NKHANI YOPHUNZIRA 38
Muzisonyeza Kuti Ndinu Wodalirika
“Wokhulupirika amabisa nkhani.”—MIY. 11:13.
NYIMBO NA. 101 Tizigwira Ntchito Mogwirizana
ZIMENE TIPHUNZIREa
1. Kodi tingadziwe bwanji munthu wodalirika?
MUNTHU wodalirika amayesetsa kuti azisunga malonjezo ake komanso amalankhula zoona. (Sal. 15:4) Munthu woteroyo anthu amamudalira. Timafuna kuti abale ndi alongo athu azitiona choncho. Kodi n’chiyani chimene chingatithandize kukhala munthu yemwe angamudalire?
2. Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife odalirika?
2 Sitingakakamize ena kuti azitikhulupirira. M’malomwake tiyenera kuchita zinthu zimene zingachititse kuti azitidalira. Pali mawu akuti kudalirika kuli ngati ndalama. Kuti anthu azitiona kuti ndife odalirika pamafunika khama. Koma zimakhalanso zosavuta kuti asiye kutiona choncho. Yehova wakhala akusonyeza kuti ndi wodalirika. Iye sangachite zinthu zimene zingachititse kuti tisiye kumudalira chifukwa “ntchito zake zonse ndi zodalirika.” (Sal. 33:4) Ndipo amayembekezera kuti tizimutsanzira. (Aef. 5:1) Tiyeni tione zitsanzo za atumiki a Yehova omwe anatsanzira Atate wawo wakumwambayu ndipo anasonyeza kuti ndi odalirika. Tikambirananso makhalidwe 5 omwe angatithandize kuti tikhale odalirika.
MUZIPHUNZIRA KWA ATUMIKI ODALIRIKA A YEHOVA
3-4. Kodi Danieli anasonyeza bwanji kuti anali wodalirika, nanga zimenezi ziyenera kutilimbikitsa kuganizira chiyani?
3 Danieli anasonyeza chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yokhala wodalirika. Ngakhale kuti anali atatengedwa monga kapolo ku Babulo, posakhalitsa anayamba kudziwika monga munthu wodalirika. Anthu anayamba kumukhulupirira kwambiri pamene mothandizidwa ndi Yehova, anamasulira maloto a Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo. Pa nthawi ina iye ankafunika kuuza mfumu kuti Yehova sankasangalala nayo. Umenewutu si uthenga womwe mfumu ikanasangalala kumva. Kuti achite zimenezi ankafunika kulimba mtima chifukwa Nebukadinezara sankachedwa kupsa mtima. (Dan. 2:12; 4:20-22, 25) Patapita zaka zambiri Danieli anasonyezanso kuti anali wodalirika pomwe molondola anamasulira uthenga wodabwitsa womwe unaonekera pakhoma la nyumba yachifumu ku Babulo. (Dan. 5:5, 25-29) Nayenso Dariyo Mmedi ndi anthu audindo mu ufumu wake anaona kuti Danieli “anali ndi luso lodabwitsa.” Iwo anazindikira kuti iye ‘anali wokhulupirika ndipo sanali kunyalanyaza kanthu kapena kuchita zachinyengo zilizonse.’ (Dan. 6:3, 4) Choncho ngakhale olamulira omwe ankalambira mafano anazindikira kuti mtumiki wa Yehovayo anali wodalirika.
4 Poganizira chitsanzo cha Danieli, tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndili ndi mbiri yotani kwa anthu amene si Akhristu anzanga? Kodi ndimadziwika monga munthu amene amakwaniritsa maudindo ake komanso yemwe anthu angamudalire?’ N’chifukwa chiyani tiyenera kudzifunsa mafunso amenewa? Chifukwa chakuti tikakhala odalirika, anthu amalemekeza Yehova.
5. N’chifukwa chiyani Hananiya ankadziwika monga munthu wodalirika?
5 Mu 455 B.C.E., Bwanamkubwa Nehemiya atamaliza kumanga mpanda wa Yerusalemu, anafufuza amuna odalirika omwe anawaika pa udindo woyang’anira mzindawo. Pa anthu omwe anawasankha panalinso Hananiya kalonga wa m’Nyumba Yachitetezo Champhamvu. Baibulo limanena kuti Hananiya “anali munthu wodalirika ndipo anali woopa kwambiri Mulungu woona kuposa anthu ena ambiri.” (Neh. 7:2) Kukonda Yehova komanso kuopa kumukhumudwitsa kunachititsa Hananiya kuona kuti utumiki uliwonse umene anapatsidwa unali wofunika kwambiri. Makhalidwe amenewa angatithandizenso ifeyo kukhala odalirika tikamatumikira Mulungu.
6. Kodi Tukiko anasonyeza bwanji kuti anali mnzake wodalirika wa mtumwi Paulo?
6 Taganizirani chitsanzo cha Tukiko yemwe anali mnzake wodalirika wa mtumwi Paulo. Pamene Paulo anali pa ukaidi wosachoka panyumba, ankadalira Tukiko ndipo anamufotokoza kuti anali “mtumiki wokhulupirika.” (Aef. 6:21, 22) Sikuti Paulo ankangomudalira pa nkhani yokapereka makalata ku Efeso ndi ku Kolose koma ankamudaliranso kuti akalimbikitsa ndi kutonthoza Akhristu kumeneko. Tukiko amatikumbutsa za abale okhulupirika komanso odalirika masiku ano, omwe amatithandiza kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova.—Akol. 4:7-9.
7. Kodi mungaphunzire chiyani kwa akulu ndi atumiki othandiza a mumpingo mwanu pa nkhani yokhala odalirika?
7 Masiku ano timayamikira kwambiri kuti tili ndi akulu ndi atumiki othandiza odalirika. Mofanana ndi Danieli, Hananiya ndi Tukiko, iwo amaona kuti udindo wawo ndi wofunika kwambiri. Mwachitsanzo, tikafika pamisonkhano ya mkati mwa mlungu, sitimakayikira kuti nkhani iliyonse ikambidwa. Ndipo akulu amayamikira ngati amene apatsidwa nkhani akonzekera bwino mbali zawo. Komanso sitimaopa kuitanira kumisonkhano ya kumapeto kwa mlungu anthu amene timaphunzira nawo Baibulo, poganiza kuti mwina amene wapatsidwa nkhani ya onse sabwera. Ndipo timakhulupirira kuti mabuku amene tikufuna kugwiritsa ntchito mu utumiki apezeka. Abale okhulupirikawa amatisamalira bwino kwambiri ndipo timayamikira Yehova chifukwa cha zimenezi. Koma kodi ifeyo tingasonyeze m’njira ziti kuti ndife odalirika?
MUZIKHALA ODALIRIKA POSUNGA CHINSINSI
8. Kodi tingatani kuti tisamapitirire malire tikafuna kudziwa mmene zinthu zilili pa moyo wa anthu ena? (Miyambo 11:13)
8 Timakonda abale ndi alongo athu ndipo timachita chidwi ndi zimene zikuchitika pa moyo wawo. Komabe sitiyenera kupitirira malire ndipo tizilemekeza nkhani zawo zachinsinsi. Ena mumpingo wa munthawi ya atumwi anali “amiseche ndi olowerera nkhani za eni, n’kumalankhula zimene sayenera kulankhula.” (1 Tim. 5:13) Ifeyo sitingafune kukhala ngati anthu amenewa. Koma tiyerekeze kuti wina watiuza nkhani yake yachinsinsi ndipo watipempha kuti tisauze aliyense. Mwina mlongo wina watifotokozera za matenda ena ake amene akudwala kapena mayesero ena ake amene akukumana nawo ndipo akufuna kuti tisauze anthu ena. Zikatero tiyenera kuchita zimene watipemphazo.b (Werengani Miyambo 11:13.) Tsopano tiyeni tikambirane zochitika zina zomwe n’zofunika kuti tizisunga chinsinsi.
9. Kodi aliyense m’banja angasonyeze bwanji kuti ndi wodalirika?
9 M’banja. Aliyense m’banja ali ndi udindo woonetsetsa kuti akusunga chinsinsi chokhudza banja lawo. Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti m’bale wina mkazi wake ali ndi khalidwe limene silimusangalatsa. Kodi iye angamangouza ena za khalidwelo kuti amuchititse manyazi? Ayi sangatero. Amakonda mkazi wakeyo ndipo sangachite zinthu zimene zingamukhumudwitse. (Aef. 5:33) Nawonso achinyamata amafuna kulemekezedwa. Makolo angachite bwino kumakumbukira zimenezi. Sayenera kuchititsa manyazi anawo pouza anthu ena zimene amalakwitsa. (Akol. 3:21) Nawonso ana amafunika kuchita zinthu mozindikira kuti asamangoulula kwa anthu ena nkhani zomwe zingachititse manyazi anthu a m’banja lawo. (Deut. 5:16) Aliyense akamayesetsa kusunga chinsinsi pa nkhani zokhudza banja lawo, zimathandiza kuti onse m’banjamo azikhala mogwirizana.
10. Kodi munthu angasonyeze bwanji kuti ndi bwenzi lenileni? (Miyambo 17:17)
10 Anzathu. Tonsefe nthawi zina timafuna kuuza mnzathu wapamtima mmene tikumvera. Koma nthawi zina kuchita zimenezi kungakhale kovuta. N’kutheka kuti sitinazolowere kufotokozera ena mmene tikumvera ndipo tingakhumudwe ngati pambuyo pake titadziwa kuti mnzathu wafotokozera ena zomwe tinamuuza. Komabe timayamikira munthu wina akatisungira chinsinsi pa nkhani ina yake. Iye amasonyeza kuti ndi “bwenzi lenileni.”—Werengani Miyambo 17:17.
11. (a) Kodi akulu ndi akazi awo amasonyeza bwanji kuti ndi odalirika? (b) Kodi tingaphunzire chiyani kwa mkulu yemwe wasamalira nkhani yachinsinsi mumpingo ndipo kenaka ali ndi banja lake? (Onani chithunzi.)
11 Mumpingo. Akulu omwe amadziwika kuti amasunga chinsinsi ali “ngati malo obisalirapo mphepo ndi malo ousapo mvula yamkuntho” kwa abale awo. (Yes. 32:2) Timadziwa kuti tingamasuke kuwafotokozera nkhani iliyonse ndipo timakhulupirira kuti sauza aliyense. Sitimawakakamiza kuti atifotokozere nkhani zachinsinsi. Kuwonjezera pamenepo timayamikira akazi a akulu chifukwa sakakamiza amuna awo kuti awauze nkhani zimene sakuyenera kuzidziwa. Kunena zoona zimakhala bwino ngati mkazi wa mkulu sanafotokozeredwe nkhani zachinsinsi zokhudza abale ndi alongo. Mkazi wa mkulu wina anafotokoza kuti: “Ndimayamikira kwambiri kuti mwamuna wanga sandifotokozera nkhani zachinsinsi zokhudza anthu omwe wacheza nawo pa ulendo wa ubusa kapena kuwathandiza mwauzimu ndipo sandiuza n’komwe mayina awo. Ndimayamikira chifukwa sindipanikizika ndi nkhani zomwe sindingachitepo kanthu. Zimenezi zimandithandiza kuti ndizicheza momasuka ndi aliyense mumpingo. Ndipo ndimakhulupirira kuti ndikamuuza mwamuna wanga nkhani kapena vuto linalake lokhudza ineyo, sakauzanso anthu ena.” Kunena zoona tonsefe timafuna kudziwika monga anthu odalirika. Ndiye kodi ndi makhalidwe ati amene angatithandize kuti tikwaniritse cholinga chimenechi? Tiyeni tikambirane makhalidwe 5, mwa amenewa.
MUZIYESETSA KUKHALA NDI MAKHALIDWE OMWE ANGAKUTHANDIZENI KUKHALA ODALIRIKA
12. N’chifukwa chiyani tinganene kuti chikondi ndi khalidwe lofunika kwambiri pa nkhani yokhulupirirana? Perekani chitsanzo.
12 Chikondi ndi khalidwe lofunika kwambiri lomwe limachititsa kuti anthu azikhulupirirana. Yesu ananena kuti malamulo awiri akuluakulu ndi akuti tizikonda Yehova komanso tizikonda anzathu. (Mat. 22:37-39) Chikondi chathu pa Yehova chimatichititsa kuti tizimutsanzira pa nkhani yokhala odalirika. Mwachitsanzo, kukonda abale ndi alongo athu kumachititsa kuti tiziwasungira chinsinsi. Sitingafune kuulula nkhani zomwe zingawachititse kuti agwere m’mavuto, achite manyazi kapena amve kupweteka.—Yoh. 15:12.
13. Kodi kudzichepetsa kungatithandize bwanji kukhala odalirika?
13 Kudzichepetsa kungatithandize kuti tikhale odalirika. Mkhristu wodzichepetsa safuna kugometsa ena pokhala woyamba kuwauza nkhani inayake. (Afil. 2:3) Iye sadzionetsa kuti ndi wofunika kwambiri pouza ena kuti akudziwa nkhani inayake yomwe sakufunika kuulula. Kudzichepetsa kungatithandizenso kuti tizipewa kufalitsa nkhani zimene sizinafotokozedwe m’Baibulo kapena m’mabuku athu.
14. Kodi kuzindikira kumatithandiza bwanji kuti tikhale odalirika?
14 Kuzindikira kungamuthandize Mkhristu kudziwa “nthawi yokhala chete ndi nthawi yolankhula.” (Mlal. 3:7) M’zikhalidwe zina muli mawu odziwika bwino akuti, “kulankhula kuli ngati siliva koma kukhala chete kuli ngati golide.” M’mawu ena, pali nthawi imene zingakhale bwino kukhala chete m’malo molankhula. N’chifukwa chake lemba la Miyambo 11:12, limatilangiza kuti: “Munthu wozindikira bwino ndi amene amakhala chete.” Taganizirani chitsanzo ichi: Mkulu wina wodziwa zambiri kawirikawiri amapemphedwa kukathandiza mipingo ina pa nkhani zovuta. Ponena za m’baleyu, mkulu mnzake ananena kuti, “Nthawi zonse amakhala wosamala kuti asamaulule nkhani zachinsinsi zokhudza mipingo ina.” Popeza kuti mkuluyu amachita zinthu mozindikira, akulu anzake mumpingo wawo amamulemekeza kwambiri. Iwo amamudalira kuti sangaulule nkhani zawo zachinsinsi kwa ena.
15. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti kukhala oona mtima kungachititse kuti ena azitidalira.
15 Kuona mtima ndi khalidwe lina lofunika kuti tikhale odalirika. Timakhulupirira munthu woona mtima chifukwa timadziwa kuti nthawi zonse amalankhula zoona. (Aef. 4:25; Aheb. 13:18) Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti mukufuna kuwonjezera luso lanu lophunzitsa. Ndiye mwapempha munthu wina kuti amvetsere nkhani yanu komanso akupatseni malangizo omwe angakuthandizeni. Kodi ndi munthu uti yemwe mungakhulupirire kuti akuuzani zinthu moona mtima? Kodi angakhale munthu yemwe amakuuzani zomwe mukufuna kumva, kapena yemwe mokoma mtima amakuuzani zoona? Yankho lake ndi lodziwikiratu. Baibulo limanena kuti: “Kudzudzula munthu mosabisa mawu, kuli bwino kusiyana ndi kumukonda koma osamusonyeza chikondicho. Zilonda zovulazidwa ndi munthu wokukonda zimakhala zokhulupirika.” (Miy. 27:5, 6) Ngakhale kuti poyamba sizingatisangalatse, zimene mnzathu watiuza moona mtima n’kupita kwa nthawi zingatithandize.
16. Kodi lemba la Miyambo 10:19, limasonyeza bwanji kufunika kokhala odziletsa?
16 Kudziletsa ndi kofunikanso kwambiri kuti tikhale munthu wodalirika. Khalidwe limeneli lingatithandize kuti tizikhala chete pamene tayesedwa kuti tiulule nkhani zinazake zachinsinsi. (Werengani Miyambo 10:19.) Nthawi zina kudziletsa kungakhale kovuta pamene tikugwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti. Ngati sitingasamale, mosadziwa tingaulule nkhani zachinsinsi kwa anthu ambiri. Tikangotumiza uthenga pamalo ochezera a pa intaneti, sitingadziwe mmene anthu amene alandira uthengawo angaugwiritsire ntchito komanso sitingachitepo kathu pa mavuto amene angatsatirepo. Komanso kudziletsa kungatithandize kuti tikhale chete otsutsa akamatinyengerera kuti tiulule zinthu zimene zingaike pangozi moyo wa abale ndi alongo athu. Zimenezi zingachitike tikamafunsidwa mafunso ndi apolisi m’dziko limene ntchito yathu ndi yoletsedwa. Tingatsatire mfundo yakuti ‘timange pakamwa pathu kuti patetezeke’ pazochitika ngati zimenezi komanso zina. (Sal. 39:1) Timafunika kukhala odalirika kaya tikuchita zinthu ndi anthu a m’banja lathu, anzathu, abale ndi alongo kapena wina aliyense. Ndipo kuti tikhale odalirika tiyenera kukhala odziletsa.
17. Kodi tingathandize bwanji kuti anthu mumpingo azidalirana?
17 Timayamikira kwambiri Yehova chifukwa chotikokera m’banja lake lomwe muli anthu achikondi komanso odalirika. Tonsefe tili ndi udindo woonetsetsa kuti ndife odalirika kwa abale ndi alongo athu. Aliyense payekha akamayesetsa kusonyeza chikondi, kudzichepetsa, kuzindikira, kuona mtima komanso kudziletsa, timathandiza kuti mumpingo anthu azidalirana. Timafunika kupitirizabe kuchita khama kuti anthu ena azitidalira. Tiyeni tizitsanzira Mulungu wathu Yehova n’kumapitirizabe kusonyeza kuti ndife odalirika.
NYIMBO NA. 123 Tizigonjera Mulungu Mokhulupirika
a Ngati tikufuna kuti ena azitikhulupirira, tiyenera kuyamba ndi ifeyo kusonyeza kuti ndife okhulupirika kapena kuti odalirika. Munkhaniyi tiona chifukwa chake kukhulupirirana kuli kofunika komanso makhalidwe amene angatithandize kuti ena azitikhulupirira.
b Tikadziwa kuti wina mumpingo wachita tchimo lalikulu, tiyenera kumulimbikitsa kuti akauze akulu. Ngati sanachite zimenezo, kufuna kukhala okhulupirika kwa Yehova ndi mpingo, kuzitilimbikitsa kukafotokozera abusa auzimuwa za nkhaniyo.
c MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mkulu sakuulula kwa anthu a m’banja lake nkhani yachinsinsi yomwe wasamalira nawo.