Mutu 110
Uminisitala wa Pakachisi Umalizidwa
YESU akupanga kuwonekera kwake kotsiriza pakachisi. M’chenicheni, iye akumaliza uminisitala wake wapoyera padziko lapansi kusiyapo za zochitika za kuyesedwa kwake ndi kuphedwa, zimene ziripo masiku anayi otsatira. Tsopano iye akupitirizabe nkhonya zake pa alembi ndi Afarisi.
Iye akudzuma katatu kuti: “Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga!” Choyamba, iye akulengeza tsoka kwa iwo chifukwa chakuti amatsuka “kunja kwake kwa chikho ndi mbale, koma mkatimo iwo adzala ndi kulanda ndi kusadziletsa.” Chotero iye akulangiza kuti: “Yambotsuka mkati mwa chikho ndi mbale, kuti kunja kwake kukhalenso koyera.
Kenako iye akulengeza tsoka pa alembi ndi Afarisi kaamba ka kuvunda kwamkati ndi zonyansa zimene akuyesayesa kubisa ndi kawonekedwe ka kunja kopembedza. “Mufanafana ndi manda opaka njereza,” iye akutero, “amene awonekera okoma kunja kwake, koma adzala mkatimo ndi mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zonse.”
Potsirizira, chinyengo chawo chikuwonekera m’kufunitsitsa kwawo kumanga manda a aneneri ndi kuwakongoletsa kuti achititse chisamaliro kusumikidwa pantchito zawo za chifundo. Komabe, monga momwe Yesu akuvumbulira, iwo ‘ali ana a iwo amene anapha aneneri.’ Ndithudi, aliyense amene amayesa kuvumbula chinyengo chawo ali paupandu!
Popitirizabe, Yesu akunena mawu ake amphamvu koposa a kudzudzula. “Njoka inu, obadwa inu a mamba,” iye akutero, “mudzatha bwanji kuthaŵa kulanga kwake kwa Gehena?” Gehena ndicho chigwa chogwiritsiridwa ntchito monga malo otayirako zinyalala ku Yerusalemu. Chotero Yesu akunena kuti chifukwa cha kulondola kwawo njira yoipa, alembi ndi Afarisi adzalandira chiwonongeko chosatha.
Ponena za awo amene iye akutumiza monga oimira ake, Yesu akuti: “Ena a iwo mudzawapha, mudzawapachika; ndi ena a iwo mudzawakwapula m’masunagoge mwanu, ndi kuwazunza, kuchokera kumudzi umodzi, kufikira kumudzi wina; kotero kuti udzafika pa inu mwazi wonse wotayidwa padziko lapansi, kuyambira kumwazi wa Abele wolungamayo, kufikira kumwazi wa Zakariya mwana wa Barakiya [wotchedwa Yehoyada m’Mbiri Wachiŵiri], amene munamupha pakati pa Kachisi ndi guwa la nsembe. Indetu ndinena kwa inu, Zinthu zonse izi zidzafika pambadwo uwu wamakono.”
Chifukwa chakuti Zakariya anadzudzula atsogoleri a Israyeli, “anampangira chiwembu, namponya miyala, mwalamulo la mfumu m’bwalo la nyumba ya Yehova.” Koma, monga momwe Yesu akuneneratu, Israyeli adzalipilira mwazi wokhetsedwa wa olungama onsewo. Iwo akuulipilira zaka 37 pambuyo pake, mu 70 C.E., pamene magulu ankhondo a Roma awononga Yerusalemu ndipo Ayuda oposa miliyoni akuwonongeka.
Pamene Yesu akulingalira mkhalidwe wowopsa umenewu, akuvutika maganizo. “Ha, Yerusalemu, Yerusalemu,” kachiŵirinso iye akulengeza motero, “Ine ndinafuna kangati kusonkhanitsa pamodzi ana ako, inde monga thadzi lisonkhanitsa anapiye ake m’mapiko ake, koma inu simunafuna ayi. Wonani, nyumba yanu yasiyidwa kwa inu yabwinja.”
Pamenepo Yesu akuwonjezera kuti: “Simudzandiwonanso Ine, kuyambira tsopano, kufikira mudzanena, Wolemekezedwa iye amene akudza m’dzina la Ambuye.” Tsiku limenelo lidzakhala pakukhalapo kwa Kristu pamene adza mu Ufumu wake wakumwamba ndipo anthu adzamuwona ndi maso achikhulupiliro.
Tsopano Yesu akumka pamalo amene angathe kuwona timabokosi tandalama m’kachisi ndipo makamuwo akuikamo ndalama. Achuma akuika ndalama zambiri. Koma pamenepo mkazi wamasiye wina akudza naponyamo tindalama tiŵiri tamtengo wochepetsetsa.
Poitanira ophunzira ake kumeneko, Yesu akuti: “Ndithu ndinena ndi inu, Mkazi wamasiye amene waumphaŵi anaponya zambiri koposa onse akuponya mosungiramo.” Iwo ayenera kudabwa mmene zimenezi zingakhalire choncho. Chotero Yesu akufotokoza kuti: “Pakuti anaponyamo onse mwa zochuluka zawo; koma iye anaponya mwa kusoŵa kwake zonse anali nazo, inde moyo wake wonse.” Atanena zimenezi, Yesu akutuluka m’kachisi kwa nthaŵi yotsiriza.
Pochita kaso ndi ukulu ndi kukongola kwa kachisiyo, ophunzira ake akulengeza kuti: “Mphunzitsi, wonani miyala yotere ndi nyumba yotere.” Ndithudi, kwasimbidwa kuti miyalayo njotalika kuposa mamitala 11, kuposa mamitala 5 m’bwambi, ndipo kuposa mamitala 3 mu utali!
“Kodi wawona nyumba izi zazikulu?” Yesu akuyankha motero. “Sudzasiyidwa pano mwala umodzi pamwamba pa unzake, umene sudzagwetsedwa.”
Atanena zimenezi, Yesu ndi ophunzira ake akudutsa Chigwa cha Kidroni ndi kukwera Phiri la Azitona. Kuchokera pamenepa iwo angathe kuwona kachisi wokongolayo. Mateyu 23:25–24:3; Marko 12:41–13:3; Luka 21:1-6; 2 Mbiri 24:20-22.
▪ Kodi Yesu akuchitanji mkati mwa kufika kwake kotsirizira kukachisi?
▪ Kodi ndimotani mmene chinyengo cha alembi ndi Afarisi chikusonyezedwera?
▪ Kodi nchiyani chimene chikutanthauzidwa ndi mawuwo “kulanga kwake kwa Gehena”?
▪ Kodi nchifukwa ninji Yesu akunena kuti mkazi wamasiye anapereka zowonjezereka koposa achuma?