Kuphunzira Kumapindulitsa
KODI munaonapo anthu akusankhula zipatso? Ambiri amayang’ana maonekedwe ndi ukulu wa zipatsozo pofuna kudziŵa ngati n’zakupsa. Ena amanunkhiza zipatsozo. Enanso amazigwira, ngakhale kuzisinika kapena kuti kuzidiniza. Ndiponso ena amayesa kulemera kwake kwa zipatsozo, atagwira china uku china uku pofuna kumva chimene chili ndi madzi ambiri. Kodi anthuwo amakhala akuganizira chiyani? Amakhala akupenda mbali zosiyanasiyana, kuona kusiyana kwa zipatsozo, kukumbukira zimene anasankhapo m’mbuyomo, ndi kuyerekeza zimene tsopano akuona ndi zimene akuzidziŵa. Pamapeto pake amapeza phindu la kusankha zipatso zokoma chifukwa chosankha mosamala kwambiri.
Koma mapindu a kuphunzira Mawu a Mulungu amaposa pamenepo. Pamene kuphunzira koteroko kukhala mbali yofunika kwambiri m’miyoyo yathu, chikhulupiriro chathu chimalimba, chikondi chathu chimazamirapo, ulaliki wathu umabala zipatso zambiri, ndipo zosankha zimene timapanga zimapereka umboni wokulirapo wakuti timagwiritsa ntchito luntha ndi nzeru yaumulungu. Ponena za mapindu oterowo, Miyambo 3:15 imati: ‘Zonse zokondweretsa sizilingana nawo.’ Kodi mumapeza mapindu oterowo? Zimadalira njira imene mumaphunzirira.—Akol. 1:9, 10.
Kodi kuphunzira ndi chiyani? Kuphunzira kumasiyana ndi kuŵerenga wamba. Kumaphatikizapo kugwiritsa ntchito luso la kuganiza popenda nkhani mosamala. Kumaphatikizaponso kupenda zimene mukuŵerenga, poziyerekeza ndi zimene mukudziŵa kale, komanso kuzindikira zifukwa zoperekedwa pa mfundo zotchulidwazo. Pamene mukuphunzira, lingalirani mozama mfundo zimene zingakhale zatsopano kwa inu. Lingaliraninso mmene inuyo mungagwiritsire ntchito mokwanira uphungu wa m’Malemba. Monga Mboni ya Yehova, muyeneranso kulingalira za mipata imene mungagwiritse ntchito mfundozo kuthandiza ena. Mwachidziŵikire, kuphunzira kumaphatikizaponso kusinkhasinkha.
Kukhala Wokonzekera M’maganizo
Pokonzekera kuti muyambe kuphunzira, mumaikiratu pafupi zinthu ngati Baibulo, zofalitsa zilizonse zimene mukufuna kugwiritsa ntchito, pensulo kapena bolopeni, mwinanso ndi notibuku. Koma kodi mumakonzekeretsanso mtima wanu? Baibulo limatiuza kuti Ezara “adaikiratu mtima wake kuchifuna chilamulo cha Yehova, ndi kuchichita, ndi kuphunzitsa m’Israyeli malemba ndi maweruzo.” (Ezara 7:10) Kodi kukonzekeretsa mtima koteroko kumachitika motani?
Pemphero limatithandiza kuyamba phunziro la Mawu a Mulungu ndi maganizo oyenera. Timafuna kuti mtima wathu, umunthu wathu wam’katikati, ukhale wolabadira malangizo amene Yehova akutipatsa. Poyamba phunziro lililonse, pemphani Yehova kuti akugaŵireni mzimu woyera. (Luka 11:13) M’pempheni kuti akuthandizeni kumvetsa tanthauzo la zimene muti muphunzire, mmene zimakhudzira chifuniro chake, mmene zingakuthandizireni kusiyanitsa chabwino ndi choipa, mmene muyenera kugwiritsira ntchito malangizo ake pamoyo wanu, ndi mmene nkhaniyo ikukhudzira ubwenzi wanu ndi iye. (Miy. 9:10) Pamene mukuphunzira panokha, pitirizani ‘kupempha nzeru kwa Mulungu.’ (Yak. 1:5) Dzifufuzeni moona mtima malinga ndi zimene mukuphunzira, ndipo pemphani Yehova kuti akuthandizeni kuchotsa malingaliro olakwika ndi maganizo achiwembu. Nthaŵi zonse “yamikani Yehova” kaamba ka zinthu zimene amavumbula. (Sal. 147:7) Kuphunzira kophatikiza pemphero kumeneku kumatiyandikiza kwa Yehova, chifukwa kumatithandiza kumulabadira pamene atilankhula kudzera m’Mawu ake.—Sal. 145:18.
Kulabadira koteroko kumasiyanitsa anthu a Yehova ndi anthu ena amene amaphunzira. Anthu osadzipereka kwa Mulungu amakhala ndi chizoloŵezi chokonda kukayikira ndi kutsutsa zinthu zolembedwa. Koma ife sitikhala ndi maganizo amenewo. Yehova timam’khulupirira ndi mtima wonse. (Miy. 3:5-7) Tikalephera kumvetsa penapake, sitimangodzigamulira kuti basi pamenepo panalakwika. Pamene tikufufuza ndi kufunafuna mayankho, timayembekezerabe kwa Yehova. (Mika 7:7) Monga Ezara, timakhala ndi cholinga cha kuchita ndi kuphunzitsa zimene timaphunzira. Pokhala ndi mtima umenewu, tidzatuta madalitso aakulu kuchokera pakuphunzira kwathu.
Kaphunziridwe Koyenera
M’malo mongoyamba pa ndime yoyamba kupitiriza mpaka kumapeto, pendani kaye nkhani yonseyo. Yambani mwa kupenda mawu a mutu wa nkhani. Umenewo ndiwo mutu wa zimene muphunzire. Kenako onetsetsani mmene mitu yaing’ono ikugwirizanira ndi mutu waukuluwo. Pendani zithunzi zonse, matchati, kapena mabokosi obwereza a nkhaniyo. Dzifunseni kuti: ‘Malinga ndi kupenda kumeneku, kodi ndikuyembekezera kuphunzira chiyani? Kodi zimene ndiphunzirezo zindipindulitsa motani?’ Njira imeneyi imakhala kalambulabwalo wa phunziro lanu.
Tsopano pezani mfundo zake. Nkhani zophunzira za mu Nsanja ya Olonda ndi mabuku ena zimakhala ndi mafunso. Pamene muŵerenga ndime iliyonse, kumakhala kothandiza kulemba mzera kunsi kwa mayankho. Ngakhale kuti palibe mafunso, mukhoza kulembabe mzera kunsi kwa mfundo zofunikira kuzikumbukira. Ngati mwapeza mfundo yatsopano kwa inu, imani pamenepo kanthaŵi kuti muimvetse bwinobwino. Funafunani zitsanzo kapena mfundo zimene zingakuthandizeni mu ulaliki kapena zimene mungaphatikize m’nkhani imene mudzakambe m’tsogolo. Ganizirani anthu ena amene mungawalimbikitse chikhulupiriro mwa kuwauza zimene mukuphunzira. Lembani mzera kunsi kwa mfundo zimene mukufuna kukazigwiritsa ntchito, ndipo zipendeninso pamene mwatsiriza phunziro lanu.
Pamene muŵerenga nkhaniyo, tsegulani malemba osagwidwa mawu. Pendani mmene lemba lililonse likukhudzira mfundo yaikulu ya ndimeyo.
Mwina mungapeze mfundo zimene simuzimvetsa bwino kapena zimene mungafune kuzifufuza mozamirapo. M’malo mododometsedwa nazo, lembani mzera kunsi kwa mfundozo kuti muziyang’ane pambuyo pake. Nthaŵi zambiri mfundo zoterozo zimamveketsedwa bwino pamene mupitiriza kuŵerenga nkhaniyo. Ngati sizinamveketsedwe, mukhoza kuzifufuza mozamirapo. Kodi ndi zinthu zotani zimene zingafune khama ngati limenelo? Mwina mungapeze lemba logwidwa mawu limene simukulimvetsa bwino. Kapena mungakhale musakuona mmene likugwirizanira ndi nkhani imene ikufotokozedwa. Mwinanso mungaone kuti mfundo inayake mukuimva m’nkhaniyo koma osati kwenikweni moti n’kuifotokozera munthu wina bwinobwino. M’malo mongozidutsa mfundo zoterozo, n’chanzeru kuzifufuza mutamaliza kuphunzira zimene mwaziyamba kale.
Pamene mtumwi Paulo analemba kalata yake yokhala ndi mfundo zambiri kwa Akristu achihebri, cham’katikati mwa kalatayo anaima kaye ndi kunena kuti: “Mutu wa izi tanenazi ndi uwu.” (Aheb. 8:1) Kodi inunso mumadzikumbutsa motero nthaŵi ndi nthaŵi? Taonani chifukwa chimene Paulo anachitira zimenezo. M’machaputala oyambirira a kalata yake, anali atasonyeza kale kuti Kristu monga Mkulu wa Ansembe wa Mulungu anali ataloŵa kale kumwamba kwenikweniko. (Aheb. 4:14–5:10; 6:20) Komabe, mwa kumveketsa ndi kugogomeza mfundo yaikulu imeneyo kumayambiriro kwa chaputala 8, Paulo anakonzekeretsa maganizo a aŵerengi a nkhani yake kuti akalingalire mozama za mmene mfundoyo imakhudzira miyoyo yawo. Anafotokoza kuti Kristu anakaonekera pamaso pa Mulungu m’malo mwa iwo ndi kuti anawatsegulira njira yokaloŵera ku “malo opatulika” kumwamba. (Aheb. 9:24; 10:19-22) Kutsimikizika kwa chiyembekezo chawo kunawathandiza kugwiritsa ntchito uphungu wa m’kalata yake wonena za chikhulupiriro, chipiriro, ndi khalidwe lachikristu. Mofananamo, pamene tikuphunzira, kuzika maganizo pa mfundo zazikulu kudzatithandiza kuona mmene nkhaniyo akuifotokozera ndipo kudzakhomereza m’maganizo mwathu zifukwa zomveka zochitira zinthu mogwirizana ndi nkhaniyo.
Kodi kuphunzira kwanu panokha kudzakulimbikitsani kuchitapo kanthu? Funso limeneli n’lofunika kwambiri. Mukaphunzira mfundo inayake, dzifunseni kuti: ‘Kodi mfundoyi iyenera kukhudza motani maganizo anga ndi zolinga zanga m’moyo? Kodi mfundo imeneyi ndingaigwiritse ntchito motani pothetsa mavuto, popanga chosankha, kapena pokwaniritsa cholinga changa? Kodi ndingaigwiritse ntchito motani m’banja langa, mu ulaliki, mumpingo?’ Ganizirani mafunso ameneŵa mwa pemphero, ndi kulingalira mikhalidwe yeniyeni imene mungagwiritsepo ntchito zimene mwaphunzirazo.
Mukamaliza mutu kapena nkhani, tengani nthaŵi yobwereza m’maganizo mwachidule. Onani ngati mungakumbukire mfundo zazikulu ndi zifukwa zake. Njira imeneyi idzakuthandizani kukumbukira mfundozo zikadzafunika m’tsogolo.
Zimene Muyenera Kuphunzira
Monga anthu a Yehova, tili ndi zambiri zoti tiphunzire. Koma kodi tiyenera kuyambira pati? Tsiku ndi tsiku, tiyenera kuphunzira lemba la tsiku ndi ndemanga zake m’kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku. Mlungu ndi mlungu, timafika pamisonkhano yampingo, ndipo kuphunzira kumene timachita pokonzekera misonkhano imeneyi kudzatithandiza kupindula zambiri. Kuwonjezera apo, ena agwiritsa ntchito nthaŵi mwanzeru mwa kuphunzira mabuku athu achikristu amene analembedwa m’mbuyomo iwo asanaphunzire choonadi. Ena amasankhula mavesi ena a kuŵerenga Baibulo kwawo kwa mlungu ndi mlungu ndi kuwaphunzira mozamirapo.
Koma bwanji ngati mikhalidwe yanu sikukulolani kuphunzira mosamala nkhani zonse zokaphunzira pamisonkhano yampingo ya mlungu ndi mlungu? Pewani chizolowezi choipa chongoŵerenga nkhanizo kungoti muzimalize, kapenanso osaziphunzira n’komwe ati chifukwa simungazimalize. M’malo mwake, onani kuti mungaphunzire kufika pati, ndipo phunzirani zomwezo bwino lomwe. Teroni mlungu ndi mlungu. M’kupita kwa nthaŵi, yesetsani kulowetsapo misonkhano inanso.
‘Manga Nyumba Yako’
Yehova amafuna kuti mitu ya mabanja izigwira ntchito zolimba kuti izipeza zofunika za mabanja awo okondekawo. “Longosola ntchito yako panjapo,” imatero Miyambo 24:27, “nuikonzeretu kumunda.” Komabe, simuyenera kunyalanyaza zosowa zauzimu za banja lanu. N’chifukwa chake vesilo likupitiriza kuti: “Pambuyo pake ndi kumanga nyumba yako.” Kodi mitu ya mabanja ingachite motani zimenezi? Miyambo 24:3 imati: ‘Luntha likhazikitsa [nyumba].’
Kodi luntha lingapindulitse motani banja lanu? Luntha ndilo luso la maganizo lozindikira zinthu zobisika. Tinganene kuti phunziro la banja logwira mtima limayamba ndi kuliphunzira banja lanu lenilenilo. Kodi a m’banja lanu akupita patsogolo motani mwauzimu? Mvetserani pamene mukukambirana nawo. Kodi pakuoneka mzimu wodandaula kapena woipidwa ndi zinthu? Kodi amakondetsa chuma? Pamene muli muulaliki limodzi ndi ana anu, kodi amachita manyazi poonekera kwa anzawo kuti ndi Mboni za Yehova? Kodi amasangalala ndi pulogalamu yoŵerenga ndi kuphunzira Baibulo monga banja? Kodi akutengadi njira ya Yehova kukhala njira ya moyo wawo? Popenda mosamala mudzazindikira zimene muyenera kuchita monga mutu wa banja, kuti mukhazikitse ndi kukulitsa makhalidwe auzimu mwa aliyense wa m’banja lanu.
Yang’anani mu Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kuti mupeze nkhani zokhudza zosowa zakutizakuti. Ndiyeno dziŵitsirantuni banja lanu zimene mudzaphunzire kotero kuti aganizirepo za nkhaniyo. Onetsetsani kuti paphunziropo pakukhala mkhalidwe wachikondi. Popanda kulanga aliyense kapena kuchititsa wina manyazi, unikani phindu la nkhaniyo, ndipo igwirizanitseni ndi zosowa za banja lanu. Onetsetsani kuti aliyense akutengapo mbali. Thandizani aliyense kuona mmene Mawu a Yehova alili “angwiro” popereka thandizo pa chosowa chilichonse pamoyo.—Sal. 19:7.
Kupeza Mapindu Ambiri
Anthu ozindikira koma opanda luntha lauzimu amatha kufufuza chilengedwe, zochitika zapadziko, ngakhalenso kudzifufuza iwo eniwo, koma amalephera kuzindikira tanthauzo lenileni la zimene amaona. Koma, mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu, anthu amene amaphunzira Mawu a Mulungu nthaŵi zonse amatha kuona mu zinthu zimenezi, dzanja la Mulungu, kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Baibulo, ndi kukwaniritsidwa kwa chifuniro cha Mulungu chodalitsa anthu omvera.—Marko 13:4-29; Aroma 1:20; Chiv. 12:12.
Komabe, luntha lodabwitsa limenelo lisatipangitse kukhala anthu onyada. M’malo mwake, kupenda Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku kuyenera kutithandiza kukhalabe odzichepetsa. (Deut. 17:18-20) Timatetezekanso ku “chenjerero la uchimo” chifukwa Mawu a Mulungu akakhala m’mitima mwathu, chikoka cha uchimo sichitha kugonjetsa mtima wathu potsutsana nacho. (Aheb. 2:1; 3:13; Akol. 3:5-10) Tikamatero, ‘tidzayenda koyenera Ambuye pom’kondweretsa monsemo, pamene tikubala zipatso m’ntchito yonse yabwino.’ (Akol. 1:10) Kuchita zimenezo ndiko cholinga chathu pophunzira Mawu a Mulungu, ndipo kuchikwaniritsa ndiko mphoto yopambana.