. 17:31) Zimenezi sizingalephereke ndipo anthu olungama adzalandira madalitso mpaka kalekale.
KODI ZIMENE ZAKHALA ZIKUCHITIKA ZASONYEZA CHIYANI?
3. Kodi tsogolo lathu linakhala lotani zikanakhala kuti Mulungu satikonda?
3 Kodi tsogolo lathu likanakhala bwanji zikanakhala kuti Mulungu satikonda? Ndiye kuti anthu akanapitiriza kulamulirana motsogoleredwa ndi Satana Mdyerekezi. Choncho zinthu sizikanayenda bwino chifukwa iye ndi wopanda chikondi ndiponso wokwiya kwambiri. (2 Akor. 4:4; 1 Yoh. 5:19; werengani Chivumbulutso 12:9, 12.) Zimenezi zikusonyeza kuti tsogolo lathu likanakhala loipa kwambiri zikanakhala kuti Mulungu satikonda.
4. N’chifukwa chiyani Yehova walola kuti Satana alamulire?
4 Satana anatsutsa zoti Yehova ndi woyenera kulamulira chilengedwe chonse. Anasonyeza kuti iyeyo ndi amene angalamulire bwino ndipo anachititsanso Adamu ndi Hava kuti asamvere zimene Mulungu anawauza. (Gen. 3:1-5) Popeza kuti Yehova ndi wanzeru, analola Satana kuti alamulire kwa nthawi yochepa n’cholinga choti zidziwike kuti zimene ananenazo ndi zabodza. Ndiyeno zimene zakhala zikuchitika m’dzikoli zasonyeza kuti Yehova yekha ndi amene angalamulire bwino osati anthu kapena Satana.
5. Kodi zimene zakhala zikuchitika m’dzikoli zikutsimikizira chiyani?
5 Panopa zinthu m’dzikoli zikuipiraipirabe. Mwachitsanzo, pa zaka 100 zapitazi, anthu opitirira 100 miliyoni aphedwa pa nkhondo. Mulungu ananeneratu kuti zimenezi zidzachitika m’masiku otsiriza ndiponso kuti “anthu oipa ndi onyenga adzaipiraipirabe.” (2 Tim. 3:1, 13) Zimene zakhala zikuchitikazi zikutsimikizira mfundo ya m’Baibulo yakuti: “Ine ndikudziwa bwino, inu Yehova, kuti munthu wochokera kufumbi alibe ulamuliro wowongolera njira ya moyo wake. Munthu amene akuyenda alibe ulamuliro wowongolera mapazi ake.” (Yer. 10:23) Yehova sanalenge anthu kuti azidzilamulira okha.
6. Kodi zimene Mulungu walola kuti zichitike, zatsimikiziranso chiyani?
6 Zimene Mulungu walola kuti zichitikezi zatsimikizira kuti ulamuliro wake wokha ndi umene ungathandize anthu. Posachedwapa Mulungu adzachotsa oipa onse. Pambuyo pa zimenezi, Yehova sadzalekereranso munthu aliyense amene angadzatsutse ulamuliro wake. Izi zidzakhala choncho chifukwa panopo tili ndi umboni wokwanira wosonyeza kuti anthu otsutsa sangalamulire bwino ndipo ayenera kuwonongedwa mwamsanga.
YEHOVA WASONYEZA KALE KUTI NDI WACHIKONDI
7, 8. Kodi Yehova wasonyeza bwanji kuti amatikonda kwambiri?
7 Yehova wakhala akusonyeza chikondi chake m’njira zambiri. Mwachitsanzo, taganizirani za chilengedwe chokongolachi. Pali milalang’amba mabiliyoni ambiri ndipo uliwonse uli ndi mapulaneti komanso nyenyezi zambirimbiri. Imodzi mwa nyenyezi zimene zili mumlalang’amba wathu ndi dzuwa ndipo limathandiza kuti padzikoli pakhale zamoyo. Yehova ndi amene analenga zinthu zonsezi ndipo zimasonyeza kuti iye ndi wamphamvu, wanzeru komanso wachikondi. Choncho tinganenedi kuti “chilengedwere dziko kupita m’tsogolo, makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekera bwino. Makhalidwe a Mulungu amenewa, ngakhalenso mphamvu zake zosatha ndiponso Umulungu wake, zikuonekera m’zinthu zimene anapanga.”—Aroma 1:20.
8 Yehova analenga dzikoli m’njira yoti pakhale zamoyo. Chilichonse padzikoli Mulungu anachipanga n’cholinga choti chizithandiza anthu ndiponso zinyama. Anakonzanso munda wokongola kuti anthu azikhalamo. Anthu amene anawalenga anali angwiro ndipo sakanafa. (Werengani Chivumbulutso 4:11.) Yehova ‘amaperekanso chakudya kwa zamoyo zonse ndipo kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.’—Sal. 136:25.
9. Kodi Yehova amadana ndi chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani tikutero?
9 Yehova ndi wachikondi koma amadana ndi zinthu zoipa. Mwachitsanzo, lemba la Salimo 5:4-6 limanena kuti: “Sindinu Mulungu wokondwera ndi zoipa . . . Mumadana ndi onse ochita zopweteka ena.” Yehova amadananso ndi “munthu wokhetsa magazi ndi wachinyengo.”
ZOIPA ZONSE ZITHA POSACHEDWAPA
10, 11. (a) Kodi anthu oipa zidzawathera bwanji? (b) Kodi Yehova adzadalitsa bwanji anthu olungama?
10 Popeza Yehova ndi wachikondi ndipo amadana ndi zoipa, pa nthawi yake adzachotsa zoipa zonse. Mawu ake amanena kuti: “Ochita zoipa adzaphedwa. Koma oyembekezera Yehova ndi amene adzalandire dziko lapansi. Patsala kanthawi kochepa, woipa sadzakhalakonso. . . . Adani a Yehova adzafanana ndi busa la msipu wobiriwira mochititsa kaso. Iwo adzatha. Adzazimiririka ndi kusanduka utsi.”—Sal. 37:9, 10, 20.
11 Koma Baibulo limalonjezanso kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.” (Sal. 37:29) Anthu olungamawo “adzasangalala ndi mtendere wochuluka.” (Sal. 37:11) Zonsezi zidzatheka chifukwa chakuti Mulungu ndi wachikondi ndipo amafunira zabwino atumiki ake. Paja Baibulo limatiuzanso kuti: “Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.” (Chiv. 21:4) Kunena zoona, anthu amene amadalira Yehova ndiponso kumumvera ali ndi tsogolo labwino kwambiri.
12. Kodi “munthu wosalakwa” amachita zotani?
12 Baibulo limanena kuti: “Ona munthu wosalakwa ndipo yang’anitsitsa munthu wolungama, pakuti tsogolo la munthu ameneyu ndi lamtendere. Koma anthu onse ochimwa adzafafanizidwa. M’tsogolo, anthu oipa adzaphedwa.” (Sal. 37:37, 38) “Munthu wosalakwa” amene akunenedwa palembali amaphunzira za Yehova ndi Yesu ndipo amachita zimene Mulunguyo amafuna. (Werengani Yohane 17:3.) Amakhulupiriranso mawu a pa 1 Yohane 2:17 akuti: “Dziko likupita limodzi ndi chilakolako chake, koma wochita chifuniro cha Mulungu adzakhala kosatha.” Choncho popeza mapeto ali pafupi kwambiri, tiyenera ‘kuyembekezera Yehova ndiponso kusunga njira zake.’—Sal. 37:34.
NJIRA YAIKULU IMENE MULUNGU WASONYEZERA CHIKONDI
13. Tchulani njira yaikulu imene Yehova wasonyezera chikondi.
13 Ngakhale kuti si ife angwiro, tikhoza kumvera Yehova. Tikhozanso kukhala naye pa ubwenzi wolimba chifukwa cha nsembe ya Yesu. Yehova anapereka nsembeyi n’cholinga choti amasule anthu omvera ku ukapolo wa uchimo ndi imfa. (Werengani Aroma 5:12; 6:23.) Popeza kuti Yesu anali wokhulupirika kumwamba kwa zaka zambirimbiri, Yehova sankakayikira kuti adzakhalanso wokhulupirika padziko lapansi. Yehova amakonda kwambiri Mwana wake Yesu ndipo anapwetekedwa mumtima ataona zinthu zopanda chilungamo zimene anthu anamuchitira. Koma zimene Yesu anachita zinasonyeza kuti munthu wangwiro akhoza kukhalabe wokhulupirika kwa Yehova ngakhale atakumana ndi mavuto aakulu kwambiri.
14, 15. Kodi imfa ya Yesu imatithandiza bwanji?
14 Yesu anasonyeza kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira ndipo anakhalabe wokhulupirika mpaka imfa ngakhale kuti anakumana ndi mavuto aakulu. Tiyenera kuyamikira kwambiri chifukwa zimene Yesu anachitazi zinatithandizanso kuti tidzapeze moyo wosatha m’dziko latsopano. Mtumwi Paulo anafotokoza bwino kukula kwa chikondi chimene Yehova ndi Yesu anasonyeza. Iye ananena kuti: “Pamene tinali ofooka, Khristu anafera anthu osapembedza Mulungu pa nthawi yoikidwiratu. Pakuti n’chapatali kuti munthu wina afere munthu wolungama. Zoonadi, mwina wina angalimbe mtima kufera munthu wabwino. Koma Mulungu akuonetsa chikondi chake kwa ife, moti pamene tinali ochimwa, Khristu anatifera.” (Aroma 5:6-8) Nayenso mtumwi Yohane analemba kuti: “Mulungu anatisonyeza ife chikondi chake pakuti anatumiza m’dziko Mwana wake wobadwa yekha kuti tipeze moyo kudzera mwa iye. Chikondi chimenechi chikutanthauza kuti ife sitinakonde Mulungu, koma iye ndi amene anatikonda ndi kutumiza Mwana wake monga nsembe yophimba machimo athu.”—1 Yoh. 4:9, 10.
15 Yesu ananena kuti: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.” (Yoh. 3:16) Ngakhale kuti zinali zopweteka kwambiri, Yehova anaperekabe Mwana wake chifukwa choti amatikonda. Chikondi chakechi sichidzatha mpaka kalekale ndipo mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndatsimikiza mtima kuti imfa, moyo, angelo, maboma, zinthu zimene zilipo, zinthu zimene zikubwera m’tsogolo, mphamvu, msinkhu, kuzama, kapena cholengedwa china chilichonse, sichidzatha kutilekanitsa ndi chikondi cha Mulungu chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.”—Aroma 8:38, 39.
UFUMU WAYAMBA KALE KULAMULIRA
16. Kodi Ufumu wa Mesiya n’chiyani, nanga Mfumu yake ndi ndani?
16 Ufumu wa Mesiya ndi boma limene Mulungu wakhazikitsa ndipo umasonyezanso kuti iye amatikonda kwambiri. Yehova wasankha Yesu kuti akhale mfumu ndipo m’pomveka chifukwa chakuti Mwana wakeyu amakonda kwambiri anthu ndipo ndi woyeneradi kulamulira. (Miy. 8:31) Yehova wasankhanso anthu 144,000 kuti akalamulire ndi Yesu kumwamba. Iwo akamaukitsidwa amakumbukira mmene moyo wa anthu umakhalira. (Chiv. 14:1) Yesu ali padzikoli ankaphunzitsa kwambiri za Ufumu umenewu ndipo anauza ophunzira ake kuti azipemphera kuti: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.” (Mat. 6:9, 10) Tikuyembekezera kwambiri madalitso amene tidzapeze mapemphero amenewa akadzayankhidwa.
17. Kodi ulamuliro wa Yesu ndi wosiyana bwanji ndi wa anthu?
17 Ulamuliro wa Yesu ndi wosiyana kwambiri ndi wa anthu. Tikutero chifukwa chakuti anthu akamalamulira amayambitsa nkhondo zimene zimaphetsa anthu ambirimbiri. Koma Yesu amasamalira bwino anthu ake chifukwa choti amatsanzira makhalidwe a Yehova, makamaka khalidwe la chikondi. (Chiv. 7:10, 16, 17) Paja Yesuyo ananena kuti: “Bwerani kwa ine nonsenu ogwira ntchito yolemetsa ndi olemedwa, ndipo ndidzakutsitsimutsani. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa ine, chifukwa ndine wofatsa ndi wodzichepetsa, ndipo mudzatsitsimulidwa, pakuti goli langa ndi lofewa ndipo katundu wanga ndi wopepuka.” (Mat. 11:28-30) Mawu amenewa ndi olimbikitsa kwambiri.
18. (a) Kodi Ufumu wa Mulungu wakhala ukuchita chiyani kuchokera pamene unakhazikitsidwa? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?
18 Ulosi wa m’Baibulo umasonyeza kuti Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa mu 1914. Kuchokera nthawi imeneyo, pakhala ntchito yosonkhanitsa anthu ena okalamulira limodzi ndi Yesu komanso a “khamu lalikulu” amene adzapulumuke pa mapeto n’kudzakhala m’dziko latsopano. (Chiv. 7:9, 13, 14) Kodi panopa chiwerengero cha khamu lalikululi chafika pati? Nanga anthu amene ali m’gulu limeneli ayenera kuchita chiyani? Nkhani yotsatira idzayankha mafunso amenewa.