Kodi Tiyenera Kukonda Ndani Kuti Tikhale Osangalala?
“Odala ndi anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.”—SAL. 144:15.
1. N’chifukwa chiyani tinganene kuti tikukhala mu nthawi yapadera?
TIKUKHALA mu nthawi yapadera kwambiri. Mogwirizana ndi ulosi wa m’Baibulo, Yehova akusonkhanitsa “khamu lalikulu la anthu . . . lochokera m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi chinenero chilichonse.” Anthu amene asonkhanitsidwa ndi “mtundu wamphamvu” wa anthu osangalala oposa 8 miliyoni, omwe “akumuchitira [Mulungu] utumiki wopatulika usana ndi usiku.” (Chiv. 7:9, 15; Yes. 60:22) Apa zikuonekeratu kuti masiku ano pali anthu ambiri amene amakonda Mulungu komanso anzawo.
2. Kodi anthu amene satumikira Mulungu amakonda zinthu ziti? (Onani chithunzi choyambirira.)
2 Komatu Malemba ananeneratu kuti masiku otsiriza ano, anthu amene satumikira Mulungu adzakhala okonda zinthu zongowakomera okha. Mtumwi Paulo analemba kuti: ‘M’masiku otsiriza anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama ndiponso okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu.’ (2 Tim. 3:1-4) Zinthu zimene anthuwa amakonda n’zosemphana kwambiri ndi zimene Akhristu amayenera kukonda. Anthu amene amangofufuza zinthu zongowakomera okha amaganiza kuti akhala osangalala koma zoona zake n’zakuti sasangalala. Ndipo anthu oterewa ndi amene amachititsa kuti nthawi yathuyi ikhale “yovuta.”
3. Kodi munkhaniyi tikambirana chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani?
3 Paulo anazindikira kuti Akhristu akhoza kusokonezeka chifukwa chokhala m’dziko limene anthu ambiri amakonda zinthu zongowakomera okha. Choncho anachenjeza Akhristu kuti ‘azipewa’ anthu amenewa. (2 Tim. 3:5) Komatu n’zosatheka kuwapeweratu. Ndiye kodi tingapewe bwanji maganizo a anthu a m’dzikoli n’kumayesetsa kuchita zinthu zosangalatsa Yehova? Tiyeni tione kusiyana pakati pa zimene anthu a Mulungu ayenera kukonda ndi zimene anthu otchulidwa pa 2 Timoteyo 3:2-4 amakonda. Zimenezi zitithandiza kudzifufuza pa nkhaniyi, n’kutsimikizira kuti tikukonda zinthu zimene zingatithandize kukhala osangalala.
TIZIKONDA MULUNGU KUPOSA MMENE TIMADZIKONDERA TOKHA
4. N’chifukwa chiyani tinganene kuti si kulakwa kudzikonda moyenerera?
4 Mtumwi Paulo analemba kuti: “Anthu adzakhala odzikonda.” Kodi n’kulakwa kudzikonda? Ayi. Kudzikonda moyenerera n’kothandiza. Yehova anatilenga m’njira yoti tizidzikonda. N’chifukwa chake Yesu ananena kuti: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.” (Maliko 12:31) Choncho ngati sitidzikonda, sitingathe kukonda anzathu. Baibulo limanenanso kuti: “Amuna akonde akazi awo monga matupi awo. Amene amakonda mkazi wake amadzikonda yekha, pakuti palibe munthu anadapo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulikonda.” (Aef. 5:28, 29) Choncho kudzikonda moyenerera si kulakwa.
5. Kodi mungafotokoze bwanji anthu amene amadzikonda mopitirira malire?
5 Kudzikonda kotchulidwa pa 2 Timoteyo 3:2 si kudzikonda moyenerera koma mopitirira malire. Anthu amene amadzikonda chonchi amadziganizira kwambiri kuposa mmene amayenera kuchitira. (Werengani Aroma 12:3.) Iwo amangoganizira za iwowo nthawi zonse ndipo saganizira anthu ena. Zinthu zikalakwika amaloza chala ena m’malo movomereza kulakwa kwawo. Buku lina lofotokoza za Baibulo limanena kuti anthu odzikonda amakhala ngati ‘kanyama kotchedwa chisoni. Kanyamaka kamatha kudzipinda n’kumaoneka ngati mpira. Kamadzipinda m’njira yoti kazingogunda mbali ya thupi lake yomwe ili ndi ubweya wofewa n’kumamva kutenthera, koma zinthu zina zonse zizigunda mbali yomwe ili ndi minga zokhazokha.’ Kunena zoona, anthu odzikonda ngati kanyamaka sakhala osangalala.
6. Kodi anthu okonda Mulungu amakhala ndi makhalidwe ati?
6 Paulo anayamba ndi kutchula anthu odzikonda asanatchule makhalidwe ena oipa amene anthu angakhale nawo m’masiku otsiriza. Akatswiri ena a Baibulo amanena kuti iye anachita zimenezi chifukwa choti makhalidwe enawo amayamba ndi kudzikonda. Mosiyana ndi zimenezi, anthu amene amakonda Mulungu amakhala ndi makhalidwe abwino. Baibulo limasonyeza kuti munthu amene amakonda Mulungu amakhala wachimwemwe, wamtendere, woleza mtima, wokoma mtima, wabwino, wachikhulupiriro, wofatsa ndiponso wodziletsa. (Agal. 5:22, 23) Wolemba masalimo ananena kuti: “Odala [kapena kuti osangalala] ndi anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.” (Sal. 144:15) Yehova ndi Mulungu wachimwemwe ndipo amafuna kuti anthu ake azikhalanso osangalala. Mosiyana ndi anthu odzikonda amene amangofuna kuti zinthu ziziwayendera iwowo basi, atumiki a Yehova amasangalala akamadzipereka pothandiza anthu ena.—Mac. 20:35.
7. Kodi ndi mafunso ati amene angatithandize kudziwa ngati timakonda Mulungu ndi mtima wonse?
7 Kodi tingadziwe bwanji ngati tayamba kudzikonda kwambiri kuposa Mulungu? Taganizirani malangizo amene akupezeka palemba la Afilipi 2:3, 4. Lembali limati: “Musachite chilichonse ndi mtima wokonda mikangano kapena wodzikuza, koma modzichepetsa, ndi kuona ena kukhala okuposani. Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.” Tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimatsatira malangizo amenewa? Kodi ndimayesetsa ndi mtima wonse kuchita zimene Mulungu amafuna? Nanga kodi ndimayesetsa kuthandiza anthu ena mumpingo komanso mu utumiki?’ Kuchita zimenezi si kophweka chifukwa pamafunika khama komanso kudzimana zinthu zina. Komatu palibe zimene zingatithandize kukhala osangalala kuposa kudziwa kuti tikusangalatsa Wolamulira chilengedwe chonse.
8. Kodi anthu ena achita chiyani chifukwa chokonda Mulungu?
8 Chifukwa chokonda Mulungu, anthu ena asankha kuti asamagwire ntchito yapamwamba n’cholinga choti azichita zambiri pomutumikira. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Ericka yemwe amakhala ku United States ndipo ndi dokotala. M’malo moyesetsa kukhala dokotala wotchuka, iye anayamba upainiya wokhazikika ndipo wakhala ndi mwayi wotumikira Yehova limodzi ndi mwamuna wake m’mayiko ambiri. Iye ananena kuti: “Takumana ndi zinthu zosangalatsa potumikira m’gawo la chilankhulo china ndipo tapeza anzathu ochuluka. Zonsezi zathandiza kuti tikhale ndi moyo wosangalala kwambiri. Ndimagwirabe ntchito monga dokotala koma ndimagwiritsa ntchito nthawi ndiponso mphamvu zanga zambiri pothandiza anthu kudziwa Yehova komanso pothandiza abale ndi alongo mumpingo wathu. Izi zimandithandiza kukhala wosangalala komanso kuona kuti ndikugwiritsa ntchito moyo wanga m’njira yoyenera.”
TIZISUNGA CHUMA KUMWAMBA OSATI PADZIKO LAPANSI
9. N’chifukwa chiyani tinganene kuti anthu okonda ndalama sakhala osangalala?
9 Paulo analembanso kuti anthu adzakhala “okonda ndalama.” Zaka zingapo zapitazo, mpainiya wina ku Ireland analankhula ndi bambo winawake zokhudza Mulungu. Bamboyo anatulutsa kachikwama kenakake ndipo anatengamo ndalama n’kunena kuti, “Uyu ndiye mulungu wanga.” N’zoona kuti anthu ambiri sanganene mawu ngati amenewa. Komabe amakonda kwambiri ndalama komanso zinthu zimene angagule. Koma Baibulo limachenjeza kuti: “Munthu wokonda siliva sakhutira ndi siliva, ndipo wokonda chuma sakhutira ndi phindu limene amapeza.” (Mlal. 5:10) Anthu okonda ndalama sakhutira ndi zimene ali nazo ndipo akamayesetsa kuti alemere, ‘amadzibweretsera zopweteka zambiri.’—1 Tim. 6:9, 10.
10. Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani ya chuma ndi umphawi?
10 N’zoona kuti tonsefe timafunikira ndalama. Zili choncho chifukwa zimatiteteza m’njira zina. (Mlal. 7:12) Koma funso n’lakuti, Kodi n’zotheka munthu amene amangopeza zofunika pa moyo zokha kukhaladi wosangalala? Inde. (Werengani Mlaliki 5:12.) Aguri mwana wa Yake anapempha Mulungu kuti: “Musandipatse umphawi kapena chuma. Ndidye chakudya chimene ndikufunika kudya.” M’pomveka kuti sankafuna kukhala mphawi wadzaoneni. Iye anafotokoza kuti sankafuna zimenezi chifukwa zikhoza kumuchititsa kuti abe n’kunyozetsa Mulungu. Koma n’chifukwa chiyani sankafuna kukhala ndi chuma? Iye anapitiriza kuti: “Kuti ndisakhute kwambiri n’kukukanani kuti: ‘Kodi Yehova ndani?’” (Miy. 30:8, 9) Mwina inuyo mwaonapo anthu amene amadalira kwambiri chuma chawo m’malo modalira Mulungu.
11. Kodi Yesu anapereka malangizo otani okhudza ndalama?
11 N’zosatheka kuti anthu amene amakonda ndalama asangalatse Mulungu. Paja Yesu ananena kuti: “Kapolo sangatumikire ambuye awiri, pakuti adzadana ndi mmodzi ndi kukonda winayo, kapena adzakhulupirika kwa mmodzi ndi kunyoza winayo. Simungathe kutumikira Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.” Ndipo asananene zimenezi ananena kuti: “Lekani kudziunjikira chuma padziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri zimawononga, ndiponso pamene mbala zimathyola ndi kuba. Koma unjikani chuma chanu kumwamba, kumene njenjete kapena dzimbiri sizingawononge, ndiponso kumene mbala sizingathyole n’kuba.”—Mat. 6:19, 20, 24.
12. Kodi kukhala moyo wosalira zambiri kungatithandize bwanji potumikira Mulungu? Perekani chitsanzo.
12 Anthu ambiri amaona kuti akamakhala moyo wosalira zambiri amasangalala komanso amakhala ndi nthawi yambiri yotumikira Yehova. M’bale wina dzina lake Jack, yemwe amakhala ku United States, anagulitsa nyumba ndiponso bizinezi yake n’cholinga choti azichita upainiya limodzi ndi mkazi wake. Iye anati: “Sizinali zophweka kuti tigulitse nyumba ndiponso malo athu okongola kwambiri. Koma kwa zaka zambiri ndinkaweruka kuntchito n’kubwera nditakhumudwa kwambiri chifukwa cha mavuto akuntchitoko. Mkazi wanga, yemwe anali mpainiya wokhazikika, nthawi zonse ankakhala wosangalala. Iye ankakonda kundiuza kuti, ‘Bwana wanga ndi wabwino kuposa mabwana onse.’ Popeza kuti panopa nanenso ndikuchita upainiya, tonse tikugwirira ntchito Yehova.”
13. Kodi tingatani kuti tidziwe mmene timaonera ndalama?
13 Kuti tidziwe mmene timaonera ndalama, tingachite bwino kuyankha moona mtima mafunso awa: ‘Kodi zimene Baibulo limanena pa nkhani ya ndalama ndimazikhulupirira ndi mtima wonse ndiponso kuzitsatira? Kodi ndimaona kuti kupeza ndalama ndi kofunika kwambiri pa moyo wanga? Nanga ndimaona kuti chuma n’chofunika kwambiri kuposa ubwenzi wanga ndi Yehova kapena ndi anthu? Kodi ndimadalira Yehova kuti azindisamalira?’ Sitiyenera kukayikira kuti tikamamudalira sadzatigwiritsa mwala ngakhale pang’ono.—Mat. 6:33.
TIZIFUNAFUNA YEHOVA OSATI ZOSANGALATSA
14. Kodi tiyenera kuona bwanji zosangalatsa?
14 Mogwirizana ndi zimene Baibulo linalosera, anthu ambiri masiku ano ndi “okonda zosangalatsa.” Monga taonera kale, kudzikonda moyenerera komanso kukhala ndi ndalama si kulakwa. Chimodzimodzinso ndi kuchita zosangalatsa. Sikuti Yehova amafuna kuti tizidzimana chilichonse chosangalatsa. Paja Baibulo limalimbikitsa anthu okhulupirika kuti: “Pita ukadye chakudya chako mokondwera ndi kumwa vinyo wako ndi mtima wosangalala.”—Mlal. 9:7.
15. Kodi lemba la 2 Timoteyo 3:4 limanena za anthu amene amakonda zosangalatsa m’njira iti?
15 Lemba la 2 Timoteyo 3:4 limanena za anthu amene sakonda Mulungu koma amakonda zosangalatsa. Onani kuti lembali silinena kuti anthu amakonda zosangalatsa kuposa Mulungu, zomwe zingasonyeze kuti anthuwo amakondabe Mulungu pang’ono. Koma limanena kuti amakonda zosangalatsa “m’malo mokonda Mulungu.” Katswiri wina wa Baibulo analemba kuti lembali “silitanthauza kuti anthuwa amakondanso Mulungu. Koma limatanthauza kuti sakonda Mulungu ngakhale pang’ono.” Ilitu ndi chenjezo lamphamvu kwambiri kwa anthu amene ayamba kukonda kwambiri zosangalatsa. Mawu oti “okonda zosangalatsa” amafotokoza za anthu amene ‘amatengeka ndi zosangalatsa za moyo uno.’—Luka 8:14.
16, 17. Kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani pa nkhani ya zosangalatsa?
16 Yesu ankaona zosangalatsa moyenerera. Nthawi ina anapita ‘kuphwando la ukwati’ ndipo nthawi inanso anapita ‘kuphwando lalikulu.’ (Yoh. 2:1-10; Luka 5:29) Paphwando la ukwatilo, vinyo anatha ndipo iye anasandutsa madzi kukhala vinyo. Pa nthawi inanso, iye sanayendere maganizo a anthu odzilungamitsa omwe ankamunena kuti amakonda kudya ndi kumwa.—Luka 7:33-36.
17 Komabe sikuti Yesu ankangokhalira kuchita zosangalatsa. Iye ankaika zofuna za Yehova pamalo oyamba ndipo ankadzipereka kwambiri pothandiza anthu ena. Analoleranso kufa imfa yopweteka kwambiri n’cholinga choti anthu adzakhale ndi moyo wosatha. Yesu anauza otsatira ake kuti: “Ndinu odala pamene anthu akukunyozani ndi kukuzunzani, komanso kukunamizirani zoipa zilizonse chifukwa cha ine. Kondwerani, dumphani ndi chimwemwe, chifukwa mphoto yanu ndi yaikulu kumwamba, pakuti umu ndi mmenenso anazunzira aneneri amene analipo inu musanakhaleko.”—Mat. 5:11, 12.
18. Kodi tingadzifunse mafunso ati kuti tidziwe ngati timakonda kwambiri zosangalatsa?
18 Kodi tingatani kuti tidziwe ngati timakonda kwambiri zosangalatsa? Tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi zosangalatsa n’zofunika kwambiri kwa ine kuposa misonkhano ndiponso utumiki? Nanga kodi ndikhoza kudzimana zinthu zimene ndimasangalala nazo n’cholinga choti ndizitumikira Mulungu? Kodi ndikamasankha zosangalatsa ndimaganizira mmene Yehova angaonere zinthuzo?’ Ngati timakondadi Mulungu tidzayesetsa kupewa zinthu zimene amadana nazo, komanso zimene tikungoganiza kuti zingamukhumudwitse.—Werengani Mateyu 22:37, 38.
ZIMENE ZINGATITHANDIZE KUKHALA OSANGALALA
19. Kodi ndi anthu otani amene sangakhale osangalala?
19 Anthu akhala akuvutika m’dziko la Satanali kwa zaka zoposa 6,000. Koma posachedwapa, dzikoli liwonongedwa. Monga tanenera, anthu ambiri m’dzikoli ndi odzikonda, okonda ndalama komanso zosangalatsa. Iwo amangoganizira ndiponso kufunafuna zinthu zokomera iwowo basi. Anthu oterewa sangakhale osangalala. Paja wolemba masalimo ananena kuti: “Wodala ndi munthu amene thandizo lake limachokera kwa Mulungu wa Yakobo, amene chiyembekezo chake chili mwa Yehova Mulungu wake.”—Sal. 146:5.
20. Kodi kukonda Mulungu kwakuthandizani bwanji inuyo kuti mukhale wosangalala?
20 Ifeyo timakonda kwambiri Mulungu ndipo chaka chilichonse, anthu ambirimbiri amalowa m’gulu lathu. Uwutu ndi umboni woti Ufumu wa Mulungu ukulamulira ndipo posachedwapa ubweretsa madalitso osaneneka padzikoli. Anthu amene amachita zofuna za Mulungu ndi amene amakhala osangalala chifukwa amadziwa kuti akusangalatsa Wolamulira wa chilengedwe chonse. Ndipotu amene amakonda Yehova adzakhala osangalala mpaka kalekale. Munkhani yotsatira, tidzakambirana makhalidwe ena amene anthu odzikonda amasonyeza, komanso tidzaona makhalidwe abwino amene atumiki a Yehova amasonyeza.