N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kupereka kwa Amene Ali ndi Chilichonse?
“Mulungu wathu, tikukuyamikani ndi kutamanda dzina lanu lokongola.”—1 MBIRI 29:13.
1, 2. Kodi Yehova amagwiritsa ntchito bwanji zinthu zimene analenga pothandiza anthu?
YEHOVA amapereka zinthu mowolowa manja moti zonse zimene tili nazo n’zochokera kwa iye. Zinthu zonse zomwe zili padzikoli, monga golide komanso siliva, ndi za Yehova ndipo amazigwiritsa ntchito kuti zinthu zamoyo zipitirize kukhala ndi moyo. (Sal. 104:13-15; Hag. 2:8) M’Baibulo muli nkhani zambiri zimene zimasonyeza mmene Yehova anagwiritsira ntchito zinthu zimene analenga kuti athandize anthu.
2 Mwachitsanzo, Yehova ankapatsa Aisiraeli mana ndi madzi pa zaka 40 zimene anali m’chipululu moti “sanasowe kanthu.” (Eks. 16:35; Neh. 9:20, 21) Pa nthawi inanso, Yehova anagwiritsa ntchito mneneri Elisa kuti achulukitse mafuta ochepa amene mkazi wina wamasiye anatsala nawo. Zimene Mulungu anamuchitirazi zinamuthandiza kuti apeze ndalama zobwezera ngongole zake komanso zoti iyeyo ndi mwana wake azigwiritsa ntchito. (2 Maf. 4:1-7) Yehova anagwiritsanso ntchito Yesu kuti athandize anthu kupeza chakudya komanso ndalama.—Mat. 15:35-38; 17:27.
3. Kodi munkhaniyi tikambirana chiyani?
3 Yehova ali ndi zinthu zambiri zimene angazigwiritse ntchito kuti zinthu ziziyenda bwino padzikoli. Koma amafunabe kuti atumiki ake azipereka zinthu zawo kuti zizithandiza pa ntchito ya gulu lake. (Eks. 36:3-7; werengani Miyambo 3:9.) N’chifukwa chiyani Yehova amafuna kuti tizimupatsa zinthu zathu zamtengo wapatali? Kodi atumiki a Mulungu akale ankapereka zinthu ziti pothandiza anthu amene Yehova ankawagwiritsa ntchito? Nanga masiku ano gulu la Yehova limagwiritsa ntchito bwanji ndalama zimene zimaperekedwa? Tikambirana mayankho a mafunsowa munkhaniyi.
N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUPEREKA KWA YEHOVA?
4. Kodi timasonyeza chiyani tikamapereka zinthu zathu kwa Yehova?
4 Timapereka zinthu kwa Yehova chifukwa chomukonda komanso kuyamikira zimene watichitira. Tikaganizira zonse zimene Yehova watichitira, timakhudzidwa kwambiri. Mfumu Davide anafotokoza zinthu zimene zinkafunika kuti amange kachisi. Pofotokoza zinthuzi ananena kuti zonse zimene tili nazo n’zochokera kwa Yehova choncho chilichonse chimene tingapereke n’chochokera kwa iyeyo.—Werengani 1 Mbiri 29:11-14.
5. Kodi Malemba amasonyeza bwanji kuti kupereka zinthu mowolowa manja ndi mbali yofunika ya kulambira kwathu?
5 Kupereka zinthu kwa Yehova ndi mbali ya kulambira kwathu. M’masomphenya, mtumwi Yohane anamva atumiki a Yehova kumwamba akunena kuti: “Ndinu woyenera, inu Yehova Mulungu wathu wamphamvu, kulandira ulemerero ndi ulemu, chifukwa munalenga zinthu zonse, ndipo mwa kufuna kwanu, zinakhalapo ndipo zinalengedwa.” (Chiv. 4:11) Tikamapatsa Yehova zinthu zabwino kwambiri, timakhala tikumupatsa ulemerero ndi ulemu womuyenerera. Yehova anauza Mose kuti alamule Aisiraeli kuti azikaonekera kwa Yehova pa zikondwerero zitatu zimene zinkachitika chaka chilichonse. Aisiraeliwo sankayenera kupita kukalambira Yehova “chimanjamanja.” (Deut. 16:16) Masiku anonso, kupereka zinthu mowolowa manja pothandiza pa ntchito ya gulu la Yehova ndi mbali yofunika ya kulambira kwathu.
6. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kupatsa kumatithandiza? (Onani chithunzi choyambirira.)
6 Kupereka zinthu kumatithandiza. Ndi bwino kuti tikhale ndi mtima wopatsa osati kumangofuna kuti anthu azitipatsa zinthu. (Werengani Miyambo 29:21.) Mwachitsanzo, mwana wamng’ono angapatse makolo ake mphatso imene wagula ndi kandalama kamene makolowo anamupatsa. Makolowo akhoza kuyamikira kwambiri. Kapena mwina wachinyamata amene adakali pakhomo ndipo akuchita upainiya angapatse makolo ake ndalama zinazake pothandiza kugula zinthu zina zofunika. N’kutheka kuti makolowo sayembekezera kuti mwana wawo azichita zimenezi. Koma akhoza kulandira mphatsoyi chifukwa chodziwa kuti ndi njira imene mwanayo akuyamikirira zimene amamuchitira. Nayenso Yehova amadziwa kuti kupereka zinthu zathu zamtengo wapatali kumatithandiza.
ATUMIKI AKALE ANKAPEREKA KWA MULUNGU
7, 8. Kodi anthu a Yehova akale anapereka bwanji chitsanzo chabwino pa nkhani yopereka zinthu zawo (a) pothandiza pa ntchito zapadera? (b) pothandiza ntchito ya Mulungu m’njira zina?
7 M’Malemba muli zitsanzo zambiri za anthu amene anapereka zinthu zawo kwa Yehova. Nthawi zina anthu a Yehova ankapereka zinthu pofuna kuthandiza pa ntchito zapadera. Mwachitsanzo, Mose anapempha anthu kuti apereke zinthu pothandiza kumanga chihema, pomwe Davide anapempha anthu kuti apereke zinthu pothandiza kumanga kachisi. (Eks. 35:5; 1 Mbiri 29:5-9) Pa nthawi ya Mfumu Yehoasi, ansembe anagwiritsa ntchito zinthu zimene anthu anapereka pokonza zimene zinawonongeka panyumba ya Yehova. (2 Maf. 12:4, 5) Nawonso Akhristu oyambirira atamva kuti abale awo akuvutika ndi njala, “anatsimikiza mtima kutumiza thandizo lililonse limene akanatha kwa abale okhala ku Yudeya.”—Mac. 11:27-30.
8 Atumiki ena anapereka zinthu pothandiza anthu amene ankatsogolera pa ntchito ya Yehova. Mogwirizana ndi Chilamulo cha Mose, Alevi sankalandira cholowa ngati mmene zinalili ndi mafuko ena. M’malomwake, Aisiraeli ankawapatsa chakhumi, kapena kuti gawo limodzi pa magawo 10 a zinthu zawo, n’cholinga choti Aleviwo aziika maganizo onse pa ntchito yawo yakuchihema. (Num. 18:21) Panalinso akazi amene ankatumikira Yesu ndi atumwi ake “pogwiritsa ntchito chuma chawo.”—Luka 8:1-3.
9. Kodi atumiki akale ankapeza kuti zinthu zimene ankapereka?
9 Koma zinthu zimene anthuwo ankapereka ankazipeza m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, zinthu zambiri zimene Aisiraeli ankapereka pothandiza kumanga chihema m’chipululu ziyenera kuti anazitenga pochoka ku Iguputo. (Eks. 3:21, 22; 35:22-24) Mu nthawi ya atumwi, Akhristu ena ankagulitsa chuma chawo, monga minda ndi nyumba, ndipo ankabweretsa ndalama zimene anapezazo kwa atumwi. Ndiyeno atumwiwo ankapereka ndalamazo kwa anthu ena kuti ziwathandize. (Mac. 4:34, 35) Koma Akhristu ena ankaika ndalama zinazake pambali n’cholinga choti azipereka pothandiza pa ntchito ya Mulungu. (1 Akor. 16:2) Choncho anthu onse, kaya olemera kapena osauka, ankatha kupereka zinthu zawo.—Luka 21:1-4.
ZIMENE TIMAPEREKA MASIKU ANO
10, 11. (a) Kodi tingatsanzire bwanji atumiki a Yehova akale amene ankapereka mowolowa manja? (b) Kodi mumaona bwanji mwayi wanu wothandiza pa ntchito za Ufumu?
10 Masiku anonso, tingapemphedwe kuti tipereke ndalama pothandiza pa ntchito zapadera. Mwachitsanzo, mwina mpingo wanu ukukonzekera kuti umange Nyumba ya Ufumu. Kapena mwina Nyumba ya Ufumu yanu ikukonzedwa. Apo ayi, tikhoza kuuzidwa kuti pakufunika ndalama zoti ofesi ya nthambi ya m’dziko lathu ikonzedwe, msonkhano waukulu uchitike kapena kuti abale athu amene akumana ndi ngozi athandizidwe. Timaperekanso ndalama zothandiza kuti abale ndi alongo amene amagwira ntchito kulikulu lathu kapena kumaofesi a nthambi azisamaliridwa. Zopereka zathu zimathandizanso posamalira amishonale, apainiya apadera ndiponso oyang’anira madera ndi akazi awo. Mpingo wanu uyenera kuti umaperekanso ndalama mwezi uliwonse pothandiza pa ntchito yomanga Malo a Misonkhano komanso Nyumba za Ufumu padziko lonse.
11 Aliyense wa ife angapereke ndalama pothandiza pa ntchito ya Yehova m’masiku otsiriza ano. Ambirife timapereka ndalama popanda ena kudziwa. Timaponya ndalamazo m’mabokosi a ku Nyumba ya Ufumu kapena timapereka kudzera pawebusaiti yathu ya jw.org. Tikhoza kuganiza kuti ndalama zochepa zimene timapereka n’zosathandiza kwenikweni. Komatu ndalama za gulu lathu zimachokera kwa anthu ambiri amene amapereka zochepa, osati kwa anthu ochepa amene amapereka zambiri. Abale athu osauka ali ngati a ku Makedoniya omwe anali pa “umphawi wadzaoneni” koma anachonderera kuti akhale ndi mwayi wopereka nawo ndipo anapereka mowolowa manja.—2 Akor. 8:1-4.
12. Kodi gulu lathu limachita chiyani pofuna kugwiritsa ntchito moyenera ndalama zimene zaperekedwa?
12 Abale a m’Bungwe Lolamulira amapemphera ndiponso kuganizira kwambiri mmene angagwiritsire ntchito ndalama za gulu, n’cholinga choti achite zinthu mokhulupirika komanso mwanzeru. (Mat. 24:45) Iwo amapanga bajeti ndipo amaitsatira pogwiritsa ntchito ndalamazo. (Luka 14:28) Kale, atumiki amene ankayang’anira ndalama za gulu la Yehova ankaonetsetsa kuti ndalamazo zikugwira ntchito yoyenera. Mwachitsanzo, Ezara anatenga zinthu zimene mfumu ya Perisiya inapereka n’kupita nazo ku Yerusalemu. Mfumuyo inapereka golide, siliva ndiponso zinthu zina ndipo zonse pamodzi mtengo wake panopa ungakwane madola a ku United States okwana 100 miliyoni. Ezara ankaona kuti zoperekazi ndi za Yehova ndipo anaonetsetsa kuti zikhale zotetezeka pa ulendowo, womwe unali woopsa. (Ezara 8:24-34) Mtumwi Paulo anatenga ndalama zimene abale anapereka kuti zikathandize Akhristu a ku Yudeya. Iye anaonetsetsa kuti anthu amene anakapereka ndalamazo ‘azisamalire moona mtima, osati pamaso pa Yehova pokha ayi, komanso pamaso pa anthu.’ (Werengani 2 Akorinto 8:18-21.) Masiku ano gulu lathu limatsanzira Ezara ndi Paulo poonetsetsa kuti zopereka zikugwiritsidwa ntchito moyenera.
13. Kodi tiyenera kuona bwanji zimene gulu lachita kuti lichepetse ndalama zimene limagwiritsa ntchito?
13 Banja likhoza kusintha zinthu zina ndi zina kuti lisamawononge ndalama zambiri kuposa zimene limapeza. Likhozanso kuchita zimenezi kuti lizikhala moyo wosalira zambiri n’cholinga choti liwonjezere zimene limachita potumikira Yehova. Nalonso gulu la Yehova limachita zimenezi. M’zaka zapitazi, gulu linayamba kuchita zinthu zina zatsopano. Nthawi zina, zimenezi zinkachititsa kuti ndalama zimene zinkagwiritsidwa ntchito zikhale zambiri kuposa zimene zinkaperekedwa. Choncho panopa gulu limayesetsa kupeza njira zochepetsera ndalama zimene limagwiritsa ntchito pa zinthu zosiyanasiyana n’cholinga choti ndalama zimene mumapereka zizigwiritsidwa ntchito moyenera.
ZOPEREKA ZANU ZIMATHANDIZA KWAMBIRI
14-16. (a) Kodi zopereka zanu zimathandiza pa zinthu ziti m’gulu la Yehova? (b) Kodi inuyo mwathandizidwa bwanji ndi zimene gulu likuchita?
14 Anthu ambiri amene anayamba kalekale kutumikira Yehova amanena kuti panopa tili ndi chakudya chauzimu chambiri kuposa kale lonse. Mwachitsanzo, tili ndi webusaiti ya jw.org komanso pulogalamu ya JW Broadcasting. Nalonso Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika likupezeka m’zilankhulo zambiri. Mu 2014 ndi 2015, m’masitediyamu 14 akuluakulu padzikoli munachitikira msonkhano wamayiko wakuti “Pitirizani Kufunafuna Ufumu wa Mulungu Choyamba.” Anthu amene anapezeka pamisonkhanoyi anasangalala kwambiri.
15 Anthu ambiri masiku ano akuyamikira zimene gulu la Yehova likuchita. Mwachitsanzo, pofotokoza za JW Broadcasting, banja lina limene likutumikira m’dziko lina la ku Asia linalemba kuti: “Timatumikira m’tauni ina yaing’ono. Ndiye nthawi zina timamva ngati tili kutali ndi gulu la Yehova ndipo n’zosavuta kuiwala zimene gululi likuchita padziko lonse. Koma tikangoonera pulogalamu ya JW Broadcasting timakumbukira kuti tili m’gulu lapadziko lonse la abale ndi alongo. Abale ndi alongo akunoko amakondanso kwambiri pulogalamu imeneyi. Nthawi zambiri amanena kuti akaonera pulogalamuyi amamva kuti ali pafupi ndi abale a m’Bungwe Lolamulira ndipo amanyadira kwambiri kuti ali m’gulu la Mulungu.”
16 Panopa, padziko lonse pali Nyumba za Ufumu zokwana 2,500 zimene zikumangidwa kapena kukonzedwa. Abale ndi alongo amumpingo wina wa ku Honduras atayamba kugwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu yawo yatsopano analemba kuti: “Tikusangalala kwambiri kukhala m’banja la Yehova komanso kukhala pa ubale ndi Akhristu anzathu padziko lonse. Zimenezi n’zimene zathandiza kuti tikhale ndi Nyumba ya Ufumu imene tinkailakalaka kwa nthawi yaitali.” Anthu ambiri amanenanso zinthu ngati zimenezi akalandira Baibulo ndi mabuku ena m’chilankhulo chawo, akathandizidwa pambuyo pokumana ndi ngozi zadzidzidzi kapena akaona ubwino wolalikira m’malo opezeka anthu ambiri.
17. Kodi zimene gulu likuchita masiku ano zikusonyeza bwanji kuti Yehova ndi amene akulithandiza?
17 Anthu ena amadabwa kuti timagwira ntchito zambiri chonchi pongodalira ndalama zimene anthu amapereka mwakufuna kwawo. Bwana wa kampani ina yaikulu anakaona malo athu ena osindikizira mabuku. Iye anadabwa kwambiri kuti ntchito yonse imagwiridwa ndi anthu ongodzipereka ndipo ndalama zake sitipeza pogulitsa zinthu kapena kupemphetsa, koma ndi zimene anthu amapereka mwa kufuna kwawo. Iye ananena kuti zimene tikuchita zimaoneka ngati zosatheka. Nafenso timaona kuti zimene ananenazi n’zoona chifukwa sitingazikwanitse patokha koma mothandizidwa ndi Yehova.—Yobu 42:2.
MADALITSO AMENE TIMAPEZA TIKAMAPEREKA KWA YEHOVA
18. (a) Kodi chimachitika n’chiyani tikakhala ndi mtima wopatsa? (b) Kodi tingaphunzitse bwanji ana athu komanso anthu atsopano kuti azipereka kwa Yehova?
18 Yehova watilemekeza kwambiri potipatsa mwayi wothandiza pa ntchito yaikulu imene gulu lake likugwira masiku ano. Iye walonjeza kuti anthu amene amapereka zinthu zawo kuti zithandize pa ntchito za Ufumu adzadalitsidwa. (Mal. 3:10) Yehova ananeneratu kuti munthu amene amapereka mowolowa manja, zinthu zidzamuyendera bwino. (Werengani Miyambo 11:24, 25.) Munthu wopatsa amasangalalanso kwambiri chifukwa Baibulo limanena kuti: “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.” (Mac. 20:35) Choncho zolankhula komanso zochita zathu ziyenera kuthandiza ana athu komanso anthu atsopano kuzindikira zimene angachite kuti azipereka kwa Yehova ndiponso madalitso amene angalandire.
19. Kodi nkhaniyi yakulimbikitsani bwanji?
19 Chilichonse chimene tili nacho n’chochokera kwa Yehova. Choncho tikamamupatsa zinthu zimenezi timasonyeza kuti timamukonda komanso timayamikira zimene amatichitira. (1 Mbiri 29:17) Baibulo limanena kuti anthu amene anapereka zinthu zothandiza pomanga kachisi “anasangalala chifukwa cha nsembe zaufulu zimene anapereka, pakuti anapereka nsembezo kwa Yehova ndi mtima wathunthu.” (1 Mbiri 29:9) Tiyeni nafenso tizipereka zinthu zimene Yehova watipatsa ndipo tikamatero tidzakhala osangalala kwambiri.