NKHANI YOPHUNZIRA 39
Kodi Dzina Lanu Lili “M’buku la Moyo”?
“Buku la chikumbutso linayamba kulembedwa pamaso pake. Buku limeneli linali lonena za anthu oopa Yehova.”—MAL. 3:16.
NYIMBO NA. 61 Pitani Patsogolo Mboninu
ZIMENE TIPHUNZIREa
1. Mogwirizana ndi Malaki 3:16, kodi ndi buku liti limene Yehova wakhala akulemba, nanga m’bukuli muli chiyani?
KWA zaka masauzande ambiri, Yehova wakhala akulemba buku lapadera. M’bukuli muli mayina ambiri ndipo dzina loyamba ndi la mboni yokhulupirika yoyamba, Abele.b (Luka 11:50, 51) Kuchokera nthawi imeneyo, Yehova wakhala akuwonjezera mayina m’bukuli ndipo panopa muli mayina mamiliyoni. M’Baibulo, bukuli limatchulidwa kuti “buku la chikumbutso,” ‘buku la moyo’ ndiponso ‘mpukutu wa moyo.’ Munkhaniyi, tizilitchula kuti ‘buku la moyo.’—Werengani Malaki 3:16; Chiv. 3:5; 17:8.
2. Kodi ndi anthu ati omwe mayina awo analembedwa m’buku la moyo, nanga tingatani kuti dzina lathu lilembedwemo?
2 M’bukuli muli mayina a anthu omwe amalambira Yehova komanso kulemekeza dzina lake. Iwo akuyembekezera kudzalandira moyo wosatha. Masiku anonso dzina lathu lingalembedwe m’bukuli ngati titayesetsa kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova, zomwe zimatheka chifukwa cha nsembe ya dipo ya Mwana wake Yesu Khristu. (Yoh. 3:16, 36) Tonsefe, kaya tikuyembekezera kukakhala kumwamba kapena kudzakhala padzikoli, timafunitsitsa dzina lathu litalembedwa m’bukuli.
3-4. (a) Ngati dzina lathu lili m’buku la moyo, kodi ndiye kuti basi tidzakhala ndi moyo wosatha? Fotokozani. (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi komanso yotsatira?
3 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti aliyense amene dzina lake lingalembedwe m’bukuli ndiye kuti basi adzapeza moyo wosatha? Timapeza yankho la funso limeneli pa mawu amene Yehova anauza Mose, opezeka pa Ekisodo 32:33. Yehova anati: “Amene wandichimwirayo ndi amene ndim’fafanize m’buku langa.” Choncho mayina amene ali m’bukuli angathe kufufutidwamo. Zili ngati Yehova walemba kaye mayinawa pogwiritsa ntchito pensulo. (Chiv. 3:5.) Tiyenera kuyesetsa kuti dzina lathu likhalebe m’bukuli mpaka pa nthawi imene silingadzafufutidwenso ngati kuti lalembedwa ndi inki.
4 Zimenezitu zingachititse kuti tikhale ndi mafunso ena. Mwachitsanzo, kodi Baibulo limatiuza chiyani za anthu omwe mayina awo alembedwa m’buku la moyo, komanso za anthu omwe mayina awo sanalembedwemo? Kodi anthu omwe mayina awo adzakhalebe m’bukuli adzalandira liti moyo wosatha? Nanga bwanji za anthu omwe anamwalira asanapeze mwayi wophunzira za Yehova? Kodi n’zotheka kuti mayina awo alembedwe m’bukuli? Tipeza mayankho a mafunso amenewa munkhaniyi komanso yotsatira.
KODI NDI ANTHU ATI OMWE MAYINA AWO ALI M’BUKU LA MOYO?
5-6. (a) Mogwirizana ndi Afilipi 4:3, kodi ndi anthu enanso ati omwe mayina awo alembedwa m’buku la moyo? (b) Kodi ndi pa nthawi iti pomwe mayina awo sadzafufutidwanso m’bukuli?
5 Kodi ndi anthu ati omwe mayina awo alembedwa mophiphiritsa m’buku la moyo? Kuti tiyankhe funsoli, tikambirana za magulu 5 a anthu. Pa magulu amenewa, ena mayina awo alembedwa m’buku la moyo, pomwe ena sanalembedwemo.
6 Gulu loyamba ndi la anthu omwe asankhidwa kuti akalamulire ndi Yesu kumwamba. Kodi anthu amenewa, mayina awo ali m’buku la moyo? Inde. Mogwirizana ndi mawu a mtumwi Paulo opita kwa ‘antchito anzake’ ku Filipi, mayina a odzozedwa, omwe aitanidwa kuti akalamulire limodzi ndi Yesu, panopo ali m’buku la moyoli. (Werengani Afilipi 4:3.) Koma kuti mayina awo apitirize kukhala m’buku lophiphiritsali, iwo ayenera kukhalabe okhulupirika. Ndiyeno akadzaikidwa chidindo chomaliza, kaya atatsala pang’ono kumwalira kapena chisautso chachikulu chitatsala pang’ono kuyamba, mayina awo sadzafufutidwanso m’bukuli.—Chiv. 7:3.
7. Kodi lemba la Chivumbulutso 7:16, 17, limatithandiza bwanji kudziwa nthawi imene mayina a anthu a m’khamu lalikulu la nkhosa zina, sadzafufutidwanso m’buku la moyo?
7 Gulu lachiwiri ndi khamu lalikulu la nkhosa zina. Kodi anthu amenewa, panopa mayina awo ali m’buku la moyo? Inde. Kodi mayina awo adzapitiriza kukhala m’bukuli akadzapulumuka pa Aramagedo? Inde. (Chiv. 7:14) Yesu ananena kuti anthu amenewa, omwe ali ngati nkhosa, adzapita “ku moyo wosatha.” (Mat. 25:46) Koma anthu omwe adzapulumuke pa Aramagedowa, sadzalandira nthawi yomweyo moyo wosathawo. Zidzakhala ngati mayina awo adakali olembedwa ndi pensulo. Mu Ulamuliro wa Zaka 1,000, Yesu “adzawaweta ndi kuwatsogolera ku akasupe a madzi a moyo.” Anthu omwe adzalole kutsogoleredwa ndi Khristu, ndipo pamapeto pake n’kuweruzidwa kuti ndi okhulupirika kwa Yehova, mayina awo sadzafufutidwanso m’buku la moyo.—Werengani Chivumbulutso 7:16, 17.
8. Kodi ndi anthu ati omwe mayina awo sanalembedwe m’buku la moyo, nanga n’chiyani chidzawachitikire?
8 Gulu lachitatu ndi la anthu omwe ali ngati mbuzi, omwe adzawonongedwe pa Aramagedo. Mayina awo sanalembedwe m’buku la moyo. Yesu ananena kuti iwo ‘adzapita ku chiwonongeko chotheratu.’ (Mat. 25:46) Mouziridwa, mtumwi Paulo ananena kuti anthu amenewa “adzawaweruza kuti alandire chilango cha chiwonongeko chamuyaya.” (2 Ates. 1:9; 2 Pet. 2:9) N’chimodzimodzinso ndi anthu omwe akhala akuchimwira mwadala mzimu woyera. Nawonso adzalandira chiwonongeko chamuyaya, osati moyo wosatha. N’zoonekeratu kuti sadzaukitsidwa. (Mat. 12:32; Maliko 3:28, 29; Aheb. 6:4-6) Tsopano tiyeni tione za magulu awiri a anthu omwe adzaukitsidwe kuti akhale padzikoli.
ANTHU OMWE ADZAUKITSIDWE
9. Mogwirizana ndi Machitidwe 24:15, kodi ndi magulu awiri ati a anthu omwe adzaukitsidwe, nanga magulu awiriwa amasiyana bwanji?
9 Baibulo limatiuza za magulu awiri a anthu amene adzaukitsidwe kuti akhale ndi moyo wosatha padzikoli, omwe ndi “olungama” ndi “osalungama.” (Werengani Machitidwe 24:15.) “Olungama” ndi anthu omwe anatumikira Yehova mokhulupirika pa nthawi yomwe anali ndi moyo. Pomwe anthu “osalungama” ndi omwe sanatumikire Yehova mokhulupirika. Ndipotu nthawi zambiri anthuwa ankachita zinthu zoipa. Popeza kuti anthu a m’magulu awiri onsewa adzaukitsidwa, kodi tinganene kuti mayina awo ali m’buku la moyo? Kuti tiyankhe funso limeneli, tiyeni tikambirane za gulu lililonse palokha.
10. N’chifukwa chiyani “olungama” adzaukitsidwe, nanga ena mwa iwo adzapatsidwa mwayi wotani? (Onaninso nkhani yakuti, “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” m’magaziniyi, kuti mudziwe zambiri pa nkhani yokhudza kuukitsidwa kwa anthu omwe adzakhale padziko lapansi.)
10 Gulu la nambala 4 ndi la“olungama.” Iwo asanamwalire, mayina awo anali atalembedwa m’buku la moyo. Ndiye kodi atamwalira, mayina awo anafufutidwa m’bukuli? Ayi, chifukwa kwa Yehova iwo ndi “amoyo.” Yehova “ndi Mulungu wa anthu amoyo, osati akufa, pakuti kwa iye onsewa ndi amoyo.” (Luka 20:38) Zimenezi zikutanthauza kuti olungama akadzaukitsidwa kuti akhale ndi moyo padzikoli, mayina awo adzakhala adakali m’buku la moyo, ngakhale kuti zidzakhala ngati alembedwa ndi pensulo. (Luka 14:14) Mosakayikira, ena mwa oukitsidwawa adzakhala ndi mwayi wotumikira monga “akalonga padziko lonse lapansi.”—Sal. 45:16.
11. Kodi “osalungama” adzafunika kuphunzira chiyani kuti mayina awo alembedwe m’buku la moyo?
11 Pomaliza, tiyeni tikambirane za gulu la nambala 5 lomwe ndi la “osalungama.” Popeza kuti mwina sankadziwa malamulo a Yehova, anthuwa sankatsatira mfundo zake pa nthawi imene anali ndi moyo. Choncho mayina awo sanalembedwe m’buku la moyo. Koma Mulungu adzawaukitsa pofuna kuwapatsa mwayi woti mayina awo alembedwe m’bukuli. Anthu “osalungamawa” adzafunika kuthandizidwa kwambiri chifukwa asanamwalire, ena mwa iwo ankachita zinthu zoipa kwambiri. Choncho iwo adzafunika kuphunzitsidwa kuti azitsatira mfundo zolungama za Yehova. Kuti zimenezi zidzatheke, Ufumu wa Mulungu udzatsogolera pa ntchito yaikulu yophunzitsa anthu yomwe sinachitikeponso.
12. (a) Kodi ndi ndani amene adzaphunzitse anthu osalungama? (b) N’chiyani chidzachitikire anthu omwe adzakane kutsatira zimene aphunzitsidwa?
12 Kodi ndi ndani amene adzaphunzitse anthu osalungama? Ndi a khamu lalikulu komanso olungama omwe adzaukitsidwe. Kuti mayina awo adzalembedwe m’buku la moyo, osalungama adzafunika kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova komanso kudzipereka kwa iye. Yesu Khristu limodzi ndi oweruza anzake, azidzachita chidwi ndi mmene osalungamawa akuchitira ndi zimene akuphunzitsidwa. (Chiv. 20:4) Aliyense amene adzakane kutsatira zimene akuphunzitsidwa, sadzaloledwa kuti apitirize kukhala ndi moyo ngakhale atakhala ndi zaka 100. (Yes. 65:20) Yehova ndi Yesu amafufuza mitima ndipo sadzalola kuti wina aliyense azidzasokoneza m’dziko latsopano.—Yes. 11:9; 60:18; 65:25; Yoh. 2:25.
ANTHU OMWE ADZAUKE KUTI ALANDIRE MOYO KOMANSO OMWE ADZAUKE KUTI AWERUZIDWE
13-14. (a) Kodi m’mbuyomu tinkakhulupirira zotani zokhudza mawu a Yesu a pa Yohane 5:29? (b) Kodi tiyenera kudziwa chiyani pa mawu akewa?
13 Yesu anafotokozanso za anthu omwe adzauke kuti akhale padzikoli. Mwachitsanzo, iye anati: “Idzafika nthawi pamene onse ali m’manda achikumbutso adzamva mawu ake ndipo adzatuluka. Amene anali kuchita zabwino adzauka kuti alandire moyo. Amene anali kuchita zoipa adzauka kuti aweruzidwe.” (Yoh. 5:28, 29) Kodi pamenepa Yesu ankatanthauza chiyani?
14 M’mbuyomu tinkakhulupirira kuti mawu a Yesuwa amanena za zochita za anthu pambuyo poti aukitsidwa, kutanthauza kuti ena adzauka n’kumachita zinthu zabwino, pomwe ena adzauka n’kumachita zoipa. Koma onani kuti Yesu sananene kuti anthu omwe adzaukitsidwe m’manda a chikumbutso azidzachita zinthu zabwino kapena azidzachita zinthu zoipa. Iye anagwiritsa ntchito mawu osonyeza kuti zinthuzo zinachitika kale. Ananena za anthu omwe “anali kuchita zabwino” ndi amene “anali kuchita zoipa.” Zimenezi zikusonyeza kuti anthuwa anachita zimenezi asanamwalire. Izitu n’zomveka. Ndipotu palibe yemwe adzaloledwe kuti azidzachita zinthu zoipa m’dziko latsopano. Choncho anthu osalungama ayenera kuti ankachita zinthu zoipa asanamwalire. Ndiye kodi tinganene kuti Yesu ankatanthauza chiyani pomwe ananena kuti anthu “adzauka kuti alandire moyo” ndiponso kuti ena “adzauka kuti aweruzidwe”?
15. Kodi ndi anthu ati omwe ‘adzaukitsidwe kuti alandire moyo,’ nanga n’chifukwa chiyani?
15 Olungama, omwe ndi anthu amene anachita zabwino, “adzauka kuti alandire moyo” chifukwa mayina awo analembedwa kale m’buku la moyo. Kuukitsidwa kwa anthu omwe “anali kuchita zabwino” kotchulidwa pa Yohane 5:29, ndi kuuka kwa “olungama” komwe kwatchulidwanso pa Machitidwe 24:15. Mafotokozedwe amenewa ndi ogwirizana ndi zimene zili pa Aroma 6:7, pomwe pamati: “Chifukwa munthu amene wafa wamasuka ku uchimo wake.” Pa nthawi imene olungamawa anamwalira, Yehova anawakhululukira zolakwa zawo, koma amakumbukirabe zinthu zosonyeza chikhulupiriro zomwe anachita ali ndi moyo. (Aheb. 6:10) Komabe, olungama omwe adzaukitsidwewa, adzafunika kukhalabe okhulupirika kuti mayina awo apitirize kukhala m’buku la moyo.
16. Kodi ‘kuuka kuti aweruzidwe’ kumatanthauza chiyani?
16 Nanga bwanji ponena za anthu omwe ankachita zoipa asanamwalire? Ngakhale kuti atafa machimo awo anakhululukidwa, sanatumikire Yehova mokhulupirika pamene anali ndi moyo ndipo mayina awo sanalembedwe m’buku la moyo. Choncho, kuuka kwa anthu “amene anali kuchita zoipa” ndi kuuka kwa “osalungama” komwe kwatchulidwanso pa Machitidwe 24:15. Anthu amenewa “adzauka kuti aweruzidwe.”c Zimenezi zikutanthauza kuti Yesu azidzaonetsetsa zimene osalungamawa adzachite pambuyo poti aukitsidwa. (Luka 22:30) Padzafunika nthawi kuti anthuwa aweruzidwe ngati mayina awo angalembedwe m’buku la moyo. Mayina awo adzalembedwa m’bukuli ngati iwo adzasiye zoipa zimene ankachita n’kudzipereka kwa Yehova.
17-18. Kodi anthu onse omwe adzaukitsidwe kuti akhale ndi moyo padzikoli adzafunika kuchita chiyani, nanga “ntchito” zotchulidwa pa Chivumbulutso 20:12, 13, n’chiyani?
17 Kaya poyamba anali olungama kapena osalungama, oukitsidwa adzafunika kumvera malamulo omwe ali m’mipukutu yatsopano yomwe idzatsegulidwe mkati mwa zaka 1,000. Mtumwi Yohane anafotokoza zimene anaona m’masomphenya kuti: “Ndinaona akufa, olemekezeka ndi onyozeka, ataimirira pamaso pa mpando wachifumuwo, ndipo mipukutu inafunyululidwa. Koma mpukutu wina unafunyululidwa, ndiwo mpukutu wa moyo. Ndipo akufa anaweruzidwa malinga ndi zolembedwa m’mipukutuyo, mogwirizana ndi ntchito zawo.”—Chiv. 20:12, 13.
18 Kodi oukitsidwawa adzaweruzidwa potengera “ntchito” ziti? Kodi zidzakhala ntchito zimene ankachita asanamwalire? Ayi. Kumbukirani kuti machimo omwe anachita poyamba anakhululukidwa pamene anamwalira. Choncho “ntchito zawo” zotchulidwa panozi, sizingakhale zomwe anachita asanamwalire. M’malomwake, ayenera akunena za ntchito zomwe adzachite pambuyo pophunzitsidwa m’dziko latsopano. Ngakhalenso anthu okhulupirika monga Nowa, Samueli, Davide ndi Danieli, adzafunika kuphunzitsidwa zokhudza Yesu Khristu komanso kukhulupirira nsembe yake. Ndiye kuli bwanji anthu osalungama?
19. Kodi n’chiyani chimene pamapeto pake chidzachitikire anthu omwe adzakane mwayi wamtengo wapataliwu?
19 Kodi n’chiyani chomwe pamapeto pake chidzachitikire anthu omwe adzakane mwayi wamtengo wapataliwu? Lemba la Chivumbulutso 20:15 limatiuza kuti: “Aliyense amene sanapezeke atalembedwa m’buku la moyo anaponyedwa m’nyanja yamoto.” Anthu amenewa adzawonongedwa ndipo sadzakhalaponso. Choncho n’zofunika kwambiri kuti tiziyesetsa kuti dzina lathu lilembedwe m’buku la moyo ndipo lisadzafufutidwemo.
20. Kodi ndi ntchito yosangalatsa iti yomwe idzachitike m’kati mwa Ulamuliro wa Zaka 1,000? (Onani chithunzi chapachikuto.)
20 Nthawi ya Ulamuliro wa Zaka 1,000, idzakhala yosangalatsatu kwambiri. Pa nthawiyi padzachitika ntchito yaikulu yophunzitsa yomwe sinachitikepo ndi kale lonse. Koma idzakhalanso nthawi imene olungama ndi osalungama adzayesedwe kuti zidziwike ngati ali okhulupirika. (Yes. 26:9; Mac. 17:31) Ndiye kodi ntchito yophunzitsayo idzachitika bwanji? Nkhani yotsatira idzatithandiza kumvetsa mmene ntchito yosangalatsayi idzachitikire.
NYIMBO NA. 147 Mulungu Watilonjeza Moyo Wosatha
a Nkhaniyi ifotokoza kamvedwe katsopano ka mawu a Yesu a pa Yohane 5:28, 29, konena za anthu omwe ‘adzauke kuti alandire moyo’ ndi amene ‘adzauke kuti aweruzidwe.’ Tiphunzira za kuuka kwa mitundu iwiriyi komanso anthu amene akukhudzidwa.
b Bukuli linayamba kulembedwa kuchokera pa “kukhazikitsidwa kwa dziko,” kutanthauza anthu omwe adzawomboledwe ku uchimo. (Mat. 25:34; Chiv. 17:8) Choncho zikuoneka kuti Abele, yemwe anali wolungama, ndi amene anali woyamba kulembedwa m’buku la moyo.
c M’mbuyomu tinkafotokoza kuti mawu akuti ‘kuweruzidwa’ omwe atchulidwa palembali, amatanthauza kupatsidwa chilango kapena chigamulo pa zolakwa zimene munthu wachita. N’zoona kuti mawuwa angatanthauzenso zimenezo. Koma pa nkhaniyi, zikuoneka kuti Yesu anagwiritsa ntchito mawu akuti ‘kuweruzidwa’ ponena za kuyang’ana winawake mosamala n’cholinga chofuna kumuyesa, kapena monga mmene buku lotanthauzira Baibulo lina la Chigiriki linanenera kuti, “kuyang’anitsitsa khalidwe la winawake.”